Anaphonya Basi
TSIKU lina James anawona mwana wake wamkazi Rebecca akuyenda mwachilendo mochedwa kupita kukakumana ndi basi ya ku sukulu. Ngakhale kuti Rebecca anawona basi ikubwera, iye anayenda ngakhale mochedwerapo ndipo mwadala anaphonya basiyo.
Madzulo amodzimodziwo James ndi mkazi wake, Veronica, anakambitsirana nkhaniyo mwakubwereramo m’nkhani ya “Yona ndi Chinsomba Chachikulu” kuchokera mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo. Inali imodzi ya nkhani za pamtima za Rebecca. Pambuyo pa kumaliza nkhaniyo, makolowo anaigwirizanitsa iyo ndi vuto la mwana wawo wamkazi. Iye anapeza nsonga yeniyeni ndi kunena kuti: “Ngakhale kuti Yona anathawa ndi kufika m’mavuto m’nyanja, ndipo iye anamezedwa ndi chinsombacho ndipo analavulidwa kunja—ntchito yake kaamba ka Yehova inali kudikirabe kaamba ka iye kuichita.”
Tsiku lotsatira Rebecca anapita ku sukulu ndi kawonedwe katsopano ndi Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo atalikupatira kukhwapa kwake.
Mungalandire kope la chofalitsidwa chochitiridwa chitsanzo mokongola, cha malemba aakulu, cha masamba 256 mwa kudzaza ndi kutumiza kapepala kotsatiraka.
Chonde tumizani, mutalipiriratu positi, bukhu la chikuto cholimba Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo, kaamba ka limene ndatsekeramo K30.00.