Mutu 10
Muzinyansidwa ndi “Zinthu Zozama za Satana”
TIYATIRA
1. Kodi mpingo wa ku Tiyatira unatalikirana bwanji ndi mipingo ina, ndipo mumzinda umene munali mpingowo munkachitika zinthu zotani zachipembedzo?
PAFUPIFUPI makilomita 65 kum’mwera chakum’mawa kwa mzinda wa Bergama (Pegamo) m’dziko la Turkey, kuli mzinda wotukuka wa Akhisar. Zaka pafupifupi 1,900 zapitazo, pamalo pamene pali mzindawu panali mzinda wa Tiyatira. Woyang’anira woyendayenda akanatha kufika mosavuta kumpingo wa ku Tiyatira podutsa mumsewu winawake wochokera ku Pegamo. Kuchokera kumeneku, akanatha kukafika kumipingo ina yonse yotsala ya m’dera limeneli yotchulidwa m’chaputala 3 cha buku la Chivumbulutso. Mipingo yake inali Sade, Filadefiya ndi Laodikaya. Mosiyana ndi mzinda wa Pegamo, zikuoneka kuti anthu ambiri a mumzinda wa Tiyatira sankalambira mfumu. Komabe, mumzindawu munali akachisi a milungu yachikunja. Ndiponso mzinda wa Tiyatira unali wotchuka pa nkhani za malonda.
2, 3. (a) Kodi malemba ena a m’Baibulo amanena za munthu wina uti wa ku Tiyatira amene anadzakhala Mkhristu? (b) Kodi mfundo yakuti Yesu ndi “Mwana wa Mulungu” komanso yakuti “maso ake ali ngati lawi la moto,” inali yofunika bwanji kwa Akhristu a ku Tiyatira?
2 Pamene Paulo ankalalikira ku Makedoniya, anakumana ndi mayi wina wa ku Tiyatira, dzina lake Lidiya, amene ankagulitsa nsalu ndi zovala zofiirira. Lidiya ndi anthu onse a m’banja lake anamvetsera mosangalala uthenga umene Paulo ankalalikira ndipo anamuchereza bwino kwambiri pamodzi ndi abale amene anali nawo. (Machitidwe 16:14, 15) Zikuoneka kuti mayi ameneyu ndiye anali munthu woyamba wa ku Tiyatira kukhala Mkhristu. Patapita nthawi, mumzindawu munadzakhala mpingo wa Akhristu. Uthenga wautali kwambiri wa Yesu unapita kumpingo umenewu. Iye anati: “Kwa mngelo wa mpingo wa ku Tiyatira lemba kuti: Izi ndi zimene Mwana wa Mulungu akunena, iye amene maso ake ali ngati lawi la moto, ndipo mapazi ake ali ngati mkuwa woyengedwa bwino.”—Chivumbulutso 2:18.
3 Awa ndi malo amodzi okha amene pakupezeka mawu akuti “Mwana wa Mulungu” m’buku la Chivumbulutso, ngakhale kuti m’mavesi ena Yesu anamutchula Yehova kuti “Atate wanga.” (Chivumbulutso 2:27; 3:5, 21) Mawu akuti “Mwana wa Mulungu” ayenera kuti anakumbutsa Akhristu a ku Tiyatira za ubwenzi wapadera wapakati pa Yesu ndi Yehova. Maso a Mwana ameneyu “ali ngati lawi la moto.” Zimenezi zinali ngati chenjezo kwa Akhristu a ku Tiyatira lakuti iye adzawapatsa chilango choopsa ngati moto akadzapeza chodetsa chilichonse mumpingomo. Iye anabwerezanso kunena kuti mapazi ake ali ngati mkuwa wonyezimira. Zimenezi zikutsindika mfundo yakuti iye anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani ya kukhulupirika pa nthawi imene anali padziko lapansi. N’zosakayikitsa kuti Akhristu a ku Tiyatira anatsatira malangizo ake, ndipo ifenso masiku ano tiyenera kutero.—1 Petulo 2:21.
4, 5. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anayamikira Akhristu a ku Tiyatira? (b) Kodi mpingo wa ku Tiyatira ukufanana bwanji ndi mipingo ya Mboni za Yehova masiku ano?
4 Koma n’zosangalatsa kuti Yesu anapeza zinthu zimene akanatha kuyamikirira mpingo wa ku Tiyatira. Iye anati: “Ndikudziwa ntchito zako, chikondi chako, chikhulupiriro chako, utumiki wako, ndi kupirira kwako. Ndikudziwanso kuti ntchito zako zapanopa n’zambiri kuposa zoyamba zija.” (Chivumbulutso 2:19) Mosiyana ndi Akhristu a ku Efeso, Akhristu odzozedwa a ku Tiyatira sanasiye kukonda Yehova ngati mmene ankamukondera poyamba. Iwo anali ndi chikhulupiriro cholimba. Komanso, ntchito zawo za pa nthawiyo zinali zambiri kuposa za poyamba, ndipo mofanana ndi mipingo ina itatu imene inatchulidwa kale m’mbuyomu, Akhristu a ku Tiyatira ankapitiriza kupirira. Zimenezi zikufanana ndi zimene zikuchitika m’mipingo ya Mboni za Yehova padziko lonse, yomwe ilipo yoposa 100,000 masiku ano. M’gulu la Yehova, zimachita kuonekeratu kuti Akhristu onse, achikulire ndi achinyamata omwe, ali ndi mtima wokonda kulalikira mwakhama. Zimenezi zimasonyeza kuti iwo amakonda kwambiri Yehova. Ambiri mwa Akhristuwa amachita upainiya, ndipo amagwiritsa ntchito bwino nthawi imene yatsalayi polengeza uthenga wopatsa chiyembekezo wonena za kubwera kwa Ufumu wa Mulungu.—Mateyu 24:14; Maliko 13:10.
5 Kwa zaka zambiri, Akhristu odzozedwa amene akadali ndi moyo padziko lapansi, komanso a khamu lalikulu, akhala akupereka chitsanzo chabwino kwambiri popitiriza kupirira pamene akutumikira Mulungu mokhulupirika. Iwo akhala akuchita zimenezi pamene zinthu m’dzikoli zikuipiraipira ndipo anthu alibenso chiyembekezo chilichonse. Koma ifeyo tisataye mtima. Buku la Chivumbulutso limatsimikizira zimene aneneri ena a Mulungu ananenapo m’mbuyomu, monga zakuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.”—Zefaniya 1:14; Yoweli 2:1; Habakuku 2:3; Chivumbulutso 7:9; 22:12, 13.
“Mayi Uja Yezebeli”
6. (a) Ngakhale kuti Akhristu a ku Tiyatira ankachita bwino kwambiri zinthu zina, kodi Yesu anaona vuto lotani mumpingowo, limene linafunika kuthetsedwa mwamsanga? (b) Kodi Yezebeli anali ndani, ndipo kodi anali ndi chilichonse chomuyenereza kukhala mneneri?
6 Maso a Yesu ooneka ngati lawi la moto anaonanso zinthu zina. Iye anaona vuto limene linafunika kuthetsedwa mwamsanga. Yesu anauza Akhristu a ku Tiyatira kuti: “Komabe, ndakupeza ndi mlandu uwu. Walekerera mayi uja Yezebeli, amene amadzitcha mneneri. Iye amaphunzitsa ndi kusocheretsa akapolo anga kuti azichita dama ndi kudya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano.” (Chivumbulutso 2:20) M’zaka za m’ma 900 B.C.E., Mfumukazi Yezebeli, amene ankalambira Baala ndipo anali mkazi wa Mfumu Ahabu ya ku Isiraeli,anatchuka ndi kupha anthu, kuchita chigololo, ndiponso kupondereza anthu. Koma Yehu, amene anadzozedwa ndi Yehova, analamula kuti Yezebeli aphedwe. (1 Mafumu 16:31; 18:4; 21:1-16; 2 Mafumu 9:1-7, 22, 30, 33) Yezebeli wolambira mafanoyo analibe chilichonse chomuyenereza kukhala mneneri. Iye sanali ngati Miriamu ndi Debora, omwe anali aneneri okhulupirika a ku Isiraeli. (Ekisodo 15:20, 21; Oweruza 4:4; 5:1-31) Ndipo mzimu wa Yehova sunamuchititse kunenera ngati mmene unathandizira ana aakazi anayi a mlaliki Filipo, komanso Anna, yemwe anali wokalamba kwambiri, kuti anenere.—Luka 2:36-38; Machitidwe 21:9.
7. (a) Ponena kuti “mayi uja Yezebeli,” kodi Yesu ayenera kuti ankatanthauza ndani? (b) Kodi azimayi ena a m’gulu limeneli mwina ankachita zotani pofuna kusonyeza kuti khalidwe lawo losafuna kuuzidwa zochita silinali lolakwika?
7 Choncho n’zoonekeratu kuti “mayi uja Yezebeli,” amene ankadzitcha mneneri ku Tiyatira, anali wonyenga chifukwa sankathandizidwa ndi mzimu wa Mulungu. Koma kodi iye anali ndani? Mwina iye anali mayi kapena gulu la azimayi limene mopanda manyazi, linkalimbikitsa ena mumpingomo kuchita zinthu zoipa. Mwina azimayi ena a m’gulu limeneli ankalimbikitsa anthu mumpingomo kuchita chiwerewere, n’kumapotoza dala malemba kuti zimene ankachitazo zioneke ngati sizinali zolakwika. Iwo analidi aneneri onyenga. Ankalimbikitsa anthu ena kuti awatsatire pochita “dama, zinthu zodetsa, chilakolako cha kugonana, chikhumbo choipa, ndi kusirira kwa nsanje, kumene ndiko kulambira mafano.” (Akolose 3:5) Iwo ankalimbikitsa anthu kukhala ndi khalidwe lachiwerewere komanso mtima wodzitukumula, zinthu zimene Matchalitchi Achikhristu ambiri masiku ano amangozisekerera.
8. (a) Kodi Yesu anapereka uthenga wotani kwa “Yezebeli” wa ku Tiyatira? (b) Kodi azimayi ena achita zinthu zotani zosokoneza ena mumpingo masiku ano?
8 Yesu anapitiriza kuuza akulu a mpingo wa ku Tiyatira kuti: “Ndamupatsa nthawi kuti alape, koma sakufuna kulapa dama lake. Taona! Ndatsala pang’ono kumudwalitsa kwambiri, ndipo ochita naye chigololo ndiwaponya m’masautso aakulu, kupatulapo ngati atalapa ntchito zawo zofanana ndi za mayiyo.” (Chivumbulutso 2:21, 22) Mofanana ndi Yezebeli, amene zikuoneka kuti ankalamulira mwamuna wake Ahabu, ndipo kenako anachitira mwano Yehu, yemwe anatumidwa ndi Mulungu kuti adzamuphe, azimayi oipawa mwina ankanyengerera amuna awo komanso akulu kuti azichita zinthu zoipa. Zikuoneka kuti akulu mumpingo wa Tiyatira ankalekerera khalidwe losokoneza langati la Yezebeli limeneli. Yesu anawachenjeza mwamphamvu Akhristu amenewa, ndipo masiku ano chenjezoli likupitanso ku mpingo wa padziko lonse wa anthu a Yehova. Masiku ano, azimayi ena osafuna kuuzidwa zochita ofanana ndi Yezebeli, anyengererapo amuna awo kuti akhale ampatuko ndipo afika ngakhale potengera ku khoti atumiki a Yehova okhulupirika.—Yerekezerani ndi Yuda 5-8.
9. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu a Yesu onena za Yezebeli sakusonyeza kuti akazi onse mumpingo ali ndi khalidwe loipa? (b) Kodi akazi amasonyeza khalidwe loipa la Yezebeli akayamba kuchita chiyani?
9 Zimenezi sizikusonyeza kuti akazi okhulupirika mumpingo wachikhristu nawonso ali ndi khalidwe loipali. Masiku ano, alongo okhulupirika ndi amene akuchita zambiri pa ntchito yolalikira. Iwo akubweretsa anthu ambiri atsopano mumpingo kudzera m’maphunziro a Baibulo apanyumba amene amachititsa. Mulungu amadalitsa dongosolo limeneli, monga mmene lemba la Salimo 68:11 likusonyezera. Lembali limati: “Yehova wapereka lamulo, ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu.” Khalidwe lofatsa komanso laulemu la akazi, limene ndi ‘lamtengo wapatali pamaso pa Mulungu,’ likhoza kuthandiza amuna awo kuti azichita zinthu bwino. (1 Petulo 3:1-4) Baibulo limasonyeza kuti mkazi wabwino ndiponso wazintchito anatamandidwa ndi Mfumu Lemueli. (Miyambo 31:10-31) Koma akazi akayamba khalidwe loipa lonyengerera amuna awo komanso akayamba kuderera kapena kunyalanyaza dongosolo la umutu, amasonyeza khalidwe loipa la Yezebeli.—Aefeso 5:22, 23; 1 Akorinto 11:3.
10. (a) N’chifukwa chiyani Yezebeli ndi ana ake anayenera kupatsidwa chilango? (b) Kodi ndi zinthu zoopsa ziti zimene zimachitikira anthu amene ndi ana a Yezebeli, ndipo anthu amenewo ayenera kuchita chiyani?
10 Popitiriza kufotokoza za “mayi uja Yezebeli,” Yesu anati: “Ana ake ndidzawapha ndi mliri wakupha, moti mipingo yonse idzadziwa kuti ineyo ndiye amene ndimafufuza impso ndi mitima, ndipo ndidzabwezera mmodzi ndi mmodzi wa inu malinga ndi ntchito zake.” (Chivumbulutso 2:23) Yesu anapatsa Yezebeli ndi ana ake nthawi yoti alape, koma iwo anapitirizabe khalidwe lawo lachiwerewere. Choncho anayenera kulangidwa. Pamenepa pali chenjezo lamphamvu kwa Akhristu masiku ano. Anthu amene amatsanzira Yezebeli, kaya ndi amuna kapena akazi, akudwala kwambiri mwauzimu. Iwo amakhala ana ake pophwanya mfundo za m’Baibulo zokhudza umutu ndi makhalidwe abwino, kapena posafuna kumva za ena n’kumanyalanyaza dongosolo limene gulu la Mulungu limachitira zinthu. Ngati munthu woteroyo ataitana akulu a mumpingo kuti amupempherere, “pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa.” Komabe iye ayenera kudzichepetsa n’kumachita zinthu zogwirizana ndi pempherolo. Ndipo aliyense asaganize kuti angapusitse Mulungu kapena Khristu poyesa kubisa khalidwe lachiwerewere kapena pochita utumiki mwakhama kwambiri kuti aphimbe tchimo.—Yakobo 5:14, 15.
11. Kodi mipingo masiku ano imathandizidwa bwanji kuti isalekerere akazi ofuna kusokoneza mumpingo?
11 N’zosangalatsa kuti mipingo yambiri ya Mboni za Yehova masiku ano imayesetsa kupewa khalidwe loipali. Akulu amakhala tcheru kwambiri kuti makhalidwe osagwirizana ndi dongosolo limene Mulungu amayendetsera zinthu komanso makhalidwe ena oipa, asalowerere mumpingo. Iwo amayesetsa kuthandiza abale ndi alongo amene ayamba kuchita zinthu zimene zingawavulaze mwauzimu, kuti asinthe mofulumira ndi kukhala olimba. (Agalatiya 5:16; 6:1) Oyang’anira achikhristu amenewa amachita zinthu molimba mtima ndiponso mwachikondi poletsa alongo amene ayamba kupanga timagulu tolimbikitsa ufulu wa amayi mumpingo. Komanso, malangizo a pa nthawi yake amaperekedwa nthawi ndi nthawi m’mabuku a Mboni za Yehova.a
12. Kodi Akhristu odzozedwa masiku ano amasonyeza bwanji mtima wosalekerera zoipa wofanana ndi wa Yehu?
12 Koma ngati munthu wachita chiwerewere, makamaka ngati wakhala akuchita zimenezi mobwerezabwereza, ayenera kuchotsedwa mumpingo akapanda kulapa. Tisaiwale kuti Yehu anali ndi mtima wosalekerera zoipa ndipo anachita khama kwambiri pofuna kuchotsa zinthu zonse zoipa zimene Yezebeli anayambitsa mu Isiraeli. Mofanana ndi Yehu, Akhristu odzozedwa masiku ano nawonso salekerera zoipa, ndipo amapereka chitsanzo chabwino kwa Akhristu a “nkhosa zina,” omwe ali ngati “Yehonadabu.” Pochita zimenezi, iwo amasonyeza kuti ndi osiyana kwambiri ndi atsogoleri a Matchalitchi Achikhristu, amene amangolekerera zoipa.—2 Mafumu 9:22, 30-37; 10:12-17.
13. Kodi chidzachitike n’chiyani kwa anthu amene ayamba kuchita zinthu zoipa chifukwa chotengera akazi osokoneza mumpingo?
13 Mwana wa Mulungu, yemwe ndi Mthenga wa Yehova komanso Woweruza, anachita zinthu moyenera podzudzula Yezebeli wamakono n’kumutaya chifukwa chakuti akudwala, popeza matenda ake auzimu ndi osachiritsika. (Malaki 3:1, 5) Anthu amene ayamba kuchita zinthu zoipa chifukwa chotengera akazi osokoneza mumpingo amakumananso ndi masautso aakulu. Masautsowa akutanthauza chisoni chimene anthuwa amamva akachotsedwa mumpingo, n’kutayidwa kunja kwa mpingo wachikhristu ngati kuti afa. Anthu amenewa akapanda kulapa, kutembenuka, n’kubwereranso mumpingo, adzafa imfa yeniyeni ndi “mliri wakupha,” pa chisautso chachikulu kapena chisautsochi chisanafike. Komabe, Mulungu akhoza kuwalandiranso ngati atalapa moona mtima n’kusiya machimo awo onse.—Mateyu 24:21, 22; 2 Akorinto 7:10.
14. (a) Kodi Yesu amagwiritsira ntchito bwanji akulu pothetsa mavuto osiyanasiyana, monga vuto la akazi ofuna kusokoneza mumpingo ngati Yezebeli? (b) Kodi mpingo uyenera kutani posonyeza kuti ukugwirizana ndi akulu amene amaweruza nkhani ngati zimenezi?
14 “Mipingo yonse” iyenera kudziwa kuti Yesu amafufuza “impso,” kutanthauza zinthu za pansi pa mtima, ndiponso amafufuza ‘mtima,’ umene umaimira munthu wamkati, kuphatikizapo zolinga za munthu pochita zinthu zinazake. Pofufuza zimenezi, Yesu amagwiritsira ntchito nyenyezi, kapena kuti akulu odalirika, pothana ndi vuto linalake monga la akazi ofuna kusokoneza mpingo ngati Yezebeli. (Chivumbulutso 1:20) Akuluwa akafufuza mokwanira nkhani ngati imeneyi n’kupereka chiweruzo, anthu ena sayenera kufunsafunsa zifukwa zimene akuluwo aweruzira nkhaniyo motero. Anthu onse mumpingo ayenera kudzichepetsa n’kuvomereza zimene akuluwo agamula, ndipo ayenera kupitiriza kugwirizana ndi akuluwo, omwe ali ngati nyenyezi za mumpingo. Anthu amene amakhalabe okhulupirika kwa Yehova n’kumagonjera dongosolo limene iye akugwiritsa ntchito m’gulu lake, adzadalitsidwa. (Salimo 37:27-29; Aheberi 13:7, 17) Choncho yesetsani kuti Yesu akamadzapereka mphoto kwa aliyense malinga ndi ntchito zake, inuyo adzakupatseni madalitso.—Agalatiya 5:19-24; 6:7-9.
“Gwirani Mwamphamvu . . . Zimene Muli Nazo”
15. (a) Kodi Yesu anawauza chiyani anthu amene sanasokonezedwe ndi Yezebeli? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti si anthu onse amene ankati ndi Akhristu mu 1918 omwe anasokonezedwa ndi Matchalitchi Achikhristu ampatuko?
15 Mawu otsatira amene Yesu ananena anali olimbikitsa. Iye anati: “Komabe, kwa ena nonse amene muli ku Tiyatira, nonsenu amene mulibe chiphunzitso chimenechi, amene simudziwa chilichonse chokhudza zinthu zimene amazitcha ‘zinthu zozama za Satana,’ ndikuti: Sindikusenzetsani katundu wina wolemera. Gwirani mwamphamvu zomwe zija, zimene muli nazo, mpaka nditabwera.” (Chivumbulutso 2:24, 25) Yesu anapeza kuti ku Tiyatira kunali anthu ena okhulupirika amene sanasokonezedwe ndi akazi ofanana ndi Yezebeli. Mofanana ndi zimenezi, kwa zaka 40 chaka cha 1918 chisanafike, ndiponso kuyambira m’chaka chimenechi mpaka panopa, si anthu onse amene amati ndi Akhristu omwe akhala akulekerera khalidwe lachiwerewere ndiponso makhalidwe ena oipa amene afala kwambiri m’Matchalitchi Achikhristu. Gulu lochepa la Ophunzira Baibulo, amene panopa amatchedwa Mboni za Yehova, anayesetsa kuthandiza anthu a matchalitchi ena kuzindikira kuti zinthu zambiri zimene Matchalitchi Achikhristu amaphunzitsa n’zachikunja. Iwo anayesetsanso kusiya kukhulupirira kapena kutsatira zinthu zonse zonyenga zochokera ku Babulo zimene Matchalitchi Achikhristu ampatuko amaphunzitsa. Zimenezi zikuphatikizapo khalidwe lolekerera zoipa la “mayi uja Yezebeli.”
16. Ngakhale kuti Yesu ndiponso bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi sanasenzetse Akhristu katundu wina wolemera, kodi ndi zinthu zotani zimene tiyenera kupewa?
16 Akhristu odzozedwa masiku ano amalimbikitsanso anzawo a khamu lalikulu kuti azipewa chiwerewere, monga chimene chimaonetsedwa mu zinthu zosangalatsa zoipa zamasiku ano. Si bwino kuonerera kapena kuchita zinthu zoipa chifukwa chochita nazo chidwi kapena pongofuna kudziwa zinthu zoyenera kupewa. M’malomwake, ndi nzeru kupeweratu “zinthu zozama za Satana.” Pa nkhani imeneyi, Yesu anati: “Sindikusenzetsani katundu wina wolemera.” Zimenezi zikutikumbutsa malangizo amene bungwe lolamulira la m’nthawi ya atumwi linapereka, akuti: “Mzimu woyera pamodzi ndi ife taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera, kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano, magazi, zopotola, ndi dama. Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri, zinthu zidzakuyenderani bwino.” (Machitidwe 15:28, 29) Kuti zinthu zikuyendereni bwino mwauzimu, muyenera kupewa chipembedzo chonyenga, kugwiritsira ntchito magazi molakwika (monga kuthiridwa magazi), ndi chiwerewere. Mukatero, zidzakuthandizaninso kuti mukhale ndi thanzi labwino.
17. (a) Kodi masiku ano Satana amakopa bwanji anthu ndi “zinthu zozama”? (b) Kodi “zinthu zozama” za m’dziko la Satana lotukukali tiyenera kuziona bwanji?
17 Masiku ano, Satana ali ndi ‘zinthu zina zozama,’ monga nkhani zovuta kumvetsa ndiponso ziphunzitso zopanda maziko zomwe zimakopa anthu amene amadziona kuti ndi anzeru. Kuwonjezera pa maganizo olekerera zoipa ndi zachiwerewere, zina mwa zinthu zozama za Satana ndi kukhulupirira mizimu ndiponso chiphunzitso chakuti zamoyo zinachita kusanduka kuchokera ku zinthu zina. Kodi Mlengi wathu, yemwe ndi wanzeru zonse, amaona bwanji “zinthu zozama” zimenezi? Mtumwi Paulo analemba zimene Mulungu ananena, zakuti: “Ndidzaononga nzeru za anzeru.” Mosiyana ndi “zinthu zozama” za Satana, “zinthu zozama za Mulungu” ndi zosavuta kumva ndiponso zolimbikitsa. Akhristu anzeru amapewa “zinthu zozama” za m’dziko la Satana lotukukali. Kumbukirani kuti “dziko likupita limodzi ndi chilakolako chake, koma wochita chifuniro cha Mulungu adzakhala kosatha.”—1 Akorinto 1:19, Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero; 2:10; 1 Yohane 2:17.
18. Kodi Yesu analonjeza madalitso otani kwa Akhristu odzozedwa amene adzakhalebe okhulupirika mpaka pa mapeto, ndipo iwo akadzaukitsidwa adzagwira ntchito yotani pa Aramagedo?
18 Tsopano Yesu anauza Akhristu a ku Tiyatira mawu olimbikitsa kwambiri. Mawu amenewa amalimbikitsanso Akhristu odzozedwa masiku ano. Iye anati: “Ndipo amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatira zochita zanga kufikira mapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu ya anthu. Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yachitsulo, ngati imenenso ine ndailandira kwa Atate wanga.” (Chivumbulutso 2:26, 27) Umenewu ndi mwayidi wapadera kwambiri. Ulamuliro umene Akhristu odzozedwa opambana pa nkhondo amalandira akaukitsidwa ukutanthauza mwayi wogwiritsira ntchito “ndodo yachitsulo” limodzi ndi Yesu powononga mitundu yosamvera Mulungu pa Aramagedo. Zida zanyukiliya zimene mitundu imeneyi ili nazo sizidzaphula kanthu pamene Khristu azidzaphwanya adani akewo ngati mbiya zadothi.—Salimo 2:8, 9; Chivumbulutso 16:14, 16; 19:11-13, 15.
19. (a) Kodi “nthanda” ikuimira ndani, ndipo idzaperekedwa bwanji kwa anthu opambana pa nkhondo? (b) Kodi anthu a khamu lalikulu amalimbikitsidwa ndi chiyani?
19 Yesu anapitiriza kuti: “Ndidzamupatsanso nthanda.” (Chivumbulutso 2:28) Kenako Yesu anafotokoza zimene “nthanda” imeneyi ikuimira, ponena kuti, “Ine ndine muzu ndi mbadwa ya Davide. Ndinenso nthanda yonyezimira.” (Chivumbulutso 22:16) Inde, Yesu ndi amene anakwaniritsa ulosi umene Yehova anakakamiza Balamu kuti anene, wakuti: “Nyenyezi idzatuluka mwa Yakobo, ndodo yachifumu idzatulukadi mu Isiraeli.” (Numeri 24:17) Kodi Yesu adzapereka bwanji “nthanda” kwa anthu opambana pa nkhondo? Zikuoneka kuti adzachita zimenezi podzipereka yekha kwa iwo, n’kuwatenga monga mabwenzi ake apamtima kwambiri. (Yohane 14:2, 3) Zimenezi ziyenera kuti zimalimbikitsa kwambiri Akhristu odzozedwa kuti apitirize kupirira. Anthu a khamu lalikulu amasangalalanso kudziwa kuti Yesu, yemwe ndi “nthanda yonyezimira,” posachedwapa adzagwiritsira ntchito mphamvu zake monga Mfumu pobwezeretsa Paradaiso padziko lapansi pano.
Pitirizani Kutumikira Mulungu ndi Mtima Wosagawanika
20. Kodi m’Matchalitchi Achikhristu mwakhala mukuchitika zinthu zotani zimene zikutikumbutsa za mavuto ena amene anali mumpingo wa ku Tiyatira?
20 Uthenga umenewu uyenera kuti unalimbikitsa kwambiri Akhristu a ku Tiyatira. Zinali zolimbikitsa kwambiri kuti Mwana wa Mulungu, ali mu ulemerero wake kumwamba, alankhule kwa Akhristu a ku Tiyatira n’kuwauza zinthu zina zimene ankafunika kukonza. Anthu ena mumpingowo ayenera kuti anatsatira malangizo ochokera kwa m’busa wachikondiyu. Uthenga umenewu, womwe ndi wautali kwambiri pa mauthenga 7 aja, umatithandizanso kudziwa mpingo woona wa Akhristu masiku ano. M’chaka cha 1918, pamene Yesu anabwera kudzapereka chiweruzo pa kachisi wa Yehova, anapeza kuti matchalitchi ambiri amene ankati ndi achikhristu ankapembedza mafano komanso ankachita chiwerewere chauzimu. (Yakobo 4:4) Matchalitchi ena ankatenga ziphunzitso zawo kwa azimayi ofuna kutsogolera mpingo a m’zaka za m’ma 1800, monga Ellen White, wa mpingo wa Seventh-Day Adventist ndiponso Mary Baker Eddy wa mpingo wa Christian Scientists. Chaposachedwapa, azimayi ambiri ayamba kumalalikira kugome m’matchalitchi ochuluka. (Yerekezerani ndi 1 Timoteyo 2:11, 12.) Magulu osiyanasiyana a Akatolika, nthawi zambiri amalemekeza kwambiri Mariya kuposa Mulungu ndi Khristu. Koma Yesu sankalemekeza Mariya mwanjira imeneyo. (Yohane 2:4; 19:26) Kodi matchalitchi amene amalola kuti akazi azitsogolera mpingo, kapena kuti azilemekezedwa motere angakhaledi Akhristu enieni?
21. Kodi Mkhristu aliyense payekha angaphunzirepo chiyani pa uthenga wa Yesu wopita kumpingo wa ku Tiyatira?
21 Mkhristu aliyense payekha, kaya wodzozedwa kapena wa nkhosa zina, ayenera kuganizira mofatsa uthenga umenewu. (Yohane 10:16) Akhristu ena angakopeke n’kuyamba kutsatira anthu ochita zoipa, ngati mmene anachitira anthu amene ankatsatira akazi ofanana ndi Yezebeli a ku Tiyatira. Komanso nthawi zina munthu angafune kupeza zifukwa zodzikhululukira pa nkhani zinazake. Mwachitsanzo, masiku ano Akhristu ayenera kusankha chochita ngati akumana ndi nkhani yokhudza kuthiridwa magazi kapena kudya zakudya zopangidwa ndi magazi. Ena angaganize kuti chifukwa chakuti amalimbikira kwambiri utumiki wa kumunda kapena chifukwa chakuti amakamba nkhani pa mpingo, ndiye kuti akhoza kumachita zinthu zina zolakwika, monga kuonerera mafilimu achiwawa kapena olaula, kapenanso kumwa mowa kwambiri. Chenjezo la Yesu kwa Akhristu a mumpingo wa ku Tiyatira likusonyeza kuti sitiyenera kuchita zinthu zolakwika zoterozo. Yehova amafuna kuti tikhale oyera ndiponso kuti tizimutumikira ndi mtima wonse, ngati mmene Akhristu ambiri a ku Tiyatira ankachitira.
22. Kodi Yesu anatsindika bwanji kufunika kokhala ndi makutu akumva?
22 Pomaliza, Yesu anati: “Amene ali ndi makutu amve zimene mzimu ukunena ku mipingo.” (Chivumbulutso 2:29) Aka n’kachinayi tsopano kuti Yesu abwereze mawu amenewa, ndipo anawabwerezanso pamapeto pa mauthenga atatu amene akubwera kutsogoloku. Kodi inuyo muli ndi makutu akumva? Ngati muli nawo, pitirizani kumvetsera pamene Mulungu, kudzera mwa mzimu wake, akupitiriza kutipatsa malangizo m’gulu lake.
[Mawu a M’munsi]
a Mwachitsanzo, onani nkhani yakuti “Akazi Achikristu Okhulupirika Ndi Olambira Mulungu Ofunika Kwambiri,” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 2003.
[Zithunzi patsamba 51]
Masiku ano, alongo okhulupirika ndi amene akuchita zambiri pa ntchito yolalikira. Iwo amagonjera modzichepetsa anthu amene akutsogolera m’gulu la Mulungu