GAWO 1
‘Mphamvu Zoopsa’
M’chigawochi, tikambirana nkhani za m’Baibulo zimene zimasonyeza kuti Yehova ali ndi mphamvu zoti angathe kulenga, kuwononga, kuteteza ndiponso kubwezeretsa zinthu. Yehova Mulungu ali ndi ‘mphamvu zoopsa’ komanso ‘zochuluka.’ Kumvetsa mmene amagwiritsira ntchito mphamvu zakezi kungatithandize kukhala ndi chiyembekezo ndiponso kukhala olimba mtima.—Yesaya 40:26.