Chipembedzo ndi Chinazi
“Hitler . . . anali ndi Chikatolika monga Wolamulira Wachiwiri ndipo mwachangu kuchokera pa tsiku loyamba la kulamulira Franz von Papen anakhala chandamali cha kukoka chisamaliro cha magawo a Chikatolika kuti achilikize Ulamuliro watsopano. Mu mbali iriyonse ya Ulamulirowo von Papen anayenera kumvedwa akulangiza okhulupilika kupereka chimvero kwa Adolf Hitler.”
“Ku chiyambi cha 1933 chilengezo cha lamulo chotstirachi chinapangidwa ndi bungwe lochilikiza la kachitidwe ndi kulingalira kwa Chikatolika mu Germany, pa nthaŵwiyo lotsogozedwa ndi [Franz] von Papen: ‘Ife Akatolika a mu Germany tidzaima, ndi miyoyo yathu yonse ndi kukhutiritsidwa kwathu kotheratu, kumbuyo kwa Adolf Hitler ndi Boma lake. Timazizwa pa chikondi chake kaamba ka dziko la makolo, nyonga yake ndi nzeru zake za umuna. . . . Chikatolika cha ku Germany . . . chiyenera kutenga mbali yokangalika m’kumangilira Ulamuliro Wachitatu.’”
Franz von Papen anali chiwiya m’kufikira chimvano pakati pa boma la Nazi limene iye anatumikira mu Germany ndi Vatican mu Roma. Chimvano chinasainidwa July 20, 1933. Ndemanga yapadera inalongosola kuti: “Cardinal ndi Mlembi wa Boma Pacelli [pambuyo pake yemwe anadzakhala Papa Pius XII] lero waika pa Wolamulira Wachiŵiri von Papen, Mtanda Waukulu wa Lamulo la Pius . . . Wolamulira Wachiŵiri von Papen wapereka kwa Cardinal Mlembi wa Boma Madonna ya White Meissen Porcelain monga mphatso ya Ulamuliro wa Boma. . . . Mphatso zonse zimachitira umboni kudzipereka: ‘A memento of the Reich Concordat (Chikumbukiro cha Chimvano cha Ulamuliro) 1933.’”—Kugwidwa mawu konse kunatengedwa kuchokera mu Franz von Papen—His Life and Times, lolembedwa ndi H. W. Blood-Ryan.