Mutu 23
Kumbukirani Kuyandikira kwa Tsiku la Yehova
1. (a) Pamene kwanthawi yoyamba munamva kuti kuwomboledwa ku zisoni za dongosolo lino lakale lazinthu kunali pafupi, kodi munachita motani? (b) Kodi ndimafunso otani onena za ichi amene tiyenera kupenda mwamphamvu?
MOSAKAIKIRA chimodzi cha zinthu zimene munaphunzira kuchokera m’phunziro la Baibulo chinali chakuti chilanditso ku zopweteka zamoyo m’dongosolo liripoli lazinthu chayandikira. (Luka 21:28) Munafikira pa kuzindikira kuti chifuno cha Mulungu nchakuti dziko lonse lapansi likhale Paradaiso. Upandu, nkhondo, matenda ndi imfa sizidzakhalakonso, ndipo ngakhale okondedwa akufa adzakhalanso ndi moyo. Ha nchiyembekezo chokondweretsa mtima chotani nanga! Kuyandikira kwa zonsezo kunagogomezeredwa ndi umboni wakuti kukhalapo kosawoneka kwa Kristu monga Mfumu yolamulira kunayamba mu 1914 C.E. ndi kuti kuyambira pa nthawiyo takhala tiri m’masiku otsiriza a dziko loipa lino. Kodi chidziwitso chimenecho chachititsa masinthidwe m’moyo wanu? Kodi njira yanu ya moyo imasonyezadi chikhutiro chakuti “tsiku la Yehova” liri pafupi?
2. (a) Kodi ndiliti pamene “tsiku la Yehova” lidzadza? (b) Kodi ndimotani mmene chenicheni chakuti Yehova sanaulule “tsiku kapena ola” chatsimikizira kukhala chopindulitsa?
2 Malemba amasonyeza poyera kuti “mbadwo” umene unawona chiyambi cha kukhalapo kwa Kristu ukawonanso “tsiku lalikulu la Yehova” mu limene adzapereka chiweruzo motsutsana ndi onse ochita zoipa. (Mat. 24:34; Zef. 1:14–2:3) “Mbadwo” umenewo tsopano wakalamba kwambiri. Koma Baibulo silimanena mwachindunji deti lenileni limene Yesu Kristu adzadza monga wopereka chiweruzo wa Yehova motsutsana ndi dongosolo lazinthu ladziko lapansi la Satana. “Koma za tsiku ilo, kapena nthawi yake sadziwa munthu, ngakhale angelo m’Mwamba, ngakhale Mwana, koma Atate,” anatero Yesu. (Marko 13:32) Uku kwakhala kopindulitsa kwambiri. Mwanjira yotani? Kwathandiza kusonyeza chimene chiri m’mitima ya anthu. Ngati ena sakukondadi Yehova, amakhoterera kukukankhira patsogolo “tsiku” lake m’maganizo mwawo ndi kutembenukira kukulondola zinthu zadziko ku zimene mitima yawo yakhoterererako. Yehova amavomereza monga atumiki ake awo okha amene amamkondadi ndi amene amakusonyeza mwa kumtumikira ndi mtima wonse, mosasamala kanthu za nthawi imene mapeto a dongosolo loipali akadza. Chivomerezo cha Mulungu ndi Mwana wake sichiri pa awo amene ali ofunda kapena a mitima iwiri.—Chiv. 3:16; Sal. 37:4; 1 Yoh. 5:3.
3. Kodi nchiyani chimene Yesu ananena monga chenjezo kwa ife pankhaniyi?
3 Mwa mawu ochenjeza kwa okonda Yehova, Yesu anati: “Yang’anirani, dikirani, pakuti simudziwa inu nthawi yake.” (Marko 13:33-37) Iye akutilimbikitsa kusalola kudya ndi kumwa kapena “nkhawa za moyo” kutenga mbali yaikulu ya chisamaliro chathu kotero kuti titaikiridwa ndi lingaliro lakuwopsa kwa nthawi.—Luka 21:34-36; Mat. 24:37-42.
4. Monga momwe Petro analongosolera, kodi nchiyani chimene “tsiku la Yehova” lidzabweretsa?
4 Pambuyo pake, mtumwi Petro anapereka uphungu kwa onse okhala ndi chikhulupiriro chowona ‘kuyembekezera ndi kukumbukira kukhalapo kwa tsiku la Yehova, m’limene miyamba potenthedwa ndi moto idzasungunuka ndi zam’mwamba zidzasungunuka chifukwa cha kutentha kwakukulu.’ Kuyandikira kwa “tsiku la Yehova” kuli chowonadi chimene palibe aliyense wa ife ayenera kunyalanyaza. Posachedwapa miyamba ya maboma owoneka ndi chitaganya cha anthu oipa zidzalowedwa mmalo ndi “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” za Mulungu, ndipo “zinthu” zonse zimene zimayendera limodzi ndi dongosolo lamakono lazinthu—makhalidwe ake a kudzigangira, mkhalidwe wake wachisembwere ndi kukondetsa zinthu zakuthupi—zidzathetsedwa m’kutentha kowononga kwa “tsiku la Yehova.” (2 Pet. 3:10-13) Tifunikira kukhala maso, kuzindikira kuti zochitika zowononga dziko izi zingayambe pamphindi iriyonse.—Mat. 24:44.
Khalani Maso ku Zochitika Zokwaniritsa Chizindikiro
5. (a) Kodi yankho la Yesu la funso lolembedwa pa Mateyu 24:3 limagwira ntchito pa mlingo wotani kumapeto a dongosolo Lachiyuda? (b) Kodi ndimagawo ati a yankho lake amene amasumika chisamaliro pa zochitika zoyambira 1914 kumkabe mtsogolo?
5 Makamaka polingalira nthawi imene tikukhalamo ndi moyo, tiyenera kukhala ozolowerana bwino ndi zochitika za chizindikiro cha chiungwe chodziwikitsa “masiku otsirza” kapena “mapeto a dongosolo lazinthu.” Kuti tiwerenge chizindikiro molondola, tiyenera kukumbukira kuti pamene Yesu anayankha funso la ophunzira ake lolembedwa pa Mateyu 24:3, zina za zimene ananena zinagwira ntchito kumapeto a dongosolo Lachiyuda m’zaka za zana loyamba, koma kugwira ntchito kwake kwakukulu kunafika patali koposa pamenepo. Chimene analongosola m’vesi 4 mpaka 22 chinali ndi kukwaniritsidwa pamlingo waung’ono pakati pa 33 ndi 70 C.E. Koma ulosiwo unali ndi kukwaniritsidwa kwake kwakukulu m’tsiku lathu ndipo umadziwikitsa nyengo yoyambira 1914 C.E. kukhala nthawi ya ‘kukhalapo kwa Kristu ndi yamapeto a dongosolo lazinthu.’ (Ndiponso Marko 13:5-20 ndi Luka 21:8-24) Mateyu 24:23-28 amasimba zimene zikanachitika kuyambira 70 C.E. kumka mtsogolo mpaka m’nthawi ya kukhalapo kwa Kristu. (Ndiponso Marko 13:21-23) Ponena za zochitika zolongosoledwa kuchokera pa Mateyu 24:29 kufikira kumapeto a mutu 25, izi zikusonya kunyengo yoyambira 1914 C.E.—Ndiponso Marko 13:24-37 ndi Luka 21:25-36.
6. (a) Kodi nchifukwa ninji ife enife tiyenera kukhala maso ponena za mmene zochitika zamakono zikukwaniritsira “chizindikiro”? (b) Yankhani mafunso pamapeto a ndime ino osonyeza mmene “chizindikiro” chakwaniritsidwira kuyambira 1914.
6 Ife sindife amene tiyenera kukhala oyang’anitsitsa a zochitika zamakono zimene zimakwaniritsa “chizindikiro.” Kugwirizanitsa kwathu zochitika zimenezi ndi ulosi wa Baibulo kudzatithandiza kupitirizabe “kukumbukira” tsiku la Yehova. Kudzatikhozetsanso kukhala ogwira mtima pochenjeza ena za kuyandikira kwa “tsiku la kubwezera la Mulungu wathu.” (Yes. 61:1, 2) Muli ndi zolinga zimenezi m’maganizo, pendani mbali zotsatirazi za “chizindikiro.”
Kodi ndim’njira yapadera iti imene kuukirana konenedweratuko kwa ‘mtundu wina ndi mtundu ndi ufumu ndi ufumu wina’ kunakwaniritsidwa kuyambira 1914 C.E.? Kodi nchiyani chimene chachitika ngakhale m’miyezi yaposachedwapa chimene chimawonjezera kukukwaniritsidwaku?
Kodi kuperewera kwa chakudya kwayambukira kumlingo wotani dziko lapansi mosasamala kanthu za chidziwitso cha sayansi cha m’zaka za zana la-20?
Kodi pakhaladi kusiyana kulikonse m’kubwerezabwereza kwa zivomezi m’malo akutiakuti chiyambire 1914 C.E.?
Mu 1918 kodi ndimliri wanji umene unapha anthu ambiri koposa nkhondo yadziko? Mosasamala kanthu za chidziwitso cha zamankhwala, kodi ndinthenda zotani zimene zikali za ukulu wa miliri?
Kodi ndi umboni wotani umene mukuwona wakuti anthu akukomokadi ndi mantha, monga kunanenedweratu pa Luka 21:26?
Kodi nchiyani chimene chimakukhutiritsani maganizo kuti mikhalidwe yolongosoledwa mu 2 Timoteo 3:1-5 siri chabe mmene moyo wakhalira nthawi zonse koma kuti ikukula kufikira mlingo wochititsa mantha pamene tikuyandikira mapeto a masiku otsiriza?
Kulekanitsidwa kwa Anthu
7. (a) Kodi nchochitika china chotani, cholongosoledwa pa Mateyu 13:36-43, chimene Yesu anagwirizanitsa ndi mapeto a dongosolo lazinthu? (b) Kodi fanizolo limatanthauzanji?
7 Palinso zochitika zina zapadera zimene Yesu anazigwirizanitsa kwambiri ndi mapeto a dongosolo lazinthu. Chimodzi cha izi ndicho kulekanitsidwa kwa “ana a ufumu” kuchokera ku “ana a oipayo.” Yesu analankhula za ichi m’fanizo lake lamunda wa tirigu umene mdani anabzalamo namsongole wambiri. M’fanizo lake “tirigu” amaimira Akristu odzozedwa owona. “Nansongole” ndiwo Akristu achiphamaso. M’nthawi yamapeto ya dongosolo lazinthu “nansongole”—awo odzinenera kukhala Akristu koma amene amatsimikizira kukhala “ana a woipayo” chifukwa chakuti amamamatira kudziko limene Mdyerekezi ali wolamulira wake—amalekanitsidwa ndi “ana aufumu [wa Mulungu]” ndipo akuyembekezera chiwonongeko. (Mat. 13:36-43) Kodi izi zachitikadi?
8. (a) Pambuyo pa Nkhondo Yadziko I, kodi nkulekanitsidwa kwakukulu kotani kwa odzinenera kukhala Akristu kumene kunachitika? (b) Kodi ndimotani mmene Akristu odzozedwa owona amaperekera umboni wakuti ndithudi, iwo anali, “ana aufumu”?
8 Ndithudi, pambuyo pa Nkhondo Yadziko I panali, kulekanitsidwa kwakukulu kwa anthu onse amene anadzinenera kukhala Akristu m’timagulu tiwiri: (1) Atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu ndi otsatira awo, amene anadziwika mwa kuchirikiza kwawo mwamphamvu Chigwirizano cha Amitundu (tsopano Mitundu Yogwirizana), pamene akuumirirabe ku utundu wawo. (2) Akristu odzozedwa owona owerengeka kwambiri a m’nyengo ya pambuyo pa nkhondo imeneyo, amene anapereka chichirikizo chathunthu ku Ufumu Waumesiya wa Mulungu. Mwachichirikizo chapoyera cha maboma adziko monga njira yopezera mtendere ndi chisungiko, kagulu koyambako kananena poyera kuti sikanali Akristu owona. (Yoh. 17:16) Mosiyana, atumiki a Yehova anadziwikitsa molondola Chigwirizano cha Amitundu monga “chonyansa cha kupululutsa” chamakono chotchulidwa m’Mateyu 24:15. Podzidziwikitsa iwo eni kukhala “ana a ufumu [wa Mulungu],” iwo anayamba kulalikidwa kwa “mbiri yabwino imeneyi yaufumu . . . m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu.” (Mat. 24:14, NW) Nzotulukapo zotani?
9. Kodi nchiyani chimene chinali chotulukapo cha ntchito ya kulalikira Ufumu iyi?
9 Choyamba, panali kusonkhanitsidwa kwa otsalira a “osankhidwa,” Akristu odzozedwa ndi mzimu. Ngakhale kuli kwakuti anali obalalikira kwambiri pakati pa mitundu, monga ngati kuti anali ku “mphepo zinai,” motsogozedwa ndi angelo anasonkhanitsidwa pamodzi m’chigwirizano cha gulu.—Mat. 24:31.
10. (a) Kodi ndimotani mmene ntchito yowonjezereka ya kulekanitsa yachitidwira, ndipo mogwirizana ndi ulosi uti? (b) Kodi kukwaniritsidwa kwa maulosi amenewa kumatanthauzanji?
10 Pamenepo, monga momwe Yesu analoserera, anayamba kulekanitsa anthu a mitundu yonse, “monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi.” Ntchitoyi, yotsogozedwa ndi Kristu kuchokera pampando wake wachifumu wakumwamba, ikupitirizabe mpaka lerolino, ndipo inu mwininu mukuyambukiridwa nayo. Unyinji wa anthu umakana Ufumu wa Mulungu ndi “ana” ake odzozedwa ndi mzimu ndipo chotero adzapititsidwa ku “kudulidwa kosatha” mu imfa. Komabe, kwa enawo Ambuye akuwapatsa chiitano cha kulowa gawo ladziko lapansi la Ufumu wake, ncholinga cha moyo wosatha. Anthu onga nkhosa amenewa adzigwirizanitsa ndi “ana aufumu” odzozedwawo, ngakhale kuti awa ali mikhole ya chizunzo chankhalwe. (Mat. 25:31-46) Mokhulupirika amathandiza kufalitsa uthenga wofunika wa Ufumu. Khamu lalikulu lofika chiwerengero chokwanira mamiliyoni chikukhala ndi phande m’ntchitoyi. Uthenga wa Ufumu ukumvedwa kumalekezero a dziko lapansi. Kodi zochitikazi zikutanthauzanji? Kuti tiri pafupi kwambiri ndi mapeto a “masiku otsiriza” ndi kuti “tsiku la Yehova” layandikira.
Kodi Patsogolopa Pali Chiyani?
11. Kodi pali ntchito yolalikira yowonjezereka yofunikira kuchitidwa “tsiku la Yehova” lisanafike?
11 Kodi pakali maulosi ofunikira kukwaniritsidwa tsiku lalikulu ndi lochititsa mantha la Yehova lisanayambe? Inde! Kulekanitsidwa kwa anthu pankhani ya Ufumu sikunathebe. M’madera ena kumene kwa zaka zambiri kunali chitsutso chachikulu, tsopano kukukololedwa zotuta zochuluka za ophunzira. Ndipo ngakhale kumene anthu akukana mbiri yabwino, chilungamo cha Yehova ndi chifundo zikuchirikizidwa mwa kupereka kwathu umboni. Chotero haya ndi ntchito! Yesu akutitsimikizira kuti, pamene itsirizidwa, “mapeto adzafika.”—Mat. 24:14, NW.
12. (a) Monga momwe kwasonyezedwera pa 1 Atesalonika 5:2, 3, kodi nchochitika chapadera chotani chimene chiti chichitike? (b) Kodi chidzatanthauzanji kwa ife?
12 Ulosi wina wa Baibulo wokhala ndi tanthauzo lalikulu ukuneneratu kuti: “Pamene kuli kwakuti iwo akunena: ‘mtendere ndi chisungiko!’ Pamenepo chiwonongeko chamwadzidzidzi chidzawafikira mofanana ndi zowawa za sautso pa mkazi wa pakati; ndipo iwo mwa njira iriyonse sadzapulumuka.” (1 Ates. 5:2, 3, NW) Kuti chilengezo chimenecho cha “mtendere ndi chisungiko chidzakhala mu mpangidwe wotani tidzawona. Koma ndithudi sichidzatanthauza kuti atsogoleri adziko athetsadi mavuto a anthu. Awo amene “akukumbukira” tsiku la Yehova sadzasokeretsedwa ndi chilengezo chimenecho. Amadziwa kuti, modzidzimutsa pambuyo pa nthawiyo, “chiwonongeko chamwadzidzidzi” chidzadza.
13. Kodi nzochitika zotani zimene zidatsatira mwamsanga pambuyo pa chilengezo cha “mtendere ndi chisungiko,” ndipo dongosolo lotani?
13 Choyamba, monga momwe Malemba amasonyezera, olamulira andale zadziko, pamlingo wa pa dziko lonse, adzaukira Babulo Wamkulu, ulamuliro wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, ndi kumuwononga. (Chiv. 17:15, 16) Kulidi koyenera kuzindikiridwa kuti mkhalidwe waudani makamaka kulinga ku zipembedzo za Dziko Lachikristu ngakhale tsopano ukuwonekadi. Maboma okhala ndi malamulo otsutsa chipembedzo akugwiritsira ntchito kale chisonkhezero champhamvu m’Mitundu Yogwirizana, ndipo anthu onse iwo eniwo m’maiko a zipembedzo zamakolo akuchoka m’zipembedzo zamakolo awo mu unyinji wawo. Kodi zonsezi zikutanthauzanji? Kuti chionongeko cha chipembedzo chonyenga chiri pafupi. Pambuyo pa zimenezo, pamene monyang’wa mitundu itembenuka, kotheratu, kuukira awo ochirikiza ufumu wa Yehova, mkwiyo wa Mulungu udzayakira maboma a ndale zadziko ndi ochirikiza awo, zikumachititsa chiwonongeko chotheratu pa iwo onse. Potsirizira, Satana iyemwiniyo ndi ziwanda zake adzaponyedwa m’phompho, oletsedwa kotheratu kusonkhezera anthu. Ndithudi iri lidzakhala “tsiku la Yehova,” tsiku limene dzina lake lidzakwezedwa pamwamba.—Ezek. 38:18, 22, 23; Chiv. 19:11–20:3.
14. Kodi nchifukwa ninji kukanakhala kupusa kulingalira kuti tsiku la Yehova likali patali?
14 Lidzadza panthawi yeniyeni, mogwirizana ndi programu ya Mulungu. Silidzachedwa. (Hab. 2:3) Kumbukirani, chiwonongeko mu 70 C.E. chinadza mofulumira, pamene Ayuda sanachiyembekezere, pamene analingalira kuti upandu unali utatha. Ndipo bwanji ponena za Babulo wakale? Anali wamphamvu, wachidaliro, wokwetezedwa ndi malinga amphamvu. Koma anagwa mu usiku umodzi. Choteronso, “chiwonongeko chamwadzidzidzi” chidzadza padongosolo lazinthu loipa liripoli. Pamene chidzatero, tipezedwetu tiri ogwirizanitsidwa m’kulambira kowona, ‘titakumbukira kuyandikira’ kwa tsiku la Yehova.
Makambitsirano Openda
● Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika “kukumbukira” tsiku la Yehova? Kodi ndimotani mmene tingachitire motero?
● Kodi ndimotani mmene ife timayambukidwira mwachindunji ndi kulekanitsidwa kwa anthu kumene kuli kuchitika?
● Kodi nchiyani chimene chikali patsogolopa tsiku la Yehova lisanayambe? Chotero kodi nchiyani chimene ife enife tiyenera kukhala tikuchita?