Kusonyeza Chikondi ndi Ulemu Monga Mkazi
“Mkazi ayenera kukhala ndi ulemu wakuya kaamba ka mwamuna wake.”—AEFESO 5:33, “NW.”
1. Ndi mafunso otani amene amabuka ponena za mkhalidwe wamakono wa ukwati?
MU NYENGO yamakono ino ya kudziimira pawokha ndi “ufulu,” kawonedwe kamwambo ka ukwati kavutika ndi kukantha koipitsitsa. Mamiliyoni angapo a mabanja akhoza kugwira ntchito pamene akusowa atate kapena amayi. Kukhala pamodzi popanda phindu la ukwati walamulo kwakhala mwambo wa ambiri. Koma kodi ichi chatsogolera ku chisungiko chokulira kwa mkazi ndi amayi? Kodi kwapereka kukhazikika kwa ana? Ndipo kodi kunyonyotsoka kwa mapindu kumeneku kwatsogolera ku ulemu wokulira mkati mwa kakonzedwe ka banja? Mosiyanako, nchiyani chimene Mawu a Mulungu amayamikira?
2. Nchifukwa ninji sichinali chabwino kaamba ka Adamu kupitirizabe yekha?
2 Pamene Mulungu analongosola cholinga chake cha kupanga mkazi woyambirira, iye analongosola kuti: “Sikwabwino kuti [mwamuna, NW] akhale yekha.” Ndipo pambuyo pakuwona mabanja a nyama—zazimuna ndi zazikazi ndi ana awo—kudzimva kwa Adamu kuyenera kukhala kunali kogwirizana ndi ndemanga imeneyo. Ngakhale kuti anali wangwiro ndipo wokhala mu paradaiso yokhutiritsa, Adamu anasoŵa ubwenzi ndi winawake wa mtundu wake. Iye anali ndi mphatso ya luntha ndi kulankhula, koma panalibe cholengedwa china cha mtundu wake chimene akagawana nacho mphatso zimenezo. Komabe, mkhalidwewo mwamsanga ukakhala wosiyana, popeza kuti Mulungu ananena kuti: “Ndidzampangira [womthandizira monga, NW] womthangatira iye.”—Genesis 2:18-20.
3. (a) Ndimotani mmene Hava analiri wa “mtundu” wa Adamu? (b) Nchiyani chimene chimatanthauza “kudziphatika” kwa mwamuna kwa mkazi wake?
3 Yehova anapanga mkazi Hava mwa kugwiritsira ntchito imodzi ya nthiti za Adamu monga maziko. Chotero, Hava anali wa “mtundu” umodzimodziwo monga Adamu. Iye sanali nyama yotsika koma anali “fupa la mafupa [ake] ndi mnofu wa minofu [yake].” Mogwirizanamo, cholembera chowuziridwa chimanena kuti: “Chifukwa chotero mwamuna adzasiya atate wake ndi amake nadzadziphatika kwa mkazi wake: ndipo adzakhala thupi limodzi.” (Genesis 2:23, 24) Liwu la Chihebri lotembenuzidwa “kudziphatika” m’chenicheni limatanthauza “kugwirira, kumamatira, makamaka zolimba, monga ngati ndi ulimbo.” (Hebrew and Chaldee Lexicon to the Old Testament Scriptures ya Gesenius) Ichi nidthudi chimalongosola lingaliro la mwamuna ndi mkazi kukhala mabwenzi osapatukana. Wophunzira wina akunena kuti “chimalozera kuposa pa kuyanjana kwa kugonana kwa mwamuna ndi mkazi ndipo kumafutukukira ku unansi wonsewo.” Chotero, ukwati suli chosangalatsa chosakhalitsa. Uli unansi wosatha. Ndipo pamene pali kulemekeza kwakuya ndi ulemu, umodzi umenewo, ngakhale kuti umatsenderezedwa pa nthaŵi zina, uyenera kukhala wosasweka.—Mateyu 19:3-9.
4. Ndi m’lingaliro lotani mmene mkazi anali wothandiza ndi wothangatira wa mwamuna?
4 Mulungu ananena kuti mkazi akakhala wothandiza ndi wothangatira wa mwamuna. Popeza kuti anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, iye akawayembekezera kuwonetsa mikhalidwe yake—chilungamo, chikondi, nzeru, ndi mphamvu—mu unansi wawo wina ndi mnzake. Chotero, Hava akakhala “wothangatira,” osati wopikisana naye. Banja silikakhala ngati chombo chokhala ndi oyendetsa aŵiri opikisana, koma umutu ukasonyezedwa ndi Adamu.—1 Akorinto 11:3; Aefeso 5:22-24; 1 Timoteo 2:12, 13.
5. Ndimotani mmene amuna ambiri achitira ndi akazi, ndipo kodi ichi chiri ndi kuvomereza kwa Mulungu?
5 Ngakhale kuli tero, kupanduka ndi chimo la anthu aŵiri oyambirira motsutsana ndi umutu wachikondi wa Mulungu zinayambitsa makhazikitsidwe osiyana kaamba ka kupangidwa kwa banja lawo ndi mabanja onse a mtsogolo. Ndi chidziŵitso chapasadakhale cha zotulukapo za chimo lawo ndi chiyambukiro chake pa mtundu wa anthu, Yehova anati kwa Hava: “Udzakhumba mwamuna wako, ndipo iye adzakulamulira iwe.” (Genesis 3:16) Mwatsoka, mkati mwa mazana amuna ambiri alamulira akazi mu mkhalidwe wankhalwe. Akazi akhala ndipo adakali kuchepetsedwabe ndi kunyalanyazidwa m’njira zambiri m’dziko lonse. Komabe, monga momwe tawonera mu nkhani yapitayo, kugwiritsira ntchito maprinsipulo a Baibulo sikumapereka maziko aliwonse a kutsendereza kotheratu kwa amuna. Kumbali ina, iko kumagogomezera phindu la ulemu wakuya.
Ulemu Wakuya—Chitokoso
6, 7. (a) Ndimotani mmene amuna osakhulupirira angakodwere ndi chowonadi? (b) Ndimotani mmene mkazi mothekera angamalephere kusonyeza “ulemu wakuya” kwa mwamuna wake wosakhulupirira?
6 Mtumwi Petro anaika mwatsatanetsatane chitsanzo cha Kristu mu mkhalidwe ndi kulongosola kuti Yesu anatisiira ife ‘chitsanzo kutsatira mapazi ake mosamalitsa.’ Kenaka Petro analongosola kuti: “Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu a inu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mawu, akakodwe opanda mawu mwa mayendedwe a akazi; [pokhala atachitira umboni mkhalidwe wanu woyera limodzi ndi ulemu wakuya, NW].” (1Petro 2:21-3:2) Ndimotani mmene akazi Achikristu angasonyezere “ulemu wakuya” umenewu?
7 Ambiri a alongo athu Achikristu ali ndi amuna osakhulupirira ndipo nthaŵi zina otsutsa. Kodi mikhalidwe imeneyi imatanthauza kuti uphungu wa Petro kenaka uli wopanda pake ndi wosagwira ntchito? Ayi, kugonjera ndi ulemu zimafunikira ngakhale ngati “ena samvera mawu.” Chotero, kodi chikakhala chizindikiro cha ulemu wakuya ngati mkazi Wachikristu wokhala ndi mwamuna wotsutsa akabwera ku Nyumba ya Ufumu ndi kuyamba kumunyodola iye, kusimba kwa alongo ambiri mu mpingo kuzunza kulikonse kumene iye walandira kuchokera kwa iye? Ngati iye akachita chimenecho kulinga kwa mbale kapena mlongo mu mpingo, kodi icho chikatchedwa chiyani? Kunyodola, kapena mwinamwake kudyerekeza. Chotero, sichiri umboni wa ulemu wakuya kwa mkazi kunyoza mwamuna wake wosakhulupirira. (1 Timoteo 3:11; 5:13) Komabe, chiyenera kuzindikiridwa kuti alongo ena otsutsidwa ali ndi vuto loipitsitsa. Kodi nchiyani chomwe chiri chothetsera Chachikristu? Iwo angapite kwa akulu ndi kufunafuna chithandizo chawo ndi chilangizo.—Ahebri 13:17.
8. Nchiyani chimene chingakhale kulingalira kwa mwamuna wotsutsa?
8 Ndimotani mmene akulu angachitire mochenjera ndi mwamuna wotsutsa? Choyamba cha zonse, iwo angayese kuwona mkhalidwewo kuchokera ku kulingalira kwa mwamunayo. Chiwawa chake chapakamwa kapena chakuthupi chingasonkhezeredwe ndi kuyankha kwa magwero a mbali zitatu a umbuli wotsogolera ku mantha ndipo kenaka kuyankha kwachiwawa. Ndipo nchifukwa ninji ichi chimachitika? Nthaŵi zina mwamunayo amadziŵa zochepera kapena osati n’chimodzi chomwe ponena za Mboni za Yehova kusiyapo kokha zimene amamva kuchokera kwa ogwira nawo ntchito oweruziratu molakwika. Iye amadziŵa kuti mkazi wake asanayambe kuphunzira Baibulo iye angakhale anali womwerekera kotheratu mwa iye ndi ana awo. Ngakhale kuti mkaziyo tsopano angakhale mkazi wabwinopo ndi amayi, mkhalidwe wa mwamunayo uli wakuti: ‘Iye amandisiya ine nthaŵi zitatu pa mulungu kupita ku misonkhano imeneyo. Sindidziŵa chimene chimachitika ku misonkhano imeneyo, koma kuli amuna owoneka bwino pa holo imeneyo, ndipo . . . ’ Inde, umbuli wake ungatsogolere ku nsanje ndi mantha. Kenaka kumabwera kuyankha kochinjiriza. Kumene mikhalidwe yotereyi yazindikiridwa, ndimotani mmene akulu angathandizire?—Miyambo 14:30; 27:4.
9. Ndi kufikira kochenjera kotani kumene kungagwiritsiridwe ntchito kwa amuna osakhulupirira ena, ndipo ndi chotulukapo chotani chimene ichi chingakhale nacho?
9 Mwinamwake mmodzi wa akulu angapite kukadziŵa mwamunayo pamaziko aumwini. (1 Akorinto 9:19-23) Mwamunayo angakhale ndi luso monga katswiri wokonza magetsi, wopala matabwa, kapena wopaka utoto. Iye angakhale wofunitsitsa kugwiritsira ntchito luso limenelo kuthandizira vuto pa Nyumba ya Ufumu. Mwanjira imeneyo iye adzawona mkati mwa Nyumbu ya Ufumu popanda kumva thayo lirilonse la kupezeka pa msonkhano. Pamene iye afika pa kudziŵa abale, mkhalidwe wake kulinga kwa mkazi wake ndi chowonadi ungasinthe. Atawona chikondi ndi mzimu wa kugwirizana mu mpingo, iye angakhoze ngakhale kuyamba kubweretsa mkazi wake ku misonkhano. Kenaka, popeza kuti chinthu chimodzi chimatsogolera ku chinzake, iye angaloŵe mkati mwa holo mkati mwa msonkhano kuti amvetsereko kwa kanthaŵi. Pasanapite nthaŵi yaitali, iye angakhale akufunsira kaamba ka phunziro la Baibulo. Zonsezi zingafikiridwe ndipo nthaŵi zina izo zatero. Pali zikwi za amuna okhulupirira lerolino, tiyamikira ku chikondi choterocho ndi kuchenjera ndi “ulemu wakuya” wa mkazi.—Aefeso 5:33, NW.
Amayang’anira Am’nyumba Yake
10, 11. Ndi mbali zosiyanasiyana zotani za mkazi wangwiro zimene Mfumu Lemueli akulongosola? (Lingalirani imodzi ndi imodzi.)
10 Mfumu Lemueli anatenga uphungu wabwino kuchokera kwa amayi ake ponena za mikhalidwe ya mkazi woyenera. (Miyambo 31:1) Kalongosoledwe kake ka mkazi ndi mayi wogwira ntchito zolimba pa Miyambo 31:10-31 kali koyenera kuŵerenga mosamalitsa. Iye mwachidziŵikire anali ndi kuzoloŵera m’kugwiritsira ntchito maprinsipulo olungama a Mulungu ndi m’kusonyeza ulemu wakuya.
11 Lemueli akulemba kuti “mkazi wangwiro” ali wokhulupirika, wodalirika, ndi wokhulupirira. (Mavesi 10-12) Iye amagwira ntchito zolimba kudyetsa ndi kusamalira kaamba ka mwamuna wake ndi ana. (Mavesi 13-19, 21, 24) Iye ali wachifundo ndi wopereka kwaulere kwa awo osowa mowonadi. (Vesi 20) Ndi ulemu wake ndi mkhalidwe wabwino, iye amawonjezera ku kutchuka kwabwino kwa mwamuna wake. (Vesi 23) Iye sali wonyodola wakabisira kapena wosuliza wowononga. Mmalomwake, ndi lirime lake iye amamangirira ndi kuchiritsa. (Vesi 26) Chifukwa chakuti sali waulesi, iye ali ndi nyumba yaudongo, yadongosolo. (Vesi 27) (M’chenicheni, nyumba Yachikristu iyenera kukhala imodzi ya zaudongo koposa m’mudzimo.) Mwamuna wake ndi ana amasonyeza kuyamikira ndi kumtamanda iye. Awo omwe ali kunja kwa banja amayamikiranso mikhalidwe yake. (Mavesi 28, 29, 31) Kukongola kwake sikuli kokha kwa pakhungu; kuli kukongola kwa mkazi wowopa Mulungu wokhala ndi umunthu waumulungu.—Vesi 30.
Mzimu Wofatsa ndi Wachete
12. Nchiyani chomwe chiri cha “mtengo wapatali pamaso pa Mulungu,” ndipo ndimotani mmene mwambi wa Chispanish ukuwunikira nsonga imeneyi?
12 Nsonga yotsirizira imeneyi ikufuulidwa ndi Petro pamene akupatsa uphungu mkazi Wachikristu kusapereka chisamaliro chonkitsa ku kawonekedwe kake kakunja. Iye akulimbikitsa kuti: “Koma [kukometsera kwanu] kukhale munthu wobisika wamtima, m’chovala chosaola cha mzimu wofatsa ndi wachete, ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.” (1 Petro 3:3, 4) Dziŵani nsonga yakuti ‘mzimu wofatsa ndi wachete ndiwo wa mtengo wake wapatali pamaso pa Mulungu.’ Chotero, mkazi Wachikristu ndi amayi yemwe ali ndi mzimu woterowo samasangalatsa kokha mwamuna wake koma, chofunika koposa, ali wosangalatsa kwa Mulungu, monga mmene anachitira akazi okhulupirika a m’nthaŵi zakale, Kukongola kwa mkati kumeneku kukuwunikiridwanso m’kunena kwa Chispanish kwakuti: “Mkazi wokongola amasangalatsa maso; mkazi wabwino amasangalatsa mtima. Ngati woyambayo ali mwala wa mtengo wapatali, wotsatirayo ali chuma.”
13. Ndi chiyambukiro chodzetsa mpumulo chotani chimene mkazi angakhale nacho pa ana ake?
13 Mkazi Wachikristu angakhale wodzetsa mpumulo kwa onse m’nyumba yake. (Yerekezani ndi Mateyu 11:28-30.) Pamene ana awona ulemu wake kaamba ka mwamuna wake, adzawunikira ulemu umenewo m’zochita zawo ndi makolo awo ndi aja omwe ali kunja kwa banja. Monga chotulukapo, ana Achikristu adzakhala achifundo ndi olingalira. Ndipo ndi chodzetsa mpumulo chotani nanga pamene ana adzipereka mwaufulu kuchita ntchito zina mmalo mwa kuwakakamiza kuzichita izo! Kupanda dyera kwawo kumathandizira ku chimwemwe cha m’nyumba, ndipo kumwetulira kovomereza kwa amayi kuli malipiro okwanira.
14. Kufunika kwa chilango kungatsogolere ku chitokoso chotani?
14 Koma bwanji ponena za nthaŵi pamene kupreka uphungu kukufunika? Mofanana ndi makolo awo, ana amapanga zolakwa. Nthaŵi zina amakhala osamvera. Ndimotani mmene mayi Wachikristu adzachitira ngati atate palibe? Kodi iye adzapitirizabe kulemekeza ulemu wa ana awo? Kapena kodi iye adzafuula ndi kunyoza m’kuyesera kupeza chimvero chawo? Chabwino, kodi mwana amaphunzira kuchokera ku kufuula kwa liwu? Kapena kodi liwu lachete, lolingalira likakhala ndi chiyambukiro chokulira?—Aefeso 4:31, 32.
15. Nchiyani chimene ofufuza apeza ponena za chimvero cha ana?
15 Kuchitira ndemanga pa chimvero cha ana, magazini ya Psychology Today inalongosola kuti: “Mogwirizana ndi phunziro la posachedwapa, ukulu wa kufuula kumene mudzauza ana kusachita chinachake, udzakhalanso wa kuthekera kwawo kutembenuka ndikuchita m’chenicheni chimene simukuwafuna iwo kuchita.” Kumbali ina, ofufuza apeza kuti pamene achikulire alankhula mofewa, ana amakhoterera kumvera popanda kusinkhasinkha kokulira. Ndithudi, chiri makamaka chofunika kulingalira ndi mwana mmalo mwa kumukwiyitsa iye ndi malamulo onkitsa opanda polekezera.—Aefeso 6:4; 1 Petro 4:8.
Ulemu mu Unansi Wakuthupi
16. Ndimotani mmene mkazi angasonyezere kulingalira kaamba ka zofunika za malingaliro za mwamuna wake, ndipo ndi phindu lotani?
16 Monga mmene mwamuna ayenera kusonyezera kulingalira kaamba ka mkazi wake chifukwa chakuti ali wa kapangidwe kosalimba kwenikweni, chotero mkazi ayenera kuzindikira zofunika za malingaliro za mwamuna wake ndi za kugonana. Baibulo limasonyeza kuti mwamuna ndi mkazi wake ayenera kupeza chisangalalo mwa wina ndi mnzake ndi kukhutiritsana wina ndi mnzake. Chimenecho chimafunikira kulingalira zofunika za wina ndi mnzake ndi kakhalidwe. Kukhutiritsidwa kwakuya kumeneku kudzathandizanso kutsimikizira kuti palibe chiŵalo chirichonse chimene chidzakhala ndi diso lowunguzawunguza lomwe likatsogolera ku thupi lowunguzawunguza.—Miyamba 5:15-20.
17. Ndimotani mmene mwamuna ndi mkazi ayenera kuwonera kupereka kwa mangawa a mu ukwati?
17 Motsimikizirika, kumene kuli ulemu wakuya, palibe chiŵalo chimene chikagwiritsira ntchito zofunika za kugonana kukhala chida cha maganizo. Aliyense ayenera kupereka mangawa a ukwati kwa mnzake, ndipo ngati pali kupuma kosakhalitsa, kuyenera kukhala mwa kuvomerezana kwabwino. (1Akorinto 7:1-5) Mwachitsanzo, nthaŵi zina mwamuna angakhale kutali ku ntchito yomanga yosakhalitsa pa ofesi ya nthambi ya kumaloko ya Watch Tower Society kapena ntchito ina ya teokratiki. M’nkhani imeneyo iye ayenera kutsimikizira kuti ali ndi chivomerezo cha mtima wonse cha mkazi wake. Kulekanitsidwa koteroko kungabweretsenso madalitso auzimu ku banjalo, uko ndiko kuti, mu mkhalidwe wa zokumana nazo zolimbikitsa zosimbidwa ndi mwamunayo pambuyo pa kubwerera kunyumba.
Thayo Lofunika la Alongo
18. Nchifukwa ninji mkazi wa mkulu ali ndi thayo lokulira?
18 Kumene mwamuna wa mkazi Wachikristu ali mkulu, mkaziyo ali ndi thayo lalikulu. Choyamba, zokhumba ziri zokulira pa mwamunayo. Iye ali woŵerengera kwa Yehova kaamba ka mkhalidwe wauzimu wa mpingo. (Ahebri 13:17) Koma monga mkazi wa mkulu ndipo mwinamwake mkazi wachikulire iyemwini, chitsanzo chake chaulemu chirinso chofunika. (Yerekezani ndi 1 Timoteo 5:9, 10; Tito 2:3-5.) Ndipo ndi chitsanzo chabwino chotani nanga chimene akazi ambiri a akulu amakhazikitsa m’kuchilikiza amuna awo! Kaŵirikaŵiri, mwamuna adzafunikira kukhala kunja kusamalira nkhani za mpingo, ndipo mwinamwake chikhumbo cha mkaziyo chimadzutsidwa. Mokhulupirika, ngakhale kuli tero, mkazi waumulungu samaloŵerera mu zochitachita za mpingo monga wodudukira.—1Petro 4:15.
19. Nchiyani chimene ‘kuyang’anira a m’nyumba yake’ kungaphatikize kwa mkulu?
19 Ngakhale kuli tero, mkulu angafunikire kulanga mkazi wake ngati iye asonyeza mikhalidwe imene iri yosamangirira kapena ngati iye sakhazikitsa chitsanzo chabwino kaamba ka alongo ena. ‘Kuyang’anira bwino am’nyumba yake’ kumaphatikizapo osati kokha ana komanso mkazi. Kugwiritsira ntchito miyezo imeneyi ya Malemba kungayese kudzichepetsa kwa akazi ena.—1 Timoteo 3:4, 5, 11; Ahebri 12:11.
20. Tchulani zitsanzo zina zabwino za alongo okwatiwa ndi osakwatiwa mu nthaŵi zakale ndi zamakono. (Onani “Life Stories of Jehovah’s Witnesses” mu Watch Tower Publications Index 1930-1985.)
20 Alongo osakwatiwa angawunikirenso pa thayo laulemu la akazi mu mpingo. Pali zitsanzo zambiri zabwino za alongo abwino, okhulupirika, ponse paŵiri m’Malemba ndi mu mpingo lerolino! Dorika, mwinamwake mlongo wosakwatiwa, anayamikiridwa mwakuya kaamba ka “ntchito [zake] zabwino.” (Machitidwe 9:36-42) Priska ndi Febe analinso achangu kaamba ka chowonadi. (Aroma 16:1-4) Mofananamo lerolino, ambiri a alongo athu, okwatiwa kapena osakwatiwa, ali amishonale abwino kwambiri, apainiya, ndi ofalitsa. Panthaŵi imodzimodziyo, akazi aumulungu oterowo amasunga nyumba zawo zaudongo, zadongosolo ndipo samanyalanyaza mabanja awo. Chifukwa cha chiŵerengero chawo ndi mikhalidwe, iwo kaŵirikaŵiri amachita mbali yokulira ya ntchito yolalikira.—Salmo 68:11.
21. Ndimotani mmene alongo okhulupirika aliri olimbikitsa kwa abale awo Achikristu?
21 Alongo okhulupirika mu mpingo amachita mbali yomangirira yofunika. Changu chawo ndi chitsanzo ziri chilimbikitso kwa abale ndi ku mpingo Wachikristu mwachisawawa. Iwo mowonadi ali othangatira ndi othandizira. (Yerekezani ndi Genesis 2:18.) Ndi chikondi chenicheni chotani nanga ndi ulemu zimene iwo amayenerera! Ndipo kaamba ka aŵiri okwatirana Achikristu, woyenerera, ndithudi, uli uphungu wa Paulo: “Komanso inu, yense payekha, yense akonde mkazi wake wa iye yekha, monga azikonda yekha; [mkazi ayenera kukhala ndi ulemu wakuya kaamba ka mwamuna wake, NW].”—Aefeso 5:33.
Kodi Mumakumbukira?
◻ Ndi ati omwe anali mathayo oyambirira a Mulungu kaamba ka mwamuna wangwiro ndi mkazi?
◻ Ndimotani mmene amuna osakhulupirira angakodwere ndi chowonadi?
◻ Ndi iti yomwe iri mikhalidwe yowonekera ya mkazi wangwiro?
◻ Ndimotani mmene mkazi Wachikristu angasonyezere ‘mzimu wofatsa ndi wachete’?
◻ Ndi kulinganiza kotani kumene kukufunika mu unansi wakuthupi pakati pa okwatirana?
[Chithunzi patsamba 16]
Banja silikakhala ngati chombo chokhala ndi oyendetsa awiri opikisana
[Chithunzi patsamba 18]
Mwamuna wosakhulupirira angakhale wansanje, ngakhale mwa njira inayake wamantha, chifukwa cha kupezeka ku msonkhano kwa mkazi wake kapena zochitachita zina Zachikristu. Ndimotani mmene iye angathandizidwire?