Mutu 20
Kodi Chiukiriro Chidzadzetsa Mapindu Yani?
MAFUNSO ambiri amabuka ponena za chiukiriro cha akufa. Kodi ndani amene adzaukitsidwa? Makanda? Ana? Olungama ndi oipa omwe? Kodi awo amene anali okwatirana adzagwirizanitsidwa’nso ndi anzao a mu ukwati akale?
Baibulo silimalongosola zonse ponena za chiukiriro. Komabe, liri ndi lonjezo labwino kwambiri lakuti akufa adzaukitsidwa ndipo limapereka nsonga zokwanira kukhazikitsa chikhulupiriro m’lonjezo limene’lo. Kodi kusanena kwake chiri chonse ponena za zinthu zina kuyenera kutiletsa kuzindikira kutsimikizirika kwa lonjezo limene’lo?
M’machitidwe athu ndi anthu anzathu sitimayembekezera chinthu chiri chonse kuti chichulidwe, kodi timatero? Mwa chitsanzo, ngati munaitanidwa ku phwando, simukanafunsa wokuitanani’yo kuti: ‘Kodi anthu onse adzakhala kuti? Kodi mwakonzekera kuphikira anthu ambiri-mbiri? Kodi ndingatsimikizire motani kuti mudzakhala ndi ziwiya zoperekerera chakudya ndi mbale zokwanira? Kufunsa mafunso otero’wo kukakhala mwano, kodi si choncho? Palibe ali yense amene akaganiza kunena kwa wolandira alendo kuti: ‘Choyamba nditsimikiziritseni kuti ndidzasangalala.’ Kulandira chiitano ndi kudziwa kumene chachokera kuyenera kukhala kokwanira kuti munthu akhale ndi chidaliro chakuti zinthu zidzayenda bwino.
Kweni-kweni, palibe ali yense akayamikira kufunsidwa kulongosola kapena kutsimikizira mau ali onse amene iye akunena. Tiyeni tinene kuti tsamwali anasimba chokumana nacho m’kupulumutsa munthu wina kuti asamire. Ngati iye anali bwenzi lolemekezedwa, sitikam’pempha kuti atsimikizire kuti iye anachita’di zinthu zimene iye analongosola. Kufunsa zimene’zi kukasonyeza kupanda chidaliro ndi chikhulupiriro. Sikukakhala maziko okulitsira ndi kusungirabe ubwenzi. Mwachionekere, pamenepa, munthu amene sakalandira lonjezo la Mulungu la chiukiriro popanda choyamba kukhala atalongosoleredwa momvekera bwino nsonga iri yonse sakawerengeredwa kukhala bwenzi Lake. Mulungu amalandira kukhala mabwenzi ake awo okha amene amasonyeza chikhulupiriro, amene amadalira mau ake. (Ahebri 11:6) Iye amapereka umboni wochuluka wozikapo chikhulupiriro chimene’cho, koma iye samaumiriza anthu kukhulupirira mwa kupereka ndi kutsimikizira nsonga iri yonse kotero kuti chikhulupiriro chikukhala chosafunika.
Chotero kusakhalapo kwa nsonga zina kumatumikira kuyesa anthu ponena za chimene iwo ali mu mtima. Pali awo amene amadziwerengera kwambiri ndi malingaliro ao a iwo eni okondedwa, ndi amene amatsatira njira ya kudzidalira. Iwo samafuna kukhala athayo kwa wina ali yense. Kukhulupirira chiukiriro kukawafunikiritsa kubvomereza kufunika kwa kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Koma iwo samafuna kuchita zimene’zi. Chifukwa cha chimene’cho, chifukwa cha kusakhalapo kwa nsonga zina zonena za chiukiriro, iwo angapeze chimene iwo amalingalira kukhala cholungamitsira kusakhulupirira kwao. Iwo ali ofanana kwambiri ndi Asaduki a m’nthawi ya utumiki wa Yesu wa pa dziko lapansi. Asaduki anakana kukhulupirira chiukiriro ndipo anasonya ku chimene iwo anachilingalira kukhala bvuto lalikulu kwambiri. Iwo anati kwa Yesu:
“Mphunzitsi Mose anatilembera ife, kuti mbale wake wa munthu akafa, wokhala ndi mkazi, ndipo alibe mwana iye, mbale adzakwatira mkazi’yo, nadzamuukitsira mbale wake mbeu. Tsono panali abale asanu ndi awiri; ndipo woyamba anakwatira mkazi, nafa wopanda mwana; ndipo wachiwiri, ndi wachitatu anam’tenga mkazi’yo; ndipo chotero’nso asanu ndi awiri onse, sanasiya mwana, namwalira. Pomalizira anamwalira’nso mkazi’yo. Potero m’kuuka iye adzakhala mkazi wa yani wa iwo? pakuti asanu ndi awiri’wo adam’kwatira iye.”—Luka 20:28-33.
Poyankha funso lao, Yesu Kristu anabvumbula kulakwika kwa lingaliro la Asaduki nagogomezera kutsimikizirika kwa lonjezo a chiukiriro. Iye anayankha kuti:
“Ana a dziko lapansi akwatira nakwatiwa; koma iwo akuyesedwa oyenera kufikira dziko lija’lo, ndi kuuka kwa akufa, sakwatira kapena kukwatiwa. . . . Koma za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye anam’chulira Ambuye, Mulungu wa Yakobo. Ndipo iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo; pakuti . . . onse akhala ndi moyo kwa Iye.”—Luka 20:34-38.
CHIFUKWA CHAKE CHIUKIRIRO SICHIPEREKA LONJEZO LA UKWATI
Chifukwa cha yankho la Yesu kwa Asaduki, ena angabvutike maganizo ndi kunena kwake kuti sikudzakhala kukwatira pakati pa awo oukitsidwa kwa akufa. Iwo angaganize’di kuti popanda ukwati chiukiriro chiri kanthu kena kosafunika, kuti sichikawapindulitsa.
Komabe, polingalira yankho la Yesu, tichita bwino kukumbukira kuti ife ndife opanda ungwiro. Zokonda ndi zosazikonda zathu kwakukulu-kulu zimalamuliridwa ndi zinthu zimene tazizolowera. Chotero palibe ali yense amene ali kweni-kweni ndi maziko ali onse okhalira wotsimikizira kuti sakakonda makonzedwe am’tsogolo amene Mulungu adzapangira anthu oukitsidwa’wo. Ndiyeno’nso si nsonga zonse, zimene zaperekedwa. Kumene’ku kwakhala’di kukoma mtima kwa Mulungu. Eya, monga anthu opanda ungwiro, choyamba tingachite mosakondwera ndi zinthu zimene kweni-kweni zikadzaza moyo wathu ndi chisangalalo mu mkhalidwe wangwiro. Chifukwa cha chimene’cho nsonga zotero’zo zingakhale zosalingana ndi luso lathu la tsopano lino’li kuzilandira. Kristu Yesu anasonyeza kuzindikira ndi kulingalira zopinga za anthu opanda ungwiro, monga momwe zikuonekera m’zimene iye ananea kwa ophunzira ake pa nthawi ina kuti: “Ndiri nazo zambiri’nso zakunena kwa inu, koma simungathe kuzisenza tsopano lino.”—Yohane 16:12.
Awo amene adzapeza chiukiriro cha ku moyo wauzimu wosafa kumwamba alibe lingaliro lakuti uwo udzakhala wotani. Iwo sangauyerekezere ndi kanthu kali konse kamene akukadziwa pa dziko lapansi. Matupi ao adzakhala ena kotheratu. Masiyanidwe onse akukhala amuna kapena akazi kwa anthu adzakhala zinthu zakale kwa iwo. Chotero sipadzakhala kukwatira pakati pa awo oukitsidwira ku moyo wakumwamba chifukwa chakuti iwo onse monga kagulu akukhala “mkwatibwi” kwa Kristu.
Bwanji ponena za awo amene akuukitsidwa kwa akufa kudzakhala ndi moyo pa dziko lapansi? Kodi iwo adzagwirizanitsidwa’nso ndi anzao a mu ukwati akale? Palibe mau ali onse m’Baibulo amene amasonyeza kuti zimene’zo zidzakhala choncho. Malemba motsimikizira amasonyeza kuti imfa imathetsa ukwati. Aroma 7:2, 3 amati: “Mkazi wokwatidwa amangidwa ndi lamulo kwa mwamuna wake wamoyo; koma mwamuna’yo akafa, iye amasulidwa ku lamulo la mwamuna’yo . . . chotero sakhala wachigololo ngati akwatiwa ndi mwamuna wina.”
Chifukwa cha chimene’cho, ngati munthu asankha kukwatira’nso tsopano, iye safunikira kubvutika maganizo ndi chiyambukiro chimene chimene’chi chingakhale nacho pa mnzake woukitsidwa m’tsogolo. Ngati iye sangathe kukhala mbeta, iye safunikira kubvutika ndi ausunge moyembekezera kudzagwirizana’nso mu ukwati ndi mnzake wakale m’chiukiriro. Pamene’pa, ndithudi, kunali kukoma mtima kwa Mulungu kusafuna kuti maunansi akale a ukwati adzakhalepo pa nthawi ya chiukiriro cha munthu’yo, monga momwe Asaduki molakwa analingalirira.
Pamene kuli kwakuti situkudziwa kumene pa dziko lapansi kapena amene oukitsidwa’wo adzakhala nawo, tingakhale otsimikizira kuti kakonzedwe kali konse kamene kalipo kadzachititsa chimwemwe cha oukitsidwa’wo. Mphatso za Mulungu, kuphatikizapo chiukiriro, zidzakhutiritsa kotheratu zikhumbo ndi zosowa za mtundu wa anthu womvera. Mphatso zake n’zangwiro ndi zopanda cholakwika. (Yakobo 1:17) Mphatso zoolowa manja zimene tazilandira kale monga zisonyezero za chikondi chake zimatikhutiritsa maganizo za chimene’cho.
ANA NDI ENA OTI AUKITSIDWE
Bwanji ponena za ana amene amafa? Kodi iwo’nso adzabwezeretsedwa ku moyo pamene chilungamo chifunga pa dziko lapansi’li? Ndithudi chimene’cho ndicho chimene makolo achikondi akafuna kaamba ka ana ali onse amene iwo angakhale atawataya mu imfa. Ndipo pali maziko amphamvu okhalira ndi chiyembekezo chotero’cho.
Pakati pa awo osimbidwa m’Baibulo kukhala ataukitsidwa panali ana. Mwana wamkazi wa Yairo, amene anakhala mu Galileya, anali pafupi-fupi wa usinkhu wa zaka khumi ndi ziwiri; Yesu anamuukitsa. (Luka 8:42, 54 55) Anyamata amene anaukitsidwa ndi aneneri’wo Eliya ndi Elisa angakhale anali okulirapo kapena ocheperapo. (1 Mafumu 17:20-23; 2 Mafumu 4:32-37) Polingalira ziukiriro zakale za ana zimene’zi, kodi sikuli koyenera kuyembekezera kuti chiukiriro chachikulu kwambiri cha ana chidzachitika m’kati mwa ulamuliro wa Yesu monga mfumu? Ndithudi! Tingakhale otsimikizira kuti chiri chonse chimene Yehova Mulungu walinganiza m’nkhani imene’yi chidzakhala chinthu cholungama, chanzeru ndi chachikondi kwa onse olowetsedwamo.
Baibulo limabvumbula kuti unyinji wochuluka kwambiri wa mtundu wa anthu—amuna, akazi ndi ana—udzaukitsidwa kwa akufa. Monga momwe mtumwi Paulo anatsimikizirira m’kudzikanira kwake pamaso pa Bwanamkubwa Felike kuti: “Ndiri ndi chiyembekezo kwa Mulungu . . . kuti kudzakhala chiukiriro cha olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15, NW) “Olungama” ndiwo awo amene anakhala m’chiyanjo cha Mulungu. “Osalungama” ndiwo ena onse a mtundu wa anthu. Koma kodi zimene’zo zikutanthauza kuti munthu ali yense wakufa adzaukitsidwa? Ai, sizikutanthauza choncho.
AWO AMENESADZAUKITSIDWA
Ena aweruzidwa ndi Mulungu kukhala osayenerera chiukiriro. Ponena za awo amene pa nthawi ino akukana kugonjera ku ulamuliro wa Kristu ndi kulephera kuchitira zabwino “abale” ake pa dziko lapansi, Baibulo limati: “Amene’wa adzachoka, kumka ku chilango cha nthawi zonse.” (Mateyu 25:46) Iwo adzakumana ndi chionongeko chosatha chimene’chi pamene Yesu Kristu, limodzi ndi magulu ake ankhondo a angelo, aononga otsutsa ulamuliro wake wolungama onse mu “chisautso chachikulu,” chimene tsopano chiri pafupi’cho.
Ponena za ali onse oyembekezera ufumu wa kumwamba amene akukhala osakhulupirika kwa Mulungu, tikuuzidwa kuti: “Siitsala’nso nsembe ya kwa machimo, koma kulindira kwina koopsya kwa chiweruziro, ndi kutentha kwake kwa moto wakuononga otsutsana nao.”—Ahebri 10:26, 27.
Ndipo’nso, pali magulu ena a anthu amene akunenedwa kukhala akulandira chionongeko chamuyaya. Yesu Kristu anasonyeza kuti Afarisi osalapa ndi atsogoleri ena achipembedzo a m’nthawi yake monga kagulu anali atachimwira mzimu woyera. Iye ponena za chimo lotero’lo anati: “Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa. Ndipo amene ali yense anganenere Mwana wa munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma amene ali yense anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi yino kapena irinkudza’yo.” (Mateyu 12:31, 32) Pokhala popanda chikhululukiro cha chimo lotero’lo, onse okhala ndi liwongo la kukana maumboni oonekera bwino a mzimu woyera wa Mulungu amalandira chilango cha chimo losakhululukidwa lotero’lo mwa kukhalabe chifere kosatha.
Kuphatikiza pa zimene Baibulo limanena kweni-kweni ponena za awo amene aonongeka kosatha, ife sitiri okhoza kunena kuti anthu akuti-akuti sadzaukitsidwa kwa akufa. Komabe, cheni-cheni chakuti ena sadzaukitsidwa, chiyenera kutumikira monga chenjezo kwa ife kuti tipewe njira yochititsa kukanidwa ndi Mulungu.
CHIUKIRIRO CHA CHIWERUZO
Cheni-cheni chakuti unyinji wa mtundu wa anthu udzaukitsidwa kwa akufa chiri’di kukoma mtima kwapadera kwa Mulungu. Chiri kanthu kena kamene Mulungu samaumirizika kuchita, koma kukonda kwake ndi kumvera chisoni mtundu wa anthu kunam’sonkhezera kukukhazikitsira maziko mwa kupereka Mwana wake monga dipo. (Yohane 3:16) Chifukwa cha chimene’cho, chakuti anthu akalephera kuyamikira kuukitsidwa kwao kwa akufa limodzi ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya, chiri chobvuta kuchiyerekezera. Komabe padzakhala ena amene sadzakulitsa chikondi chokwanira, chosasweka ndi chokhulupirika kwa Yehova Mulungu. Chifukwa cha chimene’cho iwo adzalephera madalitso osatha amene kuukitsidwa kudzawapatsa.
Yesu Kristu anasonyeza zimene’zi pamene anachula ‘chiukiriro cha chiweruzo’ nachisiyanitsa ndi ‘chiukiriro cha moyo.’(Yohane 5:29) Cheni-cheni chakuti moyo pano ukusiyanitsidwa ndi chiweruzo chikupangitsa kukhala koonekera bwino kuti chiweruzo chachitsutso chikulowetsedwamo. Kodi chitsutso chimene’chi n’chiani?
Kuti mumvetsetse zimene’zi, yerekezerani chiyamba mkhalidwe wa awo oukitsidwira ku moyo wa pa dziko lapansi ndi awo oukitsidwira ku moyo kumwamba. Baibulo ponena za awo olandira “chiukiriro choyamba” limati: “Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri iribe ulamuliro.” (Chibvumbulutso 20:6) Pokhala ataukitsidwira ku moyo wosakhoza kufa wakumwamba, olowa nyumba limodzi ndi Kristu 144,000’wo sangafe. Kukhulupirika kwao kwa Mulungu kuli kotsimikizirika kwambiri kwakuti iye angawapatse moyo wosakhoza kuonongeka. Koma zimene’zi siziri choncho ndi awo oukitsidwira ku moyo pa dziko lapansi. Padzakhala ena a achiwiri’wa amene adzakhala osakhulupirika kwa Mulungu. Chiweruzo chachitsutso choperekedwa pa iwo kaamba ka kusakhulupirika chidzakhala “imfa yachiwiri,” imfa imene mu “ulamuliro” wake mulibe kuthekera kwa kuukitsidwa.
Komabe kodi n’chifukwa ninji ali yense adzafikira kutsatira njira yomka ku chiweruzo chachitsutso pamene iye wapatsidwa chiyanjo chapadera cha kuukitsidwa kwa akufa?
Yankho la funso limene’li lingamvedwe bwino kwambiri mothandizidwa ndi zimene Yesu Kristu ananena ponena za anthu amene akaukitsidwa. Polankhula ndi anthu a mtundu wake osakhulupirira, Yesu anati:
“Anthu a ku Nineve adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iwo anatembenuka mtima ndi kulalikira kwake kwa Yona; ndipo onani, wakuposa Yona ali pano. Mfumu yaikazi ya kumwela adzauka pamlandu pamodzi ndi obadwa amakono, nadzawatsutsa; chifukwa iye anachokera ku mathero a dziko lapansi kudzamva nzeru ya Solomo; ndipo onani, wakuposa Solomo ali pano.”—Mateyu 12:41, 42; Luka 11:31, 32.
Ponena za mzinda umene mouma khosi ukakana kumvera uthenga wa choonadi, Yesu anati:
“Tsiku la kuweruza, mlandu wao wa Sodumu ndi Gomora udzachepa ndi wake wa mudzi umene’wo.”—Mateyu 10:15; onaninso Mateyu 11:21-24.
Kodi ndi motani m’mene zikakhalira zopepuka kwambiri kwa Sodomu ndi Gomora pa Tsiku la Chiweruzo? Kodi ndi motani m’mene “mfumu yaikazi ya kumwela” ndi Anineve amene analabadira kulalikira kwa Yona anatsutsira mbadwo wa anthu a mtundu wa Yesu?
Kumene’ku kudzakhala m’njira imene anthu oukitsidwa’wo adzalabadira chithandizo choperekedwa m’kati mwa ulamuliro wa Yesu Kristu ndi mafumu ndi ansembe anzake 144,000. Nyengo imene’yo ya ulamuliro idzakhala “Tsiku la Chiweruzo” m’chakuti idzapatsa anthu onse mwai wa kusonyeza kaya akufuna kugonjera ku makonzedwe a Mulungu. Ponena za awo onga anthu osakhulupirira a m’mizinda imene inaona ntchito zamphamvu za Yesu Kristu, limene’li silidzakhala lokhweka.
Kudzakhala kobvuta kwambiri kwa iwo kuzindikira modzichepetsa kuti iwo anali olakwa m’kukana Yesu monga Mesiya ndiyeno kufunika kudzigonjetsera kwa iye monga Mfumu yao. Kunyada ndi kuuma khosi zidzapangitsa kugonjera kukhala kobvuta kwambiri kwa iwo koposa anthu okhala m’Sodomu ndi Gomora, amene, pamene anali ochimwa, sanakane mwai wabwino kwambiri wonga uja umene unaikidwa pamaso pa anthu amene anaona ntchito za Yesu Kristu. Kulabadira kwabwino kwambiri kwa Anineve oukitsidwa ndi kuja kwa mfumu yaikazi ya ku Seba kudzatumikira monga chidzudzulo ku mbadwo woukitsidwa wa anthu a mtundu wa Yesu okhala ndi moyo m’nthawi ya utumuki wake wa pa dziko lapansi. Kudzakhala kosabvuta kwambiri kwa Anineve ndi ena ofanana nawo kulandira ulamuliro wa munthu wina amene iwo sanaipidwe naye maganizo.
Awo amene motsimikizirika akukana kupanga kupita patsogolo m’njira ya chilungamo pansi pa ufumu wa Kristu adzalandira chiweruzo chachitsutso cha “imfa yachiwiri.” M’zochitika zina zimene’zi zidzachitika iwo asanafikire ungwiro waumunthu.
Ndipo’nso, ena, atafikitsidwa ku ugwiro waumunthu, mosayamikira adzalephera kusonyeza kudzipereka kokhulupirika kwa Yehova Mulungu pamene atayesedwa. Motsatizana ndi ulamuliro wa zaka chikwi kwa Kristu, Satana Mdierekezi adzamasulidwa kwa kanthawi kuchokera m’kubindikiritsidwa kwake m’mphompho. Monga momwe iye anaukirira ulamuliro wa Mulungu kunyenga Hava, amene pambuyo pake anakopa Adamu, iye kachiwiri’nso adzafuna kuchititsa anthu angwiro’wo kupandukira ulamuliro wa Mulungu. Ponena za kuyesa-yesa kwa Satana ndi chotulukapo chake, Chibvumbulutso 20:7-10, 14, 15 chimati:
“Ndipo pamene zidzatha zaka chikwi, adzamasulidwa Satana m’ndende yake; nadzatuluka kudzasokeretsa amitundu ali mu ngodya zinai za dziko, Gogo, ndi Magogo, kudzawasonkhanitsa achite nkhondo: chiwerengero chao cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja. Ndipo anakwera nafalikira m’dziko, nazinga tsasa la oyera mtima ndi mudzi wokondedwa’wo: ndipo unatsika moto wakumwamba nuwanyeketsa. Ndipo Mdierekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure, . . . Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.” Chimene’chi chimasonyeza chionongeko chao chosatha kapena kufafanizidwa. Motero osakhulupirira amene’wa adzakhala ndi chimene Yesu anacha ‘chiukiriro cha chiweruzo,’ chiweruzo chachitsutso.
Ndipo’nso, awo amene akukana kugwirizana ndi Satana m’chipanduko adzalingaliridwa kukhala oyenera kulandira moyo wosatha. Iwo adzasangalala kosatha m’kukhala ndi moyo monga anthu angwiro, akumasonyeza chikondi ndi kukondedwa kwa umuyaya wonse. Chao’cho chidzatsimikizira kukhala ‘chiukiriro cha moyo.’
Ngakhale tsopano tingathe kuyamba kukulitsa mikhalidwe imene Mulungu amaiyembekezera mwa awo amene iye amawalandira kukhala atumiki ake obvomerezedwa. Ngati tidzisonyeza kukhala oyamikira zonse zimene iye wachita ndi kuyambiratu m’njira ya chilungamo, tingakhale ndi chiyembekezo chodabwitsa cha kukhala ndi woposa kwambiri moyo ulipo’wu. Inde, wopanda chisoni chonse ndi zowawa!