Mutu 6
Yesu Kristu, kupyolera mwa Amene Mulungu Adzawadalitsa Anthu
1. Kodi ndi ciani cimene ciri coyenera kotheratu kuti ife ticikhulupirire ngati tifuna kuwalandira madalitso a moyo wamuyaya?
NDI acikondi cotani nanga mmene akhalira makonzedwe amene Yehova wawapanga kupyolera mwa Mwana wace kaamba ka kuwadalitsa anthu a mitundu yonse ndi mafuko! Iye walonjeza za cimasuko ku citsenderezo, ucimo ndi imfa. Ha, ndi ciyembekezo caulemerero cotani nanga? Komabe, kuli kofunika kwa ife kuzindikira kuti madalitso amenewa adzadza kwa mtundu wa anthu kokha kupyolera mwa Yesu Kristu. Pa cifukwa ca ici, Mulungu anamuuzira mtumwi Petro kunena za Yesu kuti: “Palibe cipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.” (Macitidwe 4:12) Mwa kucipeza cidziwitso colongosoka ca makonzedwe amenewa ndi mwa kumasonyeza cikhulupiriro mu zifuno za Mulungu mogwirizana ndi Kristuyo, inu mungadziike inu mwini mu mzera woyenerera kulandira madalitso akurukuru a moyo wamuyaya.
2. (a) Kodi ndi lonjezo lotani la dalitso limene Mulungu analipanga kwa Abrahamu, ndipo kodi ndani amene anali “mbeu” yaceyo? (b) Kodi ndi kwa ndani kumene unsembe ndi nsembe zimene zinacitidwa motsogozedwa ndi cilamulo Caumose zinasonyako? (c) Kodi ndi motani mmene Baibulo limasonyezera za amene adzakhala mfumu ya mu ufumu wa Mulungu?
2 Kwa zaka zikwi zambiri amuna a cikhulupiriro ayembekezera kukuona kukwaniritsidwa kwa ciyembekezo ici, ndipo malonjezo a Mulungu anawapatsa iwo cifukwa cabwino ca kucitira conco. Kwa mutu wa banja Wacihebri Abrahamu, Yehova analipanga lonjezo lakuti “mitundu yonse ya dziko lapansi” idzadalitsidwa kupyolera mwa “mbeu” yace. “Mbeu” imeneyo inatsimikizira kwakukurukuru kukhala Yesu Kristu. (Genesis 22:18; Agalatiya 3:14-16, 28, 29) Mulungu anauperekanso unsembe ndi nsembe m’Cilamulo coperekedwa kwa Israyeli. Izinso zinasonya mtsogolo kwa Yesu. Izo zinali kupereka cisamaliro kwa iye monga Mkuru Wansembe wapamwambamwamba ndi ku nsembe ya moyo wa iye mwini waumunthu monga njira yocotsera macimo kosatha ndi kudzetsa cilanditso kucokera ku imfa. (Agalatiya 3:24; Ahebri 9:11, 12; Yohane 1:29) Kuonjezerapo, Yehova ananeneratu kuti uyo kupyolera mwa amene mtendere wamuyaya udzadzera kwa mtundu wa anthu adzakhala wa m’banja la mfumu Davide ndipo adzakhala mfumu ya ufumu wa Mulungu, kumalamulira pa dziko lonse lapansi. Mngeloyo Gabrieli, pamene anali kumakulengeza kubadwa kwaumunthu kwa Yesu, anati: “Iye adzakhala wamkuru, nadzachedwa mwana wa Wamkurukuru: ndipo Ambuye Mulungu adzampatsa mpando wacifumu wa Davide atate wace.” (Luka 1:32; onaninso Yesaya 9:6, 7; Danieli 7:13, 14.) Inde, Mau onse a Mulungu amanena za Yesu Kristu monga kukhala uyo kupyolera mwa amene Yehova Mulungu adzaperekera madalitso a moyo wamuyaya kwa mtundu wa anthu.—Luka 2:25-32; Afilipi 2:9-11.
KUKHALAPO KWACE ASANAKHALE MUNTHU
3. (a) Kodi ndi motani mmene kwakhalira kuti Yesu ali Mwana “woyamba kubadwa” wa Mulungu? (b) Ncifukwa ninji Baibulo limanena kuti Yesu ali Mwana “wobadwa yekha” wa Mulungu?
3 Kodi munayamba mwadziwa kuti Yesu anali atakhalapo kale mwaulemerero iye asanabadwe monga munthu pano pa dziko lapansi? Baibulo limatilangiza ife kuti iye ali Mwana “woyamba” wa Mulungu. Ici cimatanthauza kuti iye analengedwa asanalengedwe ana ena onse a m’banja la Mulungu. Iyenso ali Mwana “wobadwa yekha” wa Mulungu, cifukwa cakuti ali yekhayo amene analengedwa mwacindunji ndi Yehova Mulungu; zinthu zina zonse zinayamba kukhalapo kupyolera mwa iye monga Woimira Wamkuru wa Mulungu. Motero, iye asanabadwe pa dziko lapansi monga mwana wamwamuna iye anali atatumikira kale kumwamba, kumene iye anadziwikako kukhala “Mau,” womlankhulira Mulungu.—Yohane 1:3, 10, 14; Akolose 1:15-17.
4. Kodi nciani cimene Yesu ananena kupereka umboni wa ceniceni cakuti iye anali atakhalako m’mwamba asanadze pa dziko lapansi?
4 Cifukwa ca cimeneco Yesu akadanena moyenerera kuti: “Asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndiripo,” ndipo “Mkate wamoyo wotsika Kumwamba Ndine amene.” (Yohane 8:58; 6:51) Pomanena za malo okwezeka amene anali nao kumwamba, iye anapemphera kuti: “Atate Inu, lemekezani Ine ndi Inu nokha ndi ulemerero umene ndinali nao ndi Inu lisanakhale dziko lapansi.”—Yohane 17:5.
MOYO WACE PA DZIKO LAPANSI
5. (a) Pamene nthawi ya Mulungu inakwana yakuti Mwana wace afikire kukhala munthu pa dziko lapansi, kodi ndi motani mmene Mulungu anacitheketsera cimeneci? (b) Kodi ndi motani mmene mwanayo Yesu anabadwira wopanda ucimo wa Adamu?
5 Mogwirizana ndi cifuno ca Mulungu ca kuwadalitsa amuna a cikhulupiriro, nthawi yokwanira inadza yakuti Mwana wakuwamba ameneyu afikire kukhala munthu pa dziko lapansi. Ici cinafunikira cozizwitsa ca Mulungu. Yehova, mwa mzimu wace woyera kapena mwa mphamvu yogwira nchito, anausamutsa moyo wa Yesu kucokera kumwamba kulowa m’mimba ya namwali wosakhudzidwa Waciyuda wochedwa Mariya. Pomalengezeratu za ici kwa Mariya pasadakhale, mngelo Gabrieli anati; “Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkurukuru idzakuphimba iwe: cifukwa cacenso Coyeraco cikadzabadwa, cidzachedwa mwana wa Mulungu.” (Luka 1:35) Mlengiyo anali ndi mphamvu yokhoza kucicititsa ici. Ndithudi Uyo amene anampanga mkazi woyambayo ndi kukhoza kwa kuwabala ana akanatha kumcititsa mkazi kukhala ndi mimba popanda atate waumunthu, Mulungu mwiniyo kumakhala wouyambitsa moyo wa mwanayo. Mwana uyu, Yesu, sanali Mulungu, koma Mwana wa Mulungu. Iye anali munthu wangwiro, wopanda ucimo wa Adamu. Kodi ndi motani mmene cimeneco cinakhalira cothekera? Cifukwa cakuti, monga momwe mngeloyo ananenera, “mphamvu ya Wamkurukuru” ndiyo imene inacititsa; iyo inakatsogolera kakulidwe kace pamene anali m’mimba mwa Mariya.
6. (a) Monga momwe kunanenedweratu mu ulosi kodi ndi kuti kumene Yesu anabadwirako? (b) Kodi ncifukwa ninji Yesu anabatizidwa?
6 Monga momwe kunanenedweratu zaka mazana ambiri zapitazo, Yesu anabadwira mu mzinda wa Mfumu Davide, Betelehemu wa Yudeya. (Mika 5:2) Iye anakhalira limodzi ndi mai wace ndi bambo wace wongomlerayo Yosefe, akumagwira nchito yopala matabwa kufikira anaufikira usinkhu wa zaka makumi atatu. Pamenepo nthawi ya Mulungu inakwana yakuti iye acite nchito yina. Cotero iye anapita kwa Yohane Mbatizi kukabatizidwa kapena kukamizidwa kotheratu m’madzi a mu Mtsinje wa Yordano. Ici cinasonyeza kuti iye anali kudzipereka iye mwini kwa Mulungu kuti aichite nchito imene Mulungu anamtuma kudza ku dziko lapansi kudzaicita. Mwa kumadzipereka kuti abatizidwe Yesu anakhazikitsa citsanzo kwa onse amene akhulupirira mwa iye, ndipo pambuyo pace iye analamulira kuti onse amene anafikira kukhala akuphunzira ace anayenera kubatizidwa.—Mateyu 28:19, 20.
7. Kodi nciani cimene Mulungu anacita pa nthawi imene Yesu anabatizidwa?
7 Komabe, kanthu kena kanamcitikira Yesu pa Yordano. Miyamba intseguka, mzimu wa Mulungu unatera pa iye, ndipo Mulungu mwiniyo analankhula ali kumwamba, kumati: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:16, 17) Panalibe colakwika pa ici; uyuyo anali amene aneneri onse a Mulungu anali ataneneratu za iye! Kumeneko pa Yordanopo, mwa njira ya mzimu woyera, Yesu anadzozedwa ndi Mulungu kuti akhale mkuru wansembe wonenedweratuyo, mfumu ya ufumu wa Mulungu, ndi kulalikira pamene anali pano pa dziko lapansi. (Luka 4:16-21) Panali nchito yakuti iyeyo aicite.
8. Kodi Yesu anakaikira pa kugwiritsira nchito dzina laumwini la Mulungu kapena pa kulankhula coonadi? Cotero nanga ndi ciani cimene tiyenera kucita?
8 Kwa zaka zitatu ndi theka iye analalikira Mau a Mulungu m’dziko lonselo, ndipo anawaphunzitsa ophunzira acewo kuti acite cimodzimodzi. (Luka 8:1) Ngakhale kunali kwakuti ena m’masiku amene aja anali kuopa mwamwambo kulichula dzina la Mulungu, Yesu sanakaikire za kulidziwikitsa ilo. (Yohane 17:26) Iye nthawi zonse analankhula coonadi, kaya ngati anthu anacikonda kapena sanacikonde. Mu zimene anazicita iye anapereka citsanzo cimene ife tiyenera kucitsatira ngati tifuna kukondweretsa Mulungu. Komanso iye anacita zambiri koposa zimenezo.
CIMASUKO KU UCIMO NDI IMFA
9. (a) Malinga ndi kunena kwa Mateyu 20:28, kodi Yesu anadza pa dziko lapansi kaamba ka cifukwa cina cotani? (b) Kodi mtengo wa dipo umene Yesu anaupereka kutimasula ife ku ucimo ndi imfa ndi wotani?
9 Yesu anadziwa kuti kudza kwace ku dziko lapansi monga munthu kunali mbali yacindunji ya makonzedwe a Mulungu a kuumasulira mtundu wa anthu kucokera ku ucimo ndi imfa. Cotero iye anati: “Mwana wa munthu anadza . . . kudzapereka moyo wace dipo losinthanitsa ndi ambiri.” (Mateyu 20:28, NW) Kodi kwenikweni cimeneco cimatanthauzanji? Eya, dipo ndilo mtengo umene umaperekedwa kuti papezeke cilanditso kucokera ku undende. Mu nkhani iyi, moyo wangwiro wa Yesu waumunthu umene unaperekedwa mu nsembe ndiwo umene unali mtengo umene unaperekedwa kuti pakhale cimasuko ca mtundu wa anthu kucokera ku ukapolo wa ucimo ndi imfa. (1 Petro 1:18, 19) Ncifukwa ninji cimasuko ca mtundu woterowo cinali cofunika?
10.Kodi ncifukwa ninji tinayenera kulandira kucokera kwa Adamu colowa ca ucimo ndi imfa cokha?
10 Ici cinali cifukwa cakuti Adamu, kholo lathu la ife tonse, linacimwira Mulungu. Motero, Adamu anafikira kukhala wopanda ungwiro ndipo anakutaya kuyenera kwa kukhala ndi moyo. Monga woliswa mwadala lamulo la Mulungu, iye analowa mu cilango cace ca imfa. Mulungu analinso atakhazikitsa malamulo a cibadwa, amene amatsimikizira kuti ife tonse timalandira mikhalidwe yathu yakuthupi ndi zinthu zina kucokera kwa makolo athu. Mogiwirizana ndi malamulo amenewa, Adamu anali kupitirizira kwa mbadwa zace zokha zija zimene iye mwiniyo anali nazo; cotero tinalandira kucokera kwa iyeyo colowa ca ucimo ndi imfa. (Aroma 5:12) Cifukwa ca cimeneco mtundu wonse wa anthu wakhala ukumafa mwa kumacilipira cilangoco ca ucimo. Kodi ndi motani mmene cilango ca imfa cimeneci cikadacotsedwera ndipo zofunika za cilungamo ndi kuperekedwabe?
11.Pakumapereka cimasuko kwa mbadwa za Adamu, kodi ndi motani mmene Mulungu anasonyezera kalingaliridwe koyenera ka lamulo?
11 Mulungu sanawalekerere ndi kulolera molakwa pa malamulo ace. Kutero kukanangokulimbikitsa kusamvera koonjezereka mwa citsanzo coipa. Komabe iye sanaufulatire mtundu wa anthu ndi kuusiya uwo kukhala wopanda ciyembekezo. Pamene iye anali kumamatira ku malamulo ace, Mulungu mwacikondi anapereka cimasuko, osati kwa wocimwa mwadalayo Adamu, koma kwa mbadwa za Adamuzo, zimene, mopanda kucicita cosankha ciriconse mu nkhaniyo, zinasauka nazo zotsatirapo zace za kucimwa kwaceko. Mulungu anacicita ici mogwirizana ndi prinsipulo lobvomerezeka monga lamulo limene pambuyo pace analilowetsa mu cilamulo Caumose, lakuti, “moyo kulipa moyo,” (Deuteronomo 19:21) Tiyeni tione mmene prinsipulo limenelo linagwirira nchito mu dipo limene linaperekedwa kupyolera mwa Yesulo.
12. Kodi ndani yekha amene akanapereka mtengo wa dipo la cimene Adamu anatayaco? Cotero ncifukwa ninji Yesu anafunikira kubadwa monga munthu?
12 ‘Munthu wamoyoyo’ Adamu, amene anautayira mtundu wa anthu moyo, anali munthu wangwiro. Mosinthanitsa ndi cimene iye anacitayaco, moyo wina waumunthu, wofanana ndi wa Adamuyo, unafunika, munthu amene akaupereka moyo wa iye mwini wangwiro monga nsembe kaamba ka mtundu wa anthu. (1 Akorinto 15:45) Palibe mbadwa iriyonse ya Adamu imene inali yoyeneretsedwa kucicita ici, cifukwa cakuti onse anabadwa ali opanda ungwiro. Mwa cotsatirapo ca ici onse amafa cifukwa cakuti iwo ali ocimwa, ndipo alibe kuyenera kwa moyo waumunthu umene angaupereke nsembe kaamba ka ubwino wa ena. (Salmo 49:7 [48:8, Dy]) Cotero Mulungu anatumiza Mwana wace ku dziko lapansi. Yesu anabadwa monga munthu, cifukwa cakuti unali moyo waumunthu umene unali kufunikawo. Koma iye anabadwa popanda cithandizo ca atate waumunthu, kotero kuti iye akhale wangwiro monga momwe anakhalira Adamu. Mulungu mwiniyo ndiye amene anali Atate wa Yesu waumunthuyo, monganso momwe anakhalira Atate wa Adamu. (Luka 3:38) Motero Yesu anali woyeneretsedwa mokwanira kuti apereke moyo wace kukhala “dipo lolinganira.”—1 Timoteo 2:6, NW; Aefeso 1:7.
13.Ncifukwa ninji Yesu mofunitsitsa anaupereka moyo wace osalimbalimba?
13 Pa Nisani 14 wa mu caka ca 33 C.E. adani ace a Yesu anamupha iye pa mtengo wozunzirapo. Iye akanalimbalimba, koma sanatero. (Mateyu 26:53, 54) Iye mofunitsitsa anaupereka moyo wace kuti ukhale nsembe yathu. Monga momwe mtumwi wace Petro amatiuzira ife: “Anasenza macimo athu mwini yekha m’thupi mwace pa mtanda, kuti ife, titafa ku macimo, tikakhale ndi moyo kutsata cilungamo; ameneyo mikwingwirima yace munciritsidwa nayo.”—1 Petro 2:24; onaninso Ahebri 2:9.
14. Kodi nciani cimene Baibulo pa Yohane 3:16 limatiuza ife ponena za cikondi ca Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu? Cotero kodi ndi motani mmene ife tinayenera kucitira?
14 Cimeneco ndithudi cinali cisonyezero cozizwitsa ca cikondi ca Mulungu kaamba ka mtundu wa anthu! Baibulo limatithandiza ife kucizindikira ici, kumati: “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wace wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nao moyo wosatha.” (Yohane 3:16) Ngati muli kholo limene liri ndi mwana wamwamuna amene mumamkonda kwambiri, mosakaikira inu mungazindikire, pa mlingo wakuti-wakuti, cimene cimeneco cinatanthauza kwa Mulungu. Ciyenera kuitenthetsa mitima yathu kulinga kwa iye kuzindikira kuti iye amatisamalira ife kwambirimbiri.—1 Yohane 4:9-11.
15. (a) Kodi Yesu anaukitsidwa ali ndi thupi laumunthu? (b) Iye ataukitsidwa, kodi ncifukwa ninji Yesu anaonekera kwa phunzira ace? (c) Kodi kunali koyenera kwa Yesu kubwerera kumwamba? Ncifukwa ninji?
15 Yehova Mulungu sanamsiye Mwana waceyo ali wakufa m’manda, koma anamdzutsira iye ku moyo pa tsiku lacitatu. Iye sanapatsidwenso moyo waumunthu, cifukwa cakuti cimeneco cikanatanthauza kuti iye anali kuutenganso mtengo wa dipo uja. Koma iye “wopatsidwa moyo mumzimu.” (1 Petro 3:18) Mkati mwa nyengo ya masiku makumi anai kuyambira pa ciukiliro cace iye anaonekera kwa ophunzira ace kwa nthawi zingapo, atabvala thupi laumunthu, kutsimikizira kuti iye anaukitsidwadi kwa akufa. Pamenepo, akuphunzirawo akumayang’anitsitsa, iye anakwera kumwamba ndipo anabisidwa ndi mtambo. Iye anabwereranso kumwamba, kumeneko “kuonekera tsopano pamaso pa Mulungu cifukwa ca ife” akumautenga mtengo wa nsembe yace ya dipoyo monga mkuru wansembe wapamwambamwamba. (Ahebri 9:12, 24) Zofunika za cilungamo caumulungu zinali zitakwaniritsidwa; cimasuko tsopano cinalipo kaamba ka mtundu wa anthu.
16. (a) Talongosolani za mmene timapindulira ngakhale tsopano kucokera ku makonzedwe a dipowo. b) Pamene tikulingalira za mtsogolo, kodi nciani cimene dipolo limacipangitsa kukhala cothekera kwa ife ndi kwa akufa?
16 Ngakhale tsopano tingapindule nalo kwakukurukuru dipolo. Mwa kumasonyeza cikhulupiriro mwa ilo ife tingasangalale ndi kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu ndi kukhala mu cisamaliro cace cacikondi. (Cibvumbulutso 7:9, 10, 13-15) Pamene, cifukwa ca kupanda ungwiro ticita cimo, ife mwaufulu tingafunefune cikhululukiro kucokera kwa Mulungu pamaziko a dipolo, mwa citsimikiziro cakuti adzatimva ife. (1 Yohane 2:1, 2) Kuonjezerapo, dipolo latsegula njira ya cisungiko kuwapyola mapeto a dongosolo loipa ili la zinthu. Limacipangitsa kukhala cothekera ciukiliro ca akufa. Ndipo limapereka maziko a kupezera moyo wamuyaya mu dongosolo latsopano la Mulungu la zinthu, kumene lidzagwiritsiridwa nchito pa mtundu wa anthu m’malo mwa kucotsa ziyambukiro zonse za ucimo wa colowa.—1 Akorinto 15:25, 26; Cibvumbulutso 7:17.
WOLAMULIRA WA UFUMU WA MULUNGU
17. (a) Kodi ndi ciani cimene Yesu nthawi zonse anli kucichula, akumacipanga ico kukhala mutu wa kulalikira kwaceko? (b) Kodi nciani cimene Yesu anacisonyeza mwa zozizwitsa zace za kuciritsa ndi kuukitsa akufa?
17 Mkati mwa utumiki wace wa pa dziko lapansi Yesu mosasintha anali kumanena za ufumu wa Mulungu. Iye anawaphunzitsa atsatiri ace kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kucitidwe, monga kumwamba comweco pansi pano.” Ndipo anawalimbikitsa iwo kuti “muthange mwafuna Ufumu wace.” (Mateyu 6:10, 33) ambiri a mafanizo ace anali kunena za Ufumuwo. Iye anaupanga uwo kukhala mutu wa kulalikira kwace. (Mateyu 9:35) Mwa zozizwitsa zace za kuciritsa ndi kuukitsa akufa, iye anasonyeza pa mlingo waung’ono cimene cidzacitika pa dziko lapansi mu ufumu wa Mulungu. Pa nthawi imeneyo kudwala kudzakhala kutatha, maso akhungu adzaona, makutu ogontha adzatseguka, ndipo miyendo ndi mikono yopuwala idzaciritsidwa. Ha, ndi dalitso lotani nanga mmene limenelo lidzakhalira!—Cibvumbulutso 21:3, 4.
18 (a) Kodi Yesu anagwiritsira nchito mphamvu yace yacifumuyo iye atangobwerera kumwambako? Ncifukwa ninji? (b) Malinga ndi kunena kwa Mateyu 25:31, 32, kodi nciani cimene Yesu ananena kuti adzacicita iye atabwereranso ndi mphamvu ya Ufumuwo?
18 Yesu iye mwiniyo ndiye amene anadzozedwa ndi Mulungu kuti akhale wolamulira wa Ufumuwo. Komabe, pamene Yesu anabwerera kumwamba iyo sinali nthawi yokwanira kuti iye aigwiritsire nchito mphamvu yaufumu imeneyo. Iye ayenera kuiyembekezera nthawi yokhazikitsidwa ndi Atate wace. (Macitidwe 2:34-36) Komabe, iye ananena za mtsogolo ku nthawi imene iye adzabwereranso ali ndi mphamvu ya Ufumuwo, akumati: “Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wace, ndi angelo onse pamodzi naye, pomwepo Iye adzakhala pa cimpando ca kuwala kwace: ndipo adzasonkhanidwa pamaso pace anthu a mitundu yonse; ndipo Iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzace, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” (Mateyu 25:31, 32) Ife tsopano tikukhala mu nthawi imeneyo ya kulekanitsa. Posacedwapa Kristu pa mpando wace wacifumu wakumwambawo adzagwiritsira ntchito mphamvu yace yacifumuyo kuti awaononge oipa ndi kuwamasula onga nkhosa amene adzakhala pa malo a pa dziko lapansi a Ufumuwo.—Mateyu 25:34, 41, 46.
19. Kuti tisangalale ndi madalitso kupyolera mwa Yesu Kristu, kodi tiyenera kucitanji?
19 Mwanjira ya Yesu Kristu madalitso ali opezeka kwa mtundu wonse wa anthu, koma tiyenera kukhulupirira mwa iye m’malo mwakuti tiwalandire iwo. (Yohane 3:36) ife tiyenera kufikira kukhala ophunzira ace ndi kudzipereka ife eni kwa iye monga mfumu yathu yakumwamba. Kodi inu mudzacita cimeneco? Pali otsutsa amene amafuna kukutsekerezani inu, koma ngati muika cidaliro canu kotheratu mwa Yehova inu mosalephera mudzalandira madalitso amene Mulungu wawasungira awo amene amamkonda iye.—Salmo 62:7, 8 [61:8, 9, Dy].