Chidziŵitso Cholongosoka cha Mulungu ndi Mwana Wake Chimatsogolera ku Moyo
“Koma moyo wosatha ndi uwu, kuti akadziwe inu Mulungu wowona yekha, ndi Yesu Kristu amene munamtuma.”—YOHANE 17:3.
1. Nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Yesu Kristu chiri chofunika chotero?
CHIDZIŴITSO cholongosoka cha Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu, chiri chofunika kwambiri kaamba ka awo omwe amafuna moyo wosatha. “Amene [Mulungu] chifuno chake chiri chakuti anthu a mitundu yonse ayenera kupulumutsidwa ndi kufika pa chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi.” (1 Timoteo 2:4, NW) Chidziŵitso choterocho kuchokera ku Mawu owuziridwa a Mulungu, Baibulo, chidzatikonzekeretsa ife kudziwa amene Mulungu ali ndi chimene chiri thayo lathu kulinga kwa iye. (2 Timoteo 3:16, 17; 1 Yohane 2:17) Chidzatikhozetsanso ife kuzindikira bwino lomwe Yesu Kristu ndi unansi wathu kwa iye.—Masalmo 2:12; Afilipi 2:5-11.
2. Kodi nchiyani chimene chingatulukemo kuchokera ku kusoŵeka kwa chidziŵitso cholongosoka?
2 Popanda chidziŵitso cholongosoka, tingaikidwe mumsampha ndi ziphunzitso zonama zochirikizidwa ndi wotsutsa wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, amene ali “wabodza ndi atate wabodza.” (Yohane 8:44) Chotero, ngati chiphunzitso chimatsutsa Mawu a Mulungu, ngati icho chiri chabodza, kenaka kukhulupirira icho ndi kuchiphunzitsa icho kumatsutsa Yehova ndipo kumatibweretsa ife m’chitsutsano ndi iye. Chotero tifunikira kusanthula Malemba mosamalitsa kuti tisiyanitse chowonadi kuchokera ku bodza. (Machitidwe 17:11) Sitifunikira kukhala ngati awo omwe amaphunzira “nthaŵi zonse ndipo komabe osakhoza kufika ku chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi.”—2 Timoteo 3:1, 7.
3. Kodi nchiyani chimene chiri chiphunzitso chomveka cha Baibulo chonena za Mulungu, Yesu Kristu, ndi mzimu woyera?
3 Monga mmene tawonera m’nkhani yathu yapitayo, chiphunzitso cha Utatu sichiri chiphunzitso cha m’Baibulo. Mu Mawu enieni a Mulungu, iye akutiuza momvekera bwino kuti ali Mlengi wa zinthu zonse ndi kuti chilengedwe chake choyambirira m’mwamba anali Mwana wake. (Chivumbulutso 4:11; Akolose 1:15, 16) Mulungu anatumiza Mwana wake ku dziko lapansi monga munthu kudzapereka nsembe ya dipo yomwe inatumikira monga maziko kaamba ka kukhululukira kwa machimo a mtundu wa anthu, ndi kuwunikira anthu owona mtima mowonjezereka ponena za Mulungu ndi zifuno zake. (Mateyu 20:28; Yohane 6:38) Komabe, chiphunzitso chopepuka, chomvekera bwino chakuti Mulungu ndi Kristu ali anthu aŵiri osiyana, ndi kuti mzimu woyera siuli munthu koma uli mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu chapotozedwa kupyola mkati mwa mazana. M’malo mwake chiphunzitso cha Utatu chakhala maziko a chiphunzitso cha m’Chikristu cha Dziko.
“Ine ndi Atate Ndife Amodzi”
4. Nchifukwa ninji kudzinenera kumene matchalitchi amapanga ponena za Yohane 10:30 sikuli kowona?
4 Matchalitchi kaŵirikaŵiri amagwira mawu Yohane 10:30 kuyesera kuchirikiza Utatu, ngakhale kuti palibe kutchula kulikonse komwe kukupangidwa kwa munthu wachitatu aliyense m’versi limenelo. Pamenepo Yesu ananena kuti: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” Koma kodi Yesu anatanthauza kuti anali Mulungu Wamphamvuyonse iyemwini, kokha mu mkhalidwe wosiyana? Ayi, chimenecho sichikanakhala tero popeza kuti Yesu nthaŵi zonse ananena kuti anali Mwana wa Mulungu, wochepa kwa Iye ndipo wogonjera kwa Iye. Nchiyani, chotero, chimene Yesu anatanthauza pa Yohane 10:30?
5, 6. (a) Kodi ndi mlingaliro lotani limene Yesu anatanthauza kuti iye ndi Atate wake anali amodzi? (b) Ndimotani mmene ichi chikuchitidwa chitsanzo m’chigwirizano ndi ophunzira a Yesu?
5 Yesu anatanthauza kuti iye anali m’modzi m’malingaliro ndi chifuno ndi Atate ake. Ichi chingawonedwe pa Yohane 17:21, 22, pamene Yesu ankapemphera kwa Mulungu kuti ophunzira ake “onse akhale amodzi, monga inu, Atate, muli m’chigwirizano ndi ine ndi ine m’chigwirizano ndi inu, kuti iwonso akhale mwa ife; . . . kuti akhale amodzi, monga ife tiri m’modzi.” Kodi Yesu ankapemphera kuti ophunzira ake onse akakhala munthu m’modzi? Ayi, iye anali kupemphera kuti iwo akakhala m’chigwirizano, cha malingaliro amodzi ndi chifuno, monga mmene Yesu ndi Mulungu analiri.
6 Lingaliro lofananalo likulongosoledwa pa 1 Akorinto 1:10, pamene Paulo analongosola kuti Akristu ‘anene chimodzimodzi, ndi kuti pasakhale malekano pakati pawo, koma kuti amangike mu mtima womwewo ndi m’chiŵeruzo chomwecho.’ Chotero pamene Yesu ananena kuti iye ndi Atate ake anali amodzi, iye sanatanthauze kuti iye anali munthu mmodzi, mongadi pamene iye ananena kuti ophunzira ake akafunikira kukhala amodzi iye sanatanthauze kuti iwo anali munthu mmodzi.
Kodi Ndani Amene Anali “Mawu”?
7. (a) Kodi nchiyani chimene Chikristu cha Dziko chimadzinenera ponena za Yohane 1:1? (b) Kodi nchiyani chimene chiri pamenepo mu Yohane 1:1 chomwe mwamsanga chimasonyeza kuti palibe Utatu womwe ukulankhulidwa?
7 Komabe, bwanji ponena za Yohane 1:1, yemwe amanena mu King James Version kuti: “Pachiyambi panali Mawu, ndipo Mawu anali kwa Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu”? Yohane 1:14 amatiwuza kuti “Mawu anasandulika thupi nakhazikika pakati pa ife.” Chikristu cha Dziko chimadzinenera kuti “Mawu” amenewa (Chigriki, loʹgos) omwe anadza ku dziko lapansi monga Yesu Kristu anali Mulungu Wamphamvuyonse iyemwini. Komabe, dziŵani kuti ngakhale mu King James Version Yohane 1:1 amanena kuti “Mawu anali kwa Mulungu.” Winawake yemwe ali kwa munthu wina sali wofanana ndi munthu wina ameneyo. Chotero ngakhale kuchokera mu matembenuzidwe amenewa, maumunthu osiyana aŵiri akusonyezedwa. Ndiponso, palibe munthu wachitatu wa Utatu uliwonse yemwe akutchulidwa npang’ono pomwe.
8. Ndimotani mmene matembenuzidwe ena a Baibulo amaikira mbali yotsirizira ya Yohane 1:1?
8 Ponena za kunena kwa King James Version m’mbali yothera ya Yohane 1:1 kuti “Mawu anali Mulungu,” matembenuzidwe ena amanena chinachake chosiyana. Ena ali onga otsatirawa:
1808: “ndipo mawu anali ka mulungu.” The New Testament, in an Improved Version, Upon the Basis of Archbishop Newcome’s New Translation: With a Corrected Text, London.
1864: “ndipo ka mulungu kanali Mawu.” The Emphatic Diaglott, yolembedwa ndi Benjamin Wilson, New York ndi London.
1935: “ndipo Mawu anali aumulungu.” The Bible—An American Translation, lolembedwa ndi J. M. P. Smith ndi E. J. Goodspeed, Chicago.
1935: “Logos anali waumulungu.” A New Translation of the Bible, lolembedwa ndi James Moffatt, New York.
1975: “ndipo ka mulungu (kapena, wa mkhalidwe waumulungu) anali Mawu.” Das Evangelium nach Johannes, lolembedwa ndi Siegfried Schulz, Göttingen, Germany.
1978: “ndipo mkhalidwe wonga waumulungu unali Logos.” Das Evangelium nach Johannes, lolembedwa ndi Johannes Schneider, Berlin.
1979: “ndipo ka mulungu kanali Logos.” Das Evangelium nach Johannes, lolembedwa ndi Jurgen Becker, Würzburg, Germany.
Ndiponso, mu 1950 New World Translation of the Christian Greek Scriptures, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., inapereka kalongosoledwe kakuti, “ndipo Mawu anali ka mulungu.”
9. M’lemba la Chigriki, kodi nchiyani chimene chiri kutsogolo kwa kuwoneka koyamba kwa nauni the·osʹ (mulungu) pa Yohane 1:1, chimene chimasonyeza kuti likulozera kwa Mulungu Wamphamvuyonse?
9 Kodi kalongosoledwe kotereka kamavomerezana ndi kaikidwe ka mawu ka Yohane 1:1 m’chinenero cha Chigriki? Inde, kamatero. Pa Yohane 1:1 pali kupezeka kuŵiri kwa nauni ya Chigriki the·osʹ (mulungu). Kuwoneka koyamba kumalozera kwa Mulungu Wamphamvuyonse, amene anali ndi Mawu—“ndipo Mawu [loʹgos] anali kwa Mulungu [mtundu wa the·osʹ].” The·osʹ woyambirira ameneyu akutsatira mtundu wa mawu olongosola chinthu a Chigriki ho. Nauni the·osʹ yokhala ndi mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika ho kutsogolo kwake imalozera ku munthu wina wosiyana, m’nkhaniyi Mulungu Wamphamvuyonse—“ndipo Mawu anali [ndi] Mulungu.”
10. Ponena za kuwonekera kwachiŵiri kwa the·osʹ pa Yohane 1:1, kodi nchiyani chimene kusiya kwa mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika ho kumasonyeza?
10 Koma m’mbali yothera ya Yohane 1:1, matembenuzidwe oterowo monga momwe andandalitsidwira mu ndime 8 amaika the·osʹ wachiŵiri (nauni yolongosola mtundu wa chinthu) kukhala “umulungu” kapena “ka mulungu” m’malo mwa “Mulungu.” Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti the·osʹ wachiŵiri ali nauni yolongosola mtundu wa chinthu chimodzi chopezeka kumbuyo kwa verebu ndipo opanda mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika ho m’Chigriki. Mu versi limeneli, kapangidwe ka mzera wa mawu kameneka kamalozera ku mkhalidwe kapena mtundu wa mutu wa nkhani. Limawunikira mtundu wa Mawu kuti iye anali “waumulungu,” “ka mulungu,” koma osati Mulungu Wamphamvuyonse. Ichi chiri m’chigwirizano ndi malemba ambiri amene amasonyeza kuti “Mawuyo” anali wolankhulira wa Mulungu, wotumizidwa ku dziko lapansi ndi Mulungu. Monga mmene pa Yohane 1:18, (NW) pamanenera: “Kulibe munthu anawona Mulungu pa nthaŵi iriyonse; ka mulungu kobadwa kokha [Mwana yemwe analengedwa kumwamba ndi Mulungu Wamphamvuyonse] wokhala pa chifuwa cha Atate iyeyu [ali yemwe anadza ku dziko lapansi monga munthu Yesu ndipo] analongosola iye [Mulungu Wamphamvuyonse].”
11. Kodi ndi chitsanzo chiti cha m’Baibulo chimene chiripo cha kuika kwa otembenuza mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika “ka” pamene kulibe aliwonse m’Chigriki, ndipo nchifukwa ninji ichi chimachitidwa?
11 Pali maversi ena ambiri a Baibulo kumene awo omwe amatembenuza kuchokera m’Chigriki kupita m’chinenero china amaika mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika “ka” kumbuyo kwa mawu oitanira munthu ngakhale kuti mulibe mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika m’malemba a Chigriki. Kuikamo kwa mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika kumeneku m’matembenuzidwe kumazindikiritsa mkhalidwe kapena mtundu wa mawu oitanira munthu. Mwachitsanzo, pa Marko 6:49, pamene atumwi anawona Yesu akuyenda pa madzi, King James Version imanena kuti, “iwo anayesa kuti unali mzimu” (Chigriki, phanʹta·sma). New World Translation imaika mawuwo molondola kwambiri kuti, “Iwo anaganiza kuti: ‘Uli mzukwa!’” M’njira yofananayo, matembenuzidwe olondola a Yohane 1:1 amasonyeza kuti Mawu sanali “Mulungu,” koma anali “ka mulungu.”
12. Kodi ndi kugwiritsira ntchito kofananako kotani kwa mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika “ka” komwe kukupezeka pa Yohane 8:44?
12 Zitsanzo ziŵiri zofananako zikupezeka pa Yohane mutu 8, versi 44. Pamenepo Yesu, akunena za Mdyerekezi, akunena kuti: “Iyeyu anali wambanda kuyambira pa chiyambi . . . Ali wabodza ndi atate wake wa bodza.” Mofananako ndi Yohane 1:1, m’Chigriki choyambirira nauni yolongosola mtundu wa chinthu m’kalongosoledwe kaŵiri konseka (“wambanda,” “wabodza”) iri patsogolo pa verebu ndipo iribe mawu olongosola chinthu chimodzi chotsimikizirika. M’nkhani iriyonse, mkhalidwe kapena mtundu wa Mdyerekezi ukulongosoledwa ndipo m’matembenuzidwe ambiri a zinenero zamakono, chiri choyenera kuika mawu olongosola chinthu chosatsimikizirika (“ka”) kuti ilongosole ichi. Chotero, King James Version imaika malongosoledwe amenewa, “Iye anali wambanda . . . ali wabodza ndi atate wa ilo.” Onaninso Marko 11:32; Yohane 4:19; 6:70; 9:17; 10:1, 13, 21; 12:6.
“Ambuye Wanga ndi Mulungu Wanga”
13, 14. Nchifukwa ninji Tomasi akanaitana Yesu “Mulungu wanga” popanda kutanthauza kuti Yesu anali Yehova?
13 Ophunzitsa Utatu amagwiranso mawu a Yohane 20:28 kuchirikiza kudzinenera kwawo. Pamenepo Tomasi ananena kwa Yesu: “Ambuye wanga ndi Mulungu wanga!” Monga momwe zasonyezedwera pamwambapa, palibe chitsutso chirichonse kwa Tomasi ku kulozera kwa Yesu kukhala ka mulungu. Chimenecho chingakhale m’chigwirizano ndi chenicheni chakuti Yesu, m’kukhalapo kwake asanakhale munthu, m’chenicheni anali ka mulungu, uku ndiko kuti, munthu wamphamvu, waumulungu. Ndipo iye m’chenicheni wakhala tero chiyambire imfa yake ndi kuwukitsidwa kupita ku moyo wa kumwamba. Yesu anakhoza ngakhale kugwira mawu kuchokera m’Masalmo kusonyeza kuti anthu amphamvu kwambiri ankaitanidwa kukhala “timilungu.” (Masalmo 82:1-6; Yohane 10:34, 35) Mtumwi Paulo anadziŵa kuti panali “‘milungu’ yambiri ndi ‘ambuye’ ambiri.” (1 Akorinto 8:5) Ngakhale Satana amatchedwa “mulungu wa dongosolo iri la zinthu.”—2 Akorinto 4:4.
14 Kristu ali ndi malo apamwamba kwambiri kuposa anthu opanda ungwiro, kapena Satana. Ngati oterewa angalozeredwe kukhala “milungu,” motsimikizirikadi Yesu angalozeredwe ndipo analozeredwa, kukhala ka mulungu. Chifukwa cha malo ake apadera m’chiyanjano ndi Yehova, Yesu ali “mulungu wobadwa yekha” (Yohane 1:18, NW), “Mulungu wa Mphamvu” (Yesaya 9:6), ndi “ka mulungu” (Yohane 1:1). Chotero panalibe chirichonse chosayenera ponena za kulozera kwa Tomasi kwa Yesu m’njira yoteroyo. Tomasi ankanena kuti Yesu anali ka mulungu kwa iye, winawake waumulungu, wamphamvu. Koma sanali kunena kuti Yesu anali Yehova, chimene chiri chifukwa chake Tomasi ananena kuti, Mulungu “wanga” ndipo osati “ndi” Mulungu.
15. Ndimotani mmene versi 31 la Yohane mutu 20 limazindikiritsa bwino lomwe amene Yesu ali?
15 Kokha maversi atatu pambuyo pake, pa Yohane 20:31, Baibulo limalongosola kuti: “Koma zalembedwa izi kuti mukakhulupirire kuti Yesu ndiye Kristu Mwana wa Mulungu.” Kukaikira konse ponena za chimene Tomasi angakhale anatanthauza kukuchotsedwa pano. Wolemba Baibulo Yohane wanena mowonekera bwino kuti Yesu ali Mwana wa Mulungu, osati Mulungu Wamphamvuyonse iyemwini.
Osati Wolingana ndi Mulungu
16. Kodi ndi kudzinenera kotani kumene Ayuda anapanga, ndipo ndimotani mmene Yesu anatsutsira iko?
16 Lemba lina limene matchalitchi amagwiritsira ntchito liri Yohane 5:18. Limanena kuti Ayuda anafuna kupha Yesu chifukwa chakuti “anatchanso Mulungu Atate wa iye yekha, nadziyesera wolingana ndi Mulungu.” Kodi ndani yemwe anali kunena kuti Yesu anali kudzipanga iyemwini wolingana ndi Mulungu? Si Yesu. Iye akuchichotsa icho kotheratu mu versi lotsatira lenilenilo (19) mwa kulongosola kuti: “Sakhoza mwana kuchita kanthu pa yekha, koma chimene awona Atate achichita ndicho.” Chotero Yesu sanadzinenere kuti anali Mulungu Wamphamvuyonse kapena wolingana ndi Iye. Iye anali kusonyeza Ayuda kuti iwo anali olakwa, kuti iye sanali Mulungu, koma kuti anali Mwana wa Mulungu, ndipo monga wolankhulira wa Mulungu iye sakakhoza kuchita pa iye yekha. Kodi tingayerekeze Mulungu Wamphamvuyonse wa chilengedwe kunena kuti sakakhoza kuchita chirichonse pa iye yekha? Chotero Ayuda anapanga lamulo, ndipo Yesu analitsutsa ilo.
17. (a) Kodi ndi umboni wowonekera bwino wotani kuchokera ku Mawu owuziridwa a Mulungu iyemwini onena za kuzindikiridwa kwa Yehova, Yesu Kristu, ndi mzimu woyera? (b) Kodi nchiyani chimene chifunikira kuchitidwa ndi lemba lirilonse limene Ophunzitsa Utatu angalozereko m’kuyesayesa kuyesera kulungamitsa chikhulupiriro chawo?
17 Chotero, kuchokera ku umboni wa Mulungu m’Mawu ake owuziridwa, kuchokera ku umboni wa Yesu, ndi kuchokera ku umboni wa ophunzira a Yesu, umboni wokhutiritsa umasonyeza mowonekera bwino kuti Mulungu Wamphamvuyonse ndi Yesu Kristu ali anthu aŵiri osiyana, Atate ndi Mwana. Umboni umenewo umasonyezanso mowonekera bwino kuti mzimu woyera siuli munthu wachitatu wa Utatu uliwonse koma mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu. Chiri chosalongosoka kuchotsa malemba m’tanthauzo lake lenileni kapena kuyesera kuwapotoza iwo kuti achirikize Utatu. Malemba alionse oterewa afunikira kugwirizanitsidwa ndi umboni wowonekera bwino wotsalawo wa Baibulo.
Nchifukwa Ninji Utatu Unakula?
18. Ndi kuti kumene chiphunzitso cha Utatu chinachokera?
18 Ngati mufufuza tsamba 18, “Kukula kwa m’Mbiri kwa Chiphunzitso cha Utatu,” mudzawona kuti Utatu uli ndi maziko achikunja. Iwo siuli chiphunzitso cha Baibulo, koma unatengedwa ndi Chikristu cha Dziko m’zana lachinayi. Komabe, nthaŵi yaitali chimenecho chisadakhale, panali mautatu mu Babulo wakale, Igupto, ndi malo ena. Chikristu cha Dziko chotero chinagwirizanitsa chikhulupiriro cha chikunja m’ziphunzitso zake. Ichi chinasonkhezeredwa ndi mfumu ya Roma Constantine, yemwe sanali wokondweretsedwa m’chowonadi ponena za nkhaniyi koma anafuna kulimbitsa ufumu wake wopangidwa ndi akunja ndi Akristu ampatuko. Kutalitali ndi kukhala kakulidwe ka chiphunzitso cha Chikristu, Utatu unali umboni wakuti Chikristu cha Dziko chinapatuka kuchoka pa ziphunzitso za Kristu ndipo m’malomwake chinatenga ziphunzitso zachikunja.
19. Nchifukwa ninji chiphunzitso cha Utatu chinakula?
19 Nchifukwa ninji chiphunzitso choterocho chinakula? Motsimikizirika, zikondwerero za Mulungu sizimatumikiridwa mwa kumpanga Iye, Mwana Wake, ndi mzimu Wake woyera kukhala osokoneza ndi chinsinsi. Ndipo sichimatumikira zikondwerero za anthu kukhala osokonezedwa. M’malomwake, kusokoneza kokulira kumene anthu amakhala ponena za Mulungu ndi zifuno zake, kumalinga bwino kwambiri Satana Mdyerekezi, wotsutsa wa Mulungu, ‘mulungu wa dziko lino,’ yemwe amagwira ntchito ‘kuchititsa khungu maganizo a osakhulupirira.’ (2 Akorinto 4:4) Popeza kuti chiphunzitso choterechi chimachipangitsa icho kuwoneka kuti kokha akatswiri a zaumulungu angamvetsetse ziphunzitso za Baibulo chimalinganso atsogoleri achipembedzo cha Chikristu cha Dziko. Ichi chimathandiza iwo kusungirira ulamuliro wawo pa anthu wamba.
20. (a) Kodi nchiti chomwe chiri chowonadi chosavuta chonena za Utatu? (b) Kodi nchiyani chimene kutenga chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi chomasula kumatanthauza kaamba ka ife?
20 Komabe, chowonadi chonena za nkhaniyi chiri chosavuta kotero kuti mwana angakhoze kuchimvetsetsa icho. Mnyamata wachichepere amadziŵa kuti sali wofanana ndi atate wake koma kuti iwo ali anthu aŵiri osiyana. Mofananamo, pamene Baibulo limanena kuti Yesu Kristu ali Mwana wa Mulungu, chimenecho ndi chimene ilo limatanthauza. Chimenecho chiri chowonadi chosavuta, pamene kuli kwakuti chiphunzitso cha Utatu sichiri tero. Icho chiri bodza. Chotero chifunikira kuyambitsidwa ndi “wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse.” (Chivumbulutso 12:9) Koma chowonadi chosavuta, chotsitsimula chonena za Mulungu, Mwana wake, Yesu Kristu, ndi mzimu woyera wamphamvu wa Mulungu chimamasula anthu kuchokera ku ukapolo wa chiphunzitso chonama chozikidwa mu chikunja ndi choyambitsidwa ndi Satana. Monga momwe Yesu ananenera kwa ofunafuna chowonadi owona mtima: “Mudzazindikira chowonadi, ndipo chowonadi chidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Kutenga chidziŵitso cholongosoka cha chowonadi chomasula, limodzinso ndi kugwirira ntchito pa icho, “kumatanthauza moyo wosatha.”—Yohane 17:3.
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Nchifukwa ninji chidziŵitso cholongosoka cha Mulungu ndi Mwana wake chiri chofunika motero?
◻ Kodi nchiyani chimene Yesu anatanthauza pamene ananena kuti, “ine ndi Atate ndife amodzi”?
◻ Ndimotani mmene Yohane 1:1 amasiyanitsira pakati pa Mawu ndi Mulungu?
◻ Nchifukwa ninji Tomasi moyenerera akanaitana Yesu “Mulungu wanga”?
◻ Kodi ndimotani mmene chiphunzitso cha Utatu chinayambira, ndipo kodi ndani amene ali mkonzi wake?
[Bokosi patsamba 18]
Kakulidwe ka m’Mbiri ka Chiphunzitso cha Utatu
The New Encyclopædia Britannica, 1985, Micropædia, Volyumu 11, tsamba 928, imanena pansi pa nkhani ya Utatu kuti: “Osati ngakhale liwu lakuti Utatu kapena chiphunzitso chenichenicho chimawoneka m’Chipangano Chatsopano, ndipo Yesu ndi ophunzira ake sanafune kutsutsa Shema m’Chipangano Chakale: ‘Imvani, Israyeli: Ambuye Mulungu wathu ali Mbuye mmodzi.’ (Deut. 6:4)” Encyclopedia imeneyi imanenanso kuti: “Chiphunzitsocho chinakula pang’onopang’ono mkati mwa mazana angapo ndipo kupyola matsutsano ambiri. . . . Bungwe la Nicaea mu 325 linalongosola njira yovuta kaamba ka chiphunzitso chimenecho m’kuvomereza kwake kuti Mwana ali ‘wa mkhalidwe umodzimodziwo . . . monga Atate,’ ngakhale kuti linanena zochepera kwenikweni ponena za Mzimu Woyera. . . . Podzafika kumapeto kwa zana la 4 . . . chiphunzitso cha Utatu chinatenga mkhalidwe wa tsatanetsatane womwe chinasungilira chiyambire pamenepo.”
New Catholic Encyclopedia, 1967, Volyumu 14, tsamba 299, ikuvomereza kuti: “Kupangidwa kwa ‘Mulungu mmodzi mwa Anthu atatu’ sikunakhazikitsidwe molimba, m’chenicheni sichinatengedwe mokhazikika m’moyo wa Chikristu ndi kulandira kwake kwa chikhulupiriro, asanafike mapeto a zana 4. . . . Pakati pa Abambo a Atumwi, panalibe chirichonse ngakhale choyandikira pang’onopang’ono malingaliro oterowo kapena kayang’anidwe.”
Chotero, chiphunzitso cha Utatu sichiri cha m’Malemba, koma chinatengedwa mwalamulo pa Msonkhano wa Nicaea m’chaka cha 325 C.E. Chiphunzitsocho chinagwirizanitsa lingaliro lachikunja lomwe linayambitsidwa kale kwambiri mu Babulo wakale ndi Igupto ndipo chidagwiritsiridwanso ntchito m’maiko ena. Katswiri wa mbiri yakale Will Durant anawona mu The Story of Civilization: Part III, tsamba 595: “Chikristu sichinawononge mkhalidwe wa chikunja; icho chinautenga uwo. . . . Kuchokera ku Igupto kunabwera malingaliro a utatu waumulungu.”
Mu An Encyclopedia of Religion, yolembedwa ndi Vergilius Ferm, mu 1964, pa masamba 793 ndi 794, pansi pa liwu lakuti “utatu,” pandandalitsidwa mautatu achiBabulo, achiBuddha, achiHindu, achiNorse, achiTaoist, ndi zipembedzo zina, kuphatikizapo zija za Chikristu cha Dziko. Monga chitsanzo, ilo limalongosola kuti mu India, “Utatu wokulira umaphatikizapo Brahma, Mlengi, Vishnu, Mpulumutsi ndi Shiva, Wowononga. Izi zimaimira zungulirezungulire wa kukhalako, monga mmene utatu wa ku Babulo wa Anu, Enlil ndi Ea umaimira zinthu zolengedwa, mphepo, madzi, dziko lapansi.”
British Museum ya ku London iri ndi zithunzi zamakedzana zomwe zimasonyeza utatu wakale, wonga ngati Isis wa ku Igupto, Harpokratēs, ndi Nephthys. Chofalitsidwa cha Gawo Losunga Zinthu Zamakedzana za Mazana Apakati ndi Zinthu Zakale chadziŵitsa zotsatirazi zomwe zinazokotedwa pa miyala yakale ya mtengo wapatali: “Kutsogolo [m’mbali], milungu ya ku Igupto Horus-Baït (wa mutu wa chiwombankhanga), Buto-Akori (njoka), ndi Hathor (wa mutu wa chule). Kumbuyo [m’mbali], versi la Chigriki ‘Baït mmodzi, Hathor mmodzi, Akori mmodzi; mphamvu ya amenewa iri imodzi. Thokozani, atate wa dziko, thokozani, mulungu wopangidwa ndi mbali zitatu!’ Chotero milungu ikuzindikiritsidwa monga kuwonetsera kutatu kwa mphamvu imodzi, mwinamwake mulungu wa dzuŵa.”
Mbiri imatsimikizira kuti Utatu unatengedwa kuchokera kwa akunja ndipo unalipo mazana angapo Yesu asanadze ku dziko lapansi. Nthaŵi yaitali pambuyo pa imfa yake, unachirikizidwa ndi awo omwe anasonkhezeredwa ndi nthanthi za kunja ndi omwe anapatuka kuchokera ku kulambira kowona kwa Mulungu kophunzitsidwa ndi Yesu ndi atumwi.
[Chithunzi patsamba 16]
Yesu anapemphera kaamba ka ophunzira ake kuti akhale amodzi m’malingaliro ndi m’chifuno monga mmene iye ndi Atate wake anali amodzi