Chifukwa Chimene Muyenera Kudziŵa Chowonadi Ponena za Abrahamu
ABRAHAMU—ngwazi ya nthano kapena mneneri wowona? Kodi yankho ku funso limenelo liri lofunika motani? Mogwirizana ndi mbiri ya kaŵerengedwe ka zaka ya Baibulo, Abrahamu anakhalako zaka zina 4,000 zapitazo. Chotero ena angalingalire kuti, ‘Kodi ndi kusiyana kotani kumene iko kumapanga kaya ngati iye anakhalakodi kapena ayi?’
Chabwino, theka la chiŵerengero cha dziko liri ku zipembedzo zomwe zimadzinenera kukhulupirira mwa Abrahamu. 1988 Britannica Book of the Year ikundandalitsa 32.9 peresenti ya dziko kukhala Yachikristu, 17.2 peresenti ya Chisilamu, ndi 0.4 peresenti ya Chiyuda, ndipo Abrahamu ali munthu wotchuka mu zipembedzo zitatu zonsezi. Ndithudi, akhulupiriri owona mtima kuchokera ku zikhulupiriro zimenezi ayenera kufuna kutsimikizira kuti zimene iwo aphunzitsidwa ponena za Abrahamu ziri chowonadi. Ngakhale awo amene ali ku zipembedzo zina kapena awo amene amadzinenera kukhala opanda chipembedzo nkomwe ayenera kusangalatsidwanso. Nchifukwa ninji?
Chifukwa chakuti Baibulo limanena kuti Abrahamu anali mneneri. (Genesis 20:7) Limenelo ndilo liwu la Baibulo logwiritsiridwa ntchito kulongosola wolankhulira wa Mulungu wokhala ndi uthenga kaamba ka anthu ena. Ngati Abrahamu anali mneneri wowona, onse adzapindula. Nchifukwa ninji? Chifukwa chakuti uthenga umene analandira unali ndi mbiri yabwino kaamba ka mtundu wonse wa anthu. (Agalatiya 3:8) Mogwirizana ndi Baibulo, Mulungu analonjeza Abrahamu kuti: “Mwa iwe adzadalitsidwa mabanja onse a dziko lapansi.”—Genesis 12:3.
Limenelo liri lonjezo lozizwitsa, ndipo Abrahamu analimva ilo likunenedwa pa chifupifupi zochitika zina ziŵiri. (Genesis 18:18; 22:18) Kuti akwaniritse ilo, Mulungu adzawukitsa kuchokera kwa akufa oimira a mabanja onse omwe anafa. Moyo kwa owukitsidwa oterowo udzakhaladi dalitso, popeza kuti ambiri a iwo akabwereranso ku mkhalidwe wa pa dziko lapansi wofanana ndi Paradaiso imene munthu anaitaya poyambirirapo. Pambuyo pa chimenecho, iwo akaphunzitsidwa mmene angapezere dalitso la moyo wosatha.—Genesis 2:8, 9, 15-17; 3:17-23.
Ngati, ku mbali ina, Abrahamu anali kokha munthu wa nthano, sipakakhala maziko a kukhulupirira lonjezo lozizwitsa limene iye analandira. M’kuwonjezerapo, ngati malonjezo a Baibulo sangadaliridwe, ena angatsutse moyanja kudzipereka iwo eni kotheratu ku zosangulutsa za moyo uno. Monga momwe mmodzi wa Akristu oyambirira analembera kuti: “Ngati akufa sawukitsidwa, tidye timwe pakuti mawa timwalira.”—1 Akorinto 15:32.
Chotero, muli ndi chifukwa chirichonse cha kusanthulira funso lakuti, Kodi Abrahamu anali kokha ngwazi ya nthano kapena kodi anali mneneri wowona? Chingakudabwitseni kudziŵa chimene atsogoleri achipembedzo otchuka a m’zana la 19 anena ponena za ichi. Pa nthaŵi ino, ofukula zinthu zofotseredwa pansi afikira zopezedwa zozizwitsa zomwe zimatokosa malingaliro a atsogoleri achipembedzo amenewo.