Mutu 2
Kalata Yochokera kwa Mulungu Amene Amatikonda
TANDIUZA, kodi ndi buku liti limene umalikonda kwambiri pa mabuku onse?— Ana ena angasankhe buku lonena za nyama. Ena angasankhe la zithunzi zambiri. Kungakhale kosangalatsa kuŵerenga mabuku ameneŵa.
Koma mabuku abwino kwambiri pa mabuku onse ndi amene amatiuza choonadi cha Mulungu. Buku limodzi pa mabuku amenewo ndi lofunika zedi kuposa ena onse. Kodi ukuganiza kuti ndi buku liti limenelo?— Ndi Baibulo.
N’chifukwa chiyani Baibulo ndi lofunika kwambiri?— Chili chifukwa chakuti linachokera kwa Mulungu. Limatiuza za Mulungu ndi zinthu zabwino zimene adzatichitira. Komanso limatisonyeza zimene tifunika kuchita kuti timukondweretse. Baibulo lili ngati kalata imene Mulungu anatilembera.
Tsonotu Mulungu akanatha kulemba Baibulo lonse kumwamba kenako ndi kuwapatsa anthu. Koma iye sanachite zimenezo. Ngakhale kuti Mulungu ndiye ananena zimene zinalembedwazo, iye anagwiritsa ntchito atumiki ake a padziko lapansi kuti alembe mbali yaikulu ya Baibulo.
Kodi ukuganiza kuti Mulungu anachita bwanji zimenezi?— Kuti umvetsetse, talingalira izi. Tikamamva mawu pa wailesi, amene amalankhulayo amakhala munthu amene ali kutali. Tikamaonerera TV, timaona zithunzi ngakhale za anthu omwe ali m’mayiko ena, ndipo timamva zimene iwo akunena.
Anthu angathe kupita ngakhale ku mwezi ndi ndege zawo. Ndipo ali kumweziko angathe kutumiza mauthenga ku dziko lapansi. Kodi unali kuzidziŵa zimenezi?— Ndiye ngati anthu angachite zimenezi, kodi Mulungu sangathe kutumiza mauthenga kuchokera kumwamba?— Inde angatero. Ndipo iye anachita zimenezi kalekalelo anthu asanakhale ndi mawailesi kapena ma TV.
Pali munthu wina amene anamva Mulungu akulankhula. Munthu ameneyo dzina lake linali Mose. Mose sanathe kuona Mulungu, koma anamva mawu a Mulungu. Panali anthu ambirimbiri pamene izi zinachitika. Ndipotu tsikulo Mulungu anagwedeza phiri lathunthu, komanso kunali mabingu ndi mphezi. Anthu anadziŵa kuti Mulungu walankhula, komatu iwo anachita mantha kwambiri. Ndiye anauza Mose kuti: “Asalankhule nafe Mulungu, kuti tingafe.” Kenako, Mose analemba zimene Mulungu ananena. Ndipo zimene Mose analemba zili m’Baibulo.—Eksodo 20:18-21.
Mose analemba mabuku oyambirira faifi a m’Baibulo. Koma sikuti ndiye yekha amene analemba zimene zili m’Baibulo. Mulungu anagwiritsa ntchito anthu aamuna okwana pafupifupi 40 polemba mbali zosiyanasiyana za Baibulo. Anthu ameneŵa analipo kalekalelo, ndipo panatenga zaka zambiri kuti Baibulo lilembedwe lonse. Inde, panatha pafupifupi zaka 1,600! Koma chochititsa chidwi ndi chakuti, ngakhale kuti ena mwa anthu ameneŵa sanadziŵane, zonse zimene iwo analemba ndi zogwirizana kwambiri.
Amuna ena amene Mulungu anawagwiritsa ntchito polemba Baibulo anali odziŵika zedi. Ngakhale kuti poyamba Mose anali kuŵeta nkhosa, anakhala mtsogoleri wa mtundu wa Aisrayeli. Solomo anali mfumu, ndipo anali munthu wanzeru kwambiri komanso wolemera zedi kuposa wina aliyense padziko lapansi. Koma olemba ena anali osadziŵika kwenikweni. Mwachitsanzo, Amosi anali kusamalira mitengo ya mkuyu.
Ndiponso, wolemba Baibulo wina anali dokotala. Kodi ukuganiza kuti dzina lake ndani?— Anali Luka. Wolemba wina anali wokhometsa msonkho. Dzina lake linali Mateyu. Ndipo winanso anali loya, kutanthauza kuti katswiri wa malamulo a chipembedzo cha Ayuda. Analemba mabuku a m’Baibulo ambiri kuposa wina aliyense. Kodi ungandiuze dzina lake?— Anali Paulo. Ndipo Petro ndi Yohane, ophunzira a Yesu omwenso analemba Baibulo, anali asodzi.
Ambiri mwa olemba Baibulo ameneŵa analemba zinthu zimene Mulungu anali kudzachita m’tsogolo. Kodi iwo anazidziŵa bwanji zinthuzo zisanachitike?— Mulungu anauza anthuwo zinthuzo. Iye anawafotokozera zomwe zikachitika.
Nthaŵi imene Mphunzitsi Waluso,Yesu, anali padziko lapansi, mbali yaikulu ya Baibulo inali italembedwa. Ndiyeno kumbukira kuti Mphunzitsi Waluso anayamba wakhalapo kumwamba. Anali kudziŵa zimene Mulungu anachita. Kodi ukuganiza kuti iye anakhulupirira kuti Baibulo linali lochokera kwa Mulungu?— Inde, anakhulupirira.
Yesu anali kuŵerenga Baibulo pouza anthu ntchito za Mulungu. Nthaŵi zina anawauza pamtima zimene limanena. Yesu anabweretsanso zinthu zina zambiri kuchokera kwa Mulungu. Yesu anati: “Zimene ndazimva kwa Iye, zomwezo ndilankhula kwa dziko lapansi.” (Yohane 8:26) Yesu anamva zinthu zambiri kuchokera kwa Mulungu chifukwa chakuti anali kukhala ndi Mulunguyo. Ndipo kodi zinthu zimene Yesu ananenazo tingaziŵerenge kuti?— M’Baibulo. Zonse zinalembedwa kuti ife tiziŵerenge.
Tsono pamene Mulungu anauza anthu kulemba Baibulo, iwo anali kulemba m’chinenero chimene anali kulankhula tsiku ndi tsiku. Motero mbali yaikulu ya Baibulo inalembedwa m’Chihebri, ina mu Chiaramaiki, ndipo mbali inanso mu Chigiriki. Popeza kuti anthu ambiri masiku ano sadziŵa kuŵerenga zinenero zimenezo, Baibulo lalembedwa m’zinenero zinanso. Masiku ano mabuku ena a m’Baibulo akhoza kuŵerengedwa m’zinenero zoposa 2,260. Taonatu kuchuluka kwake zinenerozo! Baibulo ndi kalata imene Mulungu analembera anthu kulikonse. Koma ngakhale kuti lalembedwa m’zinenero zambiri, uthenga wake ndi wochokerabe kwa Mulungu.
Zimene Baibulo limanena ndi zofunika kwa ife. Linalembedwa kalekale, koma limanena za zinthu zimene zikuchitika masiku ano. Ndipo limatiuza zimene Mulungu adzachita posachedwa m’tsogolomu. Zimene limanena ndi zosangalatsa zedi! Timalimba mtima chifukwa cha zinthu zabwino kwambiri zimene limalonjeza.
Baibulo limatiuzanso moyo umene Mulungu amafuna kuti tizikhala nawo. Limatiuza zinthu zabwino zimene tifunika kuchita ndiponso zinthu zoipa zimene sitifunika kuchita. Iweyo ufunika kudziŵa zimenezi, inenso ndifunika kuzidziŵa. Baibulo limatiuza za anthu amene anachita zinthu zoipa ndi zomwe zinawachitikira, kuti ife tithe kupeŵa mavuto amene iwo anakumana nawo. Limatiuzanso za anthu amene anachita zolungama ndi zinthu zabwino zimene zinawachitikira. Zonse zinalembedwa kuti ife zitithandize.
Koma kuti Baibulo litithandize kwambiri, tifunika kudziŵa yankho la funso linalake. Funsolo ndi lakuti: Kodi ndani anatipatsa Baibulo? Kodi iweyo ungayankhe bwanji?— Inde, Baibulo lonse ndi lochokera kwa Mulungu. Ndiyeno, kodi ife tingasonyeze bwanji kuti ndifedi anthu anzeru?— Mwa kumvera Mulungu ndi kuchita zimene amanena.
Choncho tifunika kumakhala ndi nthaŵi yoti tiziŵerengera Baibulo pamodzi. Tikalandira kalata kuchokera kwa munthu amene timamukonda kwambiri, timaiŵerenga mobwerezabwereza. Timaiona kuti ndi yofunika. Ndi mmene ifenso tiyenera kuonera Baibulo, chifukwa ndi kalata yochokera kwa Munthu amene amatikonda kwambiri. Ndi kalata yochokera kwa Mulungu amene amatikonda.
Tsopano kwa mphindi zina zingapo ŵerengani malemba aŵa amene akusonyeza kuti Baibulo lilidi Mawu a Mulungu amene analembedwa pofuna kutithandiza: Aroma 15:4; 2 Timoteo 3:16, 17; ndi 2 Petro 1:20, 21.