Mutu 14
Mmene “Miyamba Yatsopano ndi Dziko Lapansi Latsopano” Zikuyambira
KUTCHULIDWA kwa miyamba kumapangitsa anthu ambiri kulingalira za kutali m’mlengalenga, mwezi ndi nyenyezi. Baibulo limagwirizanitsanso “kumwamba” ndi ulamuliro. (Machitidwe 7:49) Nthaŵi zina limagwiritsira ntchito mawuwo “kumwamba” kutanthauza Mulungu mwiniyo monga Wolamulira Wachilengedwe chonse. (Danieli 4:26; Mateyu 4:17) Ngakhale maboma ali ndi malo antchito apamwamba pa nzika zawo. (2 Petro 3:7) Mofananamo, “dziko lapansi” kaŵirikaŵiri linatanthauza nthaka, koma lingatanthauzenso anthu onse. (Genesis 11:1; Salmo 96:1) Kuzindikiridwa kwa zimenezi kungakuthandizeni kudziŵa tanthauzo la malonjezo ochititsa chidwi onena za “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” Ena a malonjezano amenewa anali ndi kukwaniritsidwa koyamba m’nthaŵi ya Israyeli wakale.
‘SANGALALANI NDI CHIMENE NDILENGA’
2 Mtundu wa Israyeli unali m’pangano ndi Mulungu, pokhala utavomereza mwalumbiro kumumvera. Koma iwo anakhala osakhulupirika. Chifukwa cha zimenezi, Yehova analengeza kuti akachotsa tchinjirizo lake, kulola Yerusalemu kuwonongedwa ndi anthuwo kutengeredwa mu undende mu Babulo. (Yesaya 1:2-4; 39:5-7) Koma mwachifundo ananeneratunso kubwezeretsedwa kwa otsalira olapa.—Yesaya 43:14, 15; 48:20.
3 Chifukwa cha kutsimikizirika kwa zimenezi, Yehova anatchula kubwezeretsedwa kwamtsogolo kumeneko monga ngati kuti kunali nkuchitika kale, kuti: “Pakuti tawonani ndikulenga miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano; ndipo zinthu zakale sizidzakumbukika, kapena kuloŵanso mu mtima. Koma kondwerani anthu inu, ndi kusangalala nthaŵi zonse ndi chimene ndikulenga. Pakuti tawonani ndikulenga Yerusalemu wochititsa chisangalalo ndipo anthu ake ochititsa chikondwerero.” (Yesaya 65:17, 18, NW) Kumeneku kukanatanthauza kulanditsidwa kwa Aisrayeli olapa amenewo.
4 Ngakhale kuli kwakuti chinthu chotero chidawonekera kukhala chosatheka mwalingaliro la anthu, Babulo wamphamvuyo anagonjera kwa Amedi ndi Aperisi mu 539 B.C.E. Ayuda anadzakhala pansi pa boma latsopano, “miyamba yatsopano.” Koresi Wamkulu anali ndi malo antchito apamwamba mu “miyamba yatsopano” imeneyo. Ngakhale kuli kwakuti Koresi sanakhale wotembenukira ku Chiyuda, iye anazindikira kuti Yehova anamlola kukhala ndi ulamuliro umene anali nawo ndi kuti Yehova analamulira kuchititsa kachisi m’Yerusalemu kumangidwanso. (2 Mbiri 36:23; wonani Yesaya 44:28.) Atabwerera m’Yerusalemu mu 537 B.C.E., Wolamulira Zerubabele ndi Yesuwa Mkulu wa Ansembe anatumikiranso mwachiwonekere mu “miyamba yatsopano ya boma” imeneyo ndipo otsalira Achiyuda obwezeretsedwawo adapanga “dziko lapansi latsopano,” chitaganya choyeretsedwa chimene chinabwezeretsanso kulambira koyera m’dzikolo.—Ezara 5:1, 2.
5 Monga umboni wakuti m’maganizo ndi m’mtima momwe anali anthu osasinthidwa, iwo anafunikira kuika zinthu za kulambira koyera poyamba m’miyoyo yawo, kulemekezadi ulamuliro wa Yehova ndi kumvera aneneri ake. Mogwirizana ndi zimenezi, pakati pa zinthu zoyamba zimene anachita pamene anafika ku Yuda panali “kumanga guwa lansembe la Mulungu wa Israyeli” ndi kupereka nsembe.—Ezara 3:1-6.
6 Pamene zikhoterero zokondetsa zinthu zakuthupi ndi kuwopa anthu zinawalepheretsa kutha kwa kumangidwa kwa kachisi, Yehova anadzudzula anthuwo kupyolera mwa aneneri ake, ndipo iwo analabadira. (Hagai 1:2, 7, 8, 12; 2:4, 5) Pambuyo pake, pamene kulephera kwakukulu kugwirizana ndi zofunika za Chilamulo zonena za ukwati kunasonyezedwa, anthuwo anawongolera njira zawo. (Ezara 10:10-12) Mmalo mwa kukhala ndi maso amene, mophiphiritsira, sanawone ndi makutu amene anali ogontha ku mawu a Mulungu, iwo analandira kuchiritsidwa kwauzimu nagwiritsira ntchito maganizo awo mogwirizana ndi chifuniro cha Yehova. (Yerekezerani ndi Yesaya 6:9, 10 ndi 35:5, 6) Chifukwa cha chimenecho, Mulungu anawalemereretsa mogwirizana ndi malonjezo opezeka pa Yesaya 65:20-25.
7 Koma kodi nzokhazo zimene zinalipo m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wonena za “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano”? Ndithudi ayi. Mtumwi Wachikristu Petro analongosola kuti Akristu a m’zaka za zana loyamba analinkuyembekezera mwaphamphu kukwaniritsidwa kwina. (2 Petro 3:13) Chimene analinkuyembekezera tsopano chinafunyululuka pamaso pathu. Mwanjira yotani? Mogwirizana ndi zochitika zimene zimaphatikizapo kuikidwa pampando wachifumu kwa Koresi Wamkulu, Yesu Kristu wolemekezedwayo.
8 Monga momwe tawonera kale, munali mu 1914 pamene Yehova Mulungu anapereka kwa Mwana wake ulamuliro wa kuyamba kulamulira pakati pa adani ake. Pamenepo “miyamba yatsopano” yoyembekezeredwa nthaŵi yaitaliyo inakhala. Chimene chinachitika chinali chachikulu kwambiri kuposa zochitika zogwirizanitsidwa ndi kuwomboledwa kwa Israyeli wakale. (Salmo 110:2; Danieli 7:13, 14) Boma limene linaberekedwa mu 1914 likulamuliradi kumwamba kwenikweniko, ndipo Mulungu walipatsa ulamuliro padziko lonse lapansi. Kukulitsidwa kwa boma limeneli kunachitika pambuyo pake ndi kuukitsidwa kwa otsatira odzozedwa ndi mzimu a Kristu (amene anali atafa kale) kukhala mafumu ndi ansembe kumwamba limodzi ndi Ambuye wawo. Pamene ziŵalo zina za kagulu Kaufumu kameneko zatsiriza moyo wawo wapadziko lapansi, izonso zawonjezeredwa ku chiŵerengero chowonjezereka cha “miyamba yatsopano.” (1 Atesalonika 4:14-17; Chivumbulutso 14:13) Unyinji waukulu kwambiri wa oloŵa nyumba anzake a Kristu tsopano ukugwira ntchito mu Ufumu wakumwamba umenewo. Motero Akristu obadwa ndi mzimu ogwirizana ndi Kristu amapanga Yerusalemu Watsopano, ponena za amene Yehova anati: “Ndikulenga Yerusalemu wochititsa chisangalalo ndipo anthu ake ochititsa chikondwerero.”—Yesaya 65:18, NW.
9 Sim’mwamba mokha komanso padziko lapansi pamene Yehova watulutsa ‘chochititsa chikondwerero.’ Otsalira a oloŵa nyumba Aufumu akali chikhalirebe padziko lapansi. Mkati mwa Nkhondo Yadziko I atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu anagwiritsira ntchito chinthenthe cha nthaŵi yankhondo kupereka zinenezo zonama pa Ophunzira Baibulo amenewa ndi kuchititsa ziŵalo za Bunge lawo Lolamulira kuweruziridwa kukhala m’ndende kwa nthaŵi yaitali. Koma mu 1919 iwo anamasulidwa, akumamasulidwadi ku ukapolo wochititsidwa ndi Babulo Wamkulu. Mochirikizidwa ndi mzimu wa Yehova, iwo anadzilinganizanso kukhala anthu odzipereka kotheratu ku kulambira kwangwiro ndi zinthu za Ufumu wa Mulungu.
10 Komabe, ziyembekezo ndi zoyembekezeredwa zawo, zinali zosiyana ndi zija za Ayuda amene anabwerera kudziko la kwawo mu 537 B.C.E. Ziŵalo za Israyeli wauzimu zinali kuyembekezera choloŵa “chosungikira m’mwamba” kaamba ka iwo. (1 Petro 1:3-5) Koma iwo asanalandiredi mphotho imeneyo, Yehova anali ndi ntchito yoti iwo achite. Ponena za imeneyi iye molosera anati: “Ndaika mawu anga mkamwa mwako; ndipo ndakuphimba ndi mthunzi wa dzanja, kuti ndikhazike kumwamba ndi kuika maziko a dziko lapansi, ndi kunena kwa Ziyoni, Inu ndinu anthu anga.” (Yesaya 51:16) Iye akuika “mawu” ake, uthenga wake, mkamwa mwa atumiki ake kuti iwo awalengeze padziko lonse lapansi. Ndi chidaliro iwo anayamba kulengeza kuti Mulungu wawoka “miyamba yatsopano” mwamphamvu kwambiri kwakuti anthu kapena ziŵanda sangaidzule. Njira mu imene Yehova wachitira ndi oimira a Ziyoni wakumwamba yawadziŵikitsa mwachiwonekere kukhala anthu ake. Mosiyana ndi mkhalidwe wapululu mwauzimu ndi mwa mkhalidwe wa dziko, “dziko” lokhalidwa ndi Israyeli wauzimu, mbali yawo ya ntchito, yakhala malo kumene zinthu zauzimu ndi ntchito zikukula. Ndilo paradaiso wauzimu! (Yesaya 32:1-4; 35:1-7; 65:13, 14; Salmo 85:1, 8-13) Koma bwanji ponena za “dziko lapansi latsopano” lonenedweratu pa Yesaya 65:17?
KULINGANIZIDWA KWA “DZIKO LAPANSI LATSOPANO”
11 Kuyambira makamaka mu 1935, Yehova anachititsa ziŵalo za Israyeli wauzimu kuwona kuti nthaŵi inali itafika ya kusonkhanitsidwa kwa khamu lalikulu la anthu okhala ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya padziko lapansi Laparadaiso. Poyerekezeredwa ndi “kagulu kankhosa” ka oloŵa nyumba Aufumu, iwo akhaladi khamu lalikulu. (Chivumbulutso 7:9, 10) Awa, nawonso, aloŵetsedwa m’paradaiso wauzimu. Anaphiphiritsiridwa ndi anthu osakhala Aisrayeli amene anasiya Babulo limodzi ndi Ayuda mu 537 B.C.E. kuphatikizapo awo amene anadzateronso pambuyo pake. (Ezara 2:58, 64, 65; 8:17, 20) Khamu lalikulu la mboni za Yehova zamakono lonseli lokhala ndi ziyembekezo zapadziko lapansi liri ziŵalo zoyembekezeredwa za “dziko lapansi latsopano.”
12 Awo amene akupulumuka chisautso chachikulu ndipo ali ndi chiyembekezo cha moyo waumunthu wangwiro pamaso pawo adzakhala atapangadi maziko a “dziko lapansi latsopano” limenelo, akumakhala ziŵalo zake zoyamba. Nkofunika kuti mazikowo akhale olimba. Motero, pakali pano iwo alinkuphunzitsidwa mokwanira njira za Yehova. Alinkuthandizidwa kuzindikira kwenikweni nkhani ya ulamuliro wa m’chilengedwe chonse. Iwo akuphunzira mmene kuliri kofunika ‘kukhulupirira Yehova ndi mtima wawo wonse ndi kusachirikizika pa luntha lawo.’ (Miyambo 3:5, 6) Iwo ali ndi mwaŵi wa kudzisonyeza kukhala ochirikiza Ufumu wa Mulungu achangu ndi okhulupirika mwa kuloŵa mokwanira m’kulalikira “mbiri yabwino imeneyi yaufumu” tsopano. (Mateyu 24:14, NW) Iwo akuwona chimene chimatanthauza kukhala mbali ya gulu lapadziko lonse m’limene anthu a m’mitundu yonse ndi zinenero ndi mafuko amagwirira ntchito limodzi mu ubale wachikondi. (Yohane 13:35; Machitidwe 10:34, 35) Kodi inu mwininu mukudzigwiritsira ntchito kotero kuti mupindule mokwanira ndi programu ya maphunziro imeneyi? Kwa onse amene akutero, ziyembekezo zodabwitsa ziri patsogolo.
“DZIKO LAPANSI LATSOPANO” LIKUKHALA LENILENI
13 Kukwaniritsidwa kotsiriza ndi kotheratu kwa lonjezo la Yehova la kukhazikitsa “dziko lapansi latsopano” kudzakhala kokulirapo kwambiri koposa zimene zinachitika kalero mu 537 B.C.E. Sikokha kuti awo amene akupanga “dziko lapansi latsopano” adzakhala anthu amene anamasulidwa ku Babulo Wamkulu, koma kuti ulamuliro wa padziko lonse wa chipembedzo chonyenga udzakhala utachotsedwa kosatha. (Chivumbulutso 18:21) Gulu la anthu lolungama limeneli—“dziko lapansi latsopano’—silidzakwetezedwa ndi mitundu imene imatonza Yehova ndi kuzunza atumiki ake, monga momwe zinaliri m’kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosi wa Yesaya. Maboma onse a anthu, chifukwa cha kukana kwawo kugonjera ku ulamuliro wa Yehova, adzakhala atafafanizidwa, ndipo gulu la anthu oipa liripoli lidzakhala litadulidwa kotheratu padziko lapansi. (Danieli 2:44; Miyambo 2:21, 22) Pamene Dongosolo Latsopano lolungama la Mulungu liyamba, anthu okha amene adzakhala pa Dziko Lapansi adzakhala awo amene amalemekeza Yehova, akumapeza chikondwerero chachikulu m’njira zake.—Salmo 37:4, 9.
14 Ndikunthaŵi yaulemerero imeneyo kumene mtumwi Petro anasonya m’kalata yake youziridwa yachiŵiri. (2 Petro 3:13) Akumasonya ku chiyembekezo chokondweretsa chimodzimodzicho, mtumwi Yohane anasimba tsatanetsatane wa vumbulutso loperekedwa kwa iye, kuti: “Ndinawona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano; pakuti kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zidachoka, ndipo kulibenso nyanja.” (Chivumbulutso 21:1, NW) Pamene chisautso chachikulu chapita ndipo Satana ndi ziŵanda zake aikidwa m’phompho, nyengo yatsopano idzayamba. Chisonkhezero choipa cha Satana ndi ziŵanda zake chidzakhala kulibe. Dongosolo lake lonse la zinthu lidzakhala litachotsedwa. Pamenepo “miyamba yatsopano” idzakwaniritsa chifuno chachikondi cha Yehova kaamba ka zolengedwa zake popanda chidodometso chirichonse chochokera ku maboma amene amanyalanyaza ulamuliro wa Yehova. Pansi pa “kumwamba kwatsopano” padzakhaladi “dziko lapansi latsopano,” lopangika ndi “khamu lalikulu” ku limene Mulungu akupereka chiyembekezo chamtengo wapatali cha moyo wopanda mapeto m’Paradaiso wa padziko lonse lapansi wokongola, wa mwana alirenji, wachimwemwe ndi mtendere. Pamene nthaŵi yoikidwiratu ya Mulungu ifika yakuti anthu akufa aukitsidwe, amenewa adzakhala ndi mwaŵi wa kukhala mbali ya “dziko lapansi latsopano” limenelo m’limene mudzakhala chilungamo.—Chivumbulutso 20:12, 13.
15 Ponena za chimene Mulungu wasungira anthu panthaŵiyo, mtumwi Yohane anamva chilengezo ichi kuchokera kumwamba: “Tawonani! Chihema cha Mulungu chiri ndi anthu, ndipo iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Ndipo Mulungu mwiniyo adzakhala nawo. Ndipo iye adzapukuta msozi uliwonse mmaso mwawo, ndipo sikudzakhalanso imfa, ngakhale kulira maliro ngakhale mfuu ngakhale kudwala sizidzakhalakonso. Zinthu zakale zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4, NW) Moyo udzakhala wokondweretsa motani nanga!
16 Mikhalidwe imene inali m’Edene ndi zozizwitsa zochitidwa ndi Yesu zimapereka masomphenya okondweretsa a chimene moyo udzakhala mu “dziko lapansi latsopano” limenelo. Ndiponso, mbali za maulosiwo pa Yesaya 11:6-9 ndi 35:1-7 ndi 65:20-25 zidzakhala ndi kukwaniritsidwa kwenikweni panthaŵiyo, ku dalitso lalikulu kwa anthu omvera. Kudzakhala kokondweretsa chotani nanga pamene mikhalidwe yofunika kwambiri ya thanzi lauzimu ndi kulemerera ingalandiridwe pamodzi ndi ungwiro wakuthupi ndi wamaganizo m’dziko lapansi limene m’njira iriyonse lakhala Paradaiso! Pokhala ndi chiyembekezo chodabwitsa chotero pamaso pathu, tingachite mosiyana motani nanga koposa kukweza mawu athu moyamikira Yehova, Mlengi Wamkulu wa zonsezo!
[Mafunso]
1. (a) M’Baibulo, kodi nchiyani chimene kaŵirikaŵiri chimatchedwa “miyamba”? (b) M’ndime zina, kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la “dziko lapansi”?
2. Kodi nchifukwa ninji Yehova analola Israyeli kuloŵetsedwa mu undende, koma kodi iye adaneneratu chiyani?
3. Kodi nchiyani chimene lonjezolo pa Yesaya 65:17 linatanthauza?
4. (a) Kodi nliti pamene chiwombolo chonenedweratu chinadza? (b) Kodi nchiyani chimene kalero chinali “miyamba yatsopano” ndi “dziko lapansi latsopano”?
5, 6. (a) Kodi nchiyani chimene chigapereke umboni wakuti iwo analidi anthu osinthidwa? (b) Pamene Yehova anawadzudzula, kodi kulabadira kwawo kunali kosiyana motani ndi kuja kwa panthaŵi yaundende usanachitike?
7. Kodi timadziŵa bwanji kuti panayenera kukhala kukwaniritsidwa kwina kwa ulosi wa Yesaya?
8. (a) Kodi ndiliti pamene Yehova anakhazikitsa “miyamba yatsopano” imeneyi, ndipo kodi ndimotani mmene imeneyi imafananira ndi kukwaniritsidwa koyamba kwa ulosiwo? (b) Kodi ndimotani mmene ziŵalo za “miyamba yatsopano” zawonjezerekera mopita patsogolo?
9. Kodi “nchochititsa chikondwerero” chiti chimene Yehova anatulutsa padziko lapansi pano mu 1919?
10. (a) Kodi ndimotani mmene ziyembekezo za Aisrayeli auzimu amenewa zinasiyanira ndi zija za Ayuda obwezeredwa kwawo mu 537 B.C.E.? (b) Kodi ndintchito yotani imene Yehova anawapatsa kuti achite? (c) Kodi ndimotani mmene iye wawadalitsira kwambiri pamene akali chikhalirebe padziko lapansi, ndipo kodi ndimotani mmene malemba otchulidwawo amalongosolera mikhalidwe imene iwo ali nayo?
11. (a) Kodi makamaka nkuyambira liti pamene Yehova wakhala akulinganiza ziŵalo zoyembekezeredwa za “dziko lapansi latsopano”? (b) Kodi iwo anaphiphiritsiridwa ndi anthu ati amene anasiya Babulo wakale?
12. Kodi ndimotani mmene anthu alinkulinganizidwira kotero kuti akhale maziko oyenerera a “dziko lapansi latsopano”?
13. Kodi ndimotani mmene “dziko lapansi latsopano” likudzalo lidzakhalira kukwaniritsidwa kokulirapo kwambiri kwa lonjezo la Yehova koposa chimene chinachitika mu 537 B.C.E.?
14. (a) Kodi ndiliti pamene 2 Petro 3:13 ndi Chivumbulutso 21:1 zidzakwaniritsidwa? (b) Kodi nchiyani chimene chidzakhala chosiyana ponena za mikhalidwe mu imene “kumwamba kwatsopano” kudzakhala kukugwiritsira ntchito panthaŵiyo” (c) Kodi ndani amene adzaphatikizidwa mu “dziko lapansi latsopano”?
15. Kodi nchifukwa ninji lonjezolo pa Chivumbulutso 21:3, 4 liri lofunika kwa inu?
16. Kodi ndiziyembekezo zotani ponena za mtsogolo zimene zasonkhezeredwa m’mitima yathu ndi malonjezowo pa (a) Yesaya 11:6-9? (b) Yesaya 35:1-7? (c) Yesaya 65:20-25? (d) Kodi ndani amene amapangitsa ziyembekezo zokondweretsa zimenezi kuthekera kwa ife?