Mutu 5
Ufulu Umene Uli ndi Olambira a Yehova
1, 2. (a) Kodi ndiufulu wamtundu wanji umene Mulungu anapereka kwa anthu awiri oyamba? (b) Tchulani ena a malamulo amene analamulira zochita zawo.
PAMENE Yehova analenga anthu awiri oyambirira, anali ndi ufulu wokulira kwambiri kuposa uliwonse umene anthu alinawo lerolino. Kwawo kunali ku Paradaiso. Kunalibe matenda ododometsa kusangalala kwawo ndi moyo. Imfa siinali kuwayembekezera. Koma kuchitira ulemu malamulo a Mulungu kunali chinthu chofunika m’kupitirizabe kwawo kukhala ndi ufulu wotero.
2 Ena a malamulo amenewo angakhale sanalongosoledwe mwa mawu, koma Adamu ndi Hava anapangidwa mwanjira yakuti kunali kokha kwachibadwa kuwamvera. Chotero njala inawauza kufunika kwa kudya; ludzu, kufunika kwa kumwa. Kulowa kwa dzuwa kunawalimbikitsa kupeza mpumulo wofunika ndi kugona. Yehova analankhulanso nawo nawapatsa gawo lantchito. M’chenicheni gawo limenelo linali lamulo, chifukwa chakuti linkalamulira zochita zawo. Koma ha ndilamulo lachifundo ndi lopindulitsa chotani nanga! Linawapatsa ntchito imene ikakhala yokhutiritsa kotheratu, yowakhozetsa kugwiritsira ntchito maluso awo mokwanira m’njira zopindulitsa. Iwo anayenera kubala ana, kukhala ndi ulamuliro pa nyama zadziko lapansi ndipo pang’ono ndi pang’ono kukulitsa malire a Paradaiso kufikira atafalikira padziko lonse. (Gen. 1:28; 2:15) Mulungu sanawalemetse ndi mawu osayenerera. Ufulu wokwanira unapatsidwa kwa iwo kupanga zosankha. Kodi nchiyaninso china chimene munthu akanapempha?
3. Kodi ndimotani mmene Adamu akanakhala atathandizidwa kugwiritsira ntchito mwanzeru ufulu wake wa kupanga zosankha?
3 Ndithudi, pamene Adamu anapatsidwa mwayi wakupanga zosankha, izi sizinatanthauze kuti chosankha chirichonse chimene akanapanga, mosasamala kanthu kuti chinali chotani, chikatulutsa zotulukapo zabwino. Ufulu wake wa kupanga zosankha unatanthauza thayo. Iye akanaphunzira mwa kumvetsera kwa Atate wake wakumwamba ndi kuwona ntchito Zake, ndipo Mulungu anali atapatsa Adamu luntha limene likanam’khozetsa kugwiritsira ntchito zimene anaphunzira. Popeza Adamu anapangidwa “m’chifanizo cha Mulungu,” chikhoterero chake chachibadwa chikakhala kusonyeza mikhalidwe yaumulungu popanga zosankha. Ndithudi iye akakhala wosamala kuchita zimenezo ngati anayamikiradi chimene Mulungu anamchitira ndipo anafuna kukondweretsa Mulungu.—Gen. 1:26, 27; yerekezerani Yohane 8:29.
4. (a) Kodi lamulo loletsa loperekedwa kwa Adamu linamlanda ufulu? (b) Kodi nchifukwa ninji linali chiyeneretso choyenerera?
4 Monga chikumbutso cha kudalira kwa munthuyo pa Mlengi ndi Mpatsi wa moyo wake, Yehova anapereka lamulo iri pa iye: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko; koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.” (Gen. 2:16, 17) Kodi lamulo limenelo linalanda munthu ufulu? Ndithudi ayi. Adamu anali waufulu kumvera kapena kusamvera. Chiletso sichinapereke mtolo wolemera. Iye anali ndi zakudya zambiri popanda kukhudza mtengo umodzi umenewo. Komabe, kunali kokha koyenerera kuti azindikire kuti dziko lapansi pa limene anakhala linali la Mulungu ndi kuti, monga Mlengi, Mulungu ndiye Wolamulira woyenerera wa chilengedwe chake.—Sal. 24:1, 10.
5. (a) Kodi ndimotani mmene Adamu ndi Hava anataira ufulu wa ulemerero umene anali nawo? (b) Kodi nchiyani chimene chinaulowa mmalo, ndipo kodi ife tayambukiridwa motani?
5 Koma kodi nchiyani chimene chinachitika? Mosonkhezeredwa ndi chikhumbo chadyera cha kufuna malo apamwamba, mngelo ananyenga Hava kunyengezera kukhala mtsogoleri weniweni akumamtsimikizira kanthu kena kosiyana ndi chifuniro cha Mulungu. Mmalo mwa kumvera Atate wake, Adamu anagwirizana ndi Hava kuchimwa. Mwa kusirira kanthu kena kamene sikanali kawo, Adamu ndi Hava anataya ufulu waulemerero umene anali nawo. Uchimo unakhala mbuye wawo ndipo, monga momwe Mulungu anali atachenjezera, ndithudi imfa inawayembekezera. Chotero, kodi ndi cholowa chotani chimene chinapatsidwa kwa ana awo? Uchimo, wosonyezedwa m’chikhoterero chobadwa nacho cha kuchita cholakwa, m’zofooka zimene zimachititsa munthu kugwidwa msanga ndi nthenda ndipo potsirizira pake kutha mphamvu chifukwa cha ukalamba. Ndiponso imfa. Chikhoterero cha kuchita uchimo chobadwa nacho, chokulitsidwa ndi chisonkhezero Chausatana, chatulutsa chitaganya m’chimene moyo wafikira kukhala paupandu kwa aliyense. Ha nkusiyana kotani nanga ndi ufulu umene Mulungu anapereka kwa anthu pa chiyambi!—Aroma 5:12; Yobu 14:1; Chiv. 12:9.
Kumene Ufulu Ungapezeke
6. (a) Kodi nkuti kumene ufulu weniweni ungapezeke? (b) Kodi ndi ufulu wamtundu wanji umene Yesu anali kunena pa Yohane 8:31, 32?
6 Monga momwe mikhalidwe iriri lerolino, sikuli kodabwitsa kuti anthu akulakalaka ufulu wokulirapo koposa umene alinawo. Koma kodi nkuti kumene ufulu weniweni ungapezeke? Yesu Kristu anati: “Ngati mukhala inu m’mawu anga, muli akuphunzira anga ndithu; ndipo muzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yoh. 8:31, 32) Ufulu uwu suli wokhala ndi polekezera umene anthu amayembekezera pamene akana wolamulira wina wandale zadziko kapena mpangidwe wa boma moyanja wina. Mmalo mwake, umafika pachimake penipeni pa mavuto a anthu. Chimene Yesu anali kulankhula chinali kumasuka ku uchimo, nsinga zaukapolo ku uchimo. (Wonani Yohane 8:24, 34-36.) Chotero ngati munthu akhala wophunzira wowona wa Yesu Kristu, izi zimachititsa kusintha kowoneka m’moyo wake, chimasuko.
7. (a) Pamenepa, kodi ndimulingaliro lotani, mu limene tingakhale aufulu ku uchimo tsopano lino? (b) Kuti tikhale ndi ufulu umenewo, kodi tiyenera kuchitanji?
7 Ichi sichitanthauza kuti panthawi ino Akristu owona samamvanso ziyambukiro za chikhoterero chobadwa nacho cha mkhalidwe wauchimo. Mmalo mwake, iwo ali ndi nkhondo chifukwa cha uwo. (Aroma 7:21-25) Koma ngati munthu akhaladi ndi moyo mogwirizana ndi ziphunzitso za Yesu, iye sadzakhalanso kapolo woluluzika wauchimo. Uchimo sudzakhalanso kwa iye monga mfumu yopereka malangizo amene iye amawamvera. Iye sadzakodwanso m’njira yamoyo yopanda chifuno ndi imene imamsiya ali ndi chikumbumtima chovutitsidwa. Iye adzakhala ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu chifukwa chakuti machimo akale akhululukidwa pamaziko a chikhulupiriro chake munsembe ya Kristu. Zikhoterero zauchimo zingayeseyese kudzipezera malo, koma pamene akana kuchita mogwirizana nazo chifukwa chakuti akukumbukira ziphunzitso zoyera za Kristu adzasonyeza kuti uchimo suli mbuye pa iye.—Aroma 6:12-17.
8. (a) Kodi ndiufulu wina wotani umene Chikristu chowona chimatipatsa? (b) Kodi ndimotani mmene uwu uyenera kuyambukirira mkhalidwe wathu kulinga kwa olamulira audziko?
8 Monga Akristu timasangalala ndi ufulu wochuluka. Tamasulidwa ku ziyambukiro za ziphunzitso zonyenga, ku nsinga za kukhulupirira malaulo ndi ukapolo ku uchimo. Chowonadi chodabwitsa cha mkhalidwe wa akufa ndi chiukiriro chatimasula ku mantha opanda pake a imfa yachiwawa imene imachititsa anthu kupondereza chikumbumtima chawo. Chidziwitso chakuti maboma aumunthu opanda ungwiro adzalowedwa mmalo ndi Ufumu wolungama wa Mulungu chimatimasula ku mkhalidwe wopanda chiyembekezo. Koma ufulu umenewo sumalungamitsa kunyalanyazidwa kwa lamulo kapena kunyozera akuluakulu a boma pamaziko akuti posachedwapa dongosolo lakale lidzachoka.—1 Pet. 2:16, 17; Tito 3:1, 2.
9. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova mwachikondi watithandizira kusangalala ndi mlingo waukulu koposa wa ufulu umene tsopano uli wothekera kwa anthu? (b) Popanga zosankha, kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti timazindikira bwino chimene chinali chotulukapo cha kugwiritsira ntchito molakwa ufulu wake kwa Adamu?
9 Yehova samatisiya kuti tidziwonere njira yabwino koposa yokhalira ndi moyo. Amadziwa mmene tapangidwira, chimene chidzatibweretsera chikhutiro chenicheni ndi lingaliro la kumva kukhala wolemekezeka, ndi chimene chidzakhala chopindulitsa chokhalitsa koposa kwa ife. Amadziwanso nthawi yake yoikika ya kuchitira chifuno chake ndipo, choteronso, ntchito zimene ziri zopindulitsa kopambana kwa ife kuzichita. Mofananamo amadziwa ziganizo ndi khalidwe zimene zingaluluze munthu kapena kuwononga unansi wake ndi ena, ngakhale kumlepheretsa madalitso a Ufumu wa Mulungu. Mwachikondi amatiululira zinthu zimenezi kupyolera mwa Baibulo ndi mwanjira ya gulu lake lowoneka. (Agal. 5:19-23; Marko 13:10; yerekezerani 1 Timoteo 1:12, 13.) Ndiyeno ziri kwa ife, kugwiritsira ntchito ufulu woperekedwa ndi Mulungu, kusankha mmene tidzachitira. Ngati talabadira chimene Baibulo limatiuza za mmene Adamu anatayira ufulu woperekedwa kwa anthu pachiyambi, tidzapanga zosankha zimenezo mwanzeru. Tidzasonyeza kuti unansi wabwino ndi Yehova ndiwo nkhawa yathu yaikulu m’moyo.
Kulakalaka Mtundu Wina wa Ufulu
10. Kodi ndimtundu wanji wa ufulu umene ena amene anadzitcha kukhala Akristu aukalimira?
10 Panthawi zina ana ena oleredwa monga Mboni za Yehova, kuphatikizapo ena osakhala achicheperepo, amakhala ndi malingaliro akuti akufuna mtundu wina waufulu. Dziko lingawonekere lokongola, ndipo pamene alingalira kwambiri za ilo ndi pamene chikhumbo chawo cha kuchita zinthu zimene anthu audziko amachita chimakhalanso champhamvu. Iwo sangalinganize kuledzera ndi mankhwala oledzeretsa, kumwa mopambanitsa kapena kuchita dama lachigololo. Koma amayamba kuwonongera nthawi ya pambuyo pasukulu kapena maola a pambuyo pa ntchito ndi mabwenzi audziko. Ndithudi, iwo akufuna kukhala ovomerezedwa ndi mabwenzi awo atsopano, chotero ayamba kutsanzira malankhulidwe awo ndi khalidwe lawo.—3 Yoh. 11.
11. Kodi nkuchokera kuti kumene zonyenga za kuchita ichi nthawi zina zimachokera?
11 Nthawi zina chisonkhezero cha kudzilowetsa m’khalidwe laudziko chimachokera kwa munthu wina wodzitcha kukhala akutumikira Yehova. Ndicho chimene chinachitika mu Edeni pamene Satana ananyenga Hava, ndiyeno pamene Hava anasonkhezera Adamu kugwirizana naye. Zinalinso choncho pakati pa Akristu oyambirira, ndipo chinthu chofanana chimachitika m’tsiku lathu. Kawirikawiri anthu oterowo amakonda zosangalatsa ndipo amakhumba zinthu zimene zimabweretsa chikondwerero chachikulu. Amasonkhezera ena “kukondwera.” Iwo ‘amalonjeza ufulu, pamene iwo eniwo ali akapolo a chivundi.’—2 Pet. 2:18, 19.
12. (a) Kodi nchiyani chiri zotulukapo zomvetsa chisoni za khalidwe laudziko? (b) Ngati ophatikizidwawo adziwa zotulukapo, kodi nchifukwa ninji iwo amaumirira kuchita zinthu zotero?
12 Chotulukapo sichiri chokondweretsa. Kugonana kosaloledwa kumachititsa kuvutika kwa maganizo. Kungachititsenso nthenda, mimba zosafunika ndipo mwinamwake kusweka kwa ukwati. (Miy. 6:32-35; 1 Akor. 6:18; 1 Ates. 4:3-8) Kugwiritsira ntchito mankhwala molakwa kungachititse kukhala wamtima wapachala, kulankhula kotukwana, kusawona bwino, chizwezwe, kusapuma bwino, kuwona zimene kulibe ndi imfa. (Yerekezerani ndi Miyambo 23:29-35.) Kungachititse kumwerekera, kumene kungatsogolere ku kuchita upandu m’kuchirikiza chizolowezicho. Kawirikawiri awo amene amamwerekera m’khalidwe limenelo amadziwa chimene chingakhale chotulukapo chake. Koma kulalaka kwawo kukondwera ndi chisangalalo cha maganizo kumawachititsa kunyalanyaza zotulukapo. Amadziuza kuti ndiwo ufulu, koma pambuyo pake amadzazindikira, atachedwa kwambiri kuti ali akapolo auchimo, ndipo ha ndi mbuye wankhalwe chotani nanga mmene uchimo uliri! Kulingalira nkhaniyo tsopano lino kungathandize kutitetezera ku kukhala ndi chokumana nacho chotero.—Agal. 6:7, 8.
Pamene Mavutowo Amayambira
13. (a) Kodi ndimotani mmene kawirikawiri zikhumbo zimene zimatsogolera ku mavuto amenewa zimasonkhezedwera? (b) Kuti timvetsetse chimene “mayanjano oipa” ali, kodi ndilingaliro layani limene tifunikira? (c) Pamene muyankha mafunso pa mapeto a ndime iyi, gogomezerani lingaliro la Yehova. Yankhani funso limodzi lokha panthawi imodzi.
13 Imani ndi kuganiza kumene kawirikawiri mavuto amenewo amayambira. Baibulo limalongosola kuti: “Aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, nichimnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.” (Yak. 1:14, 15) Koma kodi zikhumbo zimenezo zomasonkhezeredwa motani? Mwa zimene zimalowa m’maganizo, ndipo kawirikawiri izi ziri monga chotulukapo cha kuyanjana ndi anthu amene samagwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo. Ndithudi, tonsefe timadziwa kuti tiyenera kupewa “mayanjano oipa.” Koma funso nlakuti, Kodi ndi mayanjano ati ali oipa? Kodi ndimotani mmene Yehova amaiwonera nkhaniyo? Kusinkhasinkha pa mafunso otsatira ndi malemba kuyenera kutithandiza kufika pa zosankha zoyenera.
Kodi chenicheni chakuti anthu ena akuwonekera kukhala olemekezeka chimatanthauza kuti adzakhala mabwenzi abwino? (Yerekezerani ndi Genesis 34:1, 2, 18, 19)
Kodi makambitsirano awo, mwinamwake njerengo zawo, zingasonyeze kuti kaya tingachite nawo ubwenzi? (Aef. 5:3, 4)
Kodi pali chifukwa chirichonse chotidetsa nkhawa ngati iwo sakhulupirira zinthu zofanana ndi zimene timakhulupirira ponena za chifuno cha Mulungu? (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 15:12, 32, 33.)
Kodi ndimotani mmene Yehova akalingalirira ngati tisankha mabwenzi pakati pa anthu amene samamkonda? (Yerekezerani 2 Mbiri 19:1, 2.)
Ngakhale kuli kwakuti tingagwire ntchito ndi osakhulupirira kapena kupita nawo kusukulu, kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti sitikuwasankha iwo kukhala mabwenzi? (1 Pet. 4:3, 4)
Kuwonera televizheni ndi kuwerenga mabukhu, magazine ndi manyuzipepala nakonso ndiko njira ya kuyanjana ndi ena. Kodi ndichidziwitso cha mtundu uti kuchokera kumagwero amenewa chimene pali kufunika kwapadera kwa kusamala masiku ano? (Miy. 3:31; Yes. 8:19; Aef. 4:17-19)
Kodi nchiyani chimene kusankha kwathu mabwenzi kumauza Yehova ponena za mtundu wa anthu amene ife tiri? (Sal. 26:1, 4, 5; 97:10)
14. Kodi ndiufulu waukulu wotani uli patsogolopa kaamba ka onse ogwiritsira ntchito uphungu wa Mawu a Mulungu mokhulupirika tsopano lino?
14 Posachedwapa patsogolo pathupa pali Dongosolo Latsopano la Mulungu. Mwa Ufumu Wake anthu adzamasulidwa pa chisonkhezero chomanga ukapolo cha Satana ndi dongosolo lake lonse loipa la zinthu. Pang’ono pang’ono ziyambukiro zonse zauchimo zidzachotsedwa mwa anthu. Moyo wosatha m’Paradaiso udzakhala pamaso pawo. Potsirizira pake chilengedwe chonse chidzakhala ndi ufulu umene uli wogwirizana kotheratu ndi ‘mzimu wa Yehova.’ (2 Akor. 3:17) Kodi kungakhale kwanzeru kudziika paupandu wa kutaikiridwa ndi zonsezo chifukwa cha kululuza uphungu wa Mawu a Mulungu tsopano? Mwanjira imene tikugwiritsirira ntchito ufulu wathu Wachikristu lerolino tonsefe tisonyezetu bwino lomwe kuti chimene tikufunadi ndicho “ufulu wa ulemerero wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.
Makambitsirano a Kupenda
● Kodi ndiufulu wamtundu wanji umene anthu awiri oyamba anasangalala nawo? Kodi ndimotani mmene umenewo umayerekezedwera ndi zimene anthu akuvutika nazo tsopano?
● Mosiyana ndi dziko, kodi ndiufulu wotani umene Akristu owona alinawo? Kodi uwu uli wotheka motani?
● Kodi ndimtengo wotani umene umalipiridwa ndi awo ofunafuna mtundu wa ufulu umene dziko lirinawo?
● Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kupewa “mayanjano oipa”? Mosiyana ndi Adamu, kodi nzosankha zayani ponena za chimene chiri choipa zimene timavomereza?