Mutu 1
Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
1. Tikudziwa bwanji kuti Mulungu amafuna kuti tikhale osangalala?
CHIVUMBULUTSO KWA YOHANE. Buku la m’Baibulo lochititsa chidwi limeneli limatiuza mapeto osangalatsa a uthenga wa Mulungu. N’chifukwa chiyani tikunena kuti mapeto a uthengawu ndi osangalatsa? N’chifukwa chakuti Mulungu, yemwe ndi Wolemba Baibulo wamkulu, amatchedwa “Mulungu wachimwemwe” ndipo amapereka “uthenga wabwino waulemerero” kwa anthu amene amamukonda. Iye amafuna kuti ifenso tikhale osangalala. N’chifukwa chake chakumayambiriro kwa buku la Chivumbulutso kuli mawu otilimbikitsa akuti: ‘Wodala [kapena kuti ‘wosangalala’] ndi munthu amene amawerenga . . . mawu a ulosi umenewu.’ M’chaputala chomalizira cha bukuli muli mawu akuti: “Wodala ndi aliyense wosunga mawu a ulosi a mumpukutu uwu.”—1 Timoteyo 1:11; Chivumbulutso 1:3; 22:7.
2. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti buku la Chivumbulutso litithandize kukhala osangalala?
2 Kodi tingatani kuti buku la Chivumbulutso litithandize kukhala anthu osangalala? Lingatithandize ngati titamaganizira mozama zizindikiro zochititsa chidwi zimene zatchulidwa m’bukuli n’kufufuza tanthauzo lake, kenako n’kuchita zinthu mogwirizana ndi tanthauzolo. Anthu akhala akuchita zoipa kwa nthawi yaitali, ndipo posachedwapa adzawonongedwa Mulungu ndi Yesu Khristu akamadzaweruza dziko loipali. Kenako Mulungu ndi Yesu Khristu adzabweretsa “kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” ndipo “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:1, 4) Tonsefe timafuna kudzakhala m’dziko latsopano la bata ndi mtendere ndipo zimenezi zingatheke ngati tili ndi chikhulupiriro cholimba. Chikhulupiriro chathu chingalimbe ngati tikuphunzira Mawu a Mulungu, monga ulosi wochititsa chidwi wa m’buku la Chivumbulutso.
Kodi Chivumbulutso N’chiyani?
3. Kodi anthu ambiri amaganiza kuti mawu akuti “Chivumbulutso” ndi “Aramagedo” amatanthauza chiyani?
3 Anthu ambiri akamva mawu akuti “Chivumbulutso” amaganiza za mawu akuti “Aramagedo” amene atchulidwa m’bukuli. Anthu ena amaganiza kuti mawu awiriwa amanena za nkhondo ya zida zanyukiliya imene idzawononge dziko lonse. Mwachitsanzo, mumzinda wina wa ku Texas, m’dziko la United States, kumene kunkapangidwa mabomba ambiri anyukiliya, anthu okonda zopemphera ankanena kuti, “Tidzayambirire kufa ndife kunoko.” Iwo ankanena zimenezi chifukwa choopa nkhondo ya zida zanyukiliya. Ndipo nyuzipepala ina inafotokoza kuti atsogoleri azipembedzo a m’deralo “ankakhulupirira kuti Aramagedo ndi yosapeweka komanso kuti ili pafupi. Ankakhulupiriranso kuti nkhondo yomalizira ndiponso yoopsa imeneyi, ya pakati pa gulu la Mulungu ndi gulu la Satana, idzakhala ya zida zanyukiliya.”
4. Kodi dzina lakuti “Chivumbulutso” limatanthauza chiyani kwenikweni, ndipo n’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti buku lomaliza la m’Baibulo limatchedwa ndi dzina limeneli?
4 Dzina lakuti “Chivumbulutso” linamasuliridwa kuchokera ku mawu enaake achigiriki (a·po·kaʹly·psis) amene amatanthauza “kuulula” kapena “kuvundukula.” N’chifukwa chake n’zosadabwitsa kuti buku lomaliza la m’Baibulo limatchedwa kuti “Chivumbulutso.” Sikuti m’buku limeneli timangopezamo uthenga woopsa wonena za kuwonongedwa kwa dziko lapansi, koma timapezamonso choonadi chimene Mulungu anachiulula. Choonadichi chingatithandize kukhala ndi chiyembekezo chosangalatsa komanso chikhulupiriro cholimba.
5. (a) Kodi ndi anthu otani amene adzawonongedwe pa Aramagedo, nanga ndi anthu otani amene adzapulumuke? (b) Kodi anthu amene adzapulumuke pa Aramagedo adzakhala ndi moyo wotani?
5 Buku limeneli, lomwe ndi buku lomalizira la m’Baibulo, limanenadi kuti Aramagedo ndi “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse.” (Chivumbulutso 16:14, 16) Koma nkhondoyi idzakhala yosiyana kwambiri ndi nkhondo ya zida zanyukiliya. Tikutero chifukwa nkhondo yanyukiliya ingawononge chilichonse chamoyo padzikoli. Koma Mawu a Mulungu amatitsimikizira kuti anthu oipa okha, amene amatsutsana ndi Mulungu, ndi amene adzaphedwe pa Aramagedo. (Salimo 37:9, 10; 145:20) Khamu lalikulu la anthu ochokera m’mitundu yonse adzapulumuka chiweruzo cha Mulungu pa Aramagedo. Kenako Khristu Yesu adzatsogolera anthu amenewa ku moyo wosatha m’paradaiso padziko lapansi. Kodi mukufuna kudzakhala m’gulu la anthu amenewa? N’zosangalatsa kuti buku la Chivumbulutso limasonyeza kuti inuyo mungathe kudzakhala m’gulu limeneli.—Chivumbulutso 7:9, 14, 17.
Kufufuza Zinsinsi za M’Mawu a Mulungu
6. Kodi m’mbuyomu Mboni za Yehova zafalitsa mabuku ati othandiza kumvetsa buku la Chivumbulutso?
6 Kale kwambiri mu 1917, bungwe la Watch Tower Society linafalitsa buku lachingelezi lamutu wakuti The Finished Mystery. Buku limeneli linafotokoza vesi lililonse la mabuku a Ezekieli ndi Chivumbulutso. Ndiyeno popeza kuti zinthu zosiyanasiyana zokwaniritsa maulosi a m’Baibulo zinali kuchitikabe, mu 1930 gulu la Mulungu linatulutsanso buku lachingelezi lapanthawi yake. Buku limeneli analisindikiza m’magawo awiri ndipo linali ndi mutu wakuti Light. Bukuli linafotokoza mfundo zatsopano za m’buku la Chivumbulutso. Kuwala kunapitiriza ‘kuunikira olungama,’ moti mu 1963, Mboni za Yehova zinafalitsa buku lachingelezi la masamba 704 lamutu wakuti “Babylon the Great Has Fallen!” God’s Kingdom Rules! Buku limeneli linafotokoza mwatsatanetsatane za chiyambi ndiponso kugwa kwa Babulo Wamkulu, yemwe akuimira zipembedzo zonyenga zonse pamodzi. Chakumapeto kwake, bukuli linafotokoza mfundo za m’machaputala 9 omalizira a buku la Chivumbulutso. Pamene ‘njira ya olungama inali kuwala mowonjezereka,’ makamaka pa nkhani ya mmene mipingo iyenera kugwirira ntchito zake, mu 1969 Mboni za Yehova zinatulutsanso buku lina lachingelezi la masamba 384 lamutu wakuti “Then Is Finished the Mystery of God.” Buku limeneli linafotokoza mfundo za m’machaputala 13 oyambirira a buku la Chivumbulutso.—Salimo 97:11; Miyambo 4:18.
7. (a) N’chifukwa chiyani Mboni za Yehova zafalitsa buku lino, lomwe likufotokoza mfundo za m’buku la Chivumbulutso? (b) Kodi m’bukuli muli zinthu ziti zimene zingathandize munthu kuphunzira mosavuta?
7 N’chifukwa chiyani panopa gulu la Yehova lafalitsa buku linanso lofotokoza mfundo za m’buku la Chivumbulutso? Mabuku ambiri amene afalitsidwa kale, nkhani zake anazifotokoza mwatsatanetsatane kwambiri, ndipo zinali zosatheka kuzimasulira ndi kuzifalitsa m’zinenero zambiri za padziko lonse. Choncho gulu la Yehova linaona kuti ndi bwino kutulutsa buku limodzi lofotokoza mfundo za m’buku la Chivumbulutso, limene lingafalitsidwe m’zinenero zosiyanasiyana. Komanso m’buku lino taikamo zinthu zothandiza kuti munthu aphunzire zinthu mosavuta, monga zithunzi, matchati ndi mabokosi ofotokoza mfundo mwachidule. Zimenezi zingathandize owerenga bukuli kumvetsa kufunika kwa maulosi ochititsa chidwi amenewa.
8. Kodi pali chifukwa china chachikulu chiti chimene tafalitsira buku lino?
8 Chifukwa china chachikulu chimene tatulutsira bukuli n’chakuti tikufuna kufotokoza mfundo zogwirizana ndi mmene tikumvera choonadi panopa. Yehova akutithandizabe kumvetsa Mawu ake, ndipo tikukhulupirira kuti tipitiriza kumvetsa bwino mfundo za m’buku la Chivumbulutso komanso maulosi ena, pamene tikuyandikira kwambiri chisautso chachikulu. (Mateyu 24:21; Chivumbulutso 7:14) Kumvetsa bwino Mawu a Mulungu n’kofunika kwambiri, moti pofotokoza za mawu a ulosi, mtumwi Petulo analemba kuti: “Mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewo ali ngati nyale imene ikuwala mu mdima, m’mitima yanu, mpaka m’bandakucha, nthanda ikadzatuluka.”—2 Petulo 1:19.
9. (a) Kodi buku la Chivumbulutso ndiponso maulosi ena akusonyeza kuti Mulungu adzalenga chiyani? (b) Kodi dziko latsopano n’chiyani, ndipo mungatani kuti mudzapezekemo?
9 Buku la Chivumbulutso limagwirizana ndi maulosi ena ambiri a m’Baibulo amene amasonyeza kuti Yehova Mulungu adzalenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano. (Yesaya 65:17; 66:22; 2 Petulo 3:13; Chivumbulutso 21:1-5) Kwenikweni uthenga wa m’bukuli ndi wopita kwa Akhristu odzozedwa amene Yesu anawagula ndi magazi ake kuti adzalamulire naye limodzi ali kumwamba kwatsopano. (Chivumbulutso 5:9, 10) Komabe uthenga wabwino umenewu umalimbitsanso chikhulupiriro cha anthu ambirimbiri amene akuyembekezera kudzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi mu Ufumu wa Khristu. Kodi inuyo muli m’gulu la anthu amenewa? Ngati muli m’gulu la anthu amenewa, ndiye kuti buku la Chivumbulutso likuthandizani kulimbitsa chiyembekezo chanu chodzakhala m’Paradaiso, monga mmodzi wa anthu amene adzapange dziko lapansi latsopano. Mmenemo mudzakhala mtendere wochuluka, anthu adzakhala ndi moyo wathanzi ndipo Mulungu adzapereka madalitso ochuluka amene sadzatha. (Salimo 37:11, 29, 34; 72:1, 7, 8, 16) Ngati mukufuna kudzakhala m’dziko latsopano limenelo, musazengereze kuganizira mozama mfundo za m’buku la Chivumbulutso. Mfundo zimenezi azifotokoza momveka bwino pogwiritsira ntchito zizindikiro, ndipo zikusonyeza kuti tili m’nthawi yamapeto.—Zefaniya 2:3; Yohane 13:17.
[Chithunzi chachikulu patsamba 7]