Misondodzi Ilipo Yosiyasiyana
YOLEMBEDWA NDI WOLEMBA GALAMUKANI! KU CZECH REPUBLIC
PALI umodzi wowonda, wowongoka zedi komanso wautali. Wina umakhala ngati wawerama. Koma ngakhale kuti imaima mosiyana chonchi, yonseyi m’pachibale. Kodi tikunena za chiyani? Tikunena za mitundu iwiri ya mitengo ya msondodzi: Msondodzi wotchedwa poplar ndi msondodzi wolira.
Mitengo ya msondodzi imakonda kumera m’mphepete mwa mitsinje ndi makwawa. Kuno ku Czech Republic, imakonda m’madambo, ndipo mmenemu mphukira zake sizichedwa kukula. Misondodzi imatha kutalika mamita 30. Nthawi zina masamba ake amakhala owonda ndipo amangoti yambakata pa tinthambi tamitengoyi. Koma pali mitundu inanso ya misondodzi imene amati misondozi yonyezimira ndi misondodzi ya pusi, yomwe imakhala ndi masamba otakasuka ndithu.
Ngakhale kuti pali mitundu yoposa 350 ya misondodzi, pali mtundu umodzi wochititsa chidwi kwambiri. Mtundu umenewu ndi umene ena amautcha kuti msondodzi wolira. Mtundu winanso wotchedwa kuti msondodzi wa mbuzi, n’ngodziwika chifukwa cha maluwa ake angati ubweya wambuzi, amene amatuluka mtengowu usanamere masamba. Anthu amati timaluwa timeneti tikangotuluka, ndiye kuti nyengo iyamba kusintha.
Pali Mitundu Yosiyanasiyana ya Misondodzi
Mitengo ya misondodzi yotchedwa poplar n’njosasowa ku Bohemia, chigawo chimene kuli mzinda wa Prague, likulu la dziko la Czech Republic. Pali mitundu yosachepera 35 ya misondodziyi. Msondodzi wakuda ndiwo mtundu umene uli wofala kwambiri, ndipo umakonda kupezeka m’mphepete mwa mitsinje ndi m’nkhalango za m’madera achinyezi a ku Bohemia. Mitengo ina ya misondodzi yakudayi imatchedwa Lombardy, kapenanso kuti Italian, ndipo ili ndi thunthu lowonda, ndiponso nthambi zoloza kumwamba zomwe zimamera pafupi ndi mbali ya pakati pa mitengoyi. Mitengo yokongolayi imatha kutalika mamita 35, kufanana ndi nyumba yosanja yokhala ndi nsanja 11. Mitengoyi imapezekanso m’mphepete mwa misewu yambiri, ndipo imakongoletsa madera a kumidzi, makamaka m’nyengo ya chilimwe pamene masamba ake amayamba kuoneka achikasu kwambiri.
Mtundu wina wa misondodzi ya poplar umatchedwa Aspen. Mitengo ya mtunduwu si yaitali kwambiri, ndipo nthambi za kunsonga kwake n’zowonda ndithu. Mtunduwu ulinso ndi chizindikiro china: Kamphepo kakangowomba pang’ono chabe masamba ake amagwedezeka.
Kodi Misondodzi Imatchulidwa M’Baibulo?
Mwina mungaganize kuti misondodzi yotchedwa poplar singapezeke ku dera la kutali kwambiri la kum’mwera kwa dziko lapansi monga ku Middle East. Komatu Baibulo limalongosola kuti Aisiraeli ali ku ukapolo ku Babulo, anapachika azeze awo pa mitengo yamisondodzi. (Salmo 137:2) Kodi n’chifukwa chiyani anatero? Ngakhale kuti zeze chinali chida chogwiritsidwa ntchito potamandira Mulungu, chifukwa cha chisoni, Aisiraeli analibe chikhumbo choimba azeze awo m’nthawi yamavutoyi. (Yesaya 24:8, 9) Mawu a Mulungu amanenanso kuti mtundu umenewu wa msondodzi ndi umodzi mwa mitengo imene nthambi zake zinali zololeka kugwiritsidwa ntchito panthawi imene ankamanga misasa pa Madyerero a Kututa. (Levitiko 23:40) Buku la m’Baibulo la Yobu limalongosola kuti mvuu, yomwe ndi nyama yopanda mantha, imakhala m’mitsinje momwe “misondodzi ya kumtsinje iizinga.”—Yobu 40:21, 22.
Masiku ano, mitundu yosiyanasiyana ya misondodzi imene tatchula m’nkhani ino amaigwiritsira ntchito m’njira zambiri zopindulitsa pa zachuma. Ina amakonda kupangira matabwa a ntchito zosiyanasiyana, makileti, makatoni, ndiponso zinthu zina zosiyanasiyana zapepala. Misondodzi ina n’njofunikiranso kwambiri chifukwa cha ntchito zopindulitsa zimene imachita. Amisiri amapanga mabasiketi pogwiritsa ntchito mphukira za mitengoyi, zomwe sizivuta kupindika. Inde, misondodzi ilipo yosiyanasiyana ndipo imagwira ntchito zosiyanasiyananso.
[Chithunzi patsamba 10]
Msondodzi wolira
[Chithunzi patsamba 10]
Masamba a msondodzi wa Aspen
[Chithunzi patsamba 10]
Msondodzi wotchedwa Lombardy
[Chithunzi patsamba 10]
Msondodzi wa mbuzi
[Chithunzi patsamba 10]
Mtundu wakuda wa misondodzi yotchedwa poplar