MUTU 4
“Osaphunzira Ndiponso Anthu Wamba”
Atumwi anachita zinthu molimba mtima ndipo Yehova anawadalitsa
Nkhaniyi yachokera pa Machitidwe 3:1–5:11
1, 2. Kodi Petulo ndi Yohane anachita chozizwitsa chiti pafupi ndi khomo la kachisi?
MASANA dzuwa litachepa mphamvu, Ayuda ambiri okhulupirika komanso ophunzira a Khristu, ankapita kukachisi chifukwa “nthawi yokapemphera” inali itatsala pang’ono kukwana.a (Mac. 2:46; 3:1) Pagululo panalinso Petulo ndi Yohane ndipo ankalowera cha kukhomo lotchedwa Geti Lokongola. Ngakhale kuti anthu ankachita phokoso, panamvekanso mawu a munthu wina wa zaka za m’ma 40 wopemphetsa, amene anabadwa wolumala.—Mac. 3:2; 4:22.
2 Pamene Petulo ndi Yohane anayandikira, munthu wopemphetsayo anafuula monga mwa masiku onse kuti amupatse ndalama. Pamenepo atumwiwo anaima ndipo munthuyo ananyadira chifukwa ankayembekezera kuti alandira ndalama. Ndiyeno Petulo ananena kuti: “Siliva ndi golide ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: M’dzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda!” Tangoganizirani mmene gulu la anthuwo linadabwira pamene Petulo anamugwira dzanja, ndipo kwa nthawi yoyamba m’moyo wake, munthuyo anaimirira. (Mac. 3:6, 7) Ganiziraninso mmene zinthu zinalili pamene munthuyo anaimirira n’kumayang’anitsitsa miyendo yake yochiritsidwayo kenako n’kuyamba kuyeserera kuyenda kwa nthawi yoyamba. M’pake kuti anayamba kudumphadumpha ndi kutamanda Mulungu mofuula.
3. Kodi Petulo anapereka mphatso yofunika kwambiri iti kwa munthu yemwe anali wolumala uja ndiponso kwa anthu ena onse?
3 Gulu la anthuwo, lomwe linasangalala kwambiri, linathamangira pakhonde la zipilala la Solomo kumene kunali Petulo ndi Yohane. Petulo anauza anthuwo tanthauzo lenileni la zimene zinachitikazo ali pakhondeli, ndipo m’pamenenso nthawi ina Yesu anaimapo n’kumaphunzitsa anthu. (Yoh. 10:23) Iye anapereka mphatso yoposa siliva kapena golide kwa gululo komanso munthu amene anali wolumala uja. Mphatsoyo inali yofunika kwambiri kuposa kuchiritsidwa. Petulo anapatsa anthuwo mwayi woti alape ndi kukhululukidwa machimo awo, ndiponso kuti akhale otsatira a Yesu Khristu, amene Yehova anamusankha kukhala “Mtumiki Wamkulu wa moyo.”—Mac. 3:15.
4. (a) Kodi anthu audindo anayamba kuchita chiyani Petulo ndi Yohane atachiritsa munthu mozizwitsa? (b) Kodi tikambirana mafunso awiri ati?
4 Zimene zinachitika pa tsikuli zinali zosaiwalika. Munthu wolumala anachiritsidwa ndipo anayamba kuyenda bwinobwino. Anthu enanso ambirimbiri anapatsidwa mwayi woti achiritsidwe mwauzimu kuti aziyenda mogwirizana ndi zimene Mulungu amafuna. (Akol. 1:9, 10) Komanso, zimene zinachitika pa tsiku limeneli zinachititsa kuti anthu audindo azilimbana ndi anthu okhulupirika otsatira Khristu poyesa kuwaletsa kumvera lamulo la Yesu lakuti azilalikira uthenga wa Ufumu. (Mac. 1:8) Ngakhale kuti Petulo ndi Yohane anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba,” kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa zimene anachita polalikira gulu la anthulo?b (Mac. 4:13) Ndipo kodi tingatani kuti titsanzire njira imene iwowo komanso ophunzira ena anatsatira pamene ankatsutsidwa?
Sitinamuchiritse “ndi Mphamvu Zathu” (Machitidwe 3:11-26)
5. Kodi tikuphunzira chiyani tikaona mmene Petulo analankhulira ndi gulu la anthu?
5 Petulo ndi Yohane anaimirira n’kulankhula ndi gululo ngakhale kuti ankadziwa kuti masiku angapo m’mbuyomo, ena mwa anthuwo ankafuula kuti Yesu apachikidwe. (Maliko 15:8-15; Mac. 3:13-15) Tangoganizani kulimba mtima kumene Petulo anasonyeza pamene analankhula mopanda mantha kuti munthu wolumalayo wachiritsidwa m’dzina la Yesu. Iye sanalankhule mozungulira poopa kukhumudwitsa anthuwo. Iye anadzudzula anthuwo mosapita m’mbali kuti anali ndi mlandu wopha nawo Khristu. Komabe Petulo sanawasungire chakukhosi chifukwa anthuwo ‘anachita zinthu mosazindikira.’ (Mac. 3:17) M’malomwake, iye analankhula nawo monga abale ake ndipo anawalimbikitsa ndi mfundo zabwino za uthenga wa Ufumu. Ngati anthuwo akanalapa ndi kukhulupirira Khristu, “nyengo zotsitsimutsa” zochokera kwa Yehova zikanafika kwa iwo. (Mac. 3:19) Ifenso tiyenera kukhala olimba mtima ndipo tizilankhula mosapita m’mbali tikamalengeza uthenga wokhudza chiweruzo cha Mulungu chimene chikubwerachi. Koma tiyenera kupewa kulankhula mwachipongwe kapena kuweruziratu anthu amene tikuwalalikirawo ndipo tiziwaona kuti akhoza kukhala abale athu auzimu. Mofanana ndi Petulo, tizikambirana nawo kwambiri mfundo zolimbikitsa za uthenga wa Ufumu.
6. Kodi Petulo ndi Yohane anasonyeza bwanji kuti anali odzichepetsa?
6 Atumwiwo anali anthu odzichepetsa kwambiri. Iwo sanadzitamande n’kumati anachiritsa munthu uja chifukwa cha mphamvu zawo. Petulo anafunsa anthuwo kuti: “N’chifukwa chiyani mukutiyang’anitsitsa ngati kuti tamuyendetsa ndi mphamvu zathu, kapena chifukwa cha kudzipereka kwathu kwa Mulungu?” (Mac. 3:12) Petulo komanso atumwi enawo ankadziwa kuti chinthu chilichonse chabwino chimene anachita mu utumiki wawo, chinatheka ndi mphamvu za Mulungu osati zawo. Choncho iwo ankadzichepetsa n’kumauza anthu kuti asamawatamande chifukwa cha zimene achita, koma azitamanda Yehova ndi Yesu.
7, 8. (a) Kodi ndi mphatso iti imene tingapatse anthu? (b) Kodi lonjezo la “kubwezeretsa zinthu zonse” likukwaniritsidwa bwanji masiku ano?
7 Ifenso tiyenera kukhala odzichepetsa tikamagwira ntchito yolalikira za Ufumu. N’zoona kuti masiku ano mzimu wa Mulungu supereka mphamvu kwa Akhristu zochiritsira anthu mozizwitsa. Ngakhale zili choncho, tingathandize anthu kuti azikhulupirira Mulungu ndi Khristu ndiponso kuti alandire mphatso imene Petulo anapereka kwa gulu la anthu aja, yomwe ndi mwayi woti alape n’cholinga choti machimo awo akhululukidwe ndiponso kuti atsitsimulidwe ndi Yehova. Chaka chilichonse, anthu masauzande ambiri amalandira mwayi umenewu ndipo amabatizidwa n’kukhala ophunzira a Khristu.
8 N’zoonadi, tikukhala m’masiku amene Petulo anawatchula kuti “nthawi yobwezeretsa zinthu zonse.” Ndipo pokwaniritsa mawu amene “Mulungu ananena kudzera mwa aneneri ake oyera akale,” Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba m’chaka cha 1914. (Mac. 3:21; Sal. 110:1-3; Dan. 4:16, 17) Zimenezi zitangochitika, Khristu anayamba kuyang’anira ntchito yobwezeretsa kulambira koona padziko lapansi. Chifukwa cha zimenezi, anthu mamiliyoni ambiri abwera m’paradaiso wauzimu ndipo akugonjera Ufumu wa Mulungu. Iwo anavula umunthu wawo wakale umene unali woipa ndi kuvala “umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.” (Aef. 4:22-24) Mofanana ndi kuchiritsidwa kwa munthu wolumala amene anali wopemphetsa uja, ntchito yaikuluyi ikuchitika osati ndi mphamvu za anthu, koma ndi mzimu wa Mulungu. Mofanana ndi Petulo, tizigwiritsa ntchito Mawu a Mulungu molimba mtima ndiponso mwaluso pophunzitsa ena. Zilizonse zimene tingakwanitse kuchita pothandiza anthu kuti akhale ophunzira a Khristu, zimatheka ndi mphamvu ya Mulungu, osati ndi mphamvu zathu.
“Ife Sitingasiye Kulankhula” (Machitidwe 4:1-22)
9-11. (a) Kodi atsogoleri a Chiyuda anatani atamva zimene Petulo ndi Yohane ankaphunzitsa? (b) Kodi atumwiwo anatsimikiza mtima kuchita chiyani?
9 Zimene Petulo analankhula komanso zimene munthu yemwe anali wolumala uja anachita, monga kukuwa ndi kudumphadumpha, zinayambitsa chipwirikiti. Ataona zimenezi, woyang’anira kachisi, amene ntchito yake inali yoonetsetsa kuti pakachisi pali mtendere, ndiponso ansembe aakulu anathamangira komweko kuti akafufuze chimene chinachitika. Zikuoneka kuti anthu amenewa anali Asaduki, omwe anali gulu la anthu olemera ndiponso andale amene ankayesetsa kuti azigwirizana ndi Aroma. Iwo ankakana malamulo a pakamwa amene Afarisi ankawakonda ndiponso ankanyoza chikhulupiriro chakuti anthu akufa adzauka.c Anthu amenewa ayenera kuti anakwiya kwambiri ataona Petulo ndi Yohane m’kachisi, akuphunzitsa molimba mtima kuti Yesu anaukitsidwa.
10 Anthu otsutsa omwe anali atakwiya kwambiri anagwira Petulo ndi Yohane n’kuwatsekera m’ndende, ndipo tsiku lotsatira, anawatengera ku Khoti Lalikulu la Ayuda. Atsogoleriwo, omwe ankadziona kuti ndi anthu apamwamba, ankaona kuti Petulo ndi Yohane anali “osaphunzira ndiponso anthu wamba” ndipo analibe ufulu wophunzitsa m’kachisi. Iwo sanapite kusukulu iliyonse yapamwamba yophunzitsa zachipembedzo. Koma khotilo linadabwa litaona kuti iwo akuphunzitsa mogwira mtima ndiponso mochokera pansi pa mtima. N’chifukwa chiyani Petulo ndi Yohane ankatha kuphunzitsa chonchi? Chifukwa chimodzi chinali chakuti “ankayenda ndi Yesu.” (Mac. 4:13) Mbuye wawo ankaphunzitsa monga munthu waulamuliro, osati ngati alembi.—Mat. 7:28, 29.
11 Khotilo linalamula atumwiwo kuti asiye kulalikira. Pa nthawi imeneyo, khotilo linali ndi mphamvu zambiri. Milungu ingapo m’mbuyomo, khoti lomweli linagamula kuti Yesu anali ‘woyenera kufa basi.’ (Mat. 26:59-66) Komabe, Petulo ndi Yohane sanachite mantha. Ataimirira pamaso pa anthu amenewa omwe anali olemera, ophunzira kwambiri ndiponso otchuka, Petulo ndi Yohane analankhula mopanda mantha koma mwaulemu kuti: “Weruzani nokha, ngati n’zoyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu m’malo momvera Mulunguyo. Koma ife sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”—Mac. 4:19, 20.
12. N’chiyani chingatithandize kuti tizilalikira molimba mtima komanso mogwira mtima kwambiri?
12 Kodi inuyo mumalimba mtima ngati mmene atumwiwo anachitira? Kodi mumamva bwanji mumtima mwanu mukakhala ndi mwayi wolalikira anthu olemera, ophunzira kwambiri kapena otchuka amene ali m’dera lanu? Nanga bwanji ngati abale anu, anzanu akusukulu kapena akuntchito amakunyozani chifukwa cha zimene mumakhulupirira? Kodi mumachita mantha? Ngati mumatero, n’zotheka kuthana ndi vuto limeneli. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anaphunzitsa atumwi ake mmene angayankhire molimba mtima komanso mwaulemu ngati ena atatsutsa zimene amakhulupirira. (Mat. 10:11-18) Yesu ataukitsidwa, analonjeza ophunzira ake kuti adzapitiriza kukhala nawo “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Motsogoleredwa ndi Yesu, “kapolo wokhulupirika komanso wanzeru” masiku ano amatiphunzitsa mmene tingafotokozere zimene timakhulupirira ngati anthu ena akutitsutsa. (Mat. 24:45-47; 1 Pet. 3:15) Timaphunzira zimenezi pamisonkhano ya mpingo pogwiritsa ntchito malangizo opezeka mu Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu, komanso nkhani za pa webusaiti ya jw.org za mutu wakuti “Kuyankha Mafunso a M’Baibulo.” Kodi inuyo mumagwiritsa ntchito zinthu zimenezi? Mukamachita zimenezi, mudzatha kulalikira molimba mtima komanso mogwira mtima kwambiri. Ndipo mofanana ndi atumwi, simudzalola chinthu chilichonse kuti chikulepheretseni kulankhula mfundo zosangalatsa za choonadi zimene munaziona ndi kuzimva.
“Anafuula kwa Mulungu” (Machitidwe 4:23-31)
13, 14. Kodi tiyenera kuchita chiyani anthu ena akamatitsutsa, nanga n’chifukwa chiyani?
13 Petulo ndi Yohane atangotulutsidwa m’ndende, anakumana ndi mpingo wonse. Onse pamodzi, “anafuula kwa Mulungu” ndipo anapemphera kuti awathandize kukhala olimba mtima n’cholinga choti apitirize kulalikira. (Mac. 4:24) Petulo ankadziwa bwino kuti ndi kupusa kwambiri kudalira mphamvu zako pochita chifuniro cha Mulungu. Iye ankadziwa zimenezi chifukwa milungu ingapo m’mbuyomo, anauza Yesu modzitama kuti: “Ngakhale ena onse atathawa n’kukusiyani, ine ndekha sindingathawe!” Koma monga mmene Yesu ananenera, Petulo anaopa anthu ndipo anakana Yesu, amene anali mnzake ndiponso mphunzitsi wake. Komabe, Petulo anaphunzirapo kanthu pa zimene analakwitsazi.—Mat. 26:33, 34, 69-75.
14 Kukhala ndi mtima wofunitsitsa kutumikira Yehova, pakokha sikungakuthandizeni kukwaniritsa ntchito imene mumafunikira kugwira kuti mukhale mboni ya Khristu. Anthu akamakutsutsani n’cholinga choti akusiyitseni zimene mumakhulupirira kapena ntchito yolalikira, muzitsatira chitsanzo cha Petulo ndi Yohane. Muzipemphera kwa Yehova kuti akupatseni mphamvu. Muzipempha ena mumpingo kuti akuthandizeni. Muziuza akulu komanso anthu ena olimba mwauzimu mavuto amene mukukumana nawo. Mapemphero a anthu ena angakhale othandiza kwambiri.—Aef. 6:18; Yak. 5:16.
15. N’chifukwa chiyani anthu amene nthawi ina anasiya kulalikira sayenera kutaya mtima?
15 Ngati nthawi ina munasiya kulalikira chifukwa chotsutsidwa, musataye mtima. Kumbukirani kuti atumwi onse anasiya kulalikira kwa kanthawi Yesu atangophedwa, koma kenako anayambiranso kulalikira mwakhama. (Mat. 26:56; 28:10, 16-20) M’malo mokhumudwa ndi zimene munalakwitsapo m’mbuyomu, mukhoza kuphunzirapo kanthu pa zimenezo komanso kuzigwiritsa ntchito polimbikitsa ena.
16, 17. Kodi tingaphunzire chiyani tikaganizira pemphero limene otsatira a Khristu anapemphera ku Yerusalemu?
16 Anthu olamulira akamatizunza, kodi tiyenera kutchula mfundo zotani popemphera? Onani kuti ophunzira a Yesu sanapemphere kwa Yehova kuti awateteze kuti asakumane ndi chizunzo. Iwo ankakumbukira bwino mawu a Yesu akuti: “Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.” (Yoh. 15:20) M’malomwake, ophunzira okhulupirika amenewa anapempha Yehova kuti ‘amve’ mmene anthu otsutsawo ankawaopsezera. (Mac. 4:29) Ophunzirawo anamvetsa bwino nkhani yonse, ndipo ankadziwa kuti akuzunzidwa pokwaniritsa ulosi. Monga mmene Yesu ananenera pamene ankawaphunzitsa kupemphera, iwo ankadziwa kuti chifuniro cha Mulungu ‘chidzachitika padziko lapansi,’ ngakhale anthu olamulira atayesetsa kuwatsutsa.—Mat. 6:9, 10.
17 Kuti akwanitse kuchita chifuniro cha Mulungu, ophunzirawo anapemphera kwa Yehova kuti: “Tithandizeni ife akapolo anu kuti tipitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.” Kodi Yehova anawayankha bwanji nthawi yomweyo? “Malo amene anasonkhanawo anagwedezeka. Kenako onse anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.” (Mac. 4:29-31) Palibe chimene chingalepheretse Mulungu kukwaniritsa chifuniro chake. (Yes. 55:11) Ngakhale zinthu zitaoneka ngati n’zovuta kwambiri, kapena anthu amene amatitsutsa atakhala amphamvu kwambiri, tikapemphera kwa Mulungu, tingakhale otsimikiza kuti iye adzatipatsa mphamvu kuti tipitirize kulalikira mawu ake molimba mtima.
Tisamangochita Zinthu Kuti Tisangalatse “Anthu, Koma Mulungu” (Machitidwe 4:32–5:11)
18. Kodi anthu a mumpingo ku Yerusalemu ankathandizana bwanji?
18 Pasanapite nthawi, mpingo umene unali utangoyamba kumene ku Yerusalemu unakula kwambiri ndipo unali ndi anthu oposa 5,000.d Ngakhale kuti ophunzirawo anali ochokera m’madera osiyanasiyana, iwo anali ndi “mtima umodzi ndi maganizo amodzi” ndipo ankagwirizana. (Mac. 4:32; 1 Akor. 1:10) Ophunzirawo ankachita zinthu zambiri kuwonjezera pa kupemphera kwa Yehova kuti adalitse ntchito yawo. Iwo ankathandizana mwauzimu komanso mwakuthupi ngati panafunika kutero. (1 Yoh. 3:16-18) Mwachitsanzo, wophunzira wina dzina lake Yosefe, amene atumwi anam’patsa dzina lakuti Baranaba, anagulitsa malo ake ndipo anapereka ndalama zonse kuti athandizire anthu ochokera kutali amene anatsalira ku Yerusalemu kuti apitirize kuphunzira zambiri zokhudza chikhulupiriro chawo chatsopanocho.
19. N’chifukwa chiyani Yehova anapha Hananiya ndi Safira?
19 Hananiya ndi mkazi wake Safira nawonso anagulitsa munda wawo n’kupereka ndalama zothandizira Akhristu anzawo. Iwo ananama kuti apereka ndalama zonse zimene analandira atagulitsa mundawo, koma “anachotsapo ndalama zina n’kubisa.” (Mac. 5:2) Yehova anapha banjali, osati chifukwa choti anapereka ndalama zochepa, koma chifukwa choti anali ndi zolinga zoipa komanso anali anthu achinyengo. Sikuti iwo ananamiza “anthu, koma Mulungu.” (Mac. 5:4) Mofanana ndi anthu achinyengo amene Yesu anawadzudzula, Hananiya ndi Safira ankafuna kuti anthu aziwatama, osati kusangalatsa Mulungu.—Mat. 6:1-3.
20. Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani yopereka zinthu zathu kwa Yehova?
20 Masiku anonso, a Mboni za Yehova mamiliyoni ambiri amatsanzira mtima wopatsa umene ophunzira a Yesu oyambirira a ku Yerusalemu anali nawo ndipo amathandiza pa ntchito yolalikira padziko lonse popereka ndalama mwa kufuna kwawo. Palibe amene amakakamizidwa kupereka ndalama kapena nthawi yake pothandiza pa ntchito imeneyi. Ndithudi, Yehova safuna kuti tizimutumikira monyinyirika kapena mokakamizika. (2 Akor. 9:7) Yehova amasangalala ndi cholinga chimene tikuperekera zinthu kwa iye, osati ndi kuchuluka kwa zinthuzo. (Maliko 12:41-44) Tisayerekeze n’komwe kukhala ndi mtima ngati wa Hananiya ndi Safira, wotumikira Mulungu n’cholinga choti titchuke kapena kuti ena azititama. M’malomwake, nthawi zonse tizitumikira Yehova Mulungu chifukwa chomukondadi ndiponso chifukwa chokonda anthu ngati mmene anachitira Petulo, Yohane ndi Baranaba.—Mat. 22:37-40.
a Anthu ankapemphera kukachisi pa nthawi yopereka nsembe yam’mawa komanso yamadzulo. Nsembe yamadzulo inkaperekedwa cha m’ma “3 koloko masana,” kapena kuti pa ola la 9.
b Onani bokosi lakuti “Petulo Anasiya Kupha Nsomba N’kukhala Mtumwi Wodalirika,” ndi lakuti “Yohane Anali Wophunzira Amene Yesu Ankamukonda Kwambiri.”
c Onani bokosi lakuti “Mkulu wa Ansembe Komanso Ansembe Aakulu.”
d Zikuoneka kuti mu 33 C.E., ku Yerusalemu kunali Afarisi okwana 6,000 okha ndi Asaduki ochepa kwambiri. Zimenezi zingasonyeze chifukwa china chimene magulu awiriwa ankachitira mantha kwambiri ndi zimene ophunzirawo ankaphunzitsa zokhudza Yesu.