Mbali 2
Kodi Ndani Angatiuze?
1 Kodi ndani angatiuze chifuno chenicheni cha moyo? Eya, mutati mupite kwa munthu wopanga makina ndi kumpeza akupanga makina ocholoŵana amene simukuwadziŵa, kodi mungadziŵe motani chifuno chake? Njira yabwino koposa ikakhala yakuti mufunse wopangayo.
2 Pamenepo, bwanji nanga za zinthu zodabwitsa zimene timaona motizinga padziko lapansili, monga ngati zinthu zonse zamoyo, mpaka selo laling’onong’onolo? Ngakhale mamolekyu ndi maatomu ochepetsetsawo amene ali mkati mwa selo anapangidwa modabwitsa ndi mwadongosolo. Bwanjinso za kapangidwe kodabwitsa ka maganizo a munthu? Ndipo bwanji ponena za mapulaneti athu ozungulira dzuŵa, ndi Mlalang’amba wathu, ndi chilengedwe chonse? Kodi zinthu zolinganizidwa mochititsa mantha zonsezi sizinafunikire Wolinganiza? Ndithudi iye akhoza kutiuza chifukwa chimene analinganizira zinthu zimenezo.
Kodi Moyo Unakhalako Mwamwaŵi?
3 The Encyclopedia Americana inasonyeza “kucholoŵana kodabwitsa ndi kulinganizika m’zolengedwa zamoyo” ndipo inati: “Kupenda mosamalitsa maluŵa, tizilombo, kapena nyama zoyamwitsa kumasonyeza njira yodabwitsa imene ziŵalo zinaikidwira m’malo oyenera bwino koposa.” Katswiri wa za kuthambo wa ku Britain Bwana Bernard Lovell, akumanena za mpangidwe wamakemikolo wa zamoyo, analemba kuti: “Kuthekera kwa . . . chochitika cha mwamwaŵi chochititsa kupangika kwa imodzi ya mamolekyu aang’ono kwambiri a proteni nkwakung’ono zedi. . . . Kulidi kosatheka.”
4 Mofananamo, katswiri wa za kuthambo Fred Hoyle anati: “Dongosolo lonse la maphunziro a zamoyo losasintha limanenabe kuti moyo unayambika wokha. Komabe pamene akatswiri a misanganizo ya makemikolo a zamoyo akupeza zowonjezereka ponena za kucholoŵana kodabwitsa kwa moyo, kuli kowonekeratu kuti kuthekera kwakuti unakhalako mwamwaŵi nkwakung’ono kwakuti kunganyalanyazidwe kotheratu. Moyo sungakhaleko mwamwaŵi.”
5 Molecular biology, imodzi ya sayansi yamakono kwambiri, ndiyo kuphunzira zinthu zamoyo mwakupenda majini, mamolekyu, ndi maatomu a zinthu zamoyo. Katswiri wa molecular biology Michael Denton akunena za zimene zapezedwa: “Kucholoŵana kwa selo wamba lodziŵika kuli kwakukulu kwambiri kotero kuti kuli kosatheka kuvomereza kuti chinthu chotero chikanakhoza kudzilumikiza chokha mwadzidzidzi, popanda kulinganiza kulikonse.” “Komatu sikucholoŵana kokha kwa zinthu zamoyo kumene kuli kovuta kwambiri, palinso luntha lozizwitsa limene kaŵirikaŵiri limawonekera m’kapangidwe kake.” “Pali pa mlingo wa mamolekyu pamene . . . luntha la kapangidwe ka matupi a zamoyo ndi kugwira ntchito kwake kolongosokako zimawonekera kwambiri.”
6 Denton akunenanso kuti: “Kulikonse kumene tiyang’ana, kumalo alionse amene tingayang’ane, timaona kukongola ndi luntha lopambana koposa, limene limafooketsa kotheratu lingaliro la kuchitika mwamwaŵi. Kodi nzokhulupirikadi kuti zochitika zokha zikanakhoza kupanga chinthu chenicheni, kanthu kochepetsetsa—proteni yogwira ntchito kapena jini—kali kocholoŵana kwambiri mosakhoza kukamvetsetsa ndi maluso athu akupanga zinthu, kanthu kenikeni kamene kali kotsutsa lingaliro la kuchitika kwa mwamwaŵi, kamene kamapambana m’njira zonse chinthu chilichonse chopangidwa ndi luntha la munthu?” Iye ananenanso kuti: “Pakati pa selo lamoyo ndi mpangidwe wolinganizidwa kopambana wa kanthu kopanda moyo, monga ngati krustalo kapena kachibenthu ka chipale, pali kusiyana kwakukulu kwambiri ndi kotheratu kosamvetsetseka.” Ndipo profesa wa physics, Chet Raymo, anati: “Ndachita chidwi kwambiri . . . Molekyu iliyonse imawonekera kuti inapangidwa mozizwitsa kuchita ntchito yake.”
7 Katswiri wa molecular biology Denton akupereka chigomeko chakuti “amene akupitirizabe kuchilikiza mouma khosi kuti zinthu zatsopano zonsezi zinachitika mwamwaŵi” akukhulupirira nthanthi chabe. Kwenikwenidi, iye akutcha chikhulupiriro cha Darwin chakuti zamoyo zinakhalako mwamwaŵi kukhala “nthanthi yaikulu ya chilengedwe ya m’zaka za zana la makumi aŵiri.”
Kulinganiza Kumafunikira Wolinganiza
8 Lingaliro lakuti zinthu zopanda moyo zingakhale ndi moyo mwamwaŵi, mwangozi, nlosatheka konse. Ayi, zamoyo zonse zolinganizidwa bwino koposa padziko lapansi sizikanakhalako mwangozi, popeza kuti chinthu chilichonse cholinganizidwa chiyenera kukhala ndi wolinganiza. Kodi mumadziŵa zimene zilibe wolinganiza? Palibe nchimodzi chomwe. Ndipo pamene chinthucho chili chocholoŵana kwambiri, momwemo wolinganiza ayenera kukhala wokhoza kwambiri.
9 Tingaperekenso chitsanzo cha nkhaniyi motere: Titawona chithunzi, timadziŵa kuti chili umboni wakuti pali wojambula zithunzi. Titaŵerenga buku, timadziŵa kuti pali wolemba. Titawona nyumba, timadziŵa kuti pali mmisiri. Pamene tiwona maroboti, timadziŵa kuti pali bungwe lopanga malamulo. Anthu amene anazipangawo anazipanga ndi chifuno. Ndipo pamene kuli kwakuti sitingakhoze kudziŵa zonse ponena za anthu amene anazipangawo, sitimakayikira kuti anthuwo alipo.
10 Mofananamo, umboni wa kukhalako kwa Wolinganiza Wamkulu ungawoneke m’kulinganiza, dongosolo, ndi kucholoŵana kwa zinthu zamoyo padziko lapansi. Zonse zimasonyeza kuti pali Waluntha Wamkulu. Zilinso choncho ndi kulinganiza, dongosolo, ndi kucholoŵana kwa chilengedwe limodzi ndi makamu ake anyenyezi okwanira mamiliyoni zikwi zambiri, khamu lililonse lokhala ndi nyenyezi mamiliyoni zikwi zambirimbiri. Ndipo zinthu zonse zakuthambo zimalamulidwa ndi malamulo olondola kwenikweni, monga ngati a kayendedwe, kutentha, kuŵala, mawu, mphamvu ya magineti, ndi mphamvu yokoka. Kodi pangakhale malamulo popanda wopanga malamulo? Wodziŵa sayansi ya maroketi Dr. Wernher von Braun anati: “Malamulo a chilengedwe chonse ngotsimikizirika kwambiri kotero kuti sitimakhala ndi vuto kumanga chombo cha m’mlengalenga kuulukira kumwezi ndipo tingalinganize nthaŵi ya kuulukayo motsimikizirika kwambirimbiri kufikira kukamphindi. Malamulo ameneŵa ayenera kukhala anakhazikitsidwa ndi munthu wina.”
11 Zowonadi, sitingathe kuona Wolinganiza Wamkulu ndi Wopereka malamuloyo ndi maso athu enieni. Koma kodi timakana kukhalapo kwa zinthu zonga ngati mphamvu yokoka, mphamvu ya magineti, magetsi, kapena mphamvu ya mawu a wailesi kokha chifukwa chakuti sitimaziona? Ayi, sititero, popeza kuti tikhoza kuona ziyambukiro zake. Pamenepo kodi nkukaniranji kukhalapo kwa Wolinganiza Wamkulu ndi Wopereka malamulo kokha chifukwa chakuti sitingathe kumuona, pamene kuli kwakuti tikhoza kuona zotulukapo za ntchito yodabwitsa ya manja ake?
12 Paul Davies, profesa wa physics, akugomeka kuti kukhalapo kwa munthu sikuli ngozi yongochitika. Iye akuti: “Tinapangidwadi kuti tikhale pano.” Ndipo akunena izi ponena za chilengedwe: “Kupyolera m’ntchito yanga ya sayansi, ndafika pakukhulupirira mwamphamvu kwambiri kuti chilengedwe chakuthupi chinapangidwa ndi luntha lodabwitsa kwakuti sindingavomereze kuti chinakhalako popanda nzeru yolingalira. Ndikuwona kuti payenera kukhala malongosoledwe ozama.”
13 Motero, umboni umatiuza kuti chilengedwe, dziko lapansi, ndi zinthu zamoyo zimene zili padziko lapansi sizinakhaleko mwamwaŵi. Zonse zimapereka umboni wopanda mawu wakuti pali Mlengi waluntha, wamphamvu.
Zimene Baibulo Limanena
14 Baibulo, buku lakale kwambiri la mtundu wa anthu, limapereka chigomeko chofananacho. Mwachitsanzo, m’buku la Baibulo la Ahebri, limene linalembedwa ndi mtumwi Paulo, tikuuzidwa kuti: “Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Buku lomalizira la Baibulo, lolembedwa ndi mtumwi Yohane, limanenanso kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”—Chivumbulutso 4:11.
15 Baibulo limasonyeza kuti ngakhale kuti Mulungu sangaoneke, tikhoza kudziŵa kuti ndi Mulungu wotani mwa zimene anapanga. Ilo limati: “Mikhalidwe yosaoneka ya [Mlengiyo], kutanthauza mphamvu zake zosatha ndi umulungu, zakhala zooneka, kuyambira pamene dziko linayamba, mwa maso a kulingalira, m’zinthu zimene wapanga.”—Aroma 1:20, The New English Bible.
16 Chotero Baibulo limatiuza woyambitsa ndi zotulukapo. Zotulukapozo—zinthu zochititsa mantha zimene zinapangidwa—zili umboni wa Woyambitsa waluntha, wamphamvu: Mulungu. Ndiponso, tingakhoze kukhala oyamikira kuti iye samawoneka, chifukwa chakuti monga Mlengi wa chilengedwe chonse, mosakayikira ali ndi mphamvu zochuluka kwakuti anthu a thupi ndi mwazi sangakhoze kuyembekezera kumuwona iye ndi kukhala ndi moyo. Ndipo zimenezo nzomwe Baibulo limanena: “Palibe munthu [adzaona Mulungu] ndi kukhala ndi moyo.”—Eksodo 33:20.
17 Lingaliro la Wolinganiza Wamkulu, Wokhalako Wamkulu—Mulungu—liyenera kukhala lofunika kwambiri kwa ife. Ngati tinapangidwa ndi Mlengi, ndithudi ayenera kukhala anali ndi chifukwa, chifuno, potilengapo. Ngati tinalengedwa kukhala ndi chifuno m’moyo, pamenepo tili ndi chifukwa choyembekezera kuti zinthu zidzatikhalira bwino mtsogolo. Apo phuluzi, timangokhala ndi moyo ndi kufa popanda chiyembekezo. Chotero nkofunika kwambiri kuti tipeze chifuno cha Mulungu kwa ife. Ndiyeno tikhoza kusankha ngati tikufuna kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifunocho kapena ayi.
18 Ndiponso, Baibulo limanena kuti Mlengi ali Mulungu wachikondi amene amatisamalira kwambiri. Mtumwi Petro anati: “Iye asamalira inu.” (1 Petro 5:7; onaninso Yohane 3:16 ndi 1 Yohane 4:8, 16.) Njira imodzi imene tingawonere mmene Mulungu amatisamalirira ndiyo kulingalira njira yodabwitsa imene anatipangira, m’maganizo ndi thupi.
‘Kupangidwa Modabwitsa’
19 M’Baibulo, wamasalmo Davide anavomereza kuti: “Chipangidwe changa nchowopsa ndi chodabwiza.” (Salmo 139:14) Ndithudi zimenezo nzowona, popeza kuti ubongo wa munthu ndi thupi zinalinganizidwa ndi Wolinganiza Wamkulu.
20 Mwachitsanzo, ubongo wanu ngwocholoŵana kwambiri kuposa kompyuta iliyonse. The New Encyclopædia Britannica imati: “Katumizidwe ka mauthenga mkati mwa dongosolo lamitsempha nkocholoŵana kwambiri kuposa malo aakulu koposa otumizira mauthenga a telefoni; ubongo wa munthu umapeza yankho mofulumira kwambiri kuposa makompyuta amphamvu kwambiri.”
21 Nkhani ndi zithunzithunzi mamiliyoni mazana ambiri zasungidwa mu ubongo wanu, koma ubongowo suli kokha chiŵiya chosunga nkhani. Ndi ubongowo mukhoza kuphunzira kuimba mluzu, kuphika mkate, kulankhula zinenero zachilendo, kugwiritsira ntchito kompyuta, kapena kuulutsa ndege. Mukhoza kuyerekezera mmene tchuthi chidzakhalira kapena mmene chipatso chingakomere. Mukhoza kupenda ndi kupanga zinthu. Mukhozanso kukonzekera, kuyamikira, kukonda, ndi kugwirizanitsa malingaliro anu akale, atsopano, ndi amtsogolo. Popeza kuti anthufe sitingakhoze kulinganiza chinthu chochititsa mantha monga ubongo wa munthu, pamenepo nkowonekeratu kuti Uyo amene anaulinganiza ali ndi nzeru ndi luntha lokulirapo kuposa la munthu aliyense.
22 Ponena za ubongo, asayansi amavomereza kuti: “Mmene ntchito zimenezi zimachitidwira ndi makina adongosolo, olongosoka ndi ocholoŵana modabwitsa ameneŵa m’zosadziŵika. . . . Anthu sangakhoze kufotokoza zodabwitsa zonse zimene ubongo umasonyeza.” (Scientific American) Ndipo profesa wa physics Raymo akuti: “Kunena mowona mtima, sitimadziŵabe zambiri ponena za mmene ubongo wa munthu umasungira chidziŵitso, kapena mmene umakhozera kukumbukira wokha. . . . Mu ubongo wa munthu muli maselo amitsempha ochulukitsitsa ofika ku mamiliyoni zikwi zana limodzi. Selo lililonse limatumizirana mauthenga ndi zikwi za maselo ena onse, kudzera m’njira za mfundo zotchedwa synapse. Kuthekera kwa kulumikizana kwakeko nkocholoŵana kwambiri.”
23 Maso anu amawona bwino ndipo akhoza kusintha kuposa kamera iliyonse; kwenikwenidi, iwo ali makamera ojambula okha, odzilinganiza okha kusumika pa chinthu choti chijambulidwe, ndipo amasonyeza zithunzithunzi zoyenda zamawonekedwe osiyanasiyana. Makutu anu akhoza kumva mawu osiyanasiyana ndipo angakusonyezeni njira ndi kukuletsani kugwa. Mtima wanu ndi pompi yokhoza kuchita ntchito zimene ainjiya aluso koposa alephera kutsanzira. Ndiponso ziŵalo zina zathupi nzochititsa chidwi: mphuno yanu, lilime, ndi manja, dongosolo la mwazi ndi lopukusa zakudya, kungotchula zoŵerengeka zokha.
24 Motero, injiniya amene analembedwa ganyu kuti alinganize ndi kupanga kompyuta yaikulu anati: “Ngati kompyuta yanga inafunikira wolinganiza, bwanji za makina athupi ndi makemikolo ndi moyo amene ali thupi langa laumunthu—lomwe lili kokha mbali yochepetsetsa ya chilengedwe cholinganizika kosatha?”
25 Monga momwedi anthu amakhalira ndi chifuno popanga ndege, makompyuta, njinga, ndi zipangizo zina, moteronso Wolinganiza wa ubongo ndi thupi la anthu anali ndi chifuno potipanga. Ndipo Wolinganiza ameneyu ayenera kukhala ndi nzeru zoposa za anthu, popeza kuti palibe aliyense wa ife amene angakhoze kutsanzira zolinganiza zake. Pamenepo, nkwanzeru kuti iye ndiye Amene angatiuze chifukwa chake anatilinganiza, chifukwa chimene anatiikira padziko lapansi, ndi kumene tikumka.
26 Tikadziŵa zinthu zimenezo, pamenepo ubongo ndi thupi lodabwitsa zimene Mulungu anatipatsa zingagwiritsiridwe ntchito kukwaniritsa chifuno chathu m’moyo. Koma kodi nkuti kumene tingaphunzire zifuno zake? Kodi nkuti kumene amatipatsira chidziŵitso chimenecho?
[Study Questions]
1, 2. Kodi ndiiti imene ili njira yabwino koposa yodziŵira chifuno cha chinthu chimene chapangidwa?
3, 4. Kodi pali kuthekera kotani kuti moyo unayambika mwamwaŵi?
5-7. Kodi molecular biology imatsimikizira motani kuti zinthu zamoyo sizingakhaleko mwamwaŵi?
8, 9. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti chinthu chilichonse cholingazinidwa chiyenera kukhala ndi wolinganiza.
10. Kodi ndiumboni wotani wa kukhalako kwa Wolinganiza Wamkulu umene umaoneka?
11. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kukana kukhalako kwa Wolinganiza Wamkulu kokha chifukwa chakuti sitingathe kumuona?
12, 13. Kodi umboni umanena chiyani za kukhalako kwa Mlengi?
14. Kodi Baibulo limagomekanji ponena za Mlengi?
15. Kodi tingadziŵe motani ina ya mikhalidwe ya Mulungu?
16. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala osangalala kuti anthu sangakhoze kuwona Mulungu?
17, 18. Kodi nchifukwa ninji lingaliro la kukhalako kwa Mlengi liyenera kukhala lofunika kwa ife?
19. Kodi nchowonadi chotani chimene wamasalmo Davide akutikumbutsa?
20. Kodi buku lanazonse limafotokoza motani ubongo wa munthu?
21. Pamene tiona zimene ubongo umachita, kodi tiyenera kunenanji?
22. Kodi asayansi amavomereza chiyani ponena za ubongo wa munthu?
23, 24. Tchulani ziŵalo zina za thupi zolinganizidwa modabwitsa, ndipo kodi injiniya wina anapereka ndemanga yotani?
25, 26. Kodi Wolinganiza Wamkuluyo akhoza kutiuza chiyani?
[Picture on page 7]
Njira yabwino koposa yodziŵira chifukwa chake chinthu chalinganizidwa ndiyo kufunsa wolinganizayo
[Picture on page 8]
Kucholoŵana ndi kulinganizidwa kwa zinthu zamoyo kungaonedwe m’molekyu ya DNA
[Picture on page 9]
“Ubongo wa munthu umapeza yankho mofulumira kwambiri kuposa makompyuta amphamvu kwambiri”