Chaputala 12
Pangano Latsopano la Mulungu Liyandikira Kukwaniritsidwa Kwake
1. (a) Kodi ndichiyani chimene chikanachitika kudziko lathu lapansili ngati Mulungu sakanamamatira kupangano lake lonena za usana ndi usiku? (b) Popeza Mulungu amamamatira mokhulupirika kumapangano ake, kodi ife tingakhale otsimikizira za chiyani?
KODI tikanachitanji ngati Mulungu sakanachita mogwirizana ndi pangano lake lonena za usana ndi lonena za usiku? Mmalo mwa kukhala ndi usana ndi usiku, dziko lathu lapansili likanaunikiridwa ndi kuunika kosatha kapena kukutidwa ndi mdima wosatha. (Genesis 1:1, 2, 14-19) Koma Mulungu amamamatira mokhulupirika kumapangano ake. Motero tingatsimikizire kotheratu kuti mwezi, dzuŵa, ndi milalang’amba ya miyamba siidzawonongedwa konse; ngakhalenso planeti lathu Dziko Lapansi.
2. Kodi ndichiyani chimene Yehova anauza Ayuda mogwirizana ndi pangano lake la usana ndi usiku?
2 Polankhula za pangano lake la usana ndi la usiku, Mulungu anati kwa Ayuda okhala pansi pa ufumu wa nyumba yachifumu ya Davide: “Ngati mukhoza kuswa pangano langa lausana ndi pangano langa lausiku, kuti usakhalenso usana ndi usiku nyengo yawo; pamenepo pangano langa lidzasweka ndi Davide mtumiki wanga, kuti asakhale ndi mwana wamwamuna wa kulamulira pampando wa ufumu wake.”—Yeremiya 33:20, 21.
3. Kodi mawu ameneŵa amasonyeza chiyani ponena za pangano lake ndi Davide la Ufumu wosatha?
3 Mwa mawu amenewo tiri ndi umboni wakuti dziko lathu lapansi, limodzi ndi dzuŵa ndi mwezi, zidzakhalako kosatha. (Mlaliki 1:4) Dziko lathu lapansi lidzakhalidwa ndi nzika zaumunthu, kuti zisangalale ndi kukongola kwa usana ndi usiku, molamulidwa ndi Mulungu wosunga pangano, Mlengi wa munthu. Ndipo monga momwedi Yehova wamamatirira zolimba kupangano lake la usana ndi usiku, chotero iye wakhala wokhulupirika kupangano lake ndi Mfumu Davide wakale la Ufumu wosatha mumzera wa banja la Davide. Zimenezi ziri zowona ngakhale kuli kwakuti mpando wa Ufumuwo unafunikira kusamutsidwa padziko lapansi kuloŵetsedwa m’miyamba yosawoneka.—Salmo 110:1-3.
4. (a) Kodi pangano la Davide la Ufumu wosatha nlogwirizanitsidwa ndi pangano lina liti? (b) Kodi Yesu Kristu ananenanji za ilo, ndipo m’mikhalidwe yotani?
4 Pangano la Mulungu la Ufumu wosatha mumzera wa Davide nlogwirizanitsidwa ndi pangano lina, “pangano latsopano.” Yesu analankhula za pangano limeneli limene linali kudzaloŵedwa mmalo ndi latsopano. Zimenezi zinali pambuyo pa kuchita kwake phwando la Paskha Wachiyuda limodzi ndi ophunzira ake okhulupirika pausiku wa Nisani 14 mu 33 C.E. Iye anakhazikitsa chimene chinadzatchedwa “chakudya chamadzulo cha Ambuye.” Iye anadziŵa kuti patsiku limodzimodzilo la Paskha, iye akakhetsa mwazi wake kukhala nsembe. Chifukwa cha zimenezo, iye anatenga chikho cha vinyo wofiira, koma asanachipitirizire kwa atumwi ake okhulupirika, iye anati: “Chikho ichi ndipangano latsopano m’mwazi wanga.”—Luka 22:20; 1 Akorinto 11:20, 23-26.
5. Kodi ndikwayani kumene lonjezo la Mulungu la pangano latsopano linapangidwako, ndipo kodi Lipabuliki la Israyeli limanena kuti liri m’pangano limeneli?
5 Mofanana ndi pangano lakale, pangano latsopano lachitidwa ndi mtundu koma osati ndi mtundu uliwonse wa Dziko Lachikristu. Ngakhale kuli kwakuti lonjezo la pangano latsopano linachitidwa kupyolera mwa mneneri Yeremiya kumtundu wa Israyeli zaka zoposa 2 500 zapitazo, Lipabuliki la Israyeli lerolino silimanena kuti liri m’pangano latsopano. Mmalo mwake, Lipabuliki la Israyeli linafikira kukhala membala wa UN.
6. Mogwirizana ndi kunena kwa Yeremiya chaputala 31, kodi nchifukwa ninji Mulungu anawona kufunika kwa kupanga pangano latsopano, ndipo kodi linakhala n’chotulukapo chotani?
6 Kodi nchifukwa ninji Mulungu anafuna pangano latsopano? Yeremiya 31:31-34 akulongosola kuti: “Tawonani, masiku adza, ati Yehova, ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda; simonga pangano limene ndinapangana ndi makolo awo tsiku lija ndinawagwira manja kuŵatulutsa m’dziko la Aigupto; pangano langa limenelo analiswa, ngakhale ndinali mbuyawo, ati Yehova. Koma iri ndipangano limene ndidzapangana ndi nyumba ya Israyeli atapita masiku aja, ati Yehova; ndidzayika chilamulo changa mkati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba; ndipo ndidzakhala Mulungu wawo, nadzakhala iwo anthu anga; ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziŵe Yehova; pakuti onse adzandidziŵa, kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; ndipo ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira tchimo lawo.”
Pangano Labwinopo Lokhala ndi Mtetezi Wabwinopo
7. Kodi pangano latsopano ndilo kuyambitsidwanso kwa pangano limene Aisrayeli anaswa, ndipo nchifukwa ninji liri labwinopo kuposa pangano Lachilamulo?
7 Pangano latsopano sindiro kokha kuyambitsidwanso kwa pangano loyambirira limene Aisrayeli anaswa. Kutalitali! Chifukwa chakuti mtumwi Paulo akulembera Akristu ku Roma, kumati: “Simuli a lamulo koma achisomo.” (Aroma 6:14) Liridi pangano latsopano, ndipo likayembekezeredwa kuti likakhala labwinopo, chifukwa chakuti Yehova Mulungu Wamphamvuyonse ngwokhoza kuwongolera mikhalidwe ya awo amene amawaloŵetsa m’pangano latsopano. Mwachitsanzo, iye anadzutsa mtetezi wabwinopo, kapena nkhoswe, pokhazikitsa pangano latsopano. Mtetezi ameneyu sanali munthu wopanda ungwiro, woipitsidwa ndi uchimo mofanana ndi mneneri Mose.
8. (a) Kodi pangano latsopano liri ndi chiyani chimene chimalipangitsa kukhala labwinopo kuposa pangano Lachilamulo? (b) Kodi ndani amene ali Mtetezi wa pangano latsopano labwinopo limenelo? (c) Kodi Ahebri 8:6, 13 amanena chiyani ponena za pangano latsopano ndi kuposa kwa Mtetezi wake, ndipo ndichiyambukiro chotani pa pangano lakale?
8 Pangano Lachilamulo limene mneneri Mose anali mtetezi wake linali labwino mwa ilo lokha. Komabe, pangano limenelo linapereka nsembe za nyama zimene mwazi wake sukanachotsa konse machimo a anthu. Motero kuti Yehova Mulungu akhazikitse pangano labwinopo, panafunikira kukhala mtetezi wabwinopo wokhala ndi nsembe yabwinopo. Mtetezi wofunika kwambiri ameneyu anatsimikizira kukhala Yesu Kristu. Potchula ukulu wa Mtetezi ameneyu pomuyerekezera ndi mneneri Mose, Baibulo limatipatsa malongosoledwe otsatiraŵa: “Koma tsopano iye walandira chitumikiro chomveka choposa, umonso ali nkhoswe ya pangano labwino loposa, limene likhazikika pa malonjezano oposa. . . . Pa kunena iye, Latsopano, anagugitsa loyambali.”—Ahebri 8:6, 13.
Pangano Lakale ‘Loguga’ Liloŵedwa Mmalo
9. (a) Kodi ndipatsiku liti pa limene pangano lakale linachotsedwa? (b) Kodi ndichiyani chimene chinachitika m’mamaŵa umenewo, ndipo nkutsimikiziridwa kwa chiyani?
9 Pangano ‘loguga,’ kapena losukuluka limenelo, linatha masiku 50 pambuyo pa chiukiriro cha Mtetezi wa pangano latsopano. Zimenezi zinachitika patsiku la Pentekoste. M’mamaŵa a tsiku limenelo, Phwando lophiphiritsiridwa ndi la Masika Achiyuda linayamba kuchitika. Motani? Eya, ophunzira okhulupirika 120 a Mtetezi wa pangano latsopano anasonkhana pamodzi m’chipinda chapamwamba m’Yerusalemu ndi kulandira mzimu woyera wolonjezedwawo, m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wa Yoweli 2:28-32. Zinatsimikizira chiyambi cha Pangano latsopano mwa kupereka umboni womveka ndi wowoneka kwa onse amene analipo.
10. Patsiku la Pentekoste limenelo, kodi kunasonyezedwa motani kuti ophunzira a Yesu anadzozedwa ndi mzimu woyera?
10 Pamene Yesu anatuluka m’madzi a ubatizo ndipo mzimu woyera unatsanuliridwa pa iye, mzimuwo mozizwitsa unawonekera mu mpangidwe wa nkhunda yotera pamutu pake. Koma kwa ophunzira Achihebri 120 patsiku la Pentekoste, kodi kudzozedwa kwawo ndi mzimu woyera kunawonekera motani? Mwa kuwonekera kwa malirime onga moto pamwamba pamitu yawo ndi mwa kupatsidwa kwawo maluso a kulalikira Mawu a Mulungu m’zinenero zachilendo zimene sanaziphunzirepo konse.—Mateyu 3:16; Machitidwe 2:1-36.
11. (a) Kodi ndichiyani chimene chiyenera kukhala umboni kwa Ayuda, ndipo chifukwa ninji? (b) Kodi timadziŵa bwanji kuti Ayuda sakunena kwa wina ndi mnzake kuti, “Mdziŵe Yehova!” ndipo ndichimwemwe chotani chimene iwo alibe?
11 Kuyenera kukhala kwachiwonekere kwa Ayuda ndi arabi awo kuti pangano Lachilamulo cha Mose silikugwirabe ntchito. Chiyambire kuwonongedwa kwa Yerusalemu ndi magulu ankhondo a Roma mu 70 C.E., iwo akhala alibe kachisi. Panthaŵiyo, kaundula wa mibadwo anatayika kapena kuwonongedwa. Motero lerolino iwo samadziŵa kuti ndani amene ali wa fuko la Levi ndi amene ali mbadwa ya Aroni kotero kuti atumikire monga mkulu wa ansembe wa mtundu Wachiyuda. Mmalo mwa kunena kwa wina ndi mnzake kuti, “Mdziŵe Yehova!” iwo amalingalira kutchulidwa kwa dzina la Mulungu kukhala kudetsa chinthu chopatulika. Motero iwo alibe chimwemwe chimene Mboni za Yehova ziri nacho chochokera m’chenicheni chakuti pangano lakale ‘loguga’ laloŵedwa mmalo ndi pangano latsopano.
“Pangano Losatha”
12. (a) Kodi ndim’pemphero lotani limene Mboni za Yehova zingagwirizane kuchokera mu mtima? (b) Kodi Yesu anaukitsidwa ndichiyani kuchokera kwa akufa?
12 Mosiyana kwambiri ndi mkhalidwe Wachiyuda wamakono, Mboni za Yehova ziri ndi Mkulu wa Ansembe wogwira ntchito padzanja lamanja la Mulungu kumwamba. Iye ndiye Mtetezi wa pangano latsopano, mtetezi wamkulu kwambiri kuposa Mose. Kuchokera mu mtima, mboni za Yehova zimenezi zingathe kugwirizana ndi pemphero la wolemba pa Ahebri 13:20, 21: “Koma Mulungu wamtendere amene anabwera naye wotuluka mwa akufa Mbusa wamkulu wankhosa ndi mwazi wa chipangano chosatha, ndiye Ambuye wathu Yesu, akuyeseni inu opanda chirema m’chinthu chirichonse.” Popeza kuti “mbusa wamkulu” ameneyo anataya moyo wake waumunthu kaamba ka “nkhosa,” iye akanatha kuukitsidwa kwa akufa m’thupi losakhoza kufa, lopanda mwazi lauzimu koma ali ndi mtengo wa mwazi wa pangano latsopano limene limasungidwa mokhulupirika ndi limene ziyambukiro zake zabwino ziri zosatha.
13. (a) Kodi ndimotani mmene imfa ya Mtetezi wa pangano latsopano ikukumbukiridwira chaka chirichonse ndi Mboni za Yehova? (b) Kodi zizindikiro zimaphiphiritsira chiyani?
13 Imfa ya nsembe ya Mtetezi wa pangano latsopano, Yesu Kristu, imakumbukiridwa chaka chirichonse ndi Mboni za Yehova patsiku la chaka ndi chaka la “mgonero wa Ambuye.” Mkate wopanda chotupitsa wodyedwa ndi awo amene ali m’pangano latsopano mkati mwa “mgonero” umenewo umaphiphiritsira thupi langwiro la Mtetezi, ndipo vinyo amaphiphiritsira mwazi wangwiro, wosaipitsidwa umene, mogwirizana ndi kunena kwa Malemba, unali ndi mtengo wa moyo weniweniwo wa Mtetezi.—1 Akorinto 11:20-26; Levitiko 17:11.
14. Pamene a m’pangano latsopano adya zizindikiro za Chikumbutso, kodi iwo akuchita chiyani, mophiphiritsira?
14 Pamene okhala m’pangano latsopanowo alandira chikho cha vinyo wa Chikumbutso pa “mgonero wa Ambuye,” kuli kokha mwa njira yophiphiritsira kuti amamwa mwazi, wa Mtetezi wa pangano latsopano. Amadyanso thupi lake mwanjira yophiphiritsira pamene amalandira mkate wopanda chotupitsa wa Chikumbutso. Mwa kuchita zimenezi, m’kulankhula kophiphiritsira, iwo amasonyeza chikhulupiriro chawo m’nsembe ya dipo ya Mwana wa Mulungu, Mpulumutsi wa anthu onse.
15. (a) Kodi pangano latsopano lakhalako kale kwa utali wotani, ndipo kodi latsimikiziradi motani kukhala pangano labwinopo? (b) Kodi nchifukwa ninji pangano latsopano lingatchulidwe kuti liri “pangano losatha”?
15 Pangano latsopano, limene tsopano liri ndi zaka zoposa 1 950 zapitazo liri pafupi kukwaniritsa chifuno chake. Lakhala kale zaka mazana angapo kuposa pangano Lachilamulo cha Mose. Pokhala lozikidwa pamalonjezo abwinopo ndi nsembe yabwinopo limodzi ndi Mtetezi wabwinopo, ilo latsimikiziradi kukhala pangano labwinopo. Chifukwa cha kusafunikira kuloŵedwa mmalo ndi pangano latsopano ndi labwinopo, pangano latsopano lopeza chipambanolo likutchulidwa kukhala “pangano losatha.”—Ahebri 13:20.
16. Kodi tiyenera kuyamikira chiyani kwa Yehova Mulungu?
16 Tiyamika Mulungu Wamphamvuyonse, Yehova, kuti iye anadzutsa Mtetezi wabwinopo koposa Mose, kupyolera mwa amene Iye mwalamulo akachotsa pangano Lachilamulo cha Mose mwa kuchikhomerera pamtengo wozunzirapo ndi kupereka mwazi wa pangano latsopano losatha!
[Chithunzi patsamba 105]
Pangano latsopano limene Yesu anali mtetezi wake liri lapamwamba kwambiri kuposa pangano lakale limene Mose anali mtetezi wake