Chidziŵitso pa Nyuzi
Msanganizo wa Tsoka
“Mkati mwa masiku oyambirira a wailesi ya kanema, chiwawa chinawonetsedwa mosabwerezabwereza ndiponso osati mwachindunji kwenikweni kuposa mmene ziriri lerolino,” anazindikira Dr. Paul Wilson wa ku Australian Institute of Criminology. Ngakhale kuli tero, mkulongosola chimene akulingalira kukhala msanganizo kaamba ka tsoka la mayanjano ndi ulamuliro, Wilson anawonjezera kuti: “Tsopano, mwazi umatuluka kuchokera m’thupi ndipo zowawa za imfa zikugwidwa mu kuvutitsa kwake kochedwa. . . . Achichepere akuphedwa ndi nkhwangwa ndipo amatsamwidwa pang’onopang’ono kuchokera ku makosi odulidwa ndipo kulira kwawo kwa imfa kumagwidwa mwachikondi ndi kamera.”
Mu nkhani yake yowoneka mu The Sydney Morning Herald, Dr. Wilson anachitira ndemanga pa vuto limene amtola nkhani amakumana nalo m’kugwira chikondwerero cha unyinji cha ku Australia pa kugwetsa boma kosakhetsa mwazi kwa posachedwapa mu Fiji. Chifukwa chake? “Chiwawa chiri maziko enieni a zosangalatsa zamakono, anatero Wilson. Kukwaniritsidwa kwa nkhani ndi TV ndi osindikiza manyuzipepala kunali kolongosoka, kosanthulidwa bwino, ndipo kozikidwa pansonga, koma panalibe “zithunzi zopuma pa wailesi ya kanema za chiwawa ndiponso ndime za m’nyuzipepala zolongosola zipoloŵe,” iye analongosola tero.
Ndi momvekera bwino chotani nanga mmene kuwonjezeka kwa kusangalatsidwa ndi chiwawa kumayenerera kalongosoledwe ka Baibulo ka awo okhala ndi moyo “m’masiku otsiriza” a dongosolo limene liripoli la kachitidwe ka zinthu. M’mbadwo uno womaliriza woipa, anthu akulongosoledwa kukhala “osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda ab-wino.”—2 Timoteo 3:1, 3.
Mkazi Mmodzi kapena Mitala?
Kodi tchalitchi chiyenera kulandira ziwalo zake zomwe ziri ndi mnzawo wa mu ukwati woposa mmodzi? Kuti chithetse funso limeneli, Tchalitchi cha Anglican mu Uganda chaika gulu kuti liphunzire “mitala ndi banja la Chikristu.” Ecumenical Press Service inasimba kuti, molingana ndi chiwalo chimodzi cha gulu lophunzira, Bishopo Christopher Senyonjo, wokhala ndi anzake a mu ukwati oposa mmodzi sali kokha wolandiridwa komanso ali wopindulitsa. Nchifukwa ninji iye amamva mwanjira imeneyo? Ukwati wa mitala, iye akudzinenera, ungathandize kuletsa kufalikira kwa matenda a AIDS. Pamwamba pa chimenecho, iye akunena kuti kukwatira mitala kuli kwachosankha kwa Akristu, akumanena kuti Kristu “adzasintha maukwati athu oipa ndi osakoma kukhala vinyo wotsekemera, kaya ndi a mkazi mmodzi kapena mitala.”
Komabe, Baibulo mwachimvekere limasonyeza kuti Yehova Mulungu, myambitsi wa ukwati wa mkazi mmodzi, savomereza. Iye anauzira mtumwi Paulo kulemba kuti: “Munthu yense akhale naye mkazi wa iye yekha, ndi mkazi yense akhale naye mwamuna wa iye yekha.” (1 Akorinto 7:2) Mwachiwonekere, Paulo pomalizira analemba ponena za ziyeneretso za awo oweta gulu: “Bishopo chotero ayenera kukhala wopanda banga, mwamuna wa mkazi mmodzi.”—1 Timoteo 3:2, KJ.
Chotero Akristu owona mu Africa, mofanana ndi kwina kulikonse, amawona mitala kaamba ka chimene iri—kupalamula lamulo la Mulungu.
Kulalikira kaamba ka Malipiro
Ansembe a Tchalitchi cha Lutheran cha ku Sweden akhala osasangalala ndi malipiro awo chifukwa, monga mmene kwasimbidwira, malipiro awo ali “otsika kuyerekezera ndi awo omwe akulipiridwa ku ntchito zina zokhala ndi maphunziro ofupikirapo kapena kuphunzitsidwa kumbuyo kwawo.” Ngakhale kuli tero, molingana ndi utumiki wa nkhani wa World Council of Churches, zinthu zikuyenda bwino tsopano. Pambuyo pa “ndawala yaitali ndipo kumbali ina yowawa,” ansembe posachedwapa apeza ntchito ya maora 40 pa mlungu. Koma bwanji ngati anthu a ku Sweden akafuna thandizo la unsembe pambuyo pa maora a kugwira ntchito? Chigwirizano chatsopano cha ntchitocho chimaperekanso mwaŵi wa kulipiridwa malipiro akugwira ntchito mopitirira kaamba ka ora lirilonse lowonjezera la chisamaliro cha unsembe. Malipiro a kugwira ntchito kowonjezereka koteroko akuyembekezeredwa kuwonjezera ndalama zawo za pachaka ndi 10 kufika ku 12 peresenti.
Mosiyanako ndi kudera nkhaŵa pakati pa ansembe a ku Sweden kaamba ka malipiro abwinoko kaamba ka mautumiki awo, pamene Yesu anatumiza ophunzira ake kukalalikira iye anawauza iwo kuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere. Musadzitengere ndalama zagolidi, kapena zasiliva, kapena zakobiri m’malamba mwanu.” (Mateyu 10:8, 9) Kodi nchiyani chimene iye anatanthauza? Mbiri yabwino ya Ufumu sinayenere kugulitsidwa, ndiponso siyenera kugwiritsiridwa ntchito kaamba ka phindu ladyera laumwini. Ophunzirawo anamamatira ku chitsogozo cha Yesu, ndipo utumiki wawo unakwaniritsidwa. Nchifukwa ninji? Chifukwa Mulungu anawachirikiza iwo mu utumikiwo.