Mutu 19
Pitirizani Kulankhula Mawu a Mulungu Molimbika Mtima
ZAKA pafupifupi 2,000 zapitazo, Yesu Kristu, Mwana wa Mulungu, anadzozedwa kuti m’tsogolo adzakhale Mfumu ya dziko lonse lapansi. Kenako adani ake achipembedzo anayambitsa zoti Yesu aphedwe ndipo anaphedwadi. Koma Yehova anamuukitsa kwa akufa. Pamenepo moyo wosatha unakhala wotheka kudzera mwa Yesuyo. Komabe, pamene ophunzira ake anayamba kulengeza poyera uthenga wabwino umenewu, panabuka chizunzo. Ena a iwo anaponyedwa m’ndende, ngakhale kukwapulidwa ndi kulamulidwa kusiya kulankhula za Yesu. (Machitidwe 4:1-3, 17; 5:17, 18, 40) Kodi iwo anachitanji? Mukanakhala inuyo mukanachitanji? Kodi mukanapitiriza kuchitira umboni molimbika mtima?
2 Mu 1914 Yesu Kristu, Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, analongedwa ufumu kumwamba kuti ayambe kulamulira ‘pakati pa adani ake.’ (Salmo 110:2) Kenako, Satana ndi ziwanda zake anaponyedwa pansi ku dziko. (Chivumbulutso 12:1-5, 7-12) Masiku otsiriza a dziko ili loipa anayambira pamenepo. Pakutha nthaŵi imeneyi, Mulungu adzaphwanya dziko lonse la Satana. (Danieli 2:44; Mateyu 24:21) Opulumuka adzayembekezeka kulandira moyo wosatha padziko lapansi limene lidzakhale paradaiso. Ngati mwalandira uthenga wabwino umenewu, mufunika kuuzako ena. (Mateyu 24:14) Koma kodi muganiza anthu adzalabadira motani?
3 Mukamalengeza uthenga wabwino wa Ufumu, anthu ena amaulandira, koma ambiri amakana. (Mateyu 24:37-39) Ena angakusekeni kapena kukutsutsani. Yesu anachenjeza kuti ena amene angakutsutseni angakhale achibale anu omwe. (Luka 21:16-19) Zimenezi zingachitikenso kuntchito kwanu kapena kusukulu. M’mbali zina za dziko, Mboni za Yehova n’zoletsedwa ndi boma limene. Zimenezi zikakuchitikirani, kodi mudzapitiriza kulankhula mawu a Mulungu molimbika mtima ndi ‘kuchirimika m’chikhulupiriro’?—1 Akorinto 16:13.
Tisadalire Mphamvu Zathuzathu
4 Chofunika kwambiri kuti munthu akhale mtumiki wokhulupirika wa Yehova ndicho kudalira zimene Iye wapereka kuti zitithandize. Mwa zimenezi pali misonkhano ya mpingo. Malemba amatilimbikitsa kusainyalanyaza. (Ahebri 10:23-25) Amene akhalabe Mboni za Yehova zokhulupirika ayesetsa kumafika pa misonkhano mokhazikika pamodzi ndi olambira anzawo. Timadziŵa Malemba kwambiri chifukwa cha misonkhano imeneyi. Komanso misonkhano imatithandiza kumvetsa bwino mfundo za choonadi zimene tinali kuzidziŵa kale, ndipo luso lathu lozindikira njira zimene tingagwiritsire ntchito mfundozo limakula. Kumisonkhanoko n’kumene timayandikirana kwambiri ndi abale athu achikristu pogwirizana pa kulambira ndipo timalimbikitsidwa kuchita chifuniro cha Mulungu. Mzimu wa Yehova umatitsogolera kudzera mu mpingo, ndipo mwa mzimuwo, Yesu amakhala nafe.—Mateyu 18:20; Chivumbulutso 3:6.
5 Kodi mumafika pa misonkhano yonse mokhazikika, ndipo kodi mumazigwiritsa ntchito pamoyo wanu zimene mumamva kumeneko? Nthaŵi zina, Mboni za Yehova zikakhala zoletsedwa, pamafunika kuchita misonkhano m’timagulu tochepa m’nyumba za anthu. Malo ndi nthaŵi zingamasiyane ndipo sikuti zingakukomereni masiku onse, chifukwa misonkhano ina imachitika usiku kwambiri. Komatu abale ndi alongo okhulupirika amayesetsa kufika pa msonkhano uliwonse ngakhale kutakhala kovuta kapena koopsa kumene.
6 Ngati nthaŵi zonse timapemphera kwa Yehova kuchokera pansi pa mtima, pozindikira kuti tifunikira thandizo lake, chidaliro chathu mwa iye chimakula. Kodi mumachita zimenezo? Yesu anapemphera nthaŵi zambiri pa utumiki wake wa padziko lapansi. (Luka 3:21; 6:12, 13; 22:39-44) Ndipo usiku woti apachikidwa maŵa lake, analimbikitsa ophunzira ake kuti: “Dikirani, pempherani, kuti mungaloŵe m’kuyesedwa.” (Marko 14:38) Tikamakumana ndi anthu amene safuna kumva uthenga wa Ufumu, mwina tingayambe kubwerera m’mbuyo mu utumiki wathu. Anthu akamatiseka kapena kutizunza, tingaganize zongosiya kuti tipeŵe mavuto. Koma ngati tipempherera mzimu wa Mulungu mochokera pansi pa mtima kuti utithandize kulankhulabe molimbika mtima, udzatiteteza kuti tisagonje pa ziyeso zimenezo.—Luka 11:13; Aefeso 6:18-20.
Mbiri ya Kuchitira Umboni Molimbika Mtima
7 Mbiri imene ili m’buku la Machitidwe tifunika kuchita nayo chidwi ife tonse. Imasimba mmene atumwi ndi ophunzira ena oyambirira—amene anali ndi maganizo ngati athuŵa—anagonjetsera zopinga n’kukhala olimba mtima komanso mboni zokhulupirika za Yehova. Tiyeni tipende chigawo cha mbiri imeneyo pothandizidwa ndi mafunso otsatiraŵa ndi malemba ake. Pamene tikutero, ganizani za mmene inuyo mungapindulire ndi zimene mukuŵerenga.
Kodi atumwi anali anthu ophunzira kwambiri? Kodi mwachibadwa anali opanda mantha, zivute zitani? (Yohane 18:17, 25-27; 20:19; Machitidwe 4:13)
Kodi chinathandiza Petro n’chiyani kuti alimbe mtima polankhula m’khoti la Ayuda limene linaweruza kuti Mwana wa Mulungu aphedwe? (Mateyu 10:19, 20; Machitidwe 4:8)
Kodi atumwi anali kuchitanji milungu yoyambirira asanawatengere ku Sanihedirini? (Machitidwe 1:14; 2:1, 42)
Pamene olamulira anauza atumwi kusiya kulalikira m’dzina la Yesu, kodi Petro ndi Yohane anayankha kuti chiyani? (Machitidwe 4:19, 20)
Atawamasula, kodi atumwiwo anayang’ananso kwa ndani kuti awathandize? Kodi anapemphera kuti chizunzo chithe, kapena anatani? (Machitidwe 4:24-31)
Kodi ndi njira iti imene Yehova anaperekera thandizo pamene adani anayesa kuletsa ntchito yolalikira? (Machitidwe 5:17-20)
Kodi atumwi anasonyeza bwanji kuti anadziŵa chifukwa chimene anawalanditsira? (Machitidwe 5:21, 41, 42)
Ngakhale mmene ambiri mwa ophunzira anamwazikana chifukwa cha chizunzo, kodi anapitiriza kuchitanji? (Machitidwe 8:3, 4; 11:19-21)
8 Ntchito yolengeza uthenga wabwino sinachitike mwachabe. Ophunzira pafupifupi 3,000 anabatizidwa pa Pentekoste mu 33 C.E. “Anawonjezedwa kwa Ambuye okhulupirira ambiri, ndiwo amuna ndi akazi.” (Machitidwe 2:41; 4:4; 5:14) M’kupita kwa nthaŵi, ngakhale Saulo wa ku Tariso, amene anazunza anthu a Mulungu koopsa, anakhala Mkristu ndipo anayamba kuchitira umboni choonadi molimbika mtima. Anafika podziŵika kuti mtumwi Paulo. (Agalatiya 1:22-24) Ntchito imene inayamba m’zaka 100 zoyambirira sinaime ayi. Yawonjezeka masiku ano otsiriza ndipo yafika kwina kulikonse padziko lapansi. Ife tili ndi mwayi wochita nawo ntchito imeneyi, ndipo potero, tingatengerepo phunziro pa chitsanzo chimene zatiikira mboni zokhulupirika zimene zinayamba kukhalako ife tisanakhaleko.
9 Kodi Paulo ataphunzira choonadi cha Yesu Kristu anachitanji? “Pomwepo . . . analalikira Yesu, kuti Iye ndiye Mwana wa Mulungu.” (Machitidwe 9:20) Anayamikira kukoma mtima kwa Mulungu pa iye, ndipo anazindikira kuti aliyense anafunikira kumva uthenga wabwino umene iye analandira. Paulo anali Myuda, choncho malinga ndi mwambo wa masikuwo, anali kupita ku masunagoge kukachitira umboni. Analalikiranso nyumba ndi nyumba ndi kukambirana ndi anthu pamsika. Ndipo anali wokonzeka kusamukira ku magawo atsopano kukalalikira uthenga wabwino.—Machitidwe 17:17; 20:20; Aroma 15:23, 24.
10 Paulo anali wolimba mtima komanso wozindikira, ngati mmene ifenso tifunikira kukhalira. Ayuda anawakopa ndi malonjezo amene Mulungu anauza makolo awo. Agiriki analankhula nawo zinthu zimene iwo anali kudziŵa. Nthaŵi zina anagwiritsa ntchito njira imene iye anaphunzirira choonadi pochitira umboni. Anati: “Ndichita zonse chifukwa cha Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nawo.”—1 Akorinto 9:20-23; Machitidwe 22:3-21.
11 Pamene Paulo anaona kuti ndi bwino kukalalikira dera lina kwa kanthaŵi chifukwa cha otsutsa, anatero m’malo molimbikira kukangana ndi otsutsawo. (Machitidwe 14:5-7; 18:5-7; Aroma 12:18) Koma sanachite manyazi ndi uthenga wabwino. (Aroma 1:16) Ngakhale kuti Paulo sanakondwere ndi chipongwe— ngakhalenso chiwawa—chimene otsutsawo anam’chitira, ‘analimbika pakamwa mwa Mulungu wathu’ napitiriza kulalikira. Iye anati: “Ambuye anaima nane nandipatsa mphamvu; kuti mwa ine chilalikiro chimveke konsekonse.” (1 Atesalonika 2:2; 2 Timoteo 4:17) Yesu, Mutu wa mpingo wachikristu, akuperekabe mphamvu imene tifunikira kuti tichite ntchito imene analosera kuti idzachitika masiku athu ano.—Marko 13:10.
12 Tili ndi chifukwa chabwino chopitirizira kulankhula mawu a Mulungu molimbika mtima, mongadi mmene Yesu ndi atumiki ena okhulupirika a Mulungu anachitira m’zaka 100 zoyambirirazo. Zimenezi sizikutanthauza kuti tifunika kukhala osaganizira ena kapena kuyesa kukakamiza amene safuna kumva uthenga wathu. Koma sitisiya kulankhula chabe chifukwa chakuti anthu sakufuna kumva, ndiponso otsutsa sangatiletse kulankhula. Monga Yesu, timasonyeza anthu kuti Ufumu wa Mulungu ndiwo boma lokha loyenera kulamulira dziko lonse lapansi. Timalimba mtima polankhula chifukwa tikuimira Yehova, Wolamulira wa Chilengedwe Chonse, ndiponso chifukwa chakuti uthenga umene timalengeza si wathu koma ndi wochokera kwa iye. Ndipo kukonda kwathu Yehova ndiyo mphamvu yaikulu imene imatilimbikitsa kum’tamanda.—Afilipi 1:27, 28; 1 Atesalonika 2:13.
Bwerezani Zimene Mwakambirana
• N’chifukwa chiyani kuuza wina aliyense uthenga wa Ufumu n’kofunika, nanga timayembekeza zotani?
• Kodi tingasonyeze bwanji kuti sitikudalira mphamvu zathu potumikira Yehova?
• Kodi ndi zinthu zothandiza ziti zimene tikuphunzira m’buku la Machitidwe?
[Mafunso]
1. (a) Kodi ophunzira a Yesu analengeza uthenga wabwino wotani, koma nanga Ayuda ena anayamba kuchitanji? (b) Kodi tingafunse mafunso otani?
2. (a) Ndi uthenga wosangalatsa uti umene ufunika kulengezedwa masiku ano? (b) Kodi amene ali ndi udindo wolengeza uthenga wabwino ndani?
3. (a) Kodi anthu amaulabadira motani uthenga wa Ufumu? (b) Nanga ndi funso liti limene tifunika kuyankha?
4. (a) Kuti tionetse kuti ndife atumiki okhulupirika a Mulungu, kodi chofunika kwambiri n’chiyani? (b) N’chifukwa chiyani misonkhano yachikristu ili yofunika kwambiri?
5. Mboni za Yehova zikakhala zoletsedwa, kodi misonkhano imachitika bwanji?
6. Kodi timasonyeza bwanji kuti tikudalira Yehova, ndipo zimenezi zingatithandize bwanji kulankhulabe molimbika mtima?
7. (a) N’chifukwa chiyani mbiri ya m’buku la Machitidwe tifunika kuchita nayo chidwi? (b) Yankhani mafunso amene ali kumapeto kwa ndimeyi, ndipo tsindikani mmene tikupindulira ndi mfundozo.
8. Kodi utumiki wa ophunzira oyambirira unabala zipatso zosangalatsa zotani, ndipo zakhala bwanji kuti ifenso tikugwira ntchito yomweyo?
9. (a) Kodi Paulo anagwiritsa ntchito mipata yotani kuchitira umboni? (b) Kodi ndi njira ziti zimene mumagwiritsa ntchito kuti mufalitse uthenga wa Ufumu kwa ena?
10. (a) Kodi Paulo anasonyeza bwanji kuti ngakhale anali wolimba mtima, analinso wozindikira akamachitira umboni? (b) Kodi tingasonyeze bwanji makhalidwe amene Paulo anali nawo tikamachitira umboni kwa achibale, anzathu akuntchito, kapena akusukulu?
11. (a) Kodi Paulo anachitanji pofuna kupeŵa kumangokangana ndi otsutsa? (b) Nanga muganiza kuti ndi liti pamene ife mwanzeru tingatsanzire chitsanzo cha Paulo, ndipo tingatero motani? (c) Kodi mphamvu yakuti tizilankhulabe molimbika mtima imachokera kuti?
12. Kodi chimapereka umboni wakuti Akristu ndi olimba mtima n’chiyani, nanga amalimba mtima chifukwa chiyani?
[Zithunzi patsamba 173]
Mofanana ndi kale, atumiki a Yehova masiku ano amalankhula mawu a Mulungu molimbika mtima