Zimene Achinyamata Amadzifunsa
Kodi Ndingatani Kuti Ndizipewa Kupsa Mtima?
Kodi mumapsa mtima pafupipafupi motani?
□ Sindipsa mtima
□ Mwezi uliwonse
□ Mlungu uliwonse
□ Tsiku lililonse
Kodi ndani amakupsetsani mtima nthawi zambiri?
□ Palibe
□ Anzanga akusukulu
□ Makolo
□ Abale anga
□ Ena
Lembani pansipa zinthu zimene zimakupsetsani mtima.
□ ․․․․․
NGATI mwachonga mabokosi akuti “Sindipsa mtima,” “Palibe” ndiponso ngati simunalembe kanthu pa funso lomaliza, ndiye kuti mulibe vuto lopsa mtima.
Komabe, tonsefe tili ndi zinthu zimene sitichita bwino ndipo timapsa mtima ndi zinthu zosiyanasiyana. Wolemba Baibulo, Yakobe, anati: “Tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.” (Yakobe 3:2) Mwina mukapsa mtima mumachita zofanana ndi zimene mtsikana wina wazaka 17, dzina lake Serena, amachita.a Iye anati: “Ndikapsa mtima, ndimalusira aliyense amene angandipute, kaya akhale makolo anga, mlongo wanga kapena galu amene.”
Kudziwa Zoona ndi Zonama
Kodi zimakuvutani kuugwira mtima mukaputidwa? Ngati ndi choncho, dziwani kuti thandizo lilipo. Koma choyamba, tiyeni tione kaye zinthu zonama zimene anthu ena amaganiza.
◼ Zonama: “Sindingathe kuugwira mtima chifukwa tonse kwathu timakonda kupsa mtima.”
Zoona: N’zotheka kuti simuchedwa kupsa mtima chifukwa cha banja limene munabadwira, kumene mumakhala, kapena zinthu zina. Koma, n’zothekanso kuti inuyo mutha kuugwira mtima. (Miyambo 29:22) Funso ndi lakuti, Kodi inuyo mumafuna kuti mkwiyo uzikulamulirani kapena kuti muziulamulira? Anthu ena amene anali ndi vuto lopsa mtima, aphunzira kuugwira mtima.—Akolose 3:8-10.
Lemba Lofunika: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.”—Aefeso 4:31.
◼ Zonama: “Ndikapsa mtima ndiyenera kusonyeza n’cholinga choti aliyense adziwe, m’malo mobisa.”
Zoona: Kusonyeza kapena kubisa mkwiyo, zonsezi zingakhale zosathandiza chifukwa mukhoza kudwala nazo. N’zoona kuti nthawi zina ndi bwino “kudandaula” n’cholinga choti munene maganizo anu. (Yobu 10:1) Komabe zimenezi sizikutanthauza kuti muzikhumudwa ndi chilichonse. N’zotheka kulankhula maganizo anu popanda kusonyeza kuti mwapsa mtima.
Lemba Lofunika: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse, . . . wougwira mtima pokumana ndi zoipa.”—2 Timoteyo 2:24.
◼ Zonama: “Ndikamaugwira mtima anthu azinditola.”
Zoona: Anthu amadziwa kuti kudziletsa si kophweka, choncho angamakulemekezeni ngati mumaugwira mtima.
Lemba Lofunika: “Ngati ndi kotheka, khalani mwa mtendere ndi anthu onse, monga mmene mungathere.”—Aroma 12:18.
Mmene Mungapewere Kupsa Mtima
Ngati simuchedwa kupsa mtima, mwina mumaimba ena mlandu kuti ndiwo amakuchititsani. Mwachitsanzo, kodi munayamba mwanenapo kuti, “Anandiputa dala” kapena “Anandichititsa kuti ndipse mtima”? Ngati munanenapo zimenezi, ndiye kuti inuyo mumalola anthu ena kumalamulira mkwiyo wanu. Kodi mungatani kuti muzipewa kupsa mtima? Yesani izi:
Musamaimbe ena mlandu. Mukapsa mtima, musamathamangire kuimba mlandu ena kuti ndi amene akuchititsani. M’malo monena kuti, “Anandiputa dala,” vomerezani kuti, ‘Ndikanatha kuugwira mtima.’ Ndipo m’malo monena kuti, “Anandichititsa kuti ndipse mtima,” vomerezani kuti, ‘Sinali nkhani yakuti ndingapse nayo mtima.’ Mukavomereza kuti inuyo ndi amene munalolera kuti mupse mtima, mungasinthe mosavuta.—Agalatiya 6:5.
Muziyembekezera kuti ena angathe kukupsetsani mtima. Baibulo limati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Choncho, ndi bwino kuyembekezera kuti anthu ena angachite zinthu zimene zingakupsetseni mtima. Dzifunseni kuti, ‘Kodi n’chiyani chimandichititsa kupsa mtima?’ Mwachitsanzo, mtsikana wina dzina lake Megan anati: “Ndimagwira ntchito usiku ndipo ndikaweruka, ndimakhala wotopa kwambiri. Panthawi imeneyi sindichedwa kupsa mtima.”
Funso: Kodi n’chiyani chimakuchititsani inuyo kupsa mtima?
․․․․․
Muzikonzekera zochita. Wina akachita zinthu zokupsetsani mtima, muzidekha kaye ndipo musamalankhule mokuwa kapena mofulumira kwambiri. M’malo momuimba mlandu munthuyo (“Ndiwe wakuba! Unatenga juzi yanga popanda kupempha.”) ingonenani mmene zochita zakezo zakukhudzirani. (“Sizindisangalatsa ndikafuna kuvala juzi yanga n’kupeza kuti mwaivala popanda kundidziwitsa.”)
Zoti muchite: Ganizirani chinthu chimene chinakupsetsani mtima posachedwapa.
1. Pa zomwe zinachitikazo n’chiyani chinakupsetsani mtima?
․․․․․
2. Nanga inuyo munatani? (Munanena chiyani kapena munachita chiyani?)
․․․․․
3. Kodi mukuganiza kuti zikanakhala bwino mukanachita chiyani?
․․․․․
Ganizirani zotsatira zake. Pali mfundo zingapo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni kuchita zimenezi. Mwachitsanzo:
◼ Lemba la Miyambo 12:18 limati: “Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga.” Mawu amapweteka. Mukapsa mtima, mutha kunena zinthu zimene munganong’oneze nazo bondo pambuyo pake.
◼ Lemba la Miyambo 29:11 limati: ‘Chitsiru chivumbulutsa mkwiyo wake wonse; koma wanzeru auletsa nautontholetsa.’ Mungathe kuoneka wopusa chifukwa choyankhula zinthu mokwiya.
◼ Lemba la Miyambo 14:30 limati: “Mtima wabwino ndi moyo wa thupi.” Mutha kuyamba kudwala chifukwa chopsa mtima. Mtsikana wina dzina lake Anita anati: “Anthu ambiri m’banja mwathu amadwala matenda othamanga magazi, choncho ndimaganizira kaye mofatsa ndisanapse mtima.”
Apa mfundo ndi yakuti muyenera kuganizira zotsatira za zimene munganene kapena kuchita. Mtsikana wina wazaka 18, dzina lake Heather, anati: “Ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi nditamupsera mtima munthu ameneyu chingachitike n’chiyani? Kodi iyeyo andiganizira chiyani? Kodi zimenezi zikhudza bwanji ubwenzi wathu? Kodi ndingamve bwanji ngati munthu wina atandichitira ineyo zimenezi?’” Mungadzifunse mafunso ngati amenewa, musanalankhule kapena musanatumize uthenga wokalipa pafoni kapenanso pa Intaneti.
Funso: Kodi chingachitike n’chiyani ngati winawake wakupsetsani mtima ndiyeno inuyo n’kumutumizira uthenga wosonyeza kuti mwakwiya?
․․․․․
Ena angakuthandizeni. Lemba la Miyambo 27:17 limati: “Chitsulo chinola chitsulo; chomwecho munthu anola nkhope ya mnzake.” Mungachite bwino kupempha makolo anu kapena munthu wina wachikulire kuti akuuzeni zimene amachita ena akachita zinthu zopsetsa mtima.
Onani mmene mukuchitira. Mukhale ndi buku lolembamo mmene mukusinthira. Nthawi zonse mukapsa mtima muzilemba (1) zimene zinachitika, (2) zimene inuyo munachita, ndi (3) zimene mukanachita. M’kupita kwanthawi mudzaona kuti zimene munafunika kuchita ndi zimene mukuchitadi.
Nkhani zina zakuti Zimene Achinyamata Amafunsa, mungazipeze pa adiresi yathu ya pa Intaneti ya www.jw.org.
[Mawu a M’munsi]
a Maina ena m’nkhaniyi asinthidwa.
ZOTI MUGANIZIRE
Ngakhale anthu amene amaoneka kuti sangapse mtima, nthawi zina amapsa mtima mosayembekezereka. Kodi zimenezi zingatiphunzitse chiyani?
◼ Mose.—Numeri 20:1-12; Salmo 106:32, 33.
◼ Paulo ndi Baranaba.—Machitidwe 15:36-40.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 18]
ZIMENE ANZANU AMANENA
“Kulemba m’buku chilichonse chimene chachitika kapena kuuza mayi anga zimene zachitikazo, zimandithandiza kuugwira mtima.”—Alexis, United States.
“Ndikakhumudwa ndimapita kokayenda. Kuchita zimenezi kumandithandiza kuti ndidekhe komanso kuti ndiiganizire bwino nkhaniyo.”—Elizabeth, Ireland.
“Ndimaiganizira nkhaniyo mofatsa ndipo ndimadzifunsa kuti, ‘Kodi chingachitike n’chiyani ngati nditanena zinthu mopsa mtima?’ Mapeto ake ndimaona kuti kupsa mtima n’kosathandiza.”—Graeme, Australia.
[Chithunzi patsamba 18]
KODI MUKUDZIWA?
Ngakhale Mulungu nthawi zina amakwiya. Koma amapsa mtima pazinthu zomveka ndipo sakwiya mopitirira malire.—Onani Eksodo 34:6; Deuteronomo 32:4; ndi Yesaya 48:9.
[Chithunzi patsamba 19]
Inuyo ndi amene muli ndi ufulu wosankha kupsa mtima kapena ayi