Mutu 1
Mauthenga Ochokera Kumwamba
BAIBULO lathunthu liri, m’chenicheni, uthenga wochokera kumwamba, pokhala utaperekedwa ndi Atate wathu wakumwamba kaamba ka malangizo athu. Komabe, mauthenga aŵiri apadera anaperekedwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo ndi mngelo amene ‘amaimirira pamaso pa Mulungu.’ Dzina lake ndilo Gabrieli. Tiyeni tipende mikhalidwe ya maulendo ofunika aŵiriŵa akudziko lapansi.
Chakacho ndicho cha 3 B.C.E. M’mapiri a Yudeya, mwinamwake osati kutali kwambiri ndi Yerusalemu, kumakhala wansembe wa Yehova wotchedwa Zakariya. Iye ngwokalamba, choteronso mkazi wake, Elizabeti. Ndipo alibe ana. Zakariya akuchita ntchito yake yautumiki wansembe m’kachisi wa Mulungu mu Yerusalemu. Mwadzidzidzi Gabrieli awonekera kumbali yalamanja la guwa lansembe lazopsereza.
Zakariya akuwopa kwambiri. Koma Gabrieli akuchotsa mantha ake, akumati: “Usawope Zakariya, chifukwa kuti lamveka pemphero lako, ndipo mkazi wako adzakubalira mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yohane.” Gabrieli akupitiriza kulengeza kuti Yohane ‘adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova’ ndi kuti ‘adzakonzeratu Yehova anthu okonzeka.’
Komabe, Zakariya sangakhulupirire zimenezo. Zikuwonekera kukhala zosatheka kuti iye ndi Elizabeti angakhale ndi mwana pamsinkhu wawo. Chotero Gabrieli akumuuza kuti: “Udzakhala wotonthola ndi wosakhoza kulankhula, kufikira tsiku limene zidzachitika izi, popeza kuti sunakhulupirira mawu anga.”
Eya, panthaŵiyo, anthu ali kunja akudabwa chifukwa chake Zakariya akuchedwa m’kachisi. Potsirizira pake pamene akutuluka, satha kulankhula koma akungochita zizindikiro ndi manja ake, ndipo iwo akuzindikira kuti wawona kanthu kena kamphamvu yoposa yaumunthu.
Zakariya atamaliza nyengo yake yautumiki wa pakachisi, akupita kwawo. Ndipo mwamsanga pambuyo pake zikuchitikadi—Elizabeti akukhala ndi pakati! Pamene akuyembekezera kubadwa kwa mwana wake, Elizabeti akubindikira m’nyumba wosawonedwa ndi anthu kwa miyezi isanu.
Pambuyo pake Gabrieli akuwonekeranso. Ndipo kodi iye akulankhula kwa yani? Kwa namwali wosakwatiwa wotchedwa Mariya wa kutawuni ya Nazarete. Kodi ndiuthenga wanji umene akumubweretsera panthaŵi ino? Tamvetserani! “Wochitidwa chisomo, Ambuye ali ndi iwe,” Gabrieli akuuza Mariya motero. “Tawona udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu.” Gabrieli akuwonjezeranso kuti: “Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: . . . ndipo iye adzachita ufumu pabanja la Yakobo kunthaŵi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.”
Tingatsimikizire kuti Gabrieli akukulingalira kukhala wamwaŵi kupereka mauthenga ameneŵa. Ndipo pamene tiŵerenga zowonjezereka zonena za Yohane ndi Yesu, tidzawona bwino lomwe chifukwa chake mauthenga ameneŵa ochokera kumwamba ali ofunika kwambiri. 2 Timoteo 3:16; Luka 1:5-33.
▪ Kodi ndimauthenga aŵiri ati ofunika amene akuperekedwa kuchokera kumwamba?
▪ Kodi ndani akupereka mauthengawo, ndipo nkwa yani kumene akuperekedwa?
▪ Kodi nchifukwa ninji mauthengawo ali ovuta kwambiri kuwakhulupirira?