Mutu 16
Dziko Lapansi Lopanda Matenda ndi Imfa
HA, DZIKO lapansi lopanda matenda ndi imfa kosatha lidzatanthauza mpumulo waukulu chotani nanga kwa anthufe! Lidzathetsa misozi ya kuwawidwa mtima yokhetsedwa mosonyeza chisoni ndi kubvutika. Umene udzakhala utachoka udzakhala ululu waukulu kopambana ndi zirema zoopsya zimene matenda angadzetse. Zoononga za ukalamba sizidzafooketsa’nso anthu, kawiri-kawiri zikumalowetsa mkhalidwe wotaya mtima mopanda chiyembekezo ndi kupanda chithandizo. Anthu kuli konse adzakhala akusangalala ndi nyonga ndi mphamvu zaunyamata. Mau a kulira maliro sadzatuluka ndi amodzi omwe pa miromo yao!
Zimene’zi sizinazikidwe pa kuyerekezera kopanda maziko. Ndizo zimene Yehova Mulungu waliganiza. Iye akulingalira zochuluka kwambiri kaamba ka mtundu wa anthu koposa zaka zowerengeka chabe za moyo wodzazidwa ndi mabvuto ndi kubvutika.—Chibvumbulutso 21:3, 4.
KODI LINGACHITITSE MABVUTO AKULU KWAMBIRI?
Kodi dziko lapansi lopanda matenda ndi imfa lidzachititsa mabvuto ena akulu kwambiri? Kodi mukudabwa kuti: Kodi anthu onse’wo adzakhala kuti? Kodi kutha kwa matenda ndi imfa sikudzachititsa mikhalidwe yopanikizana, ikumapangitsa moyo kukhala wosokondweretsa, ndi kuchititsa kuperewera kwa zakudya kwakukulu?
Sichinali chifuniro cha Mulungu kudzaza anthu motayikira dziko lapansi. Kwa Adamu ndi Hava angwiro’wo, Mulungu anati: “Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.” (Genesis 1:28) Pali kusiyana pakati pa ‘kudzaza’ dziko lapansi ndi kulidzaza motayikira. Ngati wina anakupemphani kudzaza madzi a zipatso m’tambula, simukanamangothirabe mpaka tambula’yo itatayikira. Pamene tambula’yo inadzaza mokwanira, inu mukanaleka kuthira. Momwemo’nso, pamene dziko lapansi likanadzaza bwino lomwe ndi mtundu wa anthu, Mulungu akanachititsa kuti kuonjezeka kwina kwa chiwerengero cha anthu kulekeke pa pulaneti lino.
Ndipo’nso, sitiyenera chifukwa cha zimene tikuona kapena kumva lero lino, kulingalira molakwa kukhoza kwa dziko lapansi kupereka malo okhala kwa ife ndi kuchirikiza moyo wa anthu ndi wa zinyama. Pamene kuli kwakuti anthu ochuluka kwambiri akuunjikana m’mizinda, zigawo zazikulu kwambiri za dziko lapansi zakhalidwe ndi anthu moponyana-ponyana. Ngati chiwerengero cha anthu chiripo’chi chikanagawiridwa molinganira, pakanakhala pafupi-fupi maekala asanu ndi limodzi a nthaka yachonde kwa mwamuna, mkazi ndi mwana ali yense. Amene’wa akanakhala malo akulu kopambana’di!
Njala imene anthu ambiri-mbiri ayenera kuipirira m’mbali zosiyana-siyana za dziko lapansi siri chifukwa chakuti kukhoza konse kwa nthaka kutulutsa zakudya kwafikiridwa. M’malo mwake, kufala kwa kuperewera kwa zakudya kumachokera kwakukulu-kulu m’kugawiridwa kosalinganira kwa zakudya. Pamene kuli kwakuti chochuluka chikutulutsidwa m’madera ena ndipo pamakhala chotsala, m’malo ena muli kuperewera kwakukulu kwambiri. Kweni-kweni, dziko lapansi likatha kutulutsa zochuluka kwambiri koposa m’mene likuchitira pa tsopano lino. Kale’lo mu 1970 Gulu la Chakudya ndi Malimidwe la Mitundu Yogwirizana linayerekezera kuthekera kwa malimidwe kwa dziko lapansi kukhala kwakukulu mokwanira kudyetsa anthu ochuluka kuwirikiza nthawi makumi anai mphambu ziwiri chiwerengero cha anthu cha dziko lapansi chiripo’chi.
Zimene munthu wachita kale m’madera ena a dziko lapansi zimapereka chisonyezero china cha kuthekera kwakukulu kumene kulipo koonjezerera kutulutsa dzinthu kwa dziko lapansi.
Imperial Valley of California pa nthawi ina anali chidalala chopanda kanthu chosalimidwa. Koma kuthiriridwa kwa nthaka yachidala yochuluka michere kwachititsa chigwa chimene’chi kukhala chimodzi cha zigawo za malimidwe za chonde kopambana mu United States.
Pokhala ndi theka la malo ochitirapo ulimi, Yuropu, kupyolera mwa kulima kwamphamvu, amatulutsa chakudya chochuluka pafupi-fupi chofanana ndi cha ku North America.
Ndithudi sipangakhale chikaikiro chakuti malo ambiri angathe kupangidwa kukhala olimidwa kwambiri, ndipo kumene’ko popanda kuononga kukongola kwa nkhalango ndi madambo a udzu.
Pali chinthu china’nso chimene chidzatsimikiziritsa chakudya chokwanira kaamba ka dziko lapansi lodzazidwa bwino lomwe ndi zinyama ndi anthu. Kodi chimene’cho nchiani? Ndicho chithandizo ndi chitsogozo cha Mulungu chimene pa nthawi imene’yo chidzaperekedwa kwa mtundu wa anthu pansi pa kulamulira kwa ufumu wa Mulungu wokhala m’manja mwa Mwana wake Yesu Kristu. Palibe munthu ali yense amene akudziwa dziko lapansi bwino kwambiri koposa m’mene amadziwira Mulungu, pakuti iye ndiye Mlengi wake. Ndipo pansi pa kulamulira kwanzeru kwa ufumu wake nthaka idzabala zochuluka kwambiri. Monga momwe zinachitikira kwa Israyeli wakale pamene anali wokhulupirika, zidzakhala choncho pa nthawi imene’yo: “Dziko lapansi lapereka zipatso zake: Mulungu, Mulungu wathu adzatidalitsa.”—Salmo 67:6.
Zipululu za mchenga zopanda madzi ndi madera ena osabala kanthu, otenga maekaka mamiliyoni ochuluka, mosakaikira adzasandutsidwa pa mlingo waukulu kukhala malo olima. Kulandira chithandizo cha Mulungu m’kupeza madzi ofunika sikuli kopanda chofanana nacho cha mu mbiri. Kale-kale m’zaka za zana lachisanu ndi chimodzi B.C.E., m’kukwaniritsidwa kwa malonjezo olosera za Mulungu, zikwi zambiri za Ayuda okhala mu ukapolo zinabwerera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo. (Ezara 2:64-70) Iwo mwachionekere anayenda njira yolunjika kudzera m’chipululu cha mchenga chopanda kanthu cha Asuri. Komabe Mulungu anapereka zimene iwo anafunikira kuti apitirizebe kukhala ndi moyo. Ngakhale ponena za dziko la kwao iye anali ataneneratu kuti: “M’chipululu madzi adzatuluka, ndi mitsinje m’dziko loti se.”—Yesaya 35:6.
Popeza kuti Mulungu anachita chimene’chi m’nthawi yakale, tiri ndi chifukwa chabwino choyembekezerera kuti pansi pa ulamuliro wa ufumu wake wokhala m’manja mwa Kristu chimene’chi chidzachitidwa pa mlingo wokulirapo kwambiri.
Sitifunikira kuopa kuti kuyambitsidwa kwa dziko lapansi lopanda matenda ndi imfa kudzachititsa mikhalidwe yosakondweretsa. Si kokha kuti sikudzakhala kukhala mopanikizana, koma ali yense adzakhala wokhoza kudya chakudya mokhuta.
Boma lokhala m’manja mwa Mfumu yoikidwa ya Mulungu, Yesu Kristu, ndi olamulira 144,000 lidzatsimikizira kuti okhala pa dziko lapansi akusamaliridwa bwino lomwe. Posonya ku kuchuluka kwa zakudya zopatsa thanzi zoti zidzadyedwe, ulosi wa Yesaya umalongosola kuti: “M’phiri limene’li Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando . . . la zinthu zonona za mafuta okha okha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.”—Yesaya 25:6.
Tingathe kukhala ndi chidaliro mwa Yehova Mulungu, Uyo ponena za amene Baibulo limalengeza kuti: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chao.” (Salmo 145:16) Iye sanalephera konse kukwaniritsa malonjezo ake. Monga momwe Malemba amanenera ponena za Israyeli wakale kuti: “Sikadasowa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adzazinenera nyumba ya Israyeli; zidachitika zonse.”—Yoswa 21:45.
M’MENE MATENDA NDI IMFA ZIDZACHOKERA
Kuphatikiza pa kulonjeza kupereka zinthu zakuthupi zimene anthu amazifunikira m’malo mwakuti asangalale ndi moyo, Yehova Mulungu walonjeza kanthu kena kwabwino kopambana. Kodi kamene’ko nchiani? Mpumulo ku matenda ndi imfa. Chifuno chake cholengezedwa ponena za phwando lalikulu lochulidwa mu Yesaya, kunena zoona, chikutsatiridwa ndi lonjezo lakuti: “Iye wameza imfa ku nthawi yonse; ndipo Ambuye Mulungu adzaputuka misozi pa nkhope zonse.”—Yesaya 25:8.
Mogwirizana ndi lonjezo la Mulungu lochulidwa pano, boma Laufumu lokhala m’manja mwa Yesu Kristu ndi olamulira anzake lidzakhala likugwira ntchito kulinga ku kudzetsa chimasuko cha mtundu wonse wa anthu ku imfa. Popeza kuti matenda ndi imfa zinadza kupyolera mwa kubadwa kwathu tiri ochimwa opanda ungwiro chifukwa cha cholowa chochokera kwa mwamuna woyamba Adamu, ziyambukiro zochititsa imfa za uchimo ziyenera kuchotsedwa Motani?
Maziko ochitira zimene’zo ayenera kukhala kakonzedwe kamene kamakwaniritsa chiweruzo cholungama. Moyenerera kayenera kukhala kakonzedwe kamene kamasintha chibvulazo chochititsidwa ndi chipanduko cha Adamu. Chimene Adamu anataya chiyenera kubwezeretsedwa. Mtengo’wo udzayenera kukhala dipo lokhala ndi mtengo wofanana ndendende ndi chimene Adamu anataya, ndiko kuti, moyo waumunthu wangwiro limodzi ndi zoyenera ndi ziyembekezo zake zonse.
Palibe ali yense wa mbadwa zochimwa za Adamu akanatha kupereka dipo lotero’lo. Chimene’chi chikumveketsedwa bwino pa Salmo 49:7 kuti: “Kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kum’perekera dipo kwa Mulungu.” Koma Kristu Yesu anatha kutero, pakuti iye anali munthu wangwiro, ndipo iye mofunitsitsa anataya moyo wake, motero akumapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.”—Mateyu 20:28.
Chifukwa cha kupereka kwake nsembe moyo wake wangwiro waumunthu, Yesu Kristu ali wokhoza kugwiritsira ntchito mapindu a nsembe yake yotetezera machismo kaamba ka kuchotsa mtundu wa anthu ku ukapolo wa uchimo. Popeza kuti zikhoterero za uchimo zakhala mbali ya kapangidwe ka anthu, kudzafunikira nthawi ndi chithandizo kuti zimene’zi zilakidwe. Pansi pa Ufumu wokhala m’manja mwa Yesu Kristu, nzika zoake zonse zaumunthu zidzaphunzitsidwa njira ya chilungamo.—Chibvumbulutso 20:12; Yesaya 26:9.
Komabe, zimene’zi sizimatanthauza kweni-kweni kuti awo obvutika ndi kupunduka kwambiri kapena chirema chakuthupi adzafunikira kuyembekezera kwa nyengo ya nthawi yaitali m’kati mwa imene iwo potsirizira pake adzachira nthenda yao. Pamene Yesu Kristu anali pa dziko lapansi pano, iye anachiritsa odwala ndi ozunzika pa nthawi yomweyo, mozizwitsa. Machiritso angapo iye anawachita ali kutali, pamene anali wosaonedwa ndi odwala’wo ndi wosakhudzana nawo mwachindunji. (Mateyu 8:5-13; 15:21-28; Luka 7:1-10) Chifukwa cha chimene’cho anthu ali onse opunduka kwambiri, monga ngati munthu wokhala ndi mwendo umodzi kapena mkono umodzi, wokhala ndi moyo pamene Ufumuwo uyamba kuyendetsa zochitika zonse za dziko lapansi angayembekezere kuchiritsidwa kozizwitsa ndi kwa pa nthawi yomweyo pa nthawi yoikika ya Mulungu. Kudzakhala’di kodabwitsa kuona kupenya kukubwezeretsedwa kwa akhungu, kumva kwa ogontha ndi thupi labwino kwa oipitsidwa nkhope, opuwala ndi opunduka!
Komabe, kukhalitsidwa angwiro kwa anthu m’thupi ndi maganizo, kudzakhala kachitidwe kapang’ono-pang’ono, komafunikiritsa kugwiritsiridwa ntchito kwa nsembe yotetezera machimo a Yesu ndi kumvera chitsogozo cha boma Laufumu’lo. Chimene chidzachitika chingayerekezeredwe ndi kuchiritsa munthu wopunduka pansi pa chitsogozo cha katswiri wochiritsa mwa kuphunzitsa ziwalo. M’kati mwa nthawi ya kuphunzitsa kwake munthu wopunduka’yo angapange zolakwa zambiri koma potsirizira pake angafikire pakuti iye ali wokhoza kukhala ndi moyo wopindulitsa popanda kufunikira kwa kudalira pa ena. Kupita patsogolo kumene iye akupanga kumadalira pa kulabadira kwake chithandizo choperekedwa.
ZIYENERETSO ZA AWO OBWEZERETSA THANZI ANTHU OPANDA UNGWIRO
M’kubwezeretsa thanzi mtundu wa anthu, Yesu Kristu ali ndi ziyeneretso zonse zofunika. Pokhala atakhala ndi moyo monga munthu pa dziko lapansi, iye mwachindunji wadziwa zobvuta za anthu opanda ungwiro. Ngakhale kuli kwakuti iye anali wangwiro, iye, mosasamala kanthu za zimene’zo, anakhala ndi kubvutika ndi chisoni, kufikira pa kugwetsa misozi. Cholembedwa cha Baibulo chimatiuza kuti: “M’masiku a thupi lake anapereka mapemphero ndi mapembedzero pamodzi ndi kulira kwakukulu ndi misozi kwa Iye amene anakhoza kum’pulumutsa Iye muimfa, ndipo anamveka popeza anaopa Mulungu, ngakhale anali Mwana, anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo.”—Ahebri 5:7, 8.
Chifukwa cha zimene Yesu Kristu anakumana nazo pa dziko lapansi, tingakhale ndi chidaliro chakuti iye adzakhala wolamulira wozindikira. Iye sadzachita mwankhanza ndi nzika zake, pakuti iye mofunitsitsa anatayira moyo wake mtundu wa anthu. (1 Yohane 3:16) Ndiyeno’nso, popeza kuti iye ali’nso Mkulu wa Ansembe, Yesu adzachita mwachifundo m’kumasula ku uchimo awo amene amalemekeza chitsogozo chake. Iye sadzakhala wosadekha nawo kapena kuwapangitsa kuona kukhala opsyinjika chifukwa cha kugwera m’kachitidwe kamene sikamasonyeza mokwanira umunthu wa Mulungu. Ponena za utumiki waunsembe wa Yesu, Ahebri 4:15, 16 amati: “Sitiri naye mkulu wa ansembe wosatha kumva chifundo ndi zofoka zathu; koma wayesedwa m’zonse monga momwe ife, koma wopanda uchimo. Potero tilimbike mtima poyandikira mpando wochifumu wachisomo, kuti tilandire chifundo ndi kupeza chisomo cha kutithandiza nthawi ya kusowa.”
Pamene akufikira ungwiro, anthu adzakhala akuchita machimo osakhala mwadala. Koma mwa kulapa ndi kupempha chikhululukiro cha Mulungu kupyolera mwa Mkulu wao wa Ansembe Yesu Kristu, iwo adzakhululukidwa ndipo adzapitirizabe kulandira chithandizo m’kulaka zolakwa zao. Posonyeza makonzedwe a Mulungu a moyo ndi kuchiritsa, Chibvumbulutso 22:1, 2 chimachula “mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa. Pakati pa khwalala lake, ndi tsidya iri la mtsinje, ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu.”
Awo ogwirizana ndi Yesu Kristu mu ulamuliro mofananamo ali oyeneretsedwa kuthandiza mtundu wa anthu. Olamulira anzake amene’wa akuphatikizamo amuna ndi akazi omwe ochokera m’mikhalidwe yosiyana-siyana kwambiri ya moyo. (Agalatiya 3:28) Ena a iwo anachokera m’mikhalidwe imene inagonana kwa anthu ofanana ziwalo, kuba, kuledzera, kulanda ndi ina yotero. Koma iwo analapa, anatembenuka ndi kuyamba kukhala ndi moyo woyera, motamanda ndi kulemekeza Mulungu. (1 Akorinto 6:9-11) Pa nthawi ya imfa yao onse amene akukhala mafumu ndi ansembe anzake a Yesu Kristu ayenera kupezedwa kukhala okonda ndi ochita chilungamo, odana ndi zoipa, ndi anthu amene mopanda dyera anadzipereka kupititsa patsogolo thanzi la anthu anzao.—Aroma 12:9; Yakobo 1:27; 1 Yohane 3:15-17; Yuda 23.
Kusunga kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu sikunakhale kusabvuta kwa iwo. Iwo achititsidwa kukumana ndi zitsenderezo zochuluka kwambiri kuti atengere njira za dziko lapansi zadyera. Ena akumana ndi zitsenderezo zakunja mu mpangidwe wa chitonzo, kumenyedwa ndi kusakondedwa ndi kunyozedwa ndi onse. Ponena za chimene iwo ayenera kuyembekezera, Yesu Kristu anawauza kuti: “[Anthu] adzakuperekani kunsautso, nadzakuphani; ndipo anthu a mitundu yonse adzadana nanu, chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:9) Ndipo’nso, m’kati mwa nthawi yonse ya moyo wao iwo anayesa-yesa zolimba kulimbana ndi zizolowezi zao za iwo eni za uchimo. Mmodzi wa iwo, mtumwi Paulo, ponena za iye mwini anati: “Ndipumpuntha thupi langa, ndipo ndiliyesa kapolo; kuti, kapena ngakhale ndalalikira kwa ena, ndingakhale wotayika ndekha.”—1 Akorinto 9:27.
Ndithudi, pamenepa, gulu la mafumu ndi ansembe la 144,000 limene’li lingamvere chifundo zobvuta za nzika zaumunthu za Ufumu’wo. Iwo eni’wo anabvutika nazo nadzitsimikizira kukhala okhulupirika kwa Mulungu mosasamala kanthu za zobvuta zazikulu.
MIKHALIDWE YABWINO PA DZIKO LAPANSI
Ndipo’nso, pa dziko lapansi, chinthu chiri chonse chidzakhala choyenera kaamba ka kuthandiza anthu kufika ku ungwiro. Awo okha amene adzisonyeza kukhaka ofuna kuchita chifuno cha Mulungu ndi mtima wamphumphu adzatsala Ufumu’wo utaononga adani ake. Zimene’zi zikutanthauza kuti umbombo ndi dyera la anthu zimene kwakukulu zakhala zochititsa kuipitsidwa kwa chakudya chimene timadya, madzi amene timamwa ndi mpweya umene timapuma zidzakhala zinthu zakale. Opulumuka’wo sadzabvutidwa ndi zopinga zogawanitsa zaupfuko ndi zautundu. Pokhala ogwirizana m’kulambiridwa kwa Yehova Mulungu, onse adzachita mong abale ndi kulondola mtendere. Ngakhale zinyama zakuthengo sizidzabvulaza munthu kapena zifuyo zake. Mau olosera a Yesaya 11:6-9 pa nthawi imene’yo adzaposa kukwaniritsidwa kwauzimu ndi kukhala ndi kukwaniritsidwa kwakuthupi:
“M’mbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng’ombe ndi mwana wa mkango, ndi choweta chonenepa pamodzi; ndipo mwana wamng’ono adzazitsogolera. Ndipo ng’ombe yaikazi ndi chirombo zidzadya pamodzi; ndipo ana ao ang’ono adzagona pansi; ndipo mkango udzadya udzu ngati ng’ombe. Ndipo mwana wakuyamwa adzasewera pa una wa mamba, ndi mwana woleka kuyamwa adzaika dzanja lake m’pfunkha la mphiri. Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera, chifukwa kuti dziko lapansi lidzadzala ndi odziwa Yehova monga madzi adzaza nyanja.”
Kupyolera mwa boma Laufumu Yehova Mulungu adzakhala akutembenuzira chisamaliro chake kwa anthu m’njira yapadera. Zimene’zi zikusonyezedwa m’masomphenya olosera olembedwa m’bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso. Pambuyo kuyerekezera kufutukuka kwa mphamvu ya Ufumu ndi kutsika kwa Yerusalemu Watsopano kuchokera kumwamba, cholembedwa’cho chimatiuza kuti: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhala’nso imfa; kapena chowawitsa; zoyamba’zo zapita.”—Chibvumbulutso 21:2-4.
Taganizirani zimene zimene’zo zikutanthauza. Moyo wa tsopano lino’wu limodzi ndi zowawa zake ndi zisoni ndithudi sindiwo wokha umene ulipo. Mtundu wa anthu udzamasulidwa ku ululu uli wonse wamaganizo, wamalingaliro ndi wakuthupi wochititsidwa ndi kupanda ungwiro. Kubvutika maganizo chifukwa cha zozsatsimikizirika kapena masoka akulu ndi maupandu zidzakhala chinthu chakale. Kupsyinjika, kupanda pake ndi kusungulumwa kogwirizanitsidwa ndi kubvutika kwamalingaliro sizidzakhala’nso m’maso mwao ndi kuyendera m’masaya mwao. Sipadzakhala chifukwa chiri chonse kwa ali yense chogwetsera misozi. Pokhala atabwezeretsedwa ku ungiro wa maganizo ndi thupi, anthu adzapeza chisangalalo cheni-cheni m’moyo kwamuyaya. Kodi inu simukufuna kukhala pakati pa awo osangalala ndi madalitso ochokera kwa Mulungu amene’wa?