Chikristu cha Dziko Chavumbulidwa Monga Chopititsa Patsogolo Kulambira Konyenga
“Umenewu ndi mtundu wosamvera mawu a Yehova Mulungu wawo, wosalola kulangizidwa.”—YEREMIYA 7:28.
1, 2. Ndimotani mmene Yeremiya anavomerezera ku ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu?
“MOTO wachitsimikiziro chowona unali kutentha mkati mwake; panali mphamvu yosonkhezera kulankhula chowonadi, kudzudzula mwaukali komanso kulimbikitsa.” Ndi mawu amenewo ophunzira aŵiri a Chihebri analongosola thayo la Yeremiya. Ngakhale kuti ntchito yake yochokera kwa Mulungu inali yaikulu, ndi yochititsa mantha, iye anadziŵa kuti anayenera kukwaniritsa thayo lake kulinga kwa mtundu wa Yuda. Monga mmene iyemwini analongosolera icho: “Pakuti mawu a [Yehova, NW] ayesedwa kwa ine chitonzo, ndi choseketsa, dzuŵa lonse. Ndipo ngati nditi: ‘Sindidzamtchula iye, sindidzanenanso m’dzina lake.’” Inde chitsenderezo ndi chizunzo chinafikira kukhala chifupifupi chachikulu koposa kwa iye. Koma kodi iye anagonjera?—Yeremiya 20:8, 9a.
2 Yeremiya anapitiriza: “Pamenepo mu mtima mwanga muli ngati moto wotentha wotsekedwa m’mafupa anga, ndipo ndalema ndi kupirira, sindingathe kupiriranso.” (Yeremiya 20:9b) Yeremiya sananyalanyaze ntchito yake ya kulengeza ziweruzo za Mulungu kwa Ayuda.—Yeremiya 6:10, 11.
Yeremiya Wamakono
3. Ndi kawonedwe kotani kamene Yesu ndi ophunzira ake anasonyeza kulinga kwa ntchito yawo?
3 Yeremiya, Kristu Yesu ndi ophunzira Achikristu oyambirira analengeza mopanda mantha uthenga wachilendo wa Ufumu wa Mulungu kwa Ayuda ndi amitundu. Ngakhale kuti poyambapo anaikidwa m’ndende kaamba ka kulalikira, Petro ndi ena molimba mtima anayankha owasuliza awo a chipembedzo: “Tiyenera kumvera Mulungu koposa munthu.” Pa lamulo la olamulira a chipembedzo iwo anakwapulidwa chifukwa cha kulimba mtima kwawo. Ndimotani mmene atumwiwo anachitira? “Masiku onse, m’kachisi ndi m’nyumba, sanaleka kuphunzitsa ndi kulalikira Kristu Yesu.”—Machitidwe 5:29, 40-42; Mateyu 23:13-33.
4. Ndi ndani amene atsatira chitsanzo cha Yeremiya m’zana la 20, ndipo ndimotani mmene iwo achitira chimenechi?
4 Chotero Akristu odzozedwa oyambirira anachita mofanana ndi chitsanzo cha Yeremiya. Ngakhale kuti anayang’anizana ndi kusiyana kodetsa nkhaŵa ndi adani achipembedzo ouma mutu, iwo analengeza ziweruzo za Mulungu. Tsopano, kodi ndani m’zana lino la 20 omwe atsatira chitsanzo chimodzimodzicho? Ndani amene alengeza mwapoyera ndi kunyumba ndi nyumba ziweruzo za Mulungu pa dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu ndipo makamaka pa mnzake wa Yerusalemu, Chikristu cha Dziko? Chitsimikiziro cha mbiri yakale chakhala chikuwunjikika kwa zaka zoposa 68 kusonyeza kuti gulu la Yeremiya lamakono lakhala laling’ono koma gulu lolimba mtima la Mboni zodzozedwa za Yehova. Awa awonjezeredwa ndi kuthandizidwa kuyambira 1935 ndi “khamu lalikulu” lomakulakula la mamiliyoni a anzawo ofunitsitsa, odziŵikanso monga Mboni za Yehova. Ndi liwu logwirizana, iwo akwaniritsa mbali yawo ya Yeremiya ya kutsutsa chipembedzo chonyenga monga msampha ndi malonda.—Chivumbulutso 7:9, 10; 14:1-5.
Chikristu cha Dziko—Nchifukwa Ninji Chiri Chofanana ndi Yerusalemu wa Makono?
5. Ndi m’njira zotani mmene Chikristu cha Dziko chiri chofanana ndi Yerusalemu wakale?
5 ‘Koma,’ wina angafunse, ‘ndi kuti kumene timapeza kufanana pakati pa Yerusalemu wakale ndi Chikristu cha Dziko?’ Chifukwa cha kawonedwe ndi mikhalidwe yofanana imene iripo mu Chikristu cha Dziko chonyada lerolino. Iwo amaika chikhulupiriro chawo mu ‘mizinda yawo yoyera’ ndi malo opatulika, monga ngati Roma, Yerusalemu, Canterbury, Fatima, Guadalupe, ndi Zaragoza, kutchula yochepa yokha. Iwo amakwezeka macathedral awo, basilicas, akachisi, ndi matchalitchi, kumanyada ponena za kukhala kwawo achikale ndi luso lawo la kumanga, ngati kuti izi zimawapatsa iwo kaimidwe kapadera ndi Mulungu. Iwo amafikira pa kunena kuti nyumba zawo zolambirira za chipembedzo zinamangidwa ‘ku ulemerero wa Mulungu.’ Komabe, ndi zingati za nyumba zimenezi m’chenicheni zimene ziri ndi dzina la Yehova Mulungu? Mosiyanako, mmodzi amakumbutsidwa mokhazikika za akatswiri odziŵa zomanga omwe anakonza izo, akatswiri a za luso ndi okongoletsa omwe anakongoletsa izo, anthu olemera amene analipirira kaamba ka izo, kapena “oyera” kwa amene izo zimaperekedwa. Kukhulupirira kwa Chikristu cha Dziko mu kukhala kwake choyambirira ndi mwambo kuli kokha kopanda pake monga mmene chinaliri chikhulupiriro cha Ayuda m’kachisi wake woyera.—Yeremiya 7:4.
6. Ndimotani mmene chilengezo cha chiweruzo cha Yesu pa atsogoleri a chipembedzo a Chiyuda chimagwirira ntchito kwa atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko?
6 M’chigwirizano ndi chitsutso cha Yeremiya cha ansembe ndi aneneri a Chiyuda, nchiyani chimene chinganenedwe ponena za atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko lerolino? Ndi kuwona mtima konga kwa Yeremiya, Yesu anapereka kalongosoledwe ka atsogoleri a chipembedzo cha Chiyuda kamene kamayenerera atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko amakono: “Iwo sachita zimene amalalikira . . . Chirichonse chimene amachita chimachitidwa kuti akoke chisamaliro . . . kukhala ngati akufuna kutenga malo aulemerero pa phwando ndi mipando ya kutsogolo m’masunagoge.” (Mateyu 23:3-7, The Jerusalem Bible) Ndimobwerezabwereza chotani nanga mmene timawonera atsogoleri a chipembedzo apamwamba ndi alaliki akudalitsa misonkhano ya ndale zadziko ndi ya utundu ndi kuilimbikitsa mwakukhalapo kwawo—ndipo akumatengamo mbali m’malo achisamaliro a zowulutsira mawu ndi a ndale zadziko!
7. (a) Ndimotani mmene olalikira ena akusokeretsera unyinji wa anthu? (b) Ndi chitokoso chotani chimene atsogoleri a chipembedzo achipewa?
7 Tsopano, mu mbadwo wa wailesi ya kanema, tiri ndi alaliki a pa TV omwe akuthera ndalama njira yowulutsira mawu imeneyo ndi mtundu uliwonse wa chinyengo cha chiwonetsero ndi chipangizo cha malingaliro kunyenga unyinji ndi kutha ndalama za gululo. Ndi choyenerera chotani nanga chiweruzo cha Yeremiya ngakhale tsopano, zaka zina 2,600 pambuyo pake! “Pakuti kuyambira wamng’ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.” Panthaŵi imodzimodziyo, palibe aliyense wa iwo amene amafuna kulandira chitokoso cha utumiki wowona Wachikristu, kuyang’anizana mwachindunji ndi anthu, kuchokera kunyumba ndi nyumba. Kokha Mboni za Yehova—gulu lodzozedwa la Yeremiya ndi “khamu lalikulu”—alandira thayo limenelo.—Yeremiya 6:13; Machitidwe 20:20, 21.
Kodi Chikristu cha Dziko Chapulumutsidwa?
8. Nchifukwa ninji Chikristu cha Dziko chimakhulupirira kuti sichingafikiridwe ndi Armagedo?
8 Alaliki a pa TV amodzimodzi amenewa amanyengeza unyinji m’lingaliro lonyenga la chisungiko ndi kugwiritsira ntchito kwawo kopanda pake kwa mawu ofala ndi nthanthi ya zaumulungu ya “kubadwanso” ndi “kupulumutsidwa kamodzi, wapulumutsidwa nthaŵi zonse”. Mamiliyoni a anthu ochokera ku chifupifupi chipembedzo chirichonse ndi gulu la mpatuko la Chikristu cha Dziko latsogozedwa kukhulupirira kuti iwo ali “obadwanso” ndipo “opulumutsidwa.” A ndale zadziko opanda manyazi mwachimwemwe amadzinenera mofananamo. Inde, alaliki awo okondeka kwambiri amawauza iwo kuti ali pa mtendere ndi Mulungu chifukwa ali “opulumutsidwa”—ndipo kuti ichi mosasamala kanthu za kugawanika kwawo kwa chipembedzo, ndale, ndi utundu! Ndipo anthuwo amachikonda icho, monga mmene anachitira m’tsiku la Yeremiya! (Yeremiya 5:31; 14:14) Iwo amaganiza kuti sangafikiridwe ndi chiweruzo cha Mulungu cha Armagedo.—Yeremiya 6:14; 23:17; 1 Akorinto 1:10; Chivumbulutso 16:14, 16.
9. (a) Ndi kwa ndani kumene “kubadwanso” m’chenicheni kumagwira ntchito? (b) Nchiyani chimene Baibulo limanena ponena za moyo? (Kaamba ka mafunso aŵiri onsewo, perekani chirikizo lowonjezereka kuchokera mu Reasoning From the Scriptures.)
9 Komabe, phunziro losamalitsa la Mawu a Mulungu ndi ziphunzitso za Kristu zimasonyeza kuti kokha chiŵerengero chochepera chimagawana mwaŵi wa kukhala obadwanso, obadwa ‘kuchokera ku madzi ndi kuchokera ku mzimu,’ mwakutero kuti akagawane ndi ulamuliro wakumwamba ndi Kristu. (Yohane 3:3-5; Aroma 8:16, 17; Chivumbulutso 14:1-3) “Khamu lalikulu” la Akristu owona lerolino silifunikira kubadwanso, popeza kuti chiyembekezo chawo cha moyo wosatha chiri cha padziko lapansi, osati kumwamba. (2 Petro 3:13; Chivumbulutso 21:3, 4) M’kuwonjezerapo, chiphunzitso cha Chikristu cha Dziko chiri chozikidwa pa maziko onyenga—kuti munthu ali ndi moyo wosakhoza kufa wofunikira chipulumutso. Palibe kwina kulikonse m’Baibulo kumene kuli chirikizo la chiphunzitso choterocho, chimene m’chenicheni chiri chotengedwa kuchokera ku nthanthi zakale za Chigriki.a
Sakondwera ndi Mawu Ake kapena Dzina
10. Ndimotani mmene atsogoleri a chipembedzo ambiri amawonera Baibulo?
10 Pali nsonga zina zofananako pakati pa Yerusalemu wakale ndi Chikristu cha Dziko chamakono. Yeremiya ananena kuti: “Tawona! mawu a Yehova awatonzetsa iwo; sakondwera nawo.” (Yeremiya 6:10) Atsogoleri a chipembedzo amakonda kugwira mawu a nthanthi ndi asayansi, m’malo mwa Mawu a Yehova. Ambiri amachititsidwa manyazi ndi Baibulo; iwo amafikira pa kulitonza ilo kupyolera mwa “kusuliza kwawo kwakukulu.” Iwo amanena kuti ilo liri nthanthi ndi nthano chabe yoperekedwa monga bukhu labwino. (Yeremiya 7:28) Ndipo ponena za dzina la Mkonzi wake, iwo amalipeputsa ilo. Ndi umboni wotani umene tiri nawo kaamba ka kupatsa mlandu kumeneko?
11. Ndi kusiyana kotani kumene kulipo pakati pa Chikristu cha Dziko ndi Yeremiya m’kugwiritsira ntchito kwawo dzina la Mulungu?
11 Ngakhale kuti tetragrammaton ya Chihebri (יהוה) imawoneka chifupifupi nthaŵi 7,000 m’Malemba Achihebri, dzina lakuti “Yehova,” kapena “Yahweh,” lalowedwa m’malo m’maBaibulo ambiri a Chingelezi ndi liwu losakhala dzina lakuti “AMBUYE.” Mwachitsanzo, ilo linalekedwa kotheratu kuchokera m’matembenuzidwe a posachedwapa a Baibulo m’chinenero cha chiAfrikaans. Matembenuzidwe a Spanish Franquesa-Solé anagwiritsira ntchito dzinalo m’kusindikizidwa kwake koyamba. Pamene kope lolembedwanso linafalitsidwa, dzina laumulungulo linazimiririka, kulowedwa m’malo ndi Señor (Ambuye). Ndipo ngakhale pamene matembenuzidwe a Chikristu cha Dziko amaphatikiza dzina la Mulungu, atsogoleri a chipembedzo samaligwiritsira ntchito ilo kaŵirikaŵiri. Komabe, Yeremiya anagwiritsira ntchito dzina lodziŵika la Mulungu nthaŵi 726 mu uthenga wake wa ulosi!b
“Mfumu Yaikazi ya Kumwamba” ndi Kulambira Mafano
12-14. (a) Ndi m’ntchito yachangu yotani mmene mabanja a Chiyuda anadzilowetsamo? (b) Ndimotani mmene Yehova anawonera kulambira kwawo?
12 Tikupeza kufanana kwina pamene tisanthula uthenga wa Yeremiya ku Yerusalemu. Pamene Yehova anauza mneneri wake kuti asapempherere anthuwo, iye anatchula chifukwa chake. “Kodi suwona iwe chimene achichita m’midzi ya Yuda ndi m’misewu ya Yerusalemu? Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa.” Ndipo kodi ndi m’ntchito ya changu yotani imene banja lonse linalowetsedwamo? “Kuti apange mikate ya ‘mfumu yaikazi ya kumwamba’”!—Yeremiya 7:16-18; 44:15, 19.
13 Bukhu lochitira ndemanga limodzi la Chiyuda limanena kuti: “Matsenga a ‘mfumu yaikazi ya kumwamba’ anali kulondoledwa mofunitsitsa ndi mwapoyera.” Modabwitsa, mtundu wa Yuda unatsatira machitachita a mafano kulambira mulungu wachikazi wachikunja mwinamwake mulungu wachikazi wa kubala wa Chibabulo, Ishtar, wachitatu wa milungu itatu ya nyenyezi ya Chibabulo. Kapena “mfumu yaikazi” imeneyi ingakhale inali yolingana ndi mulungu wachikazi wa Chikanani, Ashtoreti.—1 Mafumu 11:5, 33.
14 M’kuwonjezera ku kulambira mulungu wachikazi kumeneku, iwo anadzilowetsa m’mitundu ina ya kulambira mafano. Yehova anawatsutsa iwo kaamba ka ichi, akumanena kuti: “Chifukwa chanji andiputa ine ndi mafano awo osema, ndi zachabe zachilendo?” Mlanduwo ukupitiriza: “Sanamvera mawu anga, osayenda mmenemo; koma anatsata kuwuma kwa mtima wawo, ndi Baala, monga makolo awo anawaphunzitsa.” (Yeremiya 8:19; 9:13, 14) Kodi Chikristu cha Dziko chagwera mumsampha umodzimodziwo?
15. (a) Ndi mkhalidwe wotani ponena za kupembedza mafano umene timapeza mu Chikristu cha Dziko lerolino? Tchulani zitsanzo za kumaloko. (b) Ndi kaimidwe kotani ka Mariya kamene Akristu owona amatenga? (Onaninso Reasoning From the Scriptures, masamba 254-61.)
15 Yenderani tchalitchi chirichonse kapena cathedral—Protesitanti, Chikatolika, kapena Orthodox—ndipo mudzapeza chifupifupi mafano a mtanda. Koma m’mabwalo a Chikatolika ndi Orthodox, pali mafano a “Mariya Woyera namwali wosatha, Mayi wa Mulungu Wowona” m’makhazikidwe osiyanasiyana ndi kaimidwe kosatha.c Dzina laulemu la pamwamba lirilonse limawunjikidwa pa iye, kuphatikizapo “Mfumu yaikazi ya kumwamba” ndi “Mfumu yaikazi ya chilengedwe”!d Kumbali ina, gulu la Yeremiya, pamene limalemekeza Mariya monga mayi wa Yesu ndi m’khulupiriri wodzozedwa, mosamalitsa atsatira uphungu wa atumwi: “Dzisungilireni nokha kupewa mafano.”—1 Yohane 5:21; Yeremiya 10:14.
Utatu Walowa M’malo Mfumu Imodzi Ambuye Yehova
16. Ndi chiphunzitso chotani chimene chinapeza njira kaamba ka kulemekeza Mariya, ndipo motani?
16 ‘Koma,’ inu mungafunse: ‘Kodi kulambira kumeneku ndi ulemu wa Mariya kunabwerapo motani?’ Kupyolera mu kachitidwe kena ka tchalitchi champatuko choyambirira cha kutenga alambiri onyenga. Lingaliro la milungu itatu mwa mmodzi linasungiliridwa mofala m’dziko la chikunja. Aroma akale anali ndi makachisi okhala ndi magulu atatu a nyumba zopempherera “zoperekedwa kwa milungu itatu yogwirizanitsidwa m’chikhulupiriro ndi kulambira. Mmenemo ndi mmene zinaliri m’kachisi ya Jupiter Optimus Maximus mu Capitol, woperekedwa ku utatu wa chicapitol Jupiter-Juno-Minerva.”e
17, 18. (a) Nchiyani chimene chatsenderezedwa, mwakutero kulola chiphunzitso cha Utatu kupita patsogolo? (b) Perekani umboni wowonjezereka kuchokera ku Reasoning From the Scriptures.
17 Ndi cholinga chofuna kupititsa patsogolo chiphunzitso chobuka cha “Utatu Woyera Koposa” m’mazana a chitatu ndi achinayi, chinali choyenerera kaamba ka Tchalitchi cha Chikatolika kutsendereza lingaliro la Chihebri lolongosoledwa momvekera bwino m’mawu a Yeremiya: “Chifukwa palibe akunga inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu liri lalikulu ndi lamphamvu. Koma Yehova ndiye Mulungu wowona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya.” Yesu anatsimikizira kamvedwe kameneko pamene iye anagwira mawu kuchokera ku mawu a Mose akuti: “Mvera, Israyeli, Yehova Mulungu wathu ndiye Yehova mmodzi.”—Yeremiya 10:6, 10; Marko 12:29, NW; Deuteronomo 6:4.
18 Mothandizidwa ndi malaulo a Chiyuda a kusatchula “Yahweh” kapena “Yehova,” kugwiritsira ntchito kwa dzina la Mulungu kunasiidwa ndi Chikristu cha Dziko champatuko. Ichi chinapereka danga mu zamaphunziro a zaumulungu limene ‘Utatu Woyera’ unalidzadza.f
19. (a) Nchiyani chimene chakhala zina za zotulukapo za kuvomereza Utatu kwa Chikristu cha Dziko? (b) Ndi kunyenga kotani kumene kunavomerezedwa ndi cholinga chofuna kuchirikiza Utatu?
19 Chotero, Chikristu cha Dziko chasankha ‘kuyenda pambuyo pa mulungu wina,’ mulungu wautatu, yemwe anali wosadziŵika kotheratu kwa Ayuda ndi kwa Kristu ndi Akristu owona. Ndipo kuti achirikize chinsinsi cha atatu mwa mmodzi chimenechi, atembenuzi a Chikristu cha Dziko anafikira ngakhale pa kutembenukira ku kunyenga mu King James Version.g M’kuwonjezerapo, monga chotulukapo chanzeru cha chiphunzitso cha Utatu, mbali yokulira ya Chikristu cha Dziko yagweranso m’kulambira kapena kulemekezedwa kwa “Mfumu yaikazi ya Kumwamba” yake.—Yeremiya 7:17, 18, New International Version.
Atsogoleri a Chipembedzo Apititsa Patsogolo Chizunzo
20, 21. Ndi njira yotani imene atsogoleri a Chikristu cha Dziko atsatira, ndipo ndi mafunso otani amene ali oyenerera tsopano?
20 M’chiyang’aniro cha zomwe zalongosoledwazo, funso la Yeremiya liri loyenerera kaamba ka atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko: “Bwanji muti: ‘Tiri ndi nzeru ife, ndi malamulo a Yehova ali ndi ife?’ Koma, tawona, peni lonyenga la alembi lachita zonyenga. . . . Tawonani! akana mawu a Yehova, ali nayo nzeru yotani?” (Yeremiya 8:8, 9) Iwo akana Yehova ndi oimira ake, Mboni zake. Monga mmene ansembe ndi aneneri anazunzira Yeremiya, choteronso atsogoleri a chipembedzo a Chikristu cha Dziko akhala kumbuyo kwa chizunzo choipa koposa cha Mboni za Yehova mkati mwa zana lino.
21 Koma nchifukwa ninji iwo amapititsa patsogolo chizunzochi? Nchiyani chimene Mboni zachita chomwe chadzutsa mkwiyo wawo ndi kudzetsa moto wawo? Nkhani yomalizira m’ndandanda ino idzasanthula zimenezo ndi mafunso ofananawo.
[Mawu a M’munsi]
a Kaamba ka kulingaliridwa kosamalitsa kwa nsongazi, onani masamba 76-80, 356-61, 379-80 mu Reasoning From the Scriptures, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
b Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka pa kutsendereza kwa dzina laumulungu, onani broshuwa ya masamba 32 Dzina La Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
c The Image of Guadalupe—Myth or Miracle?, lolembedwa ndi Jody Brant Smith, tsamba 6.
d “The Glories of Mary, lolembedwa ndi Alphonsus de Liguori, tsamba 424.
e Las Grandes Religiones Ilustradas, (Zipembedzo Zazikulu Zichitiridwa Chitsanzo) tsamba 480.
f Kaamba ka phunziro la chiphunzitso cha Utatu, onani Reasoning From the Scriptures, masamba 405-26.
g 1 Yohane 5:7 kuli kuwonjezera konama, ndipo Mateyu 24:36, lomwe silimaphatikiza “osatinso Mwana,” kuli kuphophonya konyenga. Onani The Emphatic Diaglott, mawu a m’munsi, tsamba 803 lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., ndi The Codex Sinaiticus and The Codex Alexandrinus, tsamba 27, lofalitsidwa ndi Trustees of the British Museum.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Ndimotani mmene gulu lamakono la Yeremiya lazindikiritsidwira?
◻ Ndi kuti kumene kuli kufanana kwina pakati pa Yerusalemu wakale ndi Chikristu cha Dziko?
◻ Ndimotani mmene atsogoleri a chipembedzo anyengera anthu m’kukhulupirira kuti iwo ali pa mtendere ndi Mulungu?
◻ Ndi kunyalanyaza ndi kulambira mafano kotani kumene kuli kowonekera m’Chikristu cha Dziko?
[Chithunzi patsamba 16]
Mu 1938 Mboni zinali kutsutsa chipembedzo chonyenga
[Zithunzi patsamba 17]
Chikristu cha Dziko chimakhulupirira m’kulemekezedwa kwa nthaŵi yaitali kwa malo ake opatulika monga mmene Ayuda anakhulupirira m’kachisi
[Chithunzi patsamba 18]
Alaliki a pa TV a Chikristu cha Dziko amanyenga mamiliyoni angapo m’kukhulupirira kuti iwo ali “opulumutsidwa” kapena “obadwanso”