Yehova Wakhala Pothaŵirapo Panga ndi Linga Langa
Monga momwe yalongosoledwa ndi Margaret West
TANGOLINGALIRANI kukhala m’nyumba yachifumu pamene Mfumukazi Anna Sophie wa ku Denmark anavekedwa chisoti chaufumu mu chaka cha 1721. Nyumba yokhalako ya nthaŵi ya chirimwe imeneyi ya banja lachifumu la chiDanish, yokhala mkati mwa minda ya maluŵa okongola, inali nyumba yanga ya ku ubwana. Zipinda zokongolazo, makwerero osaiwalika, denga lopakidwa utoto ndi akatswiri akale a chiFrench, inawonekera panthaŵiyo monga zinthu zomwe zinapanga maloto.
Kokha kuyenda kwakufupi kuchoka panyumba yachifumuyo kunali chimango china, chowoneka bwino mokulira, koma zaka zanga 30 m’chimango chimenechi zinalemeretsa moyo wanga mokulira. Iyo inali Beteli ya chiDanish, ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova mu Denmark.
Koma choyamba ndiloleni ndikuwuzeni mmene ndinafikira kudzakhala mu Frederiksberg Castle mu Copenhagen. Atate wanga, mkulu wankhondo mu gulu lankhondo la chiDanish, anatsogoza sukulu yapamwamba ya nkhondo imene malikulu ake anali m’nyumba yachifumuyo. Malo amenewa anawayeneretsa iwo ndi banja lawo kukhala m’malo a mwaŵi amenewa. Kwa mtsikana wachichepere, uwu unali moyo wamaloto, wotetezeredwa kuchokera ku zovulaza mkati mwa zochingirira za makhazikitsidwe okongola amenewa. Ndinaganiza kuti masiku achimwemwe, osangalatsa amenewa sakatha nkomwe. Koma loto limeneli linathetsedwa tsiku limodzi losaiwalika mu 1921.
Anafe tinaitanidwa ku chipinda chogona cha atate. Ndinawona iwo atagona potero, akuwoneka oyera kwambiri, manja onse aŵiri ali pamwamba pa nsalu yofunda. Amayi anaika mikono yawo motizungulira. Dokotala wathu, yemwe analinso pambali pa kama, anawoneka wachisoni kwambiri. Amayi ananena mu liwu lotsika kuti: “Atate amwalira.” Lingaliro langa loyamba linali lakuti: ‘Chimenecho nchosatheka! Iwo sanadwale nkomwe.” Chinali chokumana nacho cha kuswa maganizo kwa mwana wa zaka khumi. Ndinazindikira zochepa kuti imfa yadzidzidzi imeneyi ikanditsogoza ine ku kumvetsetsa chifuno cha moyo.
Imfa ya Atate inatanthauza kusintha kokulira m’miyoyo yathu. Nyumba yachifumuyo inali malo okhalako a ntchito, chotero Amayi anayenera kupeza malo ena kaamba ka ife kukhalako. Inali nthaŵi yovuta, ndipo kuti atithandize ife kulaka ngoziyo, iwo anachita chinachake chomwe chinadabwitsa banja lathu ndi mabwenzi. Iwo anatichotsa ife ku sukulu, ndi kuyamba kuyendera Europe kwa chaka chathunthu.
Kufunafuna Kwafupidwa
Titabwerera kumudzi mu Denmark, ngakhale kuli tero, imfa ya Atate inali idakalibe pa ife, ndipo Amayi anapitiriza kudzifunsa iwo eni, nthaŵi ndi nthaŵi, Nchifukwa ninji? Nchifukwa ninji? Nchifukwa ninji? Ndi cholinga chofuna kupeza yankho, iwo anayamba kufufuza mu nthanthi za Kum’mawa, koma izi sizinakhutiritse maganizo awo anzeru. Kenaka analingalira za kutembenukira ku Baibulo, akumaganiza kuti ligakhale ndi mayankho ena. Pamene ankafuna kutenga Baibulo pa shelufu ya mabukhu, iwo anawona bukhu lofiira pambali pake, bukhu limene anali asanaliwonepo. Ilo linali kutchedwa The Divine Plan of the Ages. Mbale wanga anali atangoligula ilo kuchokera kwa Wophunzira Baibulo yemwe anafikira ife.
Amayi anayamba kuŵerenga bukhulo ndipo mwamsanga anakhutiritsidwa kuti anapeza mayankho ku mafunso awo. Pa nthaŵi imeneyi, ndinali kupezeka ku sukulu mu France, koma pamene ndinabwerera kunyumba pa tchuthi miyezi ingapo pambuyo pake, Amayi motenthedwa maginizo anadiwuza ine ponena za chuma chawo chopezedwa chatsopano. Iwo anandiwuza ine ponena za Ufumu wa Mulungu—Ufumu womwe ukalamulira dziko lonse lapansi ndi kuika kumapeto nkhondo zonse, Ufumu womwe ukabweretsa madalitso osaneneka kwa mtundu wa anthu, kuphatikizapo kuwukitsidwa kwa akufa. Chinali chozizwitsa. Ife potsirizira pake tinapeza pothaŵirapo kuchokera ku kukaikira ndi kusatsimikizirika.
Madzulo amenewo pamene ndinapita kukagona, ndinapemphera kwa nthaŵi yoyamba m’moyo wanga. Tinali tisanakhalepo banja la chipembedzo, koma m’sukulu tinaphunzitsidwa Pemphero la Ambuye. Chotero mofulumira ndinayamba kubwereza pemphero limeneli. Pamene ndinafika ku mawu akuti, “Ufumu wanu udze . . . ,” mtima wanga unatsala pang’ono kusweka chifukwa cha chikondwerero. Pomalizira ndinamvetsetsa chomwe ndinali kupempha! Zaka makumi asanu ndi limodzi zapita, koma ndimakumbukirabe mowonekera bwino chimwemwe chosalongosoleka chomwe ndinachimva usiku umenewo.
Pambuyo pa kumaliza kuphunzira kwanga mu France, ndinapita ku England kwa chaka chimodzi kukazolowera Chingelezi changa. Amayi anawumiriza kuti: “Mtsikana ayenera kuphunzira zinenero, mnyamata masamu.” Pomalizira pake, ndinaphunzira zinenero zisanu, zonse zimene zakhala zothandiza koposa, ndipo m’zaka za pambuyo pake nthaŵi zonse ndayamikira Amayi chifukwa chondipatsa mwaŵi umenewu.
Pamene ndinafika mu England, ndinapeza kuti Amayi anali ataika bukhu la Zeze wa Mulungu mu sutikesi yanga. Ndinaphunzira ilo mosamalitsa ndi kuyamba kuchitira umboni za zimene ndinaphunzira kwa banja la Chingelezi lomwe ndinali kukhala nalo. Wachibale wa banja limenelo anachezera nyumbayo pa nthaŵi ina, chotero ndinachitira umboni kwa iye. (Ndinali kukhala waluso lokwanira pa ‘kuseŵera zingwe khumi’ za “zeze” ameneyu.) Popeza mkazi ameneyu anafuna bukhu la iyemwini, ndinalembera ofesi ya nthambi ya London ya Watch Tower Society, ndipo ananditsogoza ine kwa abale a kumaloko.
Chotero ndinayamba kuyanjana ndi gulu laling’ono limeneli mu Wickford, Essex, lomwe linakumana m’nyumba ya mmodzi wa Ophunzira Baibulo. Pa msonkhano wina, chinalengezedwa kuti Sande yotsatira pakakhala “ulendo wopita kunja,” ndipo ndinaitanidwanso. Ndinayang’ana kutsogolo ku ulendo wakunja wosangalatsa m’malo a kumidzi a kumaloko, koma pamene ndinafika, pemphero linanenedwa, ndipo ndinapatsidwa mabukhu ena ndi kutumizidwa ndi mlongo wachikulire kukalalikira!
Pambuyo pobwerera ku Denmark, ndinapitiriza kuyanjana ndi Ophunzira Baibulo, ndipo mu 1929 ndinabatizidwa. Chokumana nacho chosaiwalika chinali msonkhano mu Copenhagen mu 1931. Panali pa msonkhano umenewu pamene tinatenga dzina lakuti Mboni za Yehova. Ndi cholinga chofuna kudziŵitsa olamulira za ichi, nkhani ya Mbale Rutherford ndi chigamulo chotsatirapo chotengedwa pa msonkhano umenewo zinafalitsidwa mu kabukhu kakuti The Kingdom, the Hope of the World. Tinayenera kulipereka ilo mwaumwini kwa anthu onse odziŵika m’mudzimo, kuphatikizapo oweruza, ziwalo za boma, amuna otchuka amalonda, ndiponso kwa atsogoleri a chipembedzo onse.
Mkazi Wamng’ono ndi Bishopu
Mfumu ya Denmark inalandira kope lake m’khamu lomwe linaperekedwa kwa woyang’anira nthambi. Ndinapatsidwa mulu wa timabukhu, limodzi ndi maenivulupu omwe anali ndi maina ndi makeyala a anthu omwe ndinayenera kuwachezera m’ndawalayi. Dzina loyambirira pa ndandandayo ndithudi linandidabwitsa ine. Anali bishopu wotchuka wa Lutheran yemwe anali wodziŵika bwino kaamba ka chitsutso chake cha Mboni za Yehova.
Bishopuyo ankakhala mu mbali yotchuka ya Copenhagen, ndipo pamene ndinaliza belu, ndiyenera kuvomereza kuti ndinadzimva wochepera kuposa msinkhu wanga waung’ono wa mita imodzi ndi theka. Mtsikana wantchito anatsegula chitseko, kundiyang’ana ine mokweza ndi motsitsa mokaikira, ndi kufunsa kuti: “Nchiyani chimene ukufuna, chonde?” “Zikomo, ndikufuna kulankhula ndi bishopu,” ndinayankha tero mwamphamvu. Amayi anandibwereka ine khoti yokongola ya astrakhan kaamba ka chochitikacho, ndipo mwinamwake ichi chinakhutiritsa mtsikana wantchitoyo kuti chifunsiro changa chiyenera kuperededwa, popeza kuti pambuyo pa kupuma kotalikira komwe kunawoneka kukhala ngati kosatha, iye ananena kuti: “Dikira kamphindi kokha.” Mwamsanga iye anabwerera ndi kundiloŵetsa ine kupyola korido yaitali, kutsegula chitseko, ndipo kumeneko kumbuyo kwa desiki lalikulu panakhala bishopuyo. Iye anali mwamuna wamtali, wodzinzana. Iye anayang’ana mmwamba ndi kumwetulire kwa ine mwachiyanjo.
Ndinadzikumbutsa inemwini kuti Amene ali kumbuyo kwanga anali wokulira kuposa amene anali kutsogolo kwanga, ndinalongosola kwa iye chifuno cha kuchezera kwanga, ndi kumpatsa iye enivulupuyo. Iye anaitenga iyo ndipo kenaka kuiponya pa desiki ngati kuti inali pamoto. Iye analumpha, kugwira dzanja langa, ndi kundiyendetsa ine chafutambuyo mukorido yosathayo kupita ku chitseko cha kutsogolo. Chitsekocho chinatsekedwa momenyetsa, koma ndinamwetulira kwa inemwini. Kabukhuko kanali pa desiki lake; ntchito yanga inachitidwa.
Mu 1933 ndinayamba kuchita upainiya, popeza ndinadzimva kuti inali njira yoyenera ya kutumikira Yehova mokwanira. Chaka chimodzi pambuyo pake ndinakwatiwa ndi Mbale Albert West, mbale wa Chingelezi yemwe anagawiridwa gawo ku Denmark zaka zingapo kumayambiriro. Tonse pamodzi tinatumikira mu Beteli ya chiDanish kwa zaka 30.
Kutenga Dziko kwa Nazi
April 9, 1940, linali tsiku limene sindidzaiwala nkomwe. Ndinadzutsidwa pa ora lachisanu ndi chimodzi ndi kumveka kwa kuwuluka kokhazikika kwa ndege yomwe inawoneka kukhala ikuwuluka mwachindunji pa mutu panga. Nchiyani chomwe chinali kuchitika? Denmark linali dziko la uchete. Kunja, anthu anali kusonkhana m’makwalala, mphekesera zinafalikira, mkhalidwe wa malo unali wokwinjika. Kenaka wailesi inalengeza kuti: “Denmark yatengedwa ndi magulu ankhondo a chiGerman.”
Vuto la mwamsanga linali chomwe tidzachita ndi mabukhu onse omwe anasungidwa m’chimangocho. Abale mu Copenhagen anasonyeza chidziŵitso chapasadakhale chozizwitsa ndi kuchenjera. Mwamsanga mabukhuwo anagawiridwa kwa abale a kumaloko, ndipo zolembera za nthambi zinasungidwa mwachisungiko ndi mlongo wogalamuka wachikulire, yemwe anaziika izo pansi pa kama yake kwa nyengo yonse ya nkhondo.
Vuto lina linali chomwe tikachita ndi timabukhu 350,000 tomwe tinangofika kumene. Chinalingaliridwa kuwagawira iwo mwamsanga. Sindikanakhulupirira nkomwe kuti ndinakwera makwerero ambiri mu kokha masiku aŵiri. Zonsezi zinachitidwa popanda kudzutsa chikaikiro cha ankhondo a chiGerman omwe anali kulonda makwalala. Pamene iwo anadutsa, tinayesera kuwapatsa iwo chisonyezero chakuti tinali kuwona zinthu zogula m’mazenera. Abale onse, ponse paŵiri achichepere ndi achikulire, anagawanamo m’kugawira kwa mwamsanga kumeneku, ndipo kuwukira kwa mumlengalenga kwa maora 48 kutapita, timabukhu tonse tinali m’manja a unyinji.
Ndi kuloŵererako, kugwirizana konse ndi malikulu ku Brooklyn kunatsekedwa, koma zopereka za chakudya chauzimu sizinaume. Panali mbale mmodzi kapena aŵiri amene anali kugwira ntchito mu utumiki wa nthumwi, ndipo katundu wawo sanali kufufuzidwa. Pamene iwo anapanga maulendo okhazikika ku Sweden, iwo anali okhoza kutibweretsera Nsanja ya Olonda mu chiSwedish. Ndinali ndi chidziŵitso china cha chiSwedish, chotero ndinagawiridwa ntchito ya kutembenuza kope lirilonse mu chiDanish. Chitokoso chowopsya, koma ndinakhala wotanganitsidwa kuphunzira zochulukira monga momwe ndikanathera. Mwa njira imeneyi, tinali ndi chopereka chokhazikika cha Nsanja ya Olonda mkati mwa chaka chonse.
M’chenicheni, tinali ngakhale okhoza kutumiza makope ena a chiDanish kwa abale athu mu Norway. Makatoni a mazira otumizidwa kaamba ka nduna za chiNazi anali kutumizidwa mokhazikika kuchokera ku Denmark kupita ku Norway. Tinali okhoza kumanga mazirawo m’masamba a magazini ya Nsanja ya Olonda ya chiDanish, imene abale a ku Norway mosamalitsa anachotsa asanapereke mazirawo kwa a German amenewo.
Chokumana Nacho Chachilendo
Mkati mwa nkhondo, Mbale Eneroth, yemwe anali mtumiki wa nthambi mu Sweden, anapeza chilolezo cha kuchezera Denmark, ndipo Albert anapita ku doko kukakumana naye. Pamene Mbale Eneroth anatsika kuchoka pa makwerero a sitima ya m’madzi, nduna ziŵiri za chiGerman zinawonekera ndi kufunsa Albert ndi Mbale Eneroth kutsagana nawo.
Iwo anatengedwa kupita ku Hotel Cosmopolite, imodzi ya malikulu a nkhondo a gulu lankhondo la chiGerman, ndipo anaperekezedwa ku ofesi panyumba yachiŵiri ya pamwamba, kumene analandiridwa ndi m’German wovala zovala wamba. Akumalankhula nawo m’Chingelezi chabwino, iye ananena kuti: “Monga mmene mukudziŵira, pali nkondo yomwe ikupitirizabe. Ndine mwamuna wa zamalonda wochokera ku Hamburg, ndipo ndagawiridwa kubwera kuno monga wofufuza. Ndikufufuza zolembera zonse za Watchtower Bible Society [pakati pa Denmark ndi Sweden]. Chiri chinachake chomwe chiri chotsutsana nane, koma ndiribe chosankha. Lolani kuti ndikuyamikireni m’zolembera zanu, zomwe ziri zowona mtima ndi zosangalatsa kuŵerenga. Simungalingalire chinyengo chomwe ndimapeza m’makalata a makampani ena.”
Iye anafunsa abalewo. “Kodi kubwereza mopitapita nchiyani?” Albert anapitiriza kupereka chisonyezero chachifupi cha kubwereza mopitapita, kapena ulendo wobwereza, akumagwiritsira ntchito Mbale Eneroth monga mwininyumba wake. Ndunayo kenaka inamaliza kufunsako, ndi kunena kuti: “Zikomo, amuna inu, chimenecho ndicho chimene ndinafuna kudziŵa.” Mwinamwake iyi inali njira yake ya kuchenjezera abalewo kukhala osamalitsa ponena za zimene amaika m’makalata awo.
Chiitano Kupita ku Gileadi
Kumapeto kwa 1945, tinalandira ulendo wolandirika kwambiri kuchokera kwa Abale Knorr ndi Henschel. Mkati mwa kuchezera kumeneku, Albert ndi ine tinaitanidwa kupita ku Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower, ndipo tinapezeka ku kalasi la 11 la sukulu ya amishonale imeneyi mu 1948. Pambuyo pa kuphunzitsidwa kwathu kwa Gileadi, ndinatumikira ndi mwamuna wanga yemwe anagawiridwa m’ntchito yadera kwa miyezi isanu ndi umodzi mu Maryland, Virginia, ndi Washington, D.C., tisanabwerere ku Denmark.
Zaka zingapo pambuyo pake, Albert anadwala, ndipo matenda ake potsirizira pake anasonyezedwa kukhala kansa. Ndinamusamalira iye kwa zaka khumi pamene ndinali kuchita zomwe ndikanatha monga wotembenuza, kufikira iye anamwalira mu 1963. Chaka chotsatira, ndinayang’anizana ndi thayo lina lolilingalira. Amai anga tsopano anali ndi zaka 88 zakubadwa ndipo anafunikira winawake wowasamalira. Chotero, moipidwa, ndinayenera kusiya utumiki wa nthaŵi zonse. Amayi anakhala ndi moyo kufikira anali ndi zaka 101 ndi kupitirizabe okhulupirika kufikira kumapeto.
Kuleka Ntchito Kotanganitsidwa
Mkati mwa zaka zomalizira za moyo wa amayi anga, tinathera miyezi ya nyengo ya chisanu mu Spain. Chotero pamene iwo anamwalira, ndinagamulapo za kukhala kumeneko. Ndinali ndinaphunzira chiSpanish ndipo ndinadzimvanso kuti mwanjira imeneyi ndidzakhala ndikutumikira m’dziko lachilendo. Ngakhale kuti sindingachite zambiri monga momwe ndingafunire, chifukwa cha msinkhu wanga ndi mathayo ena, ndidakali wokhoza kuchita upainiya wothandizira pa maziko okhazikika.
Zoposa zaka 20 za moyo wanga zinawonongedwa ndikuyang’anira mwamuna wanga wodwala ndi amayi anga okalamba. Ngakhale kuli tero, sindinayang’ane pa ichi kukhala cholemetsa. Nthaŵi zonse ndinadzimva kuti onse aŵiri anafunikira chisamaliro choterocho ndi kulingaliridwa, ndipo ndinawona icho monga mbali ya utumiki wanga kwa Yehova, yemwe nthaŵi zonse anandithandiza ine kuyang’anizana ndi chisoni ndi ziyeso zomwe zinayenera kupiriridwa pansi pa mikhalidwe yoteroyo.
Tsopano ndimakhala m’nyumba yaing’ono, yosiyana kwambiri ndi nyumba yachifumu yosangalatsa kumene ndinabadwira. Koma zimango sizingapereke nkomwe chisungiko, monga mmene ndinapezera kumayambiriro m’moyo. Ku mbali ina, ndinapeza pothawirapo papakulu ndi linga, pamodzi pomwe sipanandilepheretse ine nkomwe. Ndinganenedi mowona mtima, monga momwe ananenera wamasalmo kuti: “Pothawirapo panga ndi linga langa, Mulungu wanga, amene ndimukhulupirira.”—Salmo 91:2.