MUTU 19
Zimene Mungachite Kuti Mulungu Apitirize Kukukondani
Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu?
Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti Mulungu apitirize kutikonda?
Kodi Yehova adzawachitira chiyani anthu amene amamukonda?
1, 2. Kodi tingathawire kwa ndani pa nthawi ya mavuto?
YEREKEZERANI kuti tsiku lina mukuyenda mumsewu ndipo kunja kwayamba kusintha. Mitambo yamvula yayamba kusonkhana moti kunja kwayamba kuoneka mdima. Mphenzi zikuyamba kung’anima, mabingu akugunda ndipo kenako chimvula champhamvu komanso champhepo chikuyamba kugwa. Mukuyamba kuthamanga kuti mupeze poti n’kubisala. Kenako, mukuona kuti m’mbali mwa msewuwo muli kanyumba ndipo mkati mwake ndi mouma. Kanyumbako kakuoneka kolimba komanso kosamalidwa bwino. Muyenera kuti mungasangalale kupeza malo obisalapo ngati amenewa.
2 Panopa tikukumana ndi mavuto ambiri omwe tingawayerekezere ndi chimvula champhamvu. Zinthu zikungoipiraipirabe m’dzikoli. Koma pali malo abwino amene tikhoza kubisalapo kuti tikhale otetezeka. Kodi malo amenewa ndi ati? Baibulo limanena kuti: “Ndidzauza Yehova kuti: ‘Inu ndinu pothawirapo panga ndi malo anga achitetezo, Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.’”—Salimo 91:2.
3. Kodi tingatani kuti Yehova akhale malo athu obisalapo?
3 N’zochititsa chidwi kudziwa kuti Yehova, yemwe ndi Mlengi komanso Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse, angakhale malo athu obisalapo. Iye akhoza kutiteteza chifukwa ali ndi mphamvu zambiri kuposa wina aliyense kapena china chilichonse chimene chingativulaze. Ndipo ngakhale titavulazidwa, Yehova angatithandize kuti zinthu zikhalenso bwino. Koma kodi tingatani kuti Yehova akhale malo athu obisalapo? Tiyenera kumudalira. Ndipotu Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani.” (Yuda 21) Lembali likusonyeza kuti tiyenera kukhalabe pa ubwenzi ndi Mulungu, yemwe ndi Atate wathu wakumwamba. Tikachita zimenezi, m’pamene iye angakhale malo athu obisalapo. Koma kodi tingatani kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu?
UMBONI WOSONYEZA KUTI MULUNGU AMAKUKONDANI
4, 5. Kodi ndi zinthu ziti zimene zikusonyeza kuti Yehova amatikonda?
4 Kuti tikhale pa ubwenzi ndi Mulungu, tiyenera kuzindikira mmene Yehova anasonyezera kuti amatikonda. Taganizirani mfundo zina za m’Baibulo zimene mwaphunzira m’bukuli. Mwachitsanzo, taphunzira kuti Yehova, yemwe ndi Mlengi, anatipatsa dziko lapansili kuti tizikhalamo. Iye anaikamo chakudya, madzi, zomera, zinyama ndiponso zinthu zambiri zokongola. Mulungu anatithandiza kudziwa dzina lake ndiponso makhalidwe ake kudzera mu zimene analemba m’Baibulo. Mawu ake amatithandizanso kudziwa kuti iye anatumiza Mwana wake wokondedwa padziko lapansi kuti adzatifere ndipo analola kuti mwana wakeyo azunzidwe. (Yohane 3:16) Kodi zimene Yehova anachitazi n’zofunika bwanji kwa ifeyo? N’zofunika chifukwa zimatipatsa mwayi wodzakhala ndi moyo wabwino kwambiri m’tsogolo.
5 Pali chinthu chinanso chimene Yehova anachita chomwe chimathandiza kuti tidzakhale ndi moyo wabwino m’tsogolo. Iye anakhazikitsa ufumu wakumwamba, womwe ndi Ufumu wa Mesiya. Ufumu umenewu udzathetsa mavuto onse amene tikukumana nawo ndipo udzasintha dziko lonse lapansi kuti likhale paradaiso. Pa nthawi imeneyo tizidzakhala mwamtendere komanso mosangalala mpaka kalekale. (Salimo 37:29) Komabe ngakhale panopo Mulungu amatipatsa malangizo amene angatithandize kukhala ndi moyo wabwino. Iye watipatsanso mwayi wa pemphero womwe umatithandiza kuti tizitha kulankhula naye nthawi iliyonse. Zimene takambiranazi ndi zitsanzo zochepa zosonyeza kuti Yehova amakonda anthu onse komanso kuti amakukondani inuyo.
6. Kodi mungasonyeze bwanji kuyamikira chikondi chimene Yehova wakusonyezani?
6 Komano funso limene muyenera kuliganizira ndi lakuti: Kodi mungasonyeze bwanji kuyamikira chikondi chimene Yehova amakusonyezani? Ambiri angayankhe kuti, “Ndiye kuti nanenso ndiyenera kumamukonda.” Kodi nanunso mukuona choncho? Yesu ananena kuti lamulo lalikulu kwambiri ndi lakuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.” (Mateyu 22:37) Muli ndi zifukwa zambiri zokondera Yehova Mulungu. Koma kodi kungomva mumtima kuti mumakonda Yehova ndi kokwanira kuti munene kuti mumam’kondadi ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndiponso maganizo anu onse?
7. Kodi kungomva mumtima kuti timakonda Mulungu ndi kokwanira? Fotokozani.
7 Monga mmene Baibulo limafotokozera, kukonda Mulungu kumaphatikizapo zambiri osati kungomva mumtima mwanu kuti mumamukonda. Ngakhale kuti kukonda Yehova kuyenera kuyambira mumtima, kungomva kuti mumam’konda sikokwanira. Mofanana ndi mmene nthangala ya chipatso ilili mbali chabe ya chipatsocho, kumva kuti mumakonda Yehova Mulungu ndi mbalinso chabe ya zimene zimafunika kuti munenedi kuti mumakonda Mulungu. Baibulo limanena kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” (1 Yohane 5:3) Choncho, zochita za munthu ndi zimene zingasonyeze kuti amakondadi Mulungu kapena ayi.—Werengani Mateyu 7:16-20.
8, 9. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Mulungu komanso timayamikira zimene watichitira?
8 Timasonyeza kuti timakonda Mulungu tikamatsatira malamulo ake. Ndipotu kuchita zimenezi sikovuta. Malamulo a Yehova amatithandiza kukhala ndi moyo wabwino komanso wosangalala. (Yesaya 48:17, 18) Tikamalola Yehova, yemwe ndi Atate wathu, kuti azititsogolera, timasonyeza kuti timayamikira mochokera pansi pa mtima zinthu zambiri zimene watichitira. Koma n’zomvetsa chisoni kuti anthu ambiri masiku ano samayamikira zimenezi. Ifeyo sitingakonde kukhala m’gulu la anthu osayamikirawo, omwe zochita zawo n’zofanana ndi za anthu ena a m’nthawi ya Yesu. Nthawi ina Yesu anachiritsa anthu 10 akhate koma ndi mmodzi yekha amene anabwerera kudzamuthokoza. (Luka 17:12-17) Tonse tingakonde kukhala ngati munthu woyamikirayu, osati ngati 9 osayamikirawo.
9 Koma kodi malamulo a Yehova omwe tiyenera kutsatirawo ndi ati? M’bukuli takambirana malamulo ambiri koma tiyeni tingobwerezanso ochepa. Kutsatira malamulowa kungachititse kuti Mulungu apitirize kutikonda.
WONJEZERANI CHIKONDI CHANU KWA MULUNGU
10. Fotokozani kufunika kophunzira za Yehova Mulungu.
10 Kuphunzira za Yehova n’kofunika kwambiri kuti tikhale naye pa ubwenzi ndipo kuphunziraku sikuyenera kutha. Tiyerekeze kuti mukuwotha moto chifukwa kunja kukuzizira kwambiri, kodi mungalole kuti motowo uyambe kuchepa mpaka kuzima? Ayi. Mungapitirizebe kusonkhezera motowo kuti usazime. Mungachite zimenezi chifukwa chodziwa kuti ngati motowo utazima, moyo wanu ungakhale pangozi. Monga mmene nkhuni zimathandizira kuti moto usazime, ‘kudziwa Mulungu’ kumatithandiza kuti tipitirizebe kukonda Yehova.—Miyambo 2:1-5.
11. Kodi zimene Yesu ankaphunzitsa otsatira ake zinkawakhudza bwanji?
11 Yesu ankafuna kuti otsatira ake apitirizebe kukonda kwambiri Yehova ndiponso Mawu ake, omwe ndi amtengo wapatali komanso oona. Yesu ataukitsidwa, anafotokozera ophunzira ake awiri maulosi ena a m’Malemba Achiheberi omwe anali atakwaniritsidwa pa iyeyo. Kodi ophunzira akewo anatani atamva zimenezi? Patapita nthawi iwo ananena kuti: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumira pamene anali kulankhula nafe mumsewu, ndi kutifotokozera Malemba momveka bwino?”—Luka 24:32.
12, 13. (a) Kodi anthu ambiri masiku ano chikondi chawo pa Yehova ndi Mawu ake chili bwanji? (b) Kodi tingatani kuti chikondi chathu chisathe?
12 Mutangophunzira mfundo zolondola za m’Baibulo, kodi munamva bwanji? Mwina munasangalala kwambiri ndipo munayamba kum’konda kwambiri Mulungu. Mmenemu ndi momwenso anthu ambiri amamvera. Komano nkhani imakhala pa kuyesetsa kuti chikondi chimenechi chisathe ndipo chipitirizebe kukula. Sitikufuna kutengera chitsanzo choipa cha anthu ambiri m’dzikoli omwe alibe chikondi. Yesu ananeneratu kuti: “Chikondi cha anthu ambiri chidzazirala.” (Mateyu 24:12) Koma kodi mungatani kuti chikondi chanu pa Yehova komanso mfundo zolondola za m’Baibulo chisathe?
13 Muyenera kupitiriza kuphunzira za Yehova Mulungu ndiponso za Yesu Khristu. (Yohane 17:3) Muyeneranso kusinkhasinkha, kapena kuti kuganizira mofatsa, mfundo zimene mwaphunzira m’Mawu a Mulungu ndipo muzidzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi zikundiphunzitsa chiyani za Yehova Mulungu? Kodi pamenepa ndaphunziranso zinthu zina ziti zondichititsa kuti ndizimukonda ndi mtima wanga wonse, maganizo anga onse ndiponso moyo wanga wonse?’ (Werengani 1 Timoteyo 4:15.) Kusinkhasinkha kotereku kungatithandize kuti chikondi chathu pa Yehova chipitirizebe mpaka kalekale.
14. Kodi kupemphera kungathandize bwanji kuti tipitirize kukonda Yehova?
14 Kupemphera nthawi zonse ndi chinthu chinanso chimene chingathandize kuti chikondi chanu pa Yehova chipitirizebe. (1 Atesalonika 5:17) M’Mutu 17, tinaphunzira kuti pemphero ndi mphatso yamtengo wapatali imene Mulungu anatipatsa. Anthu akamalankhulana kawirikawiri momasuka chikondi chawo chimakula. Mofanana ndi zimenezi, tikamapemphera kwa Yehova nthawi zonse, ubwenzi wathu ndi iye umakhala wolimba komanso umapitirira. Tiyenera kupewa mapemphero achizolowezi, omangobwereza mawu omweomwewo nthawi zonse. Tiyenera kufotokozera Yehova zinthu zochokera pansi pa mtima ngati mmene mwana amachitira akamafotokozera zinthu bambo ake omwe amawakonda. Ndi zoona kuti tiyenera kulankhula naye mwaulemu, komabe tiyenera kufotokoza zinthu momasuka, moona mtima ndiponso mochokera pansi pa mtima. (Salimo 62:8) Zimene takambiranazi zikusonyeza kuti kuphunzira Baibulo patokha komanso kupemphera mochokera pansi pa mtima n’zofunika kwambiri pa kulambira kwathu ndipo zingatithandize kuti Mulungu apitirizebe kutikonda.
MUZISANGALALA NDI ZIMENE MUKUCHITA POLAMBIRA MULUNGU
15, 16. N’chifukwa chiyani tiyenera kumaona ntchito yolalikira ngati mwayi komanso chuma?
15 Kuphunzira Baibulo patokha komanso kupemphera ndi zinthu zokhudza kulambira zimene tikhoza kuchita tili kwatokha. Komano tiyeni tikambirane za chinthu china chokhudza kulambira chimene timachita moonekera kwa onse. Chinthu chimenechi ndi kuuza ena zimene timakhulupirira. Kodi mwayamba kale kuuza ena zimene mumaphunzira m’Baibulo? Ngati ndi choncho, ndiye kuti muli ndi mwayi waukulu. (Luka 1:74) Tikamauza anthu ena zimene taphunzira zokhudza Yehova Mulungu, timakhala tikugwira ntchito yofunika kwambiri imene inaperekedwa kwa Akhristu onse. Ntchito imeneyi ndi yolalikira za uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Werengani Mateyu 24:14; 28:19, 20.
16 Mtumwi Paulo ankaona kuti utumiki wake unali wamtengo wapatali ndipo anautchula kuti ndi chuma. (2 Akorinto 4:7) Palibe ntchito yabwino kuposa kuuza ena za Yehova Mulungu ndi zolinga zake. Izi zili choncho chifukwa timatumikira Yehova, yemwe ndi bwana wabwino kwambiri, ndipo ntchito imeneyi imatipezetsa madalitso ambiri kuposa ntchito ina iliyonse. Tikamagwira nawo ntchitoyi, timathandiza anthu a mitima yabwino kuti akhale pa ubwenzi ndi Atate wathu wakumwamba komanso kuti adzapeze moyo wosatha. Kodi palinso ntchito ina yabwino kuposa imeneyi? Ayi. Kuwonjezera pamenepa, kuuza ena za Yehova ndi Mawu ake, kumatithandiza kulimbitsa chikhulupiriro chathu komanso timayamba kumukonda kwambiri. Ndipotu Yehova amayamikira kwambiri zimene mukuchita. (Aheberi 6:10) Kugwira mwakhama ntchito yolalikira kumathandiza kuti Mulungu apitirizebe kukukondani.—Werengani 1 Akorinto 15:58.
17. N’chifukwa chiyani ntchito yolalikira ikufunika kugwiridwa mwansanga makamaka panopa?
17 Nthawi zonse tizikumbukira kuti ntchito yolalikira za Ufumu ikufunika kugwiridwa mwansanga. Baibulo limati: “Lalikira mawu. Lalikira modzipereka.” (2 Timoteyo 4:2) Ntchitoyi ikufunika kugwiridwa mofulumira kwambiri panopa chifukwa Mawu a Mulungu amanena kuti: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwera mofulumira kwambiri.” (Zefaniya 1:14) Lembali likusonyeza kuti nthawi imene Yehova adzawononge dziko loipali ikuyandikira mofulumira kwambiri. Choncho anthu akufunika kuchenjezedwa. Akufunika kudziwa kuti panopa ndi nthawi yoti asankhe Yehova kukhala Wolamulira wawo. Chifukwatu mapeto afika ndithu ndipo “sadzachedwa.”—Habakuku 2:3.
18. N’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Yehova limodzi ndi Akhristu oona?
18 Yehova amafuna kuti tizimulambira limodzi ndi Akhristu oona. N’chifukwa chake Mawu ake amati: “Tiyeni tiganizirane kuti tilimbikitsane pa chikondi ndi ntchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezere kuchita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.” (Aheberi 10:24, 25) Tikakhala pamisonkhano ndi Akhristu anzathu timakhala ndi mwayi wotamanda ndi kulambira Mulungu komanso timalimbikitsana.
19. Kodi tingatani kuti tilimbikitse chikondi ndi mgwirizano mumpingo?
19 Tikamasonkhana ndi Akhristu anzathu timalimbikitsa chikondi ndi mgwirizano mumpingo. Ndi bwino kuti tiziona zabwino zimene ena amachita ngati mmene Yehova amachitira ndi ifeyo. Sitiyenera kuyembekezera kuti Akhristu anzathu azichita zinthu osalakwitsa chilichonse. Tizikumbukira kuti tili ndi misinkhu yosiyanasiyana mwauzimu ndiponso kuti aliyense akhoza kulakwitsa chinachake. (Werengani Akolose 3:13.) Muziyesetsa kugwirizana ndi anthu amene amakonda kwambiri Yehova, ndipo zimenezi zidzakuthandizani kukula mwauzimu. Choncho kulambira Yehova limodzi ndi abale ndi alongo anu auzimu kudzathandiza kuti Mulungu apitirizebe kukukondani. Koma kodi Yehova amadalitsa bwanji anthu amene amamulambira mokhulupirika?
YESETSANI KUTI MUDZAPEZE “MOYO WENIWENIWO”
20, 21. Kodi ‘moyo weniweni’ ndi uti, nanga n’chifukwa chiyani moyo umenewo uli wosangalatsa?
20 Yehova amapereka moyo kwa atumiki ake okhulupirika. Koma kodi moyo wake ndi wamtundu wanji? Moyo umene amapereka ndi wosiyana ndi umene tili nawowu. N’zoona kuti panopa timapuma, timadya, komanso timamwa, zomwe zimasonyeza kuti tili ndi moyo. Ndipotu nthawi zina tikasangalala timatha kunena kuti, “Moyotu koma umenewu.” Koma Baibulo limasonyeza kuti pakalipano palibe munthu amene tingati ali ndi moyo weniweni.
21 Mawu a Mulungu amatiuza kuti tiyenera kuyesetsa kuti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo.’ (1 Timoteyo 6:19) Mawu amenewa akusonyeza kuti ‘moyo weniweni’ si umene tili nawo panowu koma tidzakhala nawo m’tsogolo. Tikadzakhala angwiro, m’pamene tidzakhale ndi moyo weniweni chifukwa moyo wathu udzakhala mmene Mulungu ankafunira poyamba. Tikadzayamba kukhala mwamtendere komanso mosangalala m’paradaiso padziko lapansi, pa nthawi imene sitizidzadwala, ndi pamene tidzasangalale ndi ‘moyo weniweni,’ womwe ndi moyo wosatha. (1 Timoteyo 6:12) Kodi zimene tikuyembekezerazi si zosangalatsa?
22. Kodi mungatani kuti ‘mugwire mwamphamvu moyo weniweni’?
22 Koma kodi tiyenera kuchita chiyani kuti ‘tigwire mwamphamvu moyo weniweniwo’? Pofotokoza nkhaniyi, Paulo analimbikitsa Akhristu kuti “azichita zabwino” ndiponso kuti “akhale olemera pa ntchito zabwino.” (1 Timoteyo 6:18) Zimenezi zikusonyeza kuti, ‘kuti tigwire mwamphamvu moyo weniweni’ tiyenera kutsatira mfundo zolondola zimene taphunzira m’Baibulo. Koma kodi pamenepa Paulo ankatanthauza kuti ‘moyo weniweni’ ndi malipiro amene timalandira chifukwa chochita zabwino? Ayi, chifukwa kulandira moyo umenewu kukudalira pa “kukoma mtima kwakukulu” kwa Mulungu. (Aroma 5:15) Komabe Yehova amasangalala kupereka mphatso kwa anthu amene amamutumikira mokhulupirika. Amafuna kuti mukhale ndi ‘moyo weniweni.’ Moyo wosatha umenewu, womwe udzakhale wamtendere komanso wosangalala, udzaperekedwa kwa anthu amene amayesetsa kuti Mulungu apitirize kuwakonda.
23. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti Mulungu apitirizebe kutikonda?
23 Aliyense ayenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimalambira Mulungu motsatira zimene Baibulo limanena?’ Ngati titamadzifufuza tsiku ndi tsiku n’kutsimikizira kuti nthawi zonse timatsatira zimene Baibulo limanena, ndiye kuti timalambira Mulungu m’njira yolondola. Ndipo sitingakayikire kuti Yehova ndi malo athu obisalapo. Iye adzatetezera anthu ake okhulupirika m’masiku ovuta otsirizawa. Yehova adzatipulumutsanso kuti tilowe m’dziko latsopano lomwe latsala pang’ono kwambiri. Zimenezi zidzakhala zosangalatsa kwambiri. Tidzasangalala podziwa kuti tinasankha zinthu mwanzeru. Nanunso mukamayesetsa kusankha zinthu mwanzeru panopa, mudzasangalala ndi ‘moyo weniweni’ mpaka kalekale ngati mmene Yehova Mulungu ankafunira poyamba.