Mphamvu za Mulungu Zimaonekera mu Nyenyezi
“Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziwerenga; azitcha zonse mayina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoweka.”—YESAYA 40:26.
DZUWA ndi lalikulu mofanana ndi nyenyezi zambiri. Komabe, n’lalikulu kuposa dziko lapansi kuwirikiza nthawi 330,000. Nyenyezi zambiri zomwe zili pafupi ndi dziko lapansili n’zazing’ono poyerekezera ndi dzuwa. Koma pali nyenyezi zina, monga yotchedwa V382 Cygni, zomwe ndi zazikulu kwambiri kuwirikiza nthawi 27 poyerekezera ndi dzuwa.
Kodi dzuwa limatulutsa mphamvu zochuluka bwanji? Tangoganizani kuchuluka kwa moto umene ungafunike kuti muziumvabe kutentha mutaima pa mtunda wa makilomita 15 kuchokera pamene pali motowo. Komatu dzuwa lili pa mtunda wa pafupifupi makilomita 150 miliyoni kuchokera padziko lapansili. Ngakhale zili choncho, kunja kukakhala kopanda mitambo, khungu lanu likhoza kupsa ndi dzuwa. N’zochititsa chidwi kuti mphamvu ya dzuwa imene imafika padziko lapansi pano ndi yosakwana n’komwe gawo limodzi mwa magawo 1 biliyoni a mphamvu yake. Komabe, kachigawo ka mphamvu ya dzuwa kameneka kamatha kuchititsa kuti padziko pano pakhale za moyo.
Ndipotu asayansi amati mphamvu yonse imene dzuwa limatulutsa ikhoza kupangitsa kuti m’mapulaneti ofanana ndi dziko lapansili okwana 31 thililiyoni akhale ndi zamoyo. Malinga ndi zimene linanena bungwe lina, zimenezi tingazifotokozenso chonchi: Ngati mphamvu imene dzuwa limatulutsa pa sekondi imodzi yokha itagwiritsidwa ntchito kupanga mphamvu za magetsi, “ndiye kuti dziko lonse la United States likhoza kugwiritsa ntchito mphamvuyi kwa zaka 9,000,000.”—Space Weather Prediction Center.
Mphamvu ya dzuwa imachokera pakati penipeni pa dzuwalo n’kumapita m’mbali mwake. Dzuwa ndi lalikulu kwambiri moti mphamvu yake kuti ichoke pakatipo n’kufika m’mbali mwake, imatenga zaka mamiliyoni ambiri. Bungwe lija linanenanso kuti: “Ngati dzuwa litasiya kutulutsa mphamvu yake lero, pangadutse zaka 50,000,000 kuti anthufe padziko pano tizindikire zimenezo.”
Ndiyeno taganizirani mfundo iyi: Mukayang’ana kumwamba usiku kopanda mitambo, mumaona nyenyezi masauzande ambirimbiri. Nyenyezi iliyonse imatulutsa mphamvu yochuluka yofanana ndi imene dzuwa limatulutsa. Ndipo asayansi amati m’mlengalenga muli nyenyezi mabiliyoni ambirimbiri.
Kodi nyenyezi zonsezi zinachokera kuti? Masiku ano, ofufuza ambiri akukhulupirira kuti nyenyezi zonse m’mlengalenga zinangokhalapo mwadzidzidzi zaka pafupifupi 14 biliyoni zapitazo. Iwo amatinso chomwe chinachititsa zimenezi sichikudziwika. Koma Baibulo limanena momveka bwino kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Tinganene mosakayikira kuti amene analenga nyenyezi zimene zimatulutsa mphamvu zambirizi ndi “wolimba mphamvu.”—Yesaya 40:26.
Mmene Mulungu Amagwiritsira Ntchito Mphamvu Zake
Yehova Mulungu amagwiritsira ntchito mphamvu zake posamalira anthu amene amachita chifuniro chake. Mwachitsanzo, mtumwi Paulo anagwiritsira ntchito mphamvu zake pophunzitsa ena za Mulungu. Iye anali munthu ngati ifeyo koma anathandiza anthu ambiri kudziwa za Mulungu ngakhale kuti ena ankamutsutsa kwambiri. Kodi Paulo anatha bwanji kuchita zimenezi? Iye ananena kuti Mulungu anamupatsa “mphamvu yoposa yachibadwa.”—2 Akorinto 4:7-9.
Komanso Yehova Mulungu anagwiritsira ntchito mphamvu zake powononga anthu amene mwadala sankatsatira mfundo zake zamakhalidwe abwino. Yesu Khristu anapereka zitsanzo za kuwonongedwa kwa anthu m’mizinda ya Sodomu ndi Gomora komanso pa Chigumula cha m’nthawi ya Nowa pofuna kusonyeza kuti Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake powononga anthu okhawo omwe ndi oipa. Iye analosera kuti posachedwapa Yehova adzagwiritsiranso ntchito mphamvu zake powononga anthu amene amanyalanyaza malamulo Ake.—Mateyo 24:3, 37-39; Luka 17:26-30.
Kodi Inuyo Zimakukhudzani Bwanji?
Mutasinkhasinkha za mphamvu za Mulungu zimene timaziona mu nyenyezi, mungamve ngati mmene anamvera Mfumu Davide. Iye anati: “Pakuona ine thambo la kumwamba lanu, ntchito ya zala zanu, mwezi ndi nyenyezi, zimene munazikhazika, munthu ndani kuti mum’kumbukira? Ndi mwana wa munthu kuti mucheza naye?”—Salmo 8:3, 4.
Inde, timaona kuti sitingayerekezeredwe n’komwe ndi thambo limene ndi lalikulu kwambiri. Koma sitiyenera kuchita mantha kwambiri ndi mphamvu za Mulungu. Yehova anauzira mneneri Yesaya kulemba mawu olimbikitsa akuti: “[Mulungu] alimbitsa olefuka, nawonjezera mphamvu iye amene alibe mphamvu. Ngakhale anyamata adzalefuka ndi kulema ndi amisinkhu adzagwa ndithu: koma iwo amene alindira Yehova adzatenganso mphamvu; adzauluka pamwamba ndi mapiko monga ziombankhanga; adzathamanga koma osalema; adzayenda koma osalefuka.”—Yesaya 40:29-31.
Ngati mumafunitsitsa kuchita chifuniro cha Mulungu, musakayikire kuti iye adzakupatsani mzimu wake woyera kuti ukuthandizeni. Komabe inuyo muyenera kupempha kuti akupatseni mzimu woyerawo. (Luka 11:13) Ndi thandizo la Mulungu, mungathe kupirira mayesero alionse ndipo mungakhale ndi mphamvu yochitira zinthu zoyenera.—Afilipi 4:13.
[Mawu Otsindika patsamba 7]
Ndi thandizo la Mulungu, mungakhale ndi mphamvu yochitira zinthu zoyenera
[Zithunzi patsamba 7]
Kuchokera pa chithunzi chapamwamba kumanzere: Mlalang’amba wa Whirlpool, gulu la nyenyezi zotchedwa Pleiade, Orion Nebula, mlalang’amba wa Andromeda
[Zithunzi patsamba 7]
Dzuwa n’lalikulu kuposa dziko lapansi kuwirikiza nthawi 330,000
[Mawu a Chithunzi patsamba 7]
Pleiades: NASA, ESA and AURA/Caltech; all others above: National Optical Astronomy Observatories