MUTU 92
Pa Anthu 10 Akhate, Mmodzi Anathokoza Yesu
YESU ANACHIRITSA ANTHU 10 AKHATE
Yesu atachoka m’mudzi womwe unali kufupi ndi ku Betaniya anapita kumzinda wa Efuraimu, womwe unali kumpoto chakum’mawa kwa mzinda wa Yerusalemu. Iye anakonza ulendowu pofuna kulepheretsa zimene akuluakulu a khoti la Sanihedirini anakonza zoti amuphe. Yesu ndi ophunzira ake anakakhala kumzinda wa Efuraimu, komwe kunali kutali ndi adani ake. (Yohane 11:54) Koma mwambo wa Pasika wa mu 33 C.E. unali utatsala pang’ono kuchitika, choncho Yesu sanakhalitse ku Efuraimu. Ananyamuka n’kulowera chakumpoto kukadutsa m’chigawo cha Samariya mpaka anakafika ku Galileya. Umenewu unali ulendo wake womaliza kupita ku Galileya.
Yesu atangoyamba ulendowo anakumana ndi anthu 10 odwala khate pamene ankatuluka mudzi wina kuti akalowe mudzi wina. Nthawi zina matenda a khate ankachititsa kuti pang’onopang’ono munthu azidyeka ziwalo ngati zala zam’manja, zakumapazi komanso makutu. (Numeri 12:10-12) Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti munthu amene akudwala matendawa azikhala payekha komanso anthu ena akamuyandikira azikuwa kuti “Wodetsedwa, wodetsedwa!”—Levitiko 13:45, 46.
Potsatira Chilamulo cha Mulungu, anthu 10 omwe ankadwala khatewa anaima patali ndi Yesu koma ankakuwa mokweza kuti: “Yesu, Mlangizi, tichitireni chifundo!” Yesu atawaona anawauza kuti: “Pitani mukadzionetse kwa ansembe.” (Luka 17:13, 14) Powauza mawu amenewa, Yesu anasonyeza kuti ankalemekeza Chilamulo cha Mulungu chomwe chinkanena kuti ansembe ndi amene anali ndi udindo wonena kuti munthu amene anali ndi matenda a khate wachira. Zikatero anthuwo ankaloledwanso kukhala ndi anthu ena.—Levitiko 13:9-17.
Anthu 10 akhate aja ankakhulupirira kuti Yesu ali ndi mphamvu zotha kuchita zozizwitsa. Choncho ananyamuka ulendo wopita kukaonana ndi ansembe ngakhale kuti anali asanachiritsidwe. Ali m’njira, anthuwa anachira chifukwa chokhulupirira Yesu. Anayamba kuona kuti khate lawo latha ndiponso kumva kuti ali bwinobwino.
Pa anthu 10 amene anachiritsidwawo, 9 anapitiriza ulendo wawo wokadzionetsa kwa ansembe koma m’modzi anabwerera. Munthuyo anali Msamariya ndipo anabwerera kuti akafunefune Yesu. N’chifukwa chiyani ankafunafuna Yesu? Iye ankafuna kukathokoza Yesu chifukwa chomuchiritsa. Munthuyo ‘anatamanda Mulungu mokweza mawu’ chifukwa anazindikira kuti Mulungu ndi amene anamuchiritsa. (Luka 17:15) Atakumana ndi Yesu, munthuyo anagwada ndipo anamuthokoza.
Kenako Yesu anafunsa anthu amene anali naye kuti: “Amene ayeretsedwa si anthu 10 kodi? Nanga ena 9 ali kuti? Kodi sanapezeke wina aliyense wobwerera kudzalemekeza Mulungu koma munthu wa mtundu wina yekhayu?” Ndiyeno Yesu anauza munthuyo kuti: “Nyamuka uzipita. Chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”—Luka 17:17-19.
Pochiritsa anthu 10 akhatewa Yesu anasonyeza kuti Yehova Mulungu ndi amene ankamutsogolera. Pa anthu 10 onsewo, ndi munthu mmodzi yekha amene anachiritsidwa komanso amene ankayembekezera kudzapeza moyo wosatha. Masiku ano, Mulungu sakugwiritsa ntchito Yesu kuti azichiritsa anthu mozizwitsa. Koma ngati titakhulupirira Yesu tikhoza kudzapeza moyo wosatha. Kodi timayamikira mwayi umenewu ngati mmene Msamariya uja anachitira?