Mutu 8
Tiyesetse Kuti Tipambane pa Nkhondo
SIMUNA
1. (a) Kodi ndi mpingo wachiwiri uti umene unalandira uthenga kuchokera kwa Yesu amene anali atapatsidwa ulemerero kumwamba? (b) Ponena kuti iye ndi “Woyamba ndi Wotsiriza,” kodi Yesu anakumbutsa Akhristu a mpingo umenewu za chiyani?
MASIKU ano, pamalo amene panali mzinda wakale wa Efeso pali bwinja. Koma kumene kunali mpingo womwe Yesu anaulembera uthenga wachiwiri, masiku ano kuli mzinda waukulu wotchedwa Izmir. Mzindawu uli m’dziko la Turkey, ndipo uli pa mtunda wamakilomita 55 kumpoto kwa bwinja lomwe linali mzinda wa Efeso. Mumzinda wa Izmir, masiku ano muli mipingo ya Mboni za Yehova inayi mmene muli Akhristu odzipereka kwambiri. Pamene pali mzindawu, kale panali mpingo wa Simuna. Tsopano, onani uthenga umene Yesu anauza Akhristu a mpingo umenewo. Iye anati: “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Simuna lemba kuti: Izi ndi zimene akunena ‘Woyamba ndi Wotsiriza,’ amene anafa n’kukhalanso ndi moyo.” (Chivumbulutso 2:8) Ponena mawu amenewa kwa Akhristu a mpingo wa ku Simuna, Yesu anawakumbutsa kuti iye anatumikira Yehova ndi mtima wosagawanika ndipo anali munthu woyamba ndi womaliza kuukitsidwa ndi Yehova mwachindunji n’kukakhala ndi moyo umene sungafe, kumwamba. Koma Yesu ndi amene amaukitsa Akhristu ena onse odzozedwa. Choncho, iye ndi woyenera kupereka malangizo kwa abale ake amene akuyembekezera kukakhala ndi moyo wosafa kumwamba pamodzi ndi iye.
2. Kodi Akhristu onse akulimbikitsidwa bwanji ndi mawu a munthu amene “anafa n’kukhalanso ndi moyo”?
2 Pamene Yesu ankazunzidwa chifukwa cha chilungamo, anapereka chitsanzo cha kupirira ndipo analandira mphoto yoyenera. Akhristu onse ali ndi chiyembekezo chifukwa choti Yesu anakhala wokhulupirika mpaka imfa ndipo kenako anaukitsidwa. (Machitidwe 17:31) Mfundo yakuti Yesu “anafa n’kukhalanso ndi moyo” ikusonyeza kuti kupirira mavuto alionse amene tingakumane nawo chifukwa cha choonadi sikudzapita pachabe. Akhristu onse amalimbikitsidwa kwambiri chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu, makamaka ngati akuvutika chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Kodi inunso mukuvutika chifukwa cha chikhulupiriro chanu? Ngati ndi choncho, mawu a Yesu otsatirawa, amene ankapita kumpingo wa ku Simuna, angakulimbikitseni.
3. (a) Kodi Yesu analimbikitsa bwanji Akhristu a mpingo wa ku Simuna? (b) Ngakhale kuti Akhristu a ku Simuna anali osauka, n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti iwo anali “olemera”?
3 Iye anati: “Ndikudziwa masautso ako ndi umphawi wako, koma ndiwe wolemera. Ndikudziwanso za kutonza kwa odzitcha Ayudawo, pamene si Ayuda, koma ndiwo sunagoge wa Satana.” (Chivumbulutso 2:9) Yesu sanadzudzule abale ake a mumpingo wa ku Simuna, koma anangowayamikira. Iwo anazunzidwa kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Akhristuwo anali osauka, mwina chifukwa chakuti anali okhulupirika. (Aheberi 10:34) Koma chinthu chofunika kwambiri pa moyo wawo chinali zinthu zauzimu, ndipo anasunga chuma kumwamba monga mmene Yesu anawalangizira. (Mateyu 6:19, 20) Motero Yesu, yemwe ndi M’busa Wamkulu, ankawaona kuti ndi “olemera.”—Yerekezerani ndi Yakobo 2:5.
4. Kodi ndani amene ankazunza kwambiri Akhristu a ku Simuna ndipo Yesu ankawaona bwanji anthu ozunzawo?
4 Yesu anayamikira Akhristu a mpingo wa ku Simuna makamaka chifukwa choti anapirira potsutsidwa kwambiri ndi Ayuda. Chikhristu chitangoyamba kumene, anthu ambiri a m’chipembedzo cha Chiyuda ankatsutsa kwambiri Akhristuwo n’cholinga choti Chikhristu chisafalikire. (Machitidwe 13:44, 45; 14:19) Tsopano patangopita zaka zowerengeka mzinda wa Yerusalemu utawonongedwa, Ayuda a ku Simuna nawonso ankasonyeza mtima wa Satana umenewo. N’chifukwa chake Yesu ankawaona kuti iwo ndi “sunagoge wa Satana.”a
5. Kodi Akhristu a ku Simuna ankayembekezera kukumana ndi mayesero otani?
5 Popeza kuti anthu ankadana kwambiri ndi Akhristu a ku Simuna, Yesu analimbikitsa Akhristuwo kuti: “Usachite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo. Taona! Mdyerekezi adzapitiriza kuponya m’ndende ena a inu, kuti muyesedwe mpaka pamapeto, ndipo mudzakhala m’masautso masiku 10. Sonyeza kukhulupirika kwako mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsa mphoto ya moyo.” (Chivumbulutso 2:10) Palembali Yesu anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti akulankhula ndi anthu ambiri, monga akuti “ena a inu,” “muyesedwe” ndiponso “mudzakhala.” Izi zikusonyeza kuti uthengawo unkapita kumpingo wonse. Yesu sanalonjeze kuti mayesero amene Akhristu a ku Simuna ankakumana nawo atha posachedwa. Ena a iwo anapitiriza kuzunzidwa ndi kumangidwa. Iye anawauza kuti adzakhala m’masautso “masiku 10.” M’Baibulo, 10 ndi nambala imene imasonyeza kuti zinthu zinazake ndi zokwanira, makamaka za padziko lapansi. Anthu amenewa, omwe anali olemera mwauzimu ndipo anatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika, anayesedwa kwambiri ali ndi moyo padziko lapansi.
6. (a) N’chifukwa chiyani Akhristu a mpingo wa ku Simuna sanayenere kuchita mantha? (b) Kodi Yesu anamaliza uthenga wake wopita kumpingo wa ku Simuna ndi mawu otani?
6 Komabe, Akhristu a mpingo wa ku Simuna sanayenere kuchita mantha kapena kusiya chikhulupiriro chawo. Iwo anayenera kukhalabe okhulupirika mpaka imfa kuti alandire “mphoto ya moyo,” yomwe ndi moyo wa kumwamba umene sungafe. (1 Akorinto 9:25; 2 Timoteyo 4:6-8) Mtumwi Paulo ankaona kuti mphoto imeneyi ndi yapamwamba kwambiri moti akanalolera kudzimana chilichonse, ngakhale kulolera kuphedwa kumene, kuti akailandire. (Afilipi 3:8) Zikuoneka kuti Akhristu okhulupirika a mpingo wa ku Simuna ankaonanso chimodzimodzi. Yesu anamaliza uthenga wake ndi mawu akuti: “Ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo kuti: Wopambana pa nkhondo, sadzakhudzidwa ndi imfa yachiwiri.” (Chivumbulutso 2:11) Anthu amene adzapambane pa nkhondo akutsimikiziridwa kuti adzalandira moyo umene sungafe, kumwamba.—1 Akorinto 15:53, 54.
“Mudzakhala M’masautso Masiku 10”
7, 8. Mofanana ndi Akhristu a mpingo wa ku Simuna, kodi mpingo wachikhristu ‘unayesedwa bwanji mpaka pamapeto’ mu 1918?
7 Mofanana ndi Akhristu a mpingo wa ku Simuna, masiku ano Akhristu odzozedwa ndiponso anzawo a khamu lalikulu akupitirizabe ‘kuyesedwa mpaka pamapeto.’ Iwo akudziwika kuti ndi anthu a Mulungu chifukwa cha kukhulupirika kwawo poyesedwa. (Maliko 13:9, 10) Tsiku la Ambuye litangoyamba kumene, gulu lochepa la anthu a Yehova padziko lonse linalimbikitsidwa kwambiri ndi mawu a Yesu opita kwa Akhristu a mpingo wa ku Simuna. (Chivumbulutso 1:10) Kuyambira m’chaka cha 1879, anthu a m’gulu limeneli amafufuza mozama chuma chauzimu m’Mawu a Mulungu ndipo amagawira ena chumacho mosaumira. Koma nkhondo yoyamba ya padziko lonse itayamba, iwo anazunzidwa komanso kutsutsidwa kwambiri chifukwa sanalowerere nawo pa nkhondoyo ndiponso chifukwa choulula mopanda mantha zinthu zoipa zimene Matchalitchi Achikhristu ankachita. Ena mwa atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anachititsa kuti Akhristu oona azunzidwe kwambiri ndipo zimenezi zinafika pachimake mu 1918. Zimene atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anachitazi zinali zofanana kwambiri ndi zimene Ayuda a ku Simuna ankachitira Akhristu a mpingo wa kumeneko.
8 Kuzunzidwa kwa Akhristu oona ku United States kunafika pachimake pamene Joseph F. Rutherford, amene anali pulezidenti watsopano wa Watch Tower Society, ndi anzake ena 7 anamangidwa pa June 22, 1918. Ambiri mwa Akhristu amenewa anawalamula kuti akhale m’ndende zaka 20. Koma patapita miyezi 9, anawatulutsa pa belo. Kenako pa May 14, 1919, khoti la apilo linaunikanso mlanduwo ndipo linasintha chigamulo chimene Akhristuwo anapatsidwa poyamba litazindikira kuti sanaweruzidwe mwachilungamo. Khotilo linapeza kuti panali zifukwa 130 zosonyeza kuti chigamulo chimene anapatsidwa poyamba chinali cholakwika. Ndiyeno woweruza wina wa Katolika dzina lake Manton, amene anakana kuti Akhristu oonawo amasulidwe pa belo mu 1918, anamangidwa m’chaka cha 1939. Woweruza ameneyu anali wolemekezeka kwambiri chifukwa anapatsidwa ulemu wapadera wokhala m’gulu la anthu oyera mtima la St. Gregory Wamkulu. Iye analamulidwa kuti akhale m’ndende zaka ziwiri ndiponso kuti apereke chindapusa cha ndalama zokwana madola 10,000, chifukwa chopezeka ndi milandu 6 yokhudzana ndi kulandira ziphuphu.
9. Kodi Hitler anachita chiyani ndi Mboni za Yehova pa nthawi imene chipani cha Nazi chinkalamulira ku Germany, nanga atsogoleri a zipembedzo anatani?
9 Mu ulamuliro wa chipani cha Nazi ku Germany, Hitler analetseratu ntchito yolalikira ya Mboni za Yehova. Kwa zaka zambiri, anthu masauzande ambiri a Mboni anawatsekera m’ndende zozunzirako anthu. Ambiri a iwo anafa ndipo Mboni zachinyamata zokwana 200 zinaphedwa chifukwa chokana kulowa m’gulu la nkhondo la Hitler. Umboni wosonyeza kuti atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu anathandizira zimenezi ukuoneka m’mawu amene wansembe wina wa Katolika ananena m’nyuzipepala ina imene inatuluka pa May 29, 1938. Ena mwa mawu akewa anali akuti: “Tsopano pali dziko limodzi lokha padziko lonse lapansi limene anthu otchedwa . . . Ophunzira Baibulo [Mboni za Yehova] sakuloledwa. Dziko limenelo ndi Germany basi! . . . Adolph Hitler atayamba kulamulira, gulu la mabishopu a Katolika ku Germany linaperekanso pempho lawo. Ndipo Hitler anati: ‘Anthu amenewa, otchedwa Ophunzira Baibulo Mwakhama [Mboni za Yehova] ndi osokoneza; . . . Ine ndikuona kuti anthu amenewa ndi onyenga; sindingalole kuti Judge Rutherford wa ku America aipitse mbiri ya Akatolika a kuno ku Germany mwanjira imeneyi. Choncho, ndikulamula kuti [Mboni za Yehova] zisapezekenso m’dziko lino la Germany.’” Hitler atanena zimenezi, wansembe uja anati: “Mwachita bwino!”—The German Way.
10. (a) Pamene tsiku la Ambuye likupitirira, kodi Mboni za Yehova zazunzidwa motani? (b) Kodi kawirikawiri zimatha bwanji Akhristu oona akapita kukhoti kukamenyera ufulu wawo wolambira Mulungu?
10 Pamene tsiku la Ambuye likupitirira, Njoka pamodzi ndi mbewu yake ikupitirizabe kulimbana ndi gulu la Akhristu odzozedwa komanso anzawo a khamu lalikulu. Ambiri mwa Akhristu amenewa amatsekeredwa m’ndende ndiponso amazunzidwa mwankhanza. (Chivumbulutso 12:17) Adani amenewo akupitiriza ‘kuyambitsa mavuto mwa kupanga malamulo,’ koma anthu a Yehova amanena molimba mtima kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.” (Salimo 94:20; Machitidwe 5:29) Magazini ina ya Nsanja ya Olonda ya mu 1954 inati: “Mayiko oposa 70, pa nthawi ina m’zaka 40 zapitazi, anakhazikitsa malamulo oletsa ntchito ya Mboni za Yehova ndiponso ankazunza Mbonizo.” Akhristu amenewa anapita kukhoti kuti akamenyere ufulu wawo wolambira Mulungu m’mayiko amene zinali zotheka, ndipo zinthu zinawayendera bwino m’mayiko ambiri. Mwachitsanzo, m’Khoti Lalikulu Kwambiri lokha la ku United States, Mboni za Yehova zinapambana pa milandu yokwana 50.
11. Kodi ndi ulosi uti wa Yesu wonena za chizindikiro cha kukhalapo kwake umene ukukwaniritsidwa pa Mboni za Yehova m’tsiku la Ambuye?
11 Palibe gulu lina kuposa Mboni za Yehova limene limamvera mokhulupirika lamulo la Yesu lakuti tizipereka zinthu za Kaisara kwa Kaisara. (Luka 20:25; Aroma 13:1, 7) Ngakhale zili choncho, anthu a m’gulu limeneli ndi amene amamangidwanso kwambiri ndi olamulira a maboma osiyanasiyana. Zimenezi zikuchitikabe mpaka pano kumayiko ena a pakati ndi kum’mwera kwa America, ku Ulaya, ku Africa ndiponso ku Asia. Mu ulosi waukulu wa Yesu wonena za chizindikiro cha kukhalapo kwake munalinso mawu akuti: “Kenako anthu adzakuperekani ku chisautso ndipo adzakuphani. Mitundu yonse idzadana nanu chifukwa cha dzina langa.” (Mateyu 24:3, 9) Zikuonekeratu kuti ulosi umenewu ukukwaniritsidwa pa Akhristu a Mboni za Yehova m’tsiku la Ambuye.
12. Kodi Akhristu odzozedwa analimbikitsa bwanji anthu a Mulungu amene ankazunzidwa?
12 Pofuna kulimbikitsa anthu a Mulungu amene akukumana ndi masautso, Akhristu odzozedwa akupitirizabe kukumbutsa anthuwo mfundo yaikulu imene ili m’mawu a Yesu opita kwa Akhristu a mpingo wa ku Simuna. Mwachitsanzo, pamene chipani cha Nazi chinayamba kuzunza Mboni za Yehova, m’magazini achingelezi a Nsanja ya Olonda a mu 1933 ndi mu 1934 munali nkhani zosiyanasiyana zolimbikitsa. Nkhani ina inali ya mutu wakuti “Musawaope,” imene inafotokoza lemba la Mateyu 10:26-33. Ina inali ya mutu wakuti, “Mayesero Oopsa Kwambiri,” ndipo inachokera pa Danieli 3:17, 18; ndipo nkhani inanso inali ya mutu wakuti, “Pakamwa pa Mikango” ndipo mfundo yaikulu ya nkhaniyi inachokera pa Danieli 6:22. M’zaka za m’ma 1980, m’nthawi imene buku lino linatuluka koyamba m’Chingelezi, Mboni za Yehova zinkazunzidwa kwambiri m’mayiko oposa 40. Pa nthawiyi, magazini achingelezi a Nsanja ya Olonda analimbikitsa anthu a Mulungu ndi nkhani yakuti, “Osangalala Ngakhale Kuti Akuzunzidwa” ndiponso yakuti, “Akhristu Amapirira Akamazunzidwa.”b
13. Mofanana ndi Akhristu akale a mpingo wa ku Simuna, n’chifukwa chiyani Akhristu a Mboni za Yehova saopa kuzunzidwa?
13 Zoonadi, Akhristu a Mboni za Yehova akuvutika chifukwa chozunzidwa ndiponso kuyesedwa m’njira zosiyanasiyana kwa masiku 10 ophiphiritsa. Mofanana ndi Akhristu akale a mpingo wa ku Simuna, iwo sachita mantha ndipo aliyense wa ife sayenera kuchita mantha pamene mavuto akuchulukirachulukira padziko lapansi. Ife ndi okonzeka kupirira pa mavuto alionse komanso kusangalala pamene ‘katundu wathu akulandidwa.’ (Aheberi 10:32-34) Tikamaphunzira Mawu a Mulungu ndi kuwagwiritsa ntchito pa moyo wathu, timakhala ndi chikhulupiriro cholimba kwambiri. Musakayikire kuti Yehova angakutetezeni mukamayesetsa kumutumikira ndi mtima wosagawanika. Ndipotu mawu ake akutilimbikitsa kuti ‘timutulire nkhawa zathu zonse, pakuti amatidera nkhawa.’—1 Petulo 5:6-11.
[Mawu a M’munsi]
a Patapita zaka pafupifupi 60 Yohane atamwalira, munthu wina wa zaka 86 dzina lake Polycarp, anaphedwa mumzinda wa Simuna powotchedwa chifukwa chokana kusiya kukhulupirira Yesu. Buku linalake lofotokoza za kuphedwa kwa Polycarp, lomwe anthu amakhulupirira kuti linalembedwa m’nthawi imene iye anaphedwa, linanena kuti pamene anthu ankasonkhanitsa nkhuni zomuwotchera, “monga mwa chizolowezi chawo, Ayuda anajijirika kwambiri pothandizira pa ntchitoyi.” Iwo anachita zimenezi ngakhale kuti limeneli linali “tsiku la Sabata lapadera.”—The Martyrdom of Polycarp.
b Onani magazini achingelezi a Nsanja ya Olonda a November 1, 1933; October 1 ndi 15 ndiponso December 1 ndi 15, 1934; May 1, 1983.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 39]
Kwa zaka zambiri, anthu olemba mbiri yakale akhala akupereka umboni wosonyeza kuti Mboni za Yehova za ku Germany zinkatumikira Mulungu ndi mtima wosagawanika mu ulamuliro wa chipani cha Nazi. Mwachitsanzo, buku lina limene linalembedwa ndi Claudia Koonz, ndipo linatulutsidwa mu 1986, linati: “Anthu ambirimbiri amene sanali m’chipani cha Nazi m’dziko la Germany ndiponso amene ankadana ndi chipanichi ankachita nawo zinthu zina ndi zina zimene chipanichi chinkafuna n’cholinga choti azikhala mwamtendere m’dzikoli. . . . Mosiyana ndi anthu amenewa, anthu a Mboni za Yehova okwanira 20,000, aliyense payekha anakana kwam’tuwagalu kuchita zimene boma la chipani cha Nazi linkafuna. . . . Gulu la anthu ogwirizana kwambirili linakwanitsa kuchita zimenezi chifukwa cha chipembedzo chawo. Kuyambira pachiyambi, Mboni za Yehova zinakana kuchita chilichonse chosonyeza kugwirizana ndi boma la chipani cha Nazi. Ngakhale pamene apolisi a Gestapo anawononga likulu la Mbonizo mu 1933 n’kulamula kuti chipembedzocho chithe mu 1935, iwo anakanabe ngakhale kunena mawu osonyeza kulambira Hitler akuti ‘Heil Hitler.’ Pafupifupi hafu ya Mboni za Yehova zonse (makamaka amuna) zinatumizidwa kundende zozunzirako anthu. Anthu 1,000 mwa amenewa anaphedwa ndipo anthu enanso 1,000 anafa kuyambira mu 1933 mpaka mu 1945. . . . Koma atsogoleri a Katolika ndi a Pulotesitanti ankalimbikitsa anthu awo kuti azigwirizana ndi Hitler. Ngati anthuwo akanakana kuchita zimenezi, ndiye kuti akanasonyeza kuti sakumvera lamulo la tchalitchi ndiponso la boma.”—Mothers in the Fatherland.