Kutengedwa m’Thupi
Tanthauzo: Chikhulupiriro chakuti Akristu okhulupirika adzatengedwa ndi matupi awo padziko lapansi, kuchotsedwa mwadzidzidzi padziko, kugwirizana ndi Ambuye “m’mlengalenga.” Mawuwo “kutengedwa m’thupi” amamvedwa ndi ena, koma osati ndi onse, kukhala tanthauzo la 1 Atesalonika 4:17. Liwulo silikupezeka m’Malemba ouziridwa.
Pamene mtumwi Paulo adanena kuti Akristu ‘akakwatulidwa’ kukakhala ndi Ambuye, kodi anali kulankhula nkhani yanji?
1 Ates. 4:13-18: “Sitifuna, abale, kuti mukhale osadziŵa za iwo akugona [“iwo akugona mu imfa,” NE; “awo amene adamwalira,” TEV, JB], kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi Iye iwo akugona mwa Yesu. Pakuti ichi tinena kwa inu m’mawu a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo. Pakuti Ambuye adzatsika kumwamba mwini yekha ndi mfuu, ndi mawu a mngelo wamkulu, ndi lipenga la Mulungu. Ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka; pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nawo pamodzi m’mitambo, kukomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse. Chomwecho, tonthozanani ndi mawu awa.” (Mwachiwonekere mamembala ena a mpingo Wachikristu m’Tesalonika anali atafa. Paulo analimbikitsa amoyowo kutonthozana ndi chiyembekezo cha chiukiriro. Iye anawakumbutsa kuti Yesu anaukitsidwa pambuyo pa imfa yake; choteronso, pakudza kwa Ambuye, Akristu okhulupirika amene anali atamwalira pakati pawo akaukitsidwa kuti akhale ndi Kristu.)
Kodi ndani amene ‘adzakwatulidwira m’mitambo,’ monga momwe kwalongosoledwera pa 1 Atesalonika 4:17?
Vesi 15 limafotokoza kuti ndiwo okhulupirika “otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye,” ndiko kuti, iwo akali amoyobe panthaŵi ya kudza kwa Kristu. Kodi iwo adzayamba afa? Mogwirizana ndi kunena kwa Aroma 6:3-5 ndi 1 Akorinto 15:35, 36, 44 (ogwidwa mawu patsamba 215) iwo ayenera kufa asanapeze moyo wakumwamba. Koma palibe kufunika kwa kuti iwo akhalebe mumkhalidwe wa imfa kuyembekezera kubweranso kwa Kristu. Iwo “adzakwatulidwa” mwadzidzidzi “m’kuthwanima kwa diso,” kukakhala ndi Ambuye.—1 Akor. 15:51, 52; ndiponso Chivumbulutso 14:13.
Kodi Kristu adzawoneka ndi maso pamtambo ndiyeno kukwatula Akristu okhulupirika kuloŵa nawo kumwamba pamene dziko likupenyerera?
Kodi Yesu adanena kuti kaya dziko likamuona iye kachiŵirinso ndi maso awo akuthupi?
Yoh. 14:19: “Katsala kanthaŵi ndipo dziko lapansi silidzandiwonanso; koma inu [ophunzira ake okulupirika] mudzandiwona; popeza ine ndiri ndi moyo inunso mudzakala ndi moyo.” (Kanyenye wawonjezeredwa.) (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 6:16.)
Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la ‘kutsika kumwamba’ kwa Ambuye?
Kodi Ambuye ‘angatsike kumwamba,’ monga momwe kwalongosoledwera pa 1 Atesalonika 4:16, popanda kuwoneka ndi maso akuthupi? M’masiku a Sodomu ndi Gomora wakale, Yehova ananena kuti ‘akatsika kudzawona’ zimene anthu anali kuchita. (Gen. 18:21) Koma pamene Yehova anapanga kufufuza kumeneko, palibe munthu amene anamuwona, ngakhale kuli kwakuti anawona oimira aungelo amene iye anatuma. (Yoh. 1:18) Mofananamo, popanda kufunikira kubwerera m’thupi, Yesu angapereke chisamaliro chake pa otsatira ake okhulupirika padziko lapansi kuwapatsa mphotho.
Pamenepa, kodi anthu “adzawona” Ambuye “alinkudza m’mitambo” m’lingaliro lotani?
Yesu adaneneratu kuti: “Pamenepo adzawona Mwana wa munthu [Yesu Kristu] alinkudza mumtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Luka 21:27, RS) Mawu amenewa kapena ofanana nawo m’malemba ena samatsutsana konse ndi zimene Yesu adanena monga momwe kwalembedwera pa Yohane 14:19. Talingalirani: Pa Phiri la Sinai, kodi nchiyani chimene chinawoneka pamene Mulungu ‘anadza kwa anthu mumtambo wakuda bii,’ monga momwe kwafotokozedwera pa Eksodo 19:9? Mulungu analipo mosawoneka; anthu Achiisrayeli anawona umboni wowoneka wa kukhalapo kwake, koma palibe aliyense wa iwo anawonadi Mulungu ndi maso awo. Choteronso, pamene Yesu ananena kuti akadza “mumtambo,” ayenera kukhala atatanthauza kuti akakhala wosawoneka ndi maso aumunthu koma kuti anthu akazindikira kukhalapo kwake. Iwo akakhoza ‘kumuwona’ ndi maso awo amaganizo, akumazindikira chenicheni chakuti iye analipo. (Kaamba ka ndemanga zowonjezereka, wonani mutu waukulu wakuti “Kubweranso kwa Kristu.”)
Kodi nkotheka kuti Akristu atengeredwe kumwamba ndi matupi awo enieni?
1 Akor. 15:50: “Ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi zisingathe kuloŵa ufumu wa Mulungu; kapena chivundi si chiloŵa chisavundi.”
Kodi chokumana nacho cha mneneri Eliya chimatsutsa zimenezi? Kutalitali. Chiyenera kuzindikiridwa mothandizidwa ndi mawu omvekera bwino a Yesu zaka mazana ambiri pambuyo pake akuti: “Kulibe munthu amene anakwera kumwamba, koma iye wotsikayo kuchokera kumwamba, Mwana wa munthu.” (Yoh. 3:13) Ngakhale kuli kwakuti Eliya anawonekera pamene “anakwera kumwamba ndi kamvumvulu,” zimenezi sizimatanthauza kuti anapita m’dziko la mizimu. Chifukwa ninji sanatero? Chifukwa chakuti pambuyo pake iye akusimbidwa kukhala akutumiza kalata yachidzudzulo kwa mfumu ya Yuda. (2 Maf. 2:11; 2 Mbiri 21:1, 12-15) Anthu asanatulukire ndege, Yehova kalelo anagwiritsira ntchito njira yake (magaleta amoto ndi kamvumvulu) kunyamula Eliya pansi kunka m’mwamba mmene mbalame zimauluka ndi kumpititsa kumalo ena.—Yerekezerani ndi Genesis 1:6-8, 20.
Kodi mwinamwake Akristu okhulupirika adzatengedwa kumka kumwamba mobisa, kungozimilirika padziko lapansi popanda kufa?
Aroma 6:3-5: “Kodi simudziŵa kuti ife tonse amene tinabatizidwa mwa Kristu Yesu; tinabatizidwa mu imfa yake? . . . Pakuti ngati ife tinakhala olumikizidwa ndi iye m’chifanizidwe cha imfa yake, koteronso tidzakhala m’chifanizidwe cha kuuka kwake.” (Zimene zinachitika kwa Yesu zimapereka chitsanzo. Ophunzira ake limodzi ndi ena anadziŵa kuti iye anali atafa. Iye sanabwezeredwe kumoyo wakumwamba kufikira pambuyo pa imfa yake ndi chiukiriro.)
1 Akor. 15:35, 36, 44: “Koma wina adzati, Akufa aukitsidwa bwanji? Ndipo adza nalo thupi lotani? Wopusa iwe, chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwanso cha moyo, ngati sichifa. Lifesedwa thupi lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu.” (Chotero imfa imadza choyamba munthuyo asanalandire thupi lauzimu limenelo, kodi sichoncho?)
Kodi Akristu onse okhulupirika adzatengedwa mozizwitsa padziko lapansi ndi Ambuye chisautso chachikulu chisanayambe?
Mat. 24:21, 22, NW: “Nthaŵi imeneyo kudzakhala chisautso chachikulu chimene sichinachitike chiyambire chiyambi cha dziko kufikira tsopano, inde, ndipo sichidzachitikanso. Kunena zowona, ngati akadapanda kufupikitsidwa masiku amenewo palibe munthu aliyense amene akanapulumuka; koma chifukwa cha osankhidwawo masiku amenewo adzafupikitsidwa.” (Zimenezi sizitanthauza kuti “osankhidwa” onse adzakhala atatengeredwa kumwamba chisautso chachikulu chisanayambe, kodi sichoncho? Mmalo mwake, zikupereka chiyembekezo kwa iwo limodzi ndi atsamwali awo okhala m’thupi, cha kupulumuka chisautso chachikulu chimenecho padziko lapansi.)
Chiv. 7:9, 10, 14: “Zitatha izi ndinapenya, tawonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwawo; ndipo afuula ndi mawu akulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa . . . Ndiwo akutuluka m’chisautso chachikulu.” (“Kuti atuluke” m’chinthu china munthuyo ayenera kuloŵa kapena kukhala mkati mwa chinthucho. Chotero khamu lalikulu limeneli liyenera kukhala anthu amene kwenikweni amaloŵa m’chisautso chachikulu ndi kutulukamo monga opulumuka.) (Ponena za kukhala kwawo padziko lapansi, wonani tsamba 209.)
Kodi nchitetezo chotani chimene chidzakhalapo kwa Akristu owona mkati mwa chisautso chachikulu?
Aroma. 10:13: “Amene aliyense adzaitana padzina la Ambuye [“Yehova” NW] adzapulumuka.”
Zef. 2:3: “Funani Yehova [NW, AS, Yg, By], ofatsa inu nonse a m’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.” (Ndiponso Yesaya 26:20)
Kodi mwinamwake Akristu onse owona adzatengedwera kumwamba pambuyo pa chisautso chachikulu?
Mat. 5:5: “Odala ali akufatsa; chifukwa adzalandira dziko lapansi.”
Sal. 37:29, RS: “Olungama adzalandira dziko [“dziko lapansi,” Ro, NW] ndi kukhalamo kosatha.” (Ndiponso vesi 10, 11, 34)
1 Akor. 15:50: “Thupi ndi mwazi zisingathe kuloŵa Ufumu wa Mulungu.”
Wonaninso mutu waukulu wakuti “Kumwamba”
Kodi nchifukwa ninji Akristu ena amatengeredwa kumwamba kukakhala ndi Kristu?
Chiv. 20:6: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.” (Popeza kuti iwo adzalamulira limodzi ndi Kristu, payenera kukhala anthu amene iwo adzawalamulira. Kodi amenewo ndani? Wonani Mateyu 5:5 ndi Salmo 37:29.)
Wonaninso mutu waukulu wakuti “Kubadwanso.”
Kodi opita kumwambawo adzabwezeredwa padziko lapansi pambuyo pake kudzakhala pano kosatha m’Paradaiso?
Miy. 2:21: “Owongoka mtima adzakhala m’dziko [“adzakhala padziko lapansi,” NE], angwiro nadzatsalamo.” (Wonani kuti malembawo samanena kuti anthu owongoka amenewo adzabwerera kudziko lapansi koma kuti adzatsalamo.)
1 Ates. 4:17: “Potero ife [Akristu okwatulidwira kumwamba] tidzakhala ndi Ambuye nthaŵi zonse.”
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Kodi mumakhulupirira m’kutengedwa m’thupi?’
Mungayanke kuti: ‘Ndimawona kuti anthu sali ofanana palingaliro la zimene kutengedwa m’thupi kumathanthauza. Ndingafunse amene ali malingaliro anu pa mfundoyi? . . . Pankhani iriyonse, kuli kopindulitsa kuyerekezera malingaliro athu ndi zimene Baibulo lenilenilo limanena. (Gwiritsirani ntchito zigawo za nkhani yapamwambapayi zimene zimagwira ntchito.)’
Kapena mungananene kuti: ‘Kutengedwa m’thupi kwalongosoledwa kwa ine kukhala makonzedwe a Akristu akuzemba. Ambiri amalingalira kuti imeneyi ndiyo njira imene adzazemba nayo chisautso chachikulu chirinkudza. Kodi inu mumalingalira motero?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani: (1) ‘Ndithudi ife tifuna chitetezo cha Mulungu panthaŵiyo, ndipo ndimawawona kukhala olimbikitsa kwambiri malemba ena amene amasonyeza mmene tingapindulire nacho. (Zef. 2:3)’ (2) ‘Mokondweretsa, Baibulo limasonyeza kuti Mulungu adzatetezera okhulupirika pompano padziko lapansi. (Miy. 2:21, 22) Zimenezo ziri zogwirizana ndi chifuno cha Mulungu pamene iye choyamba analenga Adamu ndi kumuika m’Paradaiso poyambapo, Kodi sichoncho?’
Kuthekera kwina: ‘Mwa kunena kuti kutengedwa m’thupi inu mukutanthauza kuti Akristu okhala ndi moyo pamapeto a dongosolo la zinthu adzatengedwa kumka nawo kumwamba, kodi sichoncho? . . . Kodi mudayamba mwadabwa zimene iwo adzachita pamene afika kumwambako? . . . Tawonani zimene Chivumbulutso 20:6 (ndi 5:9, 10) chimanena. . . . Koma kodi iwo adzalamulira yani? (Sal. 37:10, 11, 29)’