Kulemekeza Dzina la Yehova mu Zisumbu za m’Nyanja
TANGOLINGALIRANI kudabwitsidwa kwa wofufuza amene pamene aponda phazi pa chisumbu “chosadziŵika” apeza mbendera ya kudziko lake kale pa malo owonekera. Kumayambiriro m’zana la 19, John Williams, chiwalo cha London Missionary Society, anakumana ndi kudabwitsidwa kofananako pamene anafika mu Rarotonga, chisumbu chaching’ono pa Zisumbu za Cook, kum’mwera kwa Pacific. Pa chisumbu chimenechi pamene anadzilingalira iyemwini kukhala woimira woyamba wa Chikristu cha Dziko, iye anapeza guwa la nsembe ku chilemekezo cha Yehova ndi Yesu Kristu. Mbiri ya maulendo ake a pa nyanja ya umishonale imapereka kulongosola kotsatiraku:
Zaka zina asanafike Williams’, mkazi anabwera kuchokera ku Tahiti ndipo anali atalankhula kwa nzikazo ponena za zozizwitsa zimene iye anawona m’dziko la kwawo. Iye analankhula za kukhala kwa anthu oyera otchedwa Cookees (otchulidwa pambuyo pa Captain Cook). Iye analongosola zida za chitsulo zimene iwo anagwiritsira ntchito m’malo mwa mafupa kudulira mitengo ndi kupangira mabwato ndi kupepuka kokulira ndi liŵiro. Koma iye anawauzanso kuti anthu oyera amalambira Mulungu Yehova ndi Yesu Kristu. Chotero mouziridwa, malume wa mfumu ya pa chisumbucho analingalira kumanga guwa la nsembe ndi marae zoperekedwa kwa iwo.a M’njira imeneyi, dzina laumwini la Mulungu linali patsogolo pa amishonale a Chikristu cha Dziko pa Zisumbu za Polynesia.
Yehova—Dzina Lotchuka Kumayambiriro
Pamene anayamba kuphunzitsa chipembedzo chawo kwa anthu a ku Polynesia, amishonale a Chikristu cha Dziko anapeza kuti milungu yambiri inali kulambiridwa pa zisumbu zimenezo. Kuti apewe kusokoneza kulikonse ndi milungu imeneyi, iwo anayamba kulozera kwa Mulungu Wamkulu ndi dzina lake m’malo mwa maina akuti Ambuye, Wosatha, kapena ngakhale Atua, liwu kaamba ka “Mulungu” m’zinenero zambiri za ku Polynesia. Chotero nzika za zisumbu zimenezo zinaphunzira kupemphera kwa Yehova, kugwiritsira ntchito dzina lake laumwini.
Pambuyo pake, matembenuzidwe oyamba a Baibulo anawoneka m’zinenero za kumaloko. Molongosoka mokwanira, iwo anagwiritsira ntchito dzina laumwini la Mulungu: Iehova mu chiHawaii, chiRarotonga, chiTahiti, ndi chiNiue; Ieova mu chiSamoa; ndi Ihowa mu Maori. Chodziŵika kwambiri koposabe, m’matembenuzidwe ambiri dzinalo linapezeka ngakhale m’Malemba a Chikristu a Chigriki (Chipangano Chatsopano).
Mbadwa zakale za Maori mu New Zealand zingakumbukirebe pamene dzina la Yehova linali kugwiritsiridwa ntchito mofala—makamaka pa marae. Pa zochitika zachifumu, kugwidwa mawu konga ngati “kuwopa Yehova chiri chiyambi cha nzeru” kunali mbali yoyambirira yolonjerera nduna zochezerazo. Mu Polynesia monse, dzinalo linali kugwiritsiridwa ntchito mwaufulu pa misonkhano ya tchalitchi. Kufikira ku tsiku lino, achikulire ali ozolowerana ndi dzina la Mulungu m’chinenero chawo. Ngakhale kuli tero, ichi sichiri chowona kwa mibadwo yocheperapo yambiri, imene yachoka ku njira ya mwambo ya moyo.
Zoyesayesa za Kutsendereza Dzinalo
M’kupita kwa nthaŵi, unyinji wa matembenuzidwe a chiPolynesia analembedwanso. Monga mmene zinachitikira ndi kulembedwanso kosiyanasiyana kopangidwa mu Europe ndi North America, amodzi a masinthidwe a akulu anali kuchotsedwa kwa dzina la Yehova (kapena zina za zofanana nazo zake koposa). Chotero, ilo linalowedwa m’malo ndi Alii (Ambuye) m’malembedwe olembedwanso a Baibulo la chiSamoa limene linawoneka mu 1969, ndipo kulembedwanso kofananako kunakonzekeretsedwa mu chiNiue.
Zowona, nzika za mu Polynesia sizinali kulambiranso milungu yawo kapena mafano monga mmene zinali kuchitira kale, ndipo osatinso Io wa Hidden Face, mulungu wapamwamba wa anthu a mtundu wa Maori. Koma kodi chimenecho m’njira iriyonse chimavomereza atembenuzi a Baibulo kuchotsa Mulungu wa Baibulo ku kusatchulidwa dzina mwakulowetsa m’malo dzina lake ndi dzina la ulemu chabe? Kodi dzina limeneli liri losafunika kwambiri lerolino? Ndithudi ayi, popeza Yesu iyemwini, m’pemphero la chitsanzo, anaphunzitsa ophunzira ake kupempherera choyamba cha zonse kuyeretsedwa kwa dzina limenelo.b
Mtetezi wa Dzinalo
Mosasamala kanthu za zochitika za posachedwapa zimenezi, dzina la Yehova siliri pafupi kuzimiririka mu Polynesia. Chifukwa ninji ayi? Chifukwa, mofanana ndi m’maiko ena onse, Mboni za Yehova mokhazikika zimachezera nzika za zisumbu zimenezi ndi cholinga chofuna kudziŵitsa dzina limenelo kwa iwo. Pakali pano Mboni zoposa 16,000 m’mbali imeneyi ya dziko zikutenga mbali mu ntchito yofunika kwambiri imeneyi, ndipo zikusonyeza kwa anthu anzawo kufunika kwa kukhala ndi chidziŵitso cholongosoka cha Mawu a Mulungu ndi kuika chidziŵitso chimenecho m’kugwiritsira ntchito. Chimenecho ndicho chimene chimatanthauza kulambira Mulungu ndi kuyeretsa dzina lake.—Yohane 4:21-24.
[Mawu a M’munsi]
a Marae poyambirira anali malo otsekeredwa opatulika ogwiritsidwa ntchito kaamba ka chipembedzo ndi zifuno za mayanjano. Lerolino iwo mofala amalozera ku malo osonkhanira a fuko.
b Pemphero la chitsanzo lophunzitsidwa ndi Yesu kwa ophunzira ake (kaŵirikaŵiri lotchedwa Atate Wathu) limayamba ndi mawu awa: “Atate Wathu wa kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.”—Mateyu 6:9.
[Mapu patsamba 14]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
Hawaii
Samoa
Niue
Tahiti
Rarotonga
New Zealand
[Zithunzi patsamba 15]
Tutuila, American Samoa
Nyanja ya Gunn, New Zealand
Savaii, Western Samoa
Gombe la Avatele pa Niue