Zimene Baibulo Limanena
Kodi N’zotheka Kukonda Adani Athu?
Yesu anati: “Ine ndikukuuzani: Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani; kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wa kumwamba, popeza kuti amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.”—Mateyo 5:44, 45.
KODI mumaona kuti chipembedzo chimalimbikitsa anthu kukondana komanso kukhala mwamtendere, kapena chimalimbikitsa udani ndi chiwawa? Masiku ano anthu ambiri amaona kuti chipembedzo chimalimbikitsa udani ndi chiwawa, makamaka chikamalowerera m’ndale, kulimbikitsa kusankhana mafuko kapena kulimbikitsa anthu kukonda kwambiri dziko lawo. Komabe, monga mmene Yesu ananenera, ‘ana a Mulungu’ amatsanzira chikondi cha Mulungu ndipo amakonda ngakhale adani awo.
Mtumiki wina wa Mulungu anati: “Ngati mdani wako ali ndi njala, m’patse chakudya; ngati ali ndi ludzu, m’patse chakumwa . . . Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.” (Aroma 12:20, 21) Koma kodi n’zothekadi kukonda adani athu masiku ano? Mboni za Yehova zimaona kuti n’zotheka. Ganizirani chitsanzo cha Yesu ndi otsatira ake oyambirira.
Ankakonda Adani Awo
Yesu ankaphunzitsa zinthu zolondola zokhudza Mulungu ndipo anthu ambiri ankamumvetsera mosangalala. Komabe, anthu ena ankamutsutsa, ndipo ena ankachita zimenezi chifukwa cha kusadziwa. (Yohane 7:12, 13; Machitidwe 2:36-38; 3:15, 17) Ngakhale zinali choncho, Yesu anapitirizabe kuuza anthu, kuphatikizapo adani ake, uthenga wopulumutsa moyo. (Maliko 12:13-34) Iye ankachita zimenezi chifukwa ankadziwa kuti ena angasinthe zochita zawo, n’kuvomereza kuti iye ndi Mesiya komanso kuyamba kuchita zinthu mogwirizana ndi choonadi chopezeka m’Mawu a Mulungu.—Yohane 7:1, 37-46; 17:17.
Ngakhale pamene Yesu anagwidwa ndi adani ake, iye anapitirizabe kuwakonda. Ndipotu, iye anachiritsa mmodzi wa anthu amene anamugwirawo, mtumwi Petulo atamudula khutu. Panthawi imeneyi, Yesu ananena mfundo inayake yofunika kwambiri imene otsatira ake amaitsatira mpaka pano. Iye anati: “Onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mateyo 26:48-52; Yohane 18:10, 11) Patapita zaka 30 kuchokera nthawi imeneyi, Petulo analemba kuti: “Khristu anavutika chifukwa cha inu, kukusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamalitsa. . . . Pamene anali kuvutika, sanawopseze, koma anali kudzipereka kwa [Mulungu].” (1 Petulo 2:21, 23) N’zoonekeratu kuti Petulo anaphunzira kuti chikondi, osati kubwezera, n’chofunika kwa Akhristu.—Mateyo 5:9.
Onse amene ‘amatsatira Yesu mosamalitsa’ amakhala anthu achikondi komanso okoma mtima ngati Yesu. Lemba la 2 Timoteyo 2:24 limati: “Kapolo wa Ambuye sayenera kukangana ndi anthu, koma ayenera kukhala wodekha kwa onse. . . . wougwira mtima pokumana ndi zoipa.” Mkhristu aliyense amafunika kusonyeza makhalidwe amenewa pamoyo wake ndipo ayenera kudziwika kuti ndi wokonda mtendere komanso wokhululukira.
‘Akazembe a Khristu’ Amakonda Mtendere
Mtumwi Paulo anauza okhulupirira anzake kuti: “Ndife akazembe m’malo mwa Khristu . . . Monga okhala m’malo mwa Khristu tikupempha kuti: ‘Yanjananinso ndi Mulungu.’” (2 Akorinto 5:20) Akazembe salowerera ndale komanso nkhondo za m’mayiko amene atumidwa kukagwira ntchito. Ntchito yawo ndi kuimira dziko lawo ndiponso kunena zabwino zokhudza dziko lawolo.
N’chimodzimodzinso ndi akazembe ndiponso nthumwi zoimira Khristu. Iwo amaona kuti Yesu ndi Mfumu ndipo amanena zabwino zokhudza Ufumu wake wakumwamba mwa kulengeza mwamtendere uthenga wabwino. (Mateyo 24:14; Yohane 18:36) Paulo analembera Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Sitikumenya nkhondo monga mwa thupi. Pakuti zida za nkhondo yathu si zili za kuthupi, koma zili zamphamvu mwa Mulungu zogwetsa nazo . . . malingaliro komanso chokwezeka chilichonse chotsutsana ndi kudziwa kwathu Mulungu.”—2 Akorinto 10:3-5; Aefeso 6:13-20.
Panthawi imene Paulo amalemba zimenezi, n’kuti m’madera ambiri Akhristu akuzunzidwa. Iwo akanatha kubwezera, koma m’malomwake anapitirizabe kukonda adani awo ndiponso kulengeza uthenga wamtendere kwa anthu achidwi. Buku lina linati: “Otsatira oyambirira a Yesu ankakana kulowa usilikali kapena kupita kunkhondo.” Iwo ankaona kuti zimenezi “n’zosagwirizana ndi chikondi chimene Yesu ankaphunzitsa ndiponso lamulo lakuti azikonda adani awo.”a—Encyclopedia of Religion and War.
Mofanana ndi Akhristu oyambirira, Mboni za Yehova zimaona kuti Yesu Khristu ndiye Mfumu yawo. Iwo amaonanso kuti iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ufumu umenewu ndi boma lakumwamba limene posachedwapa lidzabweretsa mtendere ndi chitetezo padziko lapansi. (Danieli 2:44; Mateyo 6:9, 10) Choncho, monga akazembe komanso nthumwi, iwo amalengeza zinthu zabwino zokhudza Ufumuwo. Komanso amayesetsa kukhala anthu abwino m’dziko limene akukhala. Amakhoma msonkho ndiponso amamvera malamulo amene satsutsana ndi malamulo a Mulungu.—Machitidwe 5:29; Aroma 13:1, 7.
Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti mofanana ndi mmene zinalili ndi Akhristu oyambirira, Mboni za Yehova zimadedwa, kunyozedwa, komanso kuzunzidwa. Koma iwo sabwezera. M’malomwake amayesetsa ‘kukhala mwamtendere ndi anthu onse,’ ndipo amayembekezera kuti otsutsa ena ‘angayanjanitsidwe kwa Mulungu’ n’kudzakhala ndi moyo wosatha.b—Aroma 12:18; Yohane 17:3.
[Mawu a M’munsi]
a Bukuli linanenso kuti: “Anthu onse olemba mbiri yokhudza Chikhristu amene anakhala ndi moyo Constantine asanayambe kulamulira ufumu wa Roma [306-337 C.E.] ankadana ndi nkhondo.” Koma zinthu zinasintha anthu ampatuko atachuluka, monga mmene Baibulo linaloserera.—Machitidwe 20:29, 30; 1 Timoteyo 4:1.
b Monga mmene Akhristu oyambirira ankachitira, Mboni za Yehova zikaphwanyiridwa ufulu wawo wachipembedzo zimatha kupita kukhoti pakafunika kutero.—Machitidwe 25:11; Afilipi 1:7.
KODI MWAGANIZIRAPO IZI?
◼ Kodi Akhristu ayenera kuwachitira chiyani adani awo?—Mateyo 5:43-45; Aroma 12:20, 21.
◼ Kodi Yesu anatani adani ake akumuzunza?—1 Petulo 2:21, 23.
◼ Kodi n’chifukwa chiyani Akhristu oyambirira sankamenya nkhondo?—2 Akorinto 5:20; 10:3-5.