Mutu 14
Ulemerero wa Mpando Wachifumu wa Yehova Wakumwamba
Masomphenya 2—Chivumbulutso 4:1–5:14
Nkhani yake: Zinthu zochititsa chidwi zochitika kumpando wachifumu wa Mulungu wachiweruzo
Nthawi ya kukwaniritsidwa kwake: Masomphenya amenewa ndi a zinthu zimene zinayamba kuchitika mu 1914 mpaka kumapeto kwa ulamuliro wa Yesu wa Zaka 1,000, n’kupitirirabe mpaka m’tsogolo, pamene cholengedwa chilichonse kumwamba ndi padziko lapansi chidzatamanda Yehova.—Chivumbulutso 5:13.
1. Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi kwambiri ndi masomphenya amene Yohane akutifotokozera?
TSOPANO Yohane akuyamba kutifotokozera masomphenya ena ochititsa chidwi kwambiri. Mwa mphamvu ya mzimu woyera, iye adakali m’tsiku la Ambuye. Choncho zimene akufotokoza zikutikhudza kwambiri ifeyo, amene tikukhaladi m’tsiku limeneli. Pogwiritsira ntchito masomphenya amenewa, Yehova anatithandiza kuona zinthu zosaoneka zakumwamba, ndiponso kumvetsa mmene iye amaonera chiweruzo chake, chimene akuyembekezera kupereka padziko lapansi. Komanso, kaya tili ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo kumwamba kapena padziko lapansi pompano, masomphenya amenewa amatithandiza kuona zimene tingachite kuti tigwirizane ndi chifuniro cha Yehova. Choncho tonsefe tiyenera kupitiriza kuchita chidwi kwambiri ndi mawu a Yohane akuti: ‘Wodala ndi munthu amene amawerenga mokweza, ndiponso anthu amene akumva mawu a ulosi umenewu, komanso amene akusunga zolembedwamo.’—Chivumbulutso 1:3.
2. Kodi Yohane anaona chiyani?
2 Zimene Yohane anaona n’zochititsa chidwi kwambiri kuposa vidiyo ina iliyonse imene anthu anaonapo masiku ano. Iye analemba kuti: “Zimenezi zitatha, nditayang’ana ndinaona khomo lotseguka kumwamba. Ndipo mawu oyamba amene ndinawamva akundilankhula anali ngati kulira kwa lipenga. Mawuwo anali akuti: ‘Kwera kumwamba kuno, ndikuonetse zinthu zimene ziyenera kuchitika.’” (Chivumbulutso 4:1) M’masomphenya, Yohane anaona kumwamba kosaoneka kumene Yehova amakhala, kumene n’kutali kwambiri kuposa m’mlengalenga mmene asayansi ya zakuthambo amapita, ndiponso kuposa ngakhale kumene kuli milalang’amba ya m’chilengedwechi. Yohane anakhala ngati walowa pakhomo lotsegula ndipo anaitanidwa kuti aone kumwamba kwenikweni kumene kumakhala zolengedwa zauzimu, komanso kumene kuli mpando wachifumu wa Yehova. Zimene anaonazo zinali zokongola mogometsa. (Salimo 11:4; Yesaya 66:1) Unalidi mwayi wapadera kwambiri kuona zinthu zimenezi.
3. Kodi mawu amene “anali ngati kulira kwa lipenga” akutikumbutsa za chiyani, ndipo n’zodziwikiratu kuti ndani analankhula mawuwa?
3 Baibulo silinena kuti “mawu oyamba” amene Yohane anamva anali a ndani. Mofanana ndi mawu amphamvu a Yesu amene iye anamva m’mbuyomu, mawu oyambawo anali amphamvu ngati kulira kwa lipenga. (Chivumbulutso 1:10, 11) Mawu amenewa akutikumbutsa kulira kwamphamvu kwa lipenga la nyanga ya nkhosa paphiri la Sinai kosonyeza kuti Yehova anali paphiripo. (Ekisodo 19:18-20) Choncho n’zodziwikiratu kuti Yehova ndi amene analankhula mawu amenewa. (Chivumbulutso 1:1) Iye anatsegula khomo kuti Yohane, mwa masomphenya, alowe m’malo oyera koposa m’chilengedwe chonse chimene Yehova amalamulira.
Mpando Wachifumu wa Yehova Ndi Waulemerero Kwambiri
4. (a) Kodi masomphenya amene Yohane anaona ali ndi tanthauzo lotani kwa Akhristu odzozedwa? (b) Kodi masomphenyawa ali ndi tanthauzo lotani kwa anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi?
4 Kodi Yohane anaona chiyani? Tamverani pamene iye akutifotokozera zinthu zosangalatsa kwambiri zimene anaona. Iye anati: “Zitatero, nthawi yomweyo ndinakhala mumphamvu ya mzimu, ndipo mpando wachifumu unaoneka uli pamalo ake kumwamba, wina atakhalapo.” (Chivumbulutso 4:2) M’kanthawi kochepa, mzimu woyera unathandiza Yohane kuti akhale ngati wapita kumwamba, kumene anaonako mpando wachifumu wa Yehova. Yohane ayenera kuti anasangalala kwambiri. Iye anaoneratu pang’ono chabe kumwamba kokongola kwambiri, kumene iye ndi Akhristu ena odzozedwa amalandira “cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka.” (1 Petulo 1:3-5; Afilipi 3:20) Masomphenya a Yohane amenewa alinso ndi tanthauzo lalikulu kwa anthu amene ali ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi. Masomphenyawa amawathandiza kumvetsa ulemerero waukulu wa malo amene Yehova amakhala, komanso wa dongosolo lakumwamba limene Yehova amagwiritsa ntchito poweruza mitundu ya anthu ndiponso limene adzagwiritse ntchito polamulira anthu padziko lapansi m’tsogolo muno. Zoonadi, Yehova ndi Mulungu wadongosolo kwambiri.
5. Kodi Yohane anaona zinthu zenizeni ziti, zimene zinkaimiridwa ndi chivundikiro cha likasa la pangano?
5 Zambiri zimene Yohane anaona kumwambako zinali zofanana ndi zinthu zina zimene zinali pachihema m’chipululu. Chihemachi chinamangidwa zaka pafupifupi 1,600 Yohane asanaone masomphenyawa, kuti chikhale malo opatulika oti Aisiraeli azilambirirapo Mulungu woona. M’Malo Opatulikitsa a chihemacho munali likasa la pangano limene linali ndi chivundikiro chopangidwa ndi golide yekhayekha. Yehova analankhula kuchokera pamwamba pa chivundikiro cha Likasalo. (Ekisodo 25:17-22; Aheberi 9:5) Choncho chivundikiro cha Likasalo chinkaimira mpando wachifumu wa Yehova. Koma tsopano Yohane anaona zinthu zenizeni zimene chivundikirocho chinkaimira. Iye anaona Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa atakhala pampando wake wachifumu wakumwamba, womwe ndi waulemerero kwambiri.
6. Kodi Yohane akutipatsa chithunzi chotani cha ulemerero wa Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zoyenerera?
6 Mosiyana ndi aneneri ena a m’mbuyomu amene anaonapo masomphenya a mpando wachifumu wa Yehova, Yohane sanafotokoze mwatsatanetsatane za Woyera amene anakhala pampandopo. (Ezekieli 1:26, 27; Danieli 7:9, 10) Koma Yohane anafotokoza mmene anaonera wokhala pampando wachifumuyo, ndi mawu akuti: “Wokhala pampandoyo, anali wooneka ngati mwala wa yasipi, ndi mwala wofiira wamtengo wapatali. Utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi unazungulira mpando wachifumuwo.” (Chivumbulutso 4:3) Apatu Yohane anaona ulemerero waukulu kwabasi. Iye anaona kuti malowo anali abata komanso okongola kwambiri ngati miyala yamtengo wapatali yonyezimira. Zimenezi zikugwirizana bwino ndi mmene wophunzira Yakobo anamufotokozera Yehova, kuti ndi “Atate wa zounikira zonse zakuthambo.” (Yakobo 1:17) Yohane atangomaliza kumene kulemba buku la Chivumbulutso, ananena kuti: “Mulungu ndiye kuwala ndipo mwa iye mulibe mdima ngakhale pang’ono.” (1 Yohane 1:5) Inde, Yehova ndi Mulungudi waulemerero waukulu.
7. Kodi mfundo yakuti utawaleza wazungulira mpando wachifumu wa Yehova ikutiphunzitsa chiyani?
7 Taonani kuti Yohane anaona utawaleza wobiriwira ngati mwala wa emarodi, umene unazungulira mpando wachifumuwo. Mawu achigiriki amene anawamasulira kuti utawaleza palembali (irʹis) amatanthauza chinthu chozungulira ngati mpira. Utawaleza unatchulidwa koyamba m’Baibulo pofotokoza nkhani ya Nowa. Madzi a Chigumula ataphwa, Yehova anachititsa kuti utawaleza uoneke mumtambo. Iye anafotokoza zimene utawalezawo unkaimira ponena kuti: “Ndiika utawaleza mumtambo, kuti ukhale chizindikiro cha pangano pakati pa ine ndi dziko lapansi. Ndipo ndizikumbukira ndithu pangano la pakati pa ine ndi inu ndi chamoyo chilichonse. Komanso madzi sadzachitanso chigumula ndi kuwononga zamoyo zonse.” (Genesis 9:13, 15) Choncho kodi Yohane anakumbukira chiyani ataona masomphenya akumwambawa? Utawaleza umene anaonawo uyenera kuti unamukumbutsa za kufunika kokhala pamtendere ndi Yehova, ngati mmene Akhristu odzozedwa amakhalira naye masiku ano. Unamukumbutsanso kuti pamalo pokhala Yehova ndi pa bata ndi mtendere. Yehova akadzafutukulira chihema chake anthu onse omvera okhala padziko lapansi latsopano, padziko lonse padzakhalanso bata.—Salimo 119:165; Afilipi 4:7; Chivumbulutso 21:1-4.
Kodi Akulu 24 Akuimira Ndani?
8. Kodi Yohane anaona ndani kuzungulira mpando wachifumu, ndipo kodi iwo akuimira ndani?
8 Yohane ankadziwa kuti ansembe ndi amene ankaikidwa kuti azitumikira m’chihema chakale chija. Choncho mwina anadabwa kuona zinthu zotsatira zimene anazifotokoza. Iye anati: “Kuzungulira mpando wachifumuwo, panalinso mipando yachifumu yokwanira 24. Pamipando yachifumuyo, ndinaona patakhala akulu 24 ovala malaya akunja oyera, ndi zisoti zachifumu zagolide pamitu pawo.” (Chivumbulutso 4:4) Inde, m’malo mwa ansembe, iye anaona akulu 24, atakhala pamipando yachifumu ndiponso atavala zisoti zachifumu ngati mafumu. Kodi akulu amenewa akuimira ndani? Iwo si enanso koma Akhristu odzozedwa a mumpingo wachikhristu, ataukitsidwa n’kupatsidwa udindo umene Yehova anawalonjeza kumwamba. Kodi tikudziwa bwanji zimenezi?
9, 10. Kodi tikudziwa bwanji kuti akulu 24 akuimira mpingo wonse wa Akhristu odzozedwa atapatsidwa udindo wawo waulemerero kumwamba?
9 Choyamba, iwo avala zisoti zachifumu. Baibulo limati Akhristu odzozedwa adzapatsidwa “nkhata ya kumutu yosakhoza kuwonongeka,” kapena kuti, chisoti chachifumu chosakhoza kuwonongeka. Zimenezi zikutanthauza kuti iwo adzapatsidwa moyo wosatha womwe sungafe. (1 Akorinto 9:25; 15:53, 54) Koma popeza kuti akulu 24 amenewa akhala pamipando yachifumu, zisoti zachifumu zagolide munkhani imeneyi zikutanthauza kuti iwo ndi mafumu. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 6:2; 14:14.) Zimenezi zikugwirizana ndi mfundo yakuti akulu 24 amenewa akuimira Akhristu odzozedwa atapita kumwamba. Iwo ankatsatira mapazi a Yesu ali padziko lapansi, ndipo iye anachita nawo pangano loti adzakhala pamipando yachifumu mu Ufumu wake. (Luka 22:28-30) Yesu ndi akulu 24 okhawa, osaphatikizapo ngakhale angelo, ndi amene akufotokozedwa kuti akulamulira kumwamba, kumene kuli Yehova.
10 Zimenezi zikugwirizana ndi lonjezo limene Yesu anapereka kwa Akhristu a mumpingo wa ku Laodikaya, lakuti: “Wopambana pa nkhondo ndidzamulola kukhala nane pampando wanga wachifumu.” (Chivumbulutso 3:21) Koma udindo wakumwamba umene akulu 24 amenewa adzapatsidwe si wongolamulira basi. Pofotokoza za Yesu chakumayambiriro kwa buku la Chivumbulutso, Yohane anati: ‘Iye anatipanga kukhala mafumu ndi ansembe kwa Mulungu wake ndi Atate wake.’ (Chivumbulutso 1:5, 6) Choncho iwo ndi mafumu komanso ansembe, moti “adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi naye zaka 1,000.”—Chivumbulutso 20:6.
11. N’chifukwa chiyani mpake kuti akulu alipo okwanira 24, ndipo nambala imeneyi imaimira chiyani?
11 Kodi n’chiyani chochititsa chidwi ndi nambala ya 24, pa mfundo yakuti Yohane anaona akulu 24 atakhala mozungulira mpando wachifumu? Ansembe okhulupirika a mu Isiraeli ankachitira chithunzi akulu amenewa m’njira zambiri. Mtumwi Petulo analembera Akhristu odzozedwa kuti: “Inu ndinu ‘fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera, anthu odzakhala chuma chapadera.’” (1 Petulo 2:9) Ndipotu ansembe achiyuda kalelo anagawidwa m’magulu 24. Gulu lililonse linkapatsidwa milungu ingapo pa chaka kuti litumikire Yehova pakachisi, ndipo ankachita zimenezi kuti utumiki wopatulika uzichitika nthawi zonse mosadukiza. (1 Mbiri 24:5-19) Choncho mpake kuti Yohane anaona akulu 24 m’masomphenya a ansembe akumwambawo chifukwa ansembe amenewo akutumikira Yehova mosalekeza. Odzozedwa onse akadzapita kumwamba, adzagawidwa m’magulu 24, ndipo gulu lililonse lidzakhala ndi opambana pa nkhondo okwana 6,000. Izi zili choncho chifukwa lemba la Chivumbulutso 14:1-4, limanena kuti opambana pa nkhondowa alipo 144,000 (24 x 6,000) ndipo “anagulidwa kuchokera mwa anthu” kuti akaimirire paphiri la Ziyoni limodzi ndi Mwanawankhosa, Yesu Khristu. Popeza nambala ya 12 imaimira gulu limene Mulungu amaliona kuti n’lokwanira bwino komanso ladongosolo, nambala ya 24, yomwe ndi 12 kuwirikiza kawiri, ikutsindika kwambiri mfundo yakuti gulu lakumwamba limeneli n’lokwanira bwino ndiponso ladongosolo.
Mphezi, Mawu ndi Mabingu
12. Kodi kenako Yohane anaona ndi kumva chiyani, ndipo “mphezi, mawu, ndi mabingu” zikutikumbutsa chiyani?
12 Kodi kenako Yohane anaona ndi kumva chiyani? “Kumpando wachifumuko kunali kutuluka mphezi, mawu, ndi mabingu.” (Chivumbulutso 4:5a) Zimenezi zikutikumbutsa nthawi zinanso pamene mphamvu za Yehova zinaonekera bwino kwambiri kuchokera kumwamba. Mwachitsanzo, pamene Yehova “anatsikira” paphiri la Sinai, Mose ananena kuti: “Pa tsiku lachitatu kutacha, kunayamba kuchita mabingu ndi mphezi. Mtambo wakuda unakuta phiri, ndipo kunamveka kulira kwamphamvu kwambiri kwa lipenga la nyanga ya nkhosa. . . . Pamene kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako kunali kupitiriza kukwererakwerera, Mose anayamba kulankhula, ndipo Mulungu woona anamuyankha ndi mawu amphamvu.”—Ekisodo 19:16-19.
13. Kodi mphezi zochokera kumpando wachifumu wa Yehova zikuimira chiyani?
13 M’tsiku la Ambuye, Yehova akusonyeza mphamvu ndiponso kukhalapo kwake moonekera bwino kwambiri. Yehova sakuchita zimenezi pogwiritsira ntchito mphezi zenizeni chifukwa Yohane ankaona masomphenya. Nanga mphezizo zikuimira chiyani? N’zoona kuti mphezi ingaunikire munthu, koma ingathenso kumupha. Choncho mphezi zochokera kumpando wachifumu wa Yehova zimenezi zikuimira kuwala kwa choonadi kumene iye akupereka kwa anthu ake, komanso mwapadera kwambiri, zikuimira mauthenga ake a chiweruzo omwe ali ngati moto.—Yerekezerani ndi Salimo 18:14; 144:5, 6; Mateyu 4:14-17; 24:27.
14. Kodi mawu amveka bwanji masiku ano?
14 Nanga bwanji za mawu amene Yohane anamva? Pamene Yehova anatsikira paphiri la Sinai, Mose anamva mawu ake. (Ekisodo 19:19) Malamulo ndiponso mauthenga ambiri amene analembedwa m’buku la Chivumbulutso anaperekedwa kudzera m’mawu ochokera kumwamba. (Chivumbulutso 4:1; 10:4, 8; 11:12; 12:10; 14:13; 16:1, 17; 18:4; 19:5; 21:3) Masiku ano, Yehova waperekanso malamulo ndiponso mauthenga kwa anthu ake powathandiza kumvetsa bwino maulosi ndi mfundo za m’Baibulo. Kawirikawiri mfundo zotithandiza kumvetsa bwino choonadi zimafotokozedwa pamisonkhano ya mayiko, ndipo kenako choonadi cha m’Baibulo chimenechi chimalengezedwa padziko lonse. Ponena za Akhristu okhulupirika amene akulalikira uthenga wabwino, mtumwi Paulo anati: “Pajatu ‘liwu lawo linamveka padziko lonse lapansi, ndipo mawu awo anamveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.’”—Aroma 10:18.
15. Kodi ndi mabingu otani amene akuchokera kumpando wachifumu m’chigawo chino cha tsiku la Ambuye?
15 Kawirikawiri mphezi ikawala, kenako kumamveka bingu. Davide anayerekezera “liwu la Yehova” ndi bingu lenileni. (Salimo 29:3, 4) Pamene Yehova ankathandiza Davide pomenyana ndi adani ake, malemba amanena kuti panamveka mabingu ochokera kwa Yehova. (2 Samueli 22:14; Salimo 18:13) Elihu anauza Yobu kuti Yehova ‘akamachita zinthu zazikulu zimene sitingazidziwe,’ mawu ake amamveka ngati bingu. (Yobu 37:4, 5) M’chigawo chino cha tsiku la Ambuye, Yehova ‘akubangula’ ngati mabingu popereka chenjezo la zinthu zazikulu zimene adzachite powononga adani ake. Mabingu ophiphiritsa amenewa, omwe ndi mawu ochenjeza, akumveka mobwerezabwereza padziko lonse. Ndinu odala ngati mwamvera mauthenga omveka ngati mabingu amenewa komanso ngati mukugwiritsira ntchito lilime lanu mwanzeru polengeza nawo mauthengawo.—Yesaya 50:4, 5; 61:1, 2.
Nyale Zamoto Ndiponso Nyanja Yoyera Mbee! Ngati Galasi
16. Kodi “nyale zamoto 7” zikuimira chiyani?
16 Kodi Yohane anaonanso chiyani? Iye anafotokoza zimene anaona kuti: “Panalinso nyale zamoto 7 zikuyaka patsogolo pa mpando wachifumuwo. Zimenezo zikuimira mizimu 7 ya Mulungu. Patsogolo pa mpando wachifumuwo, panali nyanja yoyera mbee! ngati galasi, yooneka ngati mwala wa kulusitalo.” (Chivumbulutso 4:5b, 6a) Yohane anafotokoza yekha tanthauzo la nyale 7 zimenezo kuti: “Zimenezo zikuimira mizimu 7 ya Mulungu.” Nambala ya 7 imaimira zinthu zimene Mulungu akuona kuti n’zokwanira, choncho nyale 7 ziyenera kuti zikuimira mphamvu zokwanira za mzimu woyera zothandiza anthu kumvetsa choonadi. Ndithudi Akhristu odzozedwa masiku ano akuyamikira kwambiri mwayi umene apatsidwa womvetsa choonadi, ndipo apatsidwanso udindo wophunzitsa choonadicho kwa anthu amene ali ndi njala yauzimu padziko lapansi. Tikusangalala kwambiri kuti chaka chilichonse magazini a Nsanja ya Olonda mamiliyoni ambirimbiri akupitiriza kuwalitsa choonadi chimenechi m’zinenero zoposa 188.—Salimo 43:3.
17. Kodi “nyanja yoyera mbee! ngati galasi, yooneka ngati mwala wa kulusitalo” ikuimira chiyani?
17 Yohane anaonanso “nyanja yoyera mbee! ngati galasi, yooneka ngati mwala wa kulusitalo.” Kodi nyanja imeneyi ikuimira chiyani kwa oitanidwa m’bwalo la Yehova lakumwamba? Paulo ananena za njira imene Yesu anagwiritsira ntchito poyeretsa mpingo kuti, “anauyeretsa pousambitsa m’madzi a mawu a Mulungu.” (Aefeso 5:26) Yesu asanaphedwe, anauza ophunzira ake kuti: “Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ine ndalankhula kwa inu.” (Yohane 15:3) Choncho nyanja yoyera mbee! ngati galasi, yooneka ngati mwala wa kulusitalo imeneyi, iyenera kuti ikuimira Mawu a Mulungu olembedwa, amene ali ndi mphamvu yoyeretsa anthu. Mafumu komanso ansembe amenewo, omwe anafika pamaso pa Yehova, ayenera kuti anayeretsedwa bwino kwambiri ndi Mawu ake.
Yohane Anaonanso “Zamoyo Zinayi”
18. Kodi Yohane anaona chiyani pakati m’pakati pa mpando wachifumuwo komanso mouzungulira?
18 Kenako Yohane anaonanso zinthu zina. Iye analemba kuti: “Pakati m’pakati pa mpando wachifumuwo, ndiponso mouzungulira, panali zamoyo zinayi zokhala ndi maso ambirimbiri, kutsogolo ndi kumbuyo komwe.”—Chivumbulutso 4:6b.
19. Kodi zamoyo zinayi zikuimira chiyani, ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?
19 Kodi zamoyo zimenezi zikuimira chiyani? Masomphenya amene mneneri Ezekieli anaona akutithandiza kupeza yankho. Ezekieli anaona Yehova atakhala pampando wachifumu womwe unali pagaleta lakumwamba, ndipo pafupi ndi galetalo panali zamoyo zooneka mofanana ndi zamoyo zimene Yohane anaona. (Ezekieli 1:5-11, 22-28) Kenako, Ezekieli anaonanso galeta lokhala ndi mpando wachifumu lomwe lija limodzi ndi zamoyo zija. Koma pa nthawi ino, iye ananena kuti zamoyozo zinali akerubi. (Ezekieli 10:9-15) Choncho, zamoyo zinayi zimene Yohane anaona ziyenera kuti zikuimira akerubi ambirimbiri a Mulungu. Ndipotu akerubi ndi zolengedwa za udindo waukulu m’gulu la Mulungu la zolengedwa zauzimu. Yohane ayenera kuti sanadabwe ataona akerubi ataima pafupi kwambiri ndi Yehova. Izi zili choncho chifukwa kale pamene Aisiraeli ankalambira Mulungu kuchihema, akerubi awiri agolide anaikidwa pamwamba pa chivundikiro cha likasa la pangano, lomwe linkaimira mpando wachifumu wa Yehova. Mawu a Yehova anamveka kuchokera pakati pa akerubi awiri amenewa popereka malamulo ku mtunduwo.—Ekisodo 25:22; Salimo 80:1.
20. Kodi mfundo yakuti zamoyo zinayi zili “pakati m’pakati pa mpando wachifumuwo, ndiponso mouzungulira,” ingatanthauze chiyani?
20 Zolengedwa zamoyo zinayizi zili “pakati m’pakati pa mpando wachifumuwo, ndiponso mouzungulira.” Kodi mawu amenewa akutanthauza chiyani kwenikweni? Mawuwa angatanthauze kuti akerubiwo aima mozungulira mpando wachifumuwo, ndipo aliyense waima pakati kumbali zonse za mpandowo. Motero, anthu amene anamasulira Baibulo linalake lachingelezi (Today’s English Version), anamasulira mawu achigiriki amene anagwiritsidwa ntchito palembali kuti: “mozungulira mpando wachifumuwo kumbali zake zonse.” Komanso, mawuwa angatanthauze kuti zamoyo zinayizo zili pakatikati penipeni kumwamba, pamalo amene pali mpando wachifumu. Mwina n’chifukwa chake Baibulo la Chipangano Chatsopano mu Chichewa cha Lero linamasulira vesili kuti: “pakatipo, kuzungulira mpando wachifumuwo.” Mfundo yofunika kwambiri ndi yakuti akerubiwo ali pafupi kwambiri ndi mpando wachifumu wa Yehova, mofanana ndi akerubi amene Ezekieli anaona aliyense ataima pakona la galeta la Yehova, lomwe likuimira gulu lake. (Ezekieli 1:15-22) Mfundo zonsezi zikugwirizana ndi lemba la Salimo 99:1, lomwe limati: “Yehova wakhala mfumu. . . . Iye wakhala pa akerubi.”
21, 22. (a) Kodi Yohane anafotokoza kuti zamoyo zinayi zinali ndi maonekedwe otani? (b) Kodi maonekedwe a chamoyo chilichonse pa zamoyo zinayizo akuimira chiyani?
21 Yohane anapitiriza kuti: “Chamoyo choyamba chinali ngati mkango. Chamoyo chachiwiri chinali ngati mwana wa ng’ombe wamphongo. Chamoyo chachitatu chinali ndi nkhope ngati ya munthu, ndipo chamoyo chachinayi chinali ngati chiwombankhanga chimene chikuuluka.” (Chivumbulutso 4:7) N’chifukwa chiyani zamoyo zinayizi zili ndi maonekedwe osiyanasiyana? Zikuoneka kuti maonekedwe osiyanasiyana a zamoyo zimenezi akuimira makhalidwe apadera a Mulungu. Chamoyo choyamba chinali ngati mkango. Baibulo limagwiritsa ntchito mkango ngati chizindikiro chosonyeza kulimba mtima, makamaka poyesetsa kutsatira chilungamo. (2 Samueli 17:10; Miyambo 28:1) Choncho, mkango ndi chizindikiro choyenera choimira khalidwe la Mulungu lolimba mtima pofuna kuchita zinthu mwachilungamo. (Deuteronomo 32:4; Salimo 89:14) Chamoyo chachiwiri chinali chooneka ngati mwana wa ng’ombe wamphongo. Kodi ng’ombe yamphongo ikukukumbutsani khalidwe liti? Aisiraeli ankaona kuti ng’ombe yamphongo ndi chuma chapadera kwambiri chifukwa cha mphamvu zake. (Miyambo 14:4; onaninso Yobu 39:9-11.) Motero, chamoyo chooneka ngati mwana wa ng’ombe wamphongo chikuimira mphamvu, makamaka mphamvu zochuluka kwambiri zimene Yehova amapereka.—Salimo 62:11; Yesaya 40:26.
22 Chamoyo chachitatu chinali ndi nkhope ngati ya munthu. Zimenezi ziyenera kuti zikuimira khalidwe la chikondi ngati cha Mulungu. Munthu amatha kusonyeza khalidwe lalikulu kwambiri la Mulungu, lomwe ndi chikondi. Izi zili choncho chifukwa padziko lonse lapansi ndi munthu yekha amene analengedwa m’chifaniziro cha Mulungu. (Genesis 1:26-28; Mateyu 22:36-40; 1 Yohane 4:8, 16) N’zosakayikitsa kuti akerubi amasonyeza khalidwe limeneli akamatumikira Yehova atazungulira mpando wake wachifumu. Nanga kodi chamoyo chachinayi chinali chiyani? Chamoyo chimenechi chinali chooneka ngati chiwombankhanga chimene chikuuluka. Pa nthawi ina, Yehova anachita kunena yekha kuti chiwombankhanga chimaona patali kwambiri. Iye anati: “Maso ake amaona kutali kwambiri.” (Yobu 39:29) Motero, chiwombankhanga ndi chizindikiro choyenerera choimira nzeru zotha kuona patali kwambiri. Yehova ndi kuchimake kwa nzeru, ndipo akerubi ake amasonyeza nzeru zochokera kwa iye akamamvera malamulo ake.—Miyambo 2:6; Yakobo 3:17.
Mawu Ofuula Otamanda Yehova
23. Kodi mfundo yakuti zamoyo zinayizo “zinali ndi maso thupi lonse” ikutanthauza chiyani, ndipo mapiko awiriawiri amene anali kumbali zitatu akusonyeza chiyani?
23 Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “Zamoyo zinayizo, chilichonse chinali ndi mapiko 6. Zinali ndi maso thupi lonse ngakhalenso kunsi kwa mapiko. Zamoyo zimenezi sizinali kupuma usana ndi usiku. Zinali kunena kuti: ‘Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, amene analipo, amene alipo, ndi amene akubwera.’” (Chivumbulutso 4:8) Mfundo yakuti zamoyozo zinali ndi maso thupi lonse ikutanthauza kuti zimatha kuona bwino komanso zimaona patali. Zamoyo zinayizo zimachita zimenezi mosalekeza chifukwa sizifunika kugona. Zamoyo zimenezi zimatsanzira Mulungu, ndipo ponena za iye malemba amati: “Pajatu maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wawo uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Popeza kuti akerubi ali ndi maso ambiri choncho, amatha kuona pena paliponse, ndipo palibe chimene chili chobisika kwa iwo. Choncho iwo ndi oyenerera bwino kutumikira Mulungu pa ntchito yake yopereka chiweruzo. Ponena za Mulungu, Malemba amati: “Maso a Yehova ali paliponse. Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.” (Miyambo 15:3) Akerubiwo anali ndi mapiko awiriawiri kumbali zitatu, kudzanja lamanja, lamanzere komanso kutsogolo. M’Baibulo, 3 ndi nambala imene imagwiritsidwa ntchito posonyeza kutsindika. Choncho mfundo yakuti akerubiwo ali ndi mapiko awiriawiri kumbali zitatu ikusonyeza kuti iwo angathamange mofulumira kwambiri ngati mphezi pokalengeza chiweruzo cha Yehova ndiponso pokachipereka.
24. Kodi akerubi amatamanda bwanji Yehova, ndipo zimenezi n’zofunika chifukwa chiyani?
24 Yohane anamva akerubiwo akuimba nyimbo yokoma ndiponso yogwira mtima yotamanda Yehova, yakuti: “Woyera, woyera, woyera ndiye Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, amene analipo, amene alipo, ndi amene akubwera.” Panonso mawu akuti “woyera” abwerezedwa katatu, kusonyeza kuti akerubiwo anatsindika kwambiri za kuyera kwa Yehova Mulungu. Iye ndiye Kuchimake kwa chiyero ndiponso Muyezo wapamwamba kwambiri wa chiyero. Komanso iye ndi “Mfumu yamuyaya,” ndipo nthawi zonse ndiye “Alefa ndi Omega, woyamba ndi wotsiriza, chiyambi ndi mapeto.” (1 Timoteyo 1:17; Chivumbulutso 22:13) Akerubi amenewa sapuma pa ntchito yawo yolengeza m’chilengedwe chonse makhalidwe apamwamba kwambiri a Yehova, amene ndi oposa a wina aliyense.
25. Kodi zamoyo zija zinagwirizana bwanji ndi akulu 24 polemekeza Yehova?
25 Mawu otamanda Yehova anamveka kumwamba kwenikweniko. Yohane anapitiriza kufotokoza kuti: “Nthawi zonse zamoyozo zikamapereka ulemerero, ndi ulemu, ndiponso zikamayamikira Wokhala pampando wachifumuyo, Iye amene adzakhalabe ndi moyo kwamuyaya, akulu 24 aja anali kugwada ndi kuwerama pamaso pa Wokhala pampando wachifumuyo, ndi kulambira wokhala ndi moyo kwamuyayayo. Iwo anali kuponya pansi zisoti zawo zachifumu pamaso pa mpando wachifumuwo, ndi kunena kuti: ‘Ndinu woyenera, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandira ulemerero ndi ulemu, chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.’” (Chivumbulutso 4:9-11) M’Malemba monse, awa ndi amodzi mwa mawu amphamvu kwambiri opereka ulemu kwa Yehova, Mulungu wathu komanso Ambuye Wamkulu Koposa.
26. N’chifukwa chiyani akulu 24 anaponya pansi zisoti zawo zachifumu pamaso pa Yehova?
26 Akulu 24 anasonyeza mtima ngati umene Yesu amasonyeza, ndipo anafika ngakhale poponya pansi zisoti zawo zachifumu pamaso pa Yehova. Iwo saganiza ngakhale pang’ono zochita zinthu zodzikweza pamaso pa Mulungu. Modzichepetsa, iwo amazindikira kuti cholinga chimene akhalira mafumu n’choti azipereka ulemu ndi ulemerero kwa Mulungu, ngati mmene Yesu amachitira nthawi zonse. (Afilipi 2:5, 6, 9-11) Iwo ndi ogonjera ndipo amadziwa kuti udindo wawo ndi wotsika kwambiri poyerekezera ndi udindo wa Yehova Mulungu. Komanso iwo amavomereza kuti ulamuliro wawo umadalira ulamuliro wa Yehova. Motero, iwo amagwirizana ndi akerubi ndiponso zolengedwa zonse zokhulupirika potamanda ndi kulemekeza Mulungu amene analenga zinthu zonse.—Salimo 150:1-6.
27, 28. (a) Kodi tiyenera kukhudzidwa bwanji tikaganizira zimene Yohane anafotokoza m’masomphenya amenewa? (b) Kodi pali mafunso otani okhudza zinthu zotsatira zimene Yohane anaona ndi kumva?
27 Palibe amene sangakhudzidwe mtima atawerenga nkhani yofotokoza za masomphenya amene Yohane anaona. Masomphenyawo anali aulemerero ndiponso ochititsa chidwi kwambiri. Popeza Yohane anaona masomphenya chabe, ndiye kuti kumwamba kwenikweniko kumene kuli mpando wachifumu wa Yehova, n’kogometsa kwambiri. Aliyense akaganizira za ulemerero wa Yehova, ayenera kukhala ndi mtima woyamikira kwambiri komanso ayenera kugwirizana ndi zamoyo zinayi ndiponso akulu 24 aja pomutamanda, popemphera komanso polengeza za dzina lake. Akhristu masiku ano ali ndi mwayi wokhala mboni za Mulungu ameneyu. (Yesaya 43:10) Kumbukirani kuti masomphenya a Yohane anali onena za tsiku la Ambuye, limene tikukhalamoli. Komanso “mizimu 7” ndi yokonzeka nthawi zonse kutitsogolera ndi kutilimbikitsa. (Agalatiya 5:16-18) Masiku ano, tilinso ndi Mawu a Mulungu amene amatithandiza kukhala oyera pamene tikutumikira Mulungu, yemwenso ndi woyera. (1 Petulo 1:14-16) Ndipo ndife osangalala kwambiri kuwerenga mokweza mawu a ulosi umenewu. (Chivumbulutso 1:3) Mawu amenewa amatilimbikitsa kwambiri kuti tikhale okhulupirika kwa Yehova ndiponso kuti tisalole dzikoli kutilepheretsa kutamanda Mulungu mwakhama.—1 Yohane 2:15-17.
28 Pofika pano, Yohane wafotokoza zimene anaona pamene anaitanidwa kuti alowe pakhomo lotseguka kumwamba. Chosangalatsa kwambiri n’chakuti iye anafotokoza kuti anaona Yehova, yemwe ndi wolemekezeka kwambiri komanso waulemerero waukulu, atakhala pampando wake wachifumu kumwamba. Iye anazunguliridwa ndi zolengedwa zomwe zapanga gulu lamphamvu kwambiri kuposa gulu lina lililonse. Gulu limeneli ndi laulemerero ndiponso lokhulupirika kwambiri. Yohane anaona bwalo la milandu la kumwamba limeneli litakhala pansi. (Danieli 7:9, 10, 18) Tsopano zonse zinali m’malo kuti chinthu chinachake chapadera chichitike. Kodi chinthu chimenecho n’chiyani, ndipo chikutikhudza bwanji ifeyo masiku ano? Tiyeni tione pamene Yohane akupitiriza kufotokoza.
[Chithunzi chachikulu pasamba 75]
[Chithunzi chachikulu pasamba 78]