Mungapeze Chuma cha Mtengo Wake!
“KODI mukuwona chirichonse?” anafunsa tero mwamuna Wachingelezi wachuma. “Inde, zinthu zokongola,” anayankha tero katswiri wa mbiri yakale ya Igupto. Chakacho chinali 1922, ndipo Howard Carter anali atangosunzumira m’manda a Farao Tutankhamen mu Chigwa cha Igupto cha Mafumu. Chisangalalo chinadzadza mawu a Carter akuti:
“Pamene maso anga anazoloŵera kuwona kuwunikako, zinthu za m’chipinda mkatimo zinawonekera pang’onopang’ono kuchoka m’chizimezime, nyama zachilendo, zowumba, ndi golidi—paliponse panali kunyezimira kwa golidi. Kwa kanthaŵiko—chinayenera kukhala zochulukira kosatha kwa ena oimirira pambali—ndinalibe mawu chifukwa cha kudabwitsidwa . . . Sitinaganizepo nkomweza chirichonse chonga ichi, chipinda chodzadza—inawoneka monga nyumba yathunthu yosungiramo zinthu zakale—ya zinthu.” Carter movomereza anachimva “chiyembekezo chomangika . . . cha wofunafuna chuma.”
Kupeza kumeneko kunavumbula chuma chachikulu chobisika zaka zoposa 3,000 zapitazo. Koma Mulungu akufuna ife kudzilowetsa m’kusaka chuma kokulira. Kuli kufufuza kokulira kopatsa mphoto kwenikweni kuposa kufufuza kwina kulikonse kaamba ka miyala ya mtengo wapatali, golidi, kapena siliva. Kusaka chuma kumeneku kuli kaamba ka nzeru yaumulungu, ndipo chimodzi cha mapindu ake a mtengo wapatali koposa chiri moyo wosatha.—Yohane 17:3.
Kuyesayesa Nkofunika
Kuyesayesa kokulira kuli kofunika kukumba malo a zofotseredwa pansi zakale. Sichiri chopepuka kukumba malo osalambulidwa kapena kulowa m’madzi owopsya kwambiri m’kufunafuna chuma chobisika, chokwiriridwa, kapena chomira. Koma ofunafuna chuma owona mtima mwachikondwerero amapanga kuyesayesa kotero. Iwo kaŵirikaŵiri amapirira kuvutika kowopsya ndi mavuto amene angawoneke kukhala zopinga zosathekera. Chabwino, kodi kufufuza kaamba ka chuma cha nzeru yaumulungu sikuli koyenerera ngakhale kuyesayesa kokulirapo?
Tingapeze chuma cha mtengo wake ngati tiika kuyesetsa kofunikira kuphunzira Baibulo ndi zofalitsidwa zowona Zachikristu chowona zolinganizidwa kutithandiza ife kupeza miyala ya mtengo wapatali ya nzeru imene zirinayo. Kuyesayesa kopitirizidwa nkofunika. Sitingakhale olemera ngati tinayamba kukumba kaamba ka chuma cha kuthupi koma kuleka pambuyo pa kungopalasa pamwamba. Chofananacho chingakhale chowona ngati tiyamba kukumba kaamba ka chuma chauzimu ndipo mwamsanga kuleka chifukwa tinaganizira kuti chinali chotopetsa kupitiriza. “Nzeru yochokera kumwamba” iri kaamba ka awo omwe akuzikakamiza iwo eni kuipeza iyo. (Yakobo 3:17) Kodi simuyenera kupanga kuyesayesa kofunikira kupeza chuma cha mtengo wake cha nzeru yaumulungu?
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Chithunzi cha pa chikuto ndi cha pa tsamba 3: K. Scholz/H. Armstrong Roberts