Paradaiso Wobwezeretsedwanso Alemekeza Mulungu
“Ndidzachititsa malo a mapazi anga ulemerero.”—YESAYA 60:13.
1, 2. (a) Kupyolera mwa mneneri wake Yesaya, kodi nchiyani chomwe Mulungu ananeneratu ponena za dziko lapansi? (b) Kuyang’ana zaka chikwi mtsogolo, nchiyani chomwe tikuwona?
YEHOVA analenga dziko lapansi monga pulaneti pansi pa mapazi ake, monga chopondapo mapazi ake chophiphiritsira. Kupyolera mwa mneneri wake Yesaya, Mulungu ananeneratu kuti iye ‘akachititsa malo a mapazi ake ulemerero.’ (Yesaya 60:13) Ndi thandizo la Baibulo lowuziridwa, tingayang’ane, monga ngati ndi chokulitsira zinthu champhamvu, zaka zikwi zingapo kuloŵa mtsogolo mwa munthu. Ndi malo osangalatsa chotani nanga omwe akulonjera maso athu! Dziko lonse lapansi likuwala ndi kukongola kosayerekezeka kopangidwa ndi Mlimi wamkulu koposa m’chilengedwe chonse chaponseponse. Paradaiso adzakhala atabwezeretsedwanso pa dziko lonse lapansi ku mtundu wa anthu!
2 Inde, Wokhalako Wamkulu waumulungu yemwe anayambitsa kukhalapo kwa munthu m’munda wa paradaiso ali ndi chimwemwe chachikulu cha munthu m’maganizo. Ndithudi ali Mlengi wachikondi chotani nanga kaamba ka mtundu wa anthu kukhala naye, kwa amene sikuli kukamba kopeka kunena kuti, “Mulungu ndiye chikondi”! (1 Yohane 4:8, 16) Mu Paradaiso wobwezeretsedwanso, amuna ndi akazi achikulire mu ungwiro wopanda banga akukhala pamodzi monga abale ndi alongo achikondi. (Yesaya 9:6) Pokhala osonkhezeredwa ndi chikondi, iwo ali m’kugonjera kwangwiro kwa Mlengi waulemerero wa kumwamba ndi dziko lapansi, Yehova Mulungu.
3, 4. (a) Kodi ndi m’njira yotani mmene miyamba ndi dziko lapansi zidzalinganirana ina ndi inzake? (b) Kodi ndimotani mmene angelo adzavomerezera pamene Paradaiso adzabwezeretsedwanso ku dziko lapansi?
3 Zaka zikwi zingapo kumbuyoko, m’kulongosola kowuziridwa mwaumulungu kwa ufumu wake, Mulungu analankhula mawu osangalatsa awa kwa anthu ake osankhidwa: “Kumwamba kuli mpando wanga wachifumu, ndipo dziko lapansi liri chopondapo mapazi anga.” (Yesaya 66:1) Ulemerero wonse wa “chopondapo mapazi” ake, dziko lapansi la Paradaiso, uyenera molondola kulingana ndi ulemerero wa mpando wake wachifumu m’mwamba mosawoneka.
4 Pa nthaŵi ya kulengedwa kwa dziko lapansi, awo omwe anali akalinde pa mpando wachifumu wa Mulungu mu ufumu wa kumiyamba analingalira malo a dziko lapansi pansipo. Ndimothuzitsa mtima chotani nanga mmene iwo angakhale anadzimverera pamene maso awo anawona kukongola kwake kwa ulemerero! Ndimotani mmene iwo akalekera kufuula chapamodzi mu nyimbo? (Yerekezani ndi Zefaniya 3:17, Revised Standard Version; Salmo 100:2, The Jerusalem Bible.) Mlengi wokondweretsedwa ndi wachimwemwe anawuzira mlembi wake wa pa dziko lapansi kuwunikira kulongosola kolongosoka kwa malo a kumwamba, akumanena kuti: “Muja nyenyezi zakumwamba zinayimba limodzi mokondwera, ndi ana onse a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.” (Yobu 38:7) Ndimochulukira tero motani nanga mmene ana aungelo a Mulungu adzafuulira m’chisangalalo, ku ulemerero wa Mulungu, pamene Paradaiso adzabwezeretsedwanso!
5. Kodi ndimotani mmene tiyenera kudzimverera ponena za kufikiridwa kwa cholinga choyambirira cha Mulungu ponena za dziko lapansi?
5 Ndithudi chiri chopumitsa mtima kwa ife kutsimikiziridwa ndi Malemba Oyera owuziridwa kuti kufikiridwa kokulira kwa paradaiso ya dziko lapansi kunali chonulirapo pa chimene Yehova Mulungu analinganiza kuchokera pachiyambi penipeni. Chodzetsa chisangalalo, ndi choyambitsa chitamando chimenechi chothera mu chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansili chiri kokha chinthu cholondola choyembekezeredwa kwa Mulungu yemwe amapita kuchokera ku ulemerero kupita ku ulemerero popanda kulephera m’kusonyeza ukulu wake. Chitamando chonse chipite kwa iye!—Salmo 150:1, 2; Yesaya 45:18; Chibvumbulutso 21:3-5.
Owukitsidwa Athandizira Kubwezeretsanso Paradaiso
6. Pamapeto pa Armagedo, kodi ndimotani mmene dziko lapansi lidzadzazidwira ndi anthu?
6 Ngakhale kuti opulumuka Armagedo adzakhala m’chenicheni oŵerengeka m’chiŵerengero, sichidzakhala kotheratu kupyolera m’kubala ana kumbali yawo kumene dziko lapansi lidzadzazidwa mokwanira ndi anthu. Yehova ‘adzachititsanso malo a mapazi ake ulemerero’ mwa kubwezeretsanso moyo kwa awo omwe ali m’manda a chikumbukiro ndi omwe amadza pansi pa mapindu a dipo la nsembe ya Kristu. Awa, kachiŵirinso, adzakhala ndi mwaŵi wa kugawana m’ntchito yosangalatsa ya kusintha chiwunda cha dziko lathu lapansi kukhala paradaiso yokongola moposerapo.—Machitidwe 24:15.
7. Kodi ndi mawu otani a Yesu amene opulumuka Armagedo adzasunga m’maganizo?
7 Opulumuka Armagedo adzasunga m’maganizo kosatha mawu okondweretsa mtima a Ambuye Yesu Kristu pa nthaŵi imene anafulumizidwa kunena kuti: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.” (Yohane 5:28, 29) Limenelo lidzakhala ora lotani nanga pamene anthu akufa m’manda awo a chikumbukiro ayamba kumva liwu la Mwana wa Mulungu akunena mawu ofanana ndi aja olunjikitsidwa kwa Lazaro, amene mtembo wake unali m’manda pa Betaniya: “Lazaro tuluka!”—Yohane 11:43.
8, 9. Kodi ndani omwe mwachidziŵikire adzakhala oyambirira kuwukitsidwa ku moyo watsopano pa dziko lapansi, kubweretsa chisangalalo chotani kwa opulumuka Armagedo?
8 Ndani omwe mwachidziŵikire adzakhala oyamba kuwukitsidwa ku moyo wokonzedwa chatsopano pa dziko lapansi pansi pa Kulamulira kwa Zaka Chikwi kwa Yesu Kristu ndi kuyankha ku lamulo lake? Adzakhala moyenerera “nkhosa zina” omwe anafa mkati mwa masiku otsiriza otsatira mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu. Iwo adzakumana ndi chiwukiriro choyambirira. (Yohane 10:16) Iwo mwinamwake adzakhala ndi vuto lochepera la kudzisinthira iwo eni ku dziko latsopano.—Yerekezani ndi Mateyu 25:34; Yohane 6:53, 54.
9 Chidzakhala chosangalatsa chotani nanga kwa opulumuka Armagedo pamene adzawona akuwukitsidwa aja a “nkhosa zina” omwe anamwalira mkati mwa mbadwo wa “chisautso chachikulu” chisadakhale! (Mateyu 24:21) Ndi mphamvu yowonekera ya kuzindikiritsa, opulumuka Armagedo awazindikira iwo, kuwalonjera, ndipo ndi iwo apitiriza kukonzanso chatsopano utumiki wawo wogwirizana kwa Mulungu Wam’mwambamwamba!
10. Mwa kupulumuka Armagedo, kodi nchiyani chomwe mungachitire umboni?
10 Mwakukhala mmodzi wa opulumuka Armagedo, inu mungachitire umboni kuwuka kwa woyamba wa achibale anu a pa dziko lapansi. Ndimotani mmene chiyambukiro cha maganizo cha chimenechi chidzakhalira pa inu ngati sikufanana ndi chija chamakolo omwe anawona Ambuye Yesu akubwezeretsa moyo wa mwana wawo wamkazi wa zaka 12 zakubadwa kumikono yawo yokhumbira? “Ndipo anadabwa pomwepo ndi kudabwa kwakukulu.” (Marko 5:42) Inde, ndithudi, chisangalalo chosaneneka chidzakhala chanu pa chiwukiriro cha akufa kuchokera ku Hade ndi nyanja. (Chibvumbulutso 20:13) Ha, lidzakhala tsiku la mawa lolemekezeka chotani nanga, tsiku la mawa lomwe posachedwapa lidzakhala pano!
“Akalonga m’Dziko Lonse Lapansi”
11, 12. (a) Kodi nchiyani chimene Salmo 45:16 likugogomezera? (b) Kodi ndi kuchokera pakati pa yani pamene Mfumu, Yesu Kristu, angaike “akalonga m’dziko lonse lapansi”?
11 Mwa kuchita mphamvu zake za kuwukitsa anthu akufa kaamba ka amene iye anaika pansi moyo wake wangwiro waumunthu monga nsembe ya dipo, Yesu adzakhala wokhoza kubweretsa kukwaniritsidwa kwa Salmo 45:16, (NW.) Salmo limeneli likulunjikitsidwa mwaulosi kwa Yesu Kristu monga Mfumu yokhazikitsidwa: “M’malo mwa atate ako [apa dziko lapansi] padzakhala ana ako, omwe udzaika monga akalonga m’dziko lonse lapansi.” Salmo limeneli likugogomezera kuti Yesu Kristu adzakhala atate wakumwamba kwa ana pano pa dziko lapansi ndi kuti adzakhazikitsa ana kuchokera pakati pawo kukhala “akalonga m’dziko lonse lapansi.” Monga “mwana wa Davide” ndipo monga mwana woyamba kubadwa wa namwali Wachiyuda Mariya, Yesu anali ndi makolo a pa dziko lapansi kubwerera kumbuyo kwa atate woyamba, Adamu.—Luka 3:23-38.
12 Kodi Salmo 45:16 likunena kuti awo omwe anali poyambapo makolo achibadwa a Yesu adzakhala ana ake mwa kuwawukitsa iwo kuchoka kwa akufa? Inde. Kodi Salmo 45:16 likunenanso kuti kokha chifukwa cha kubadwa kwake kuchokera kwa iwo, Yesu adzawasonyeza chiyanjo cha ufumu chapadera ndi kuika kokha iwo kukhala “akalonga m’dziko lonse lapansi” mu mkhalidwe wake wa Paradaiso? Ayi. Kukwaniritsidwa kwa ulosiwo m’njira yoteroyo kukalola kokha chiŵerengero chokhala ndi polekezera cha “akalonga” m’dziko lonse lapansi. Pa mbali pa nsonga imeneyo, simakolo ake onse amenewa omwe anali opambana kwenikweni kotero kuti ayenerere kutchuka kwapadera pa dziko lapansi mkati mwa Ulamuliro wake wa Zaka Chikwi. Mfumu, Yesu Kristu, adzakhala ndi ena owonjezereka osaŵerengeka oposa makolo ake a pa dziko lapansi owaika kukhala “akalonga”—opulumuka Armagedo oyeneretsedwa, owukitsidwa a “nkhosa zina,” kuphatikizapo amuna a chikhulupiriro a Chikristu chisadakhale. Kuchokera pakati pa amenewa, iye angaike ofikapo oyenerera kutenga ntchito ya ukalonga monga oimira ake a pa dziko lapansi.
13, 14. Kodi ndi owukitsidwa ati omwe opulumuka Armagedo adzakhala ndi mwaŵi wa kuwona ndi maso awo?
13 Ganizani ponena za oterowo amene ali m’njira ya kuwukitsidwa pansi pa Ufumu wa Umesiya. Tawonani! Kodi tingakhulupirire zimene tikuwona? Suuyo Abele, munthu wophedwera chikhulupiriro woyambirira, ndi Enoke, yemwe anapitiriza kuyenda ndi Mulungu wowona. Kujako, kachiŵirinso, kuli Nowa, womanga chingalawa. Pali Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, makolo a mtundu wa Israyeli. Pali Mose (wa fuko la unsembe la Levi) ndi Davide kwa amene pangano losatha kaamba ka Ufumu linapangidwa. Ndipo kujanso, Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, Danieli, ndi aneneri ena onse olemba Baibulo Achihebri kupyola kudzafika ku wotsirizira wa iwo, Malaki, ndipo, ndithudi, Yohane Mbatizi ndiponso Yosefe, atate wopeza wa Yesu.
14 Pa chochitika china Yesu ananena kwa Ayuda kuti iwo akakhoza “kuwona Abrahamu, ndi Isake, ndi Yakobo, ndi aneneri onse, mu Ufumu wa Mulungu, koma [iwo eni] kutulutsidwa kunja.” (Luka 13:28) “Khamu lalikulu” la opulumuka a pa dziko lapansi a “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” adzayanjidwa ndi mwaŵi wa kuwona m’chenicheni akuwukitsidwa “Abrahamu ndi Isake ndi Yakobo ndi aneneri ena onse” m’Paradaiso wa pano pa dziko lapansi ndi mu utumiki wa ufumu pansi pa Ufumu wa Mulungu mwa “Atate Wosatha,” Yesu Kristu.—Chibvumbulutso 7:9, 14; 16:14; Yesaya 9:6.
15. Kodi ndi mwaŵi wosayerekezeka wotani womwe ukuyembekezera awo opulumuka Armagedo?
15 Chidzakhala chotenthetsa mtima chotani nanga kwa inu amene mudzapulumuka mapeto a dziko loipa iri kuyerekezera zidziŵitso ndi Nowa ndi banja lake lenileni, “miyoyo isanu ndi itatu,” yomwe inapulumuka mapeto a dziko loyamba m’Chigumula cha dziko lonse mu 2370 B.C.E.! Kulibe wina aliyense ku nthaŵi yosatha yemwe adzakhala ndi zokumana nazo zofanana ndi zanu ndipo chotero kukhala wokhoza kutumikira monga Mboni ya Yehova Mulungu m’chilozero chapadera ichi, chosabwerezekanso.—1 Petro 3:20; Marko 13:19; 2 Petro 3:5-7.
Wochita Zoipa Womvera Chifundo Akumbukiridwa
16, 17. (a) Pamene Yesu akumbukira wochita zoipa womvera chifundo, kodi ndi mwaŵi wotani umene opulumuka Armagedo ndi ena okhala ndi moyo nthaŵiyo adzakhala nawo? (b) Kodi ndi chiyembekezo chotani chomwe chikupezedwa ponena za kuwukitsidwa kwa wochita zoipayo?
16 Mosakaikira, podzafika nthaŵiyo kubwezeretsedwanso kwa Paradaiso pa dziko lapansi kudzakhala kukuchitidwa. Mwamuna yemwe anapachikidwa pa Kalivali kumbali kwa Yesu ndi amene ananena pozindikira chizindikiro chomwe chinali pamwamba pa mutu Wake kuti, “Yesu, ndikumbukireni inu pamene muloŵa Ufumu wanu,” adzawukitsidwa ku moyo wa pa dziko lapansi m’Paradaiso wobwezeretsedwanso. (Luka 23:42) Udzakhala mwaŵi wa Armagedo ndi ena omwe adzakhala ndi moyo kumlandira iye kuchokera kwa akufa. Iwo adzamphunzitsa iye mokwanira ponena za Mfumu yolamulira yatsopano, Yesu Kristu, kwa amene iye anasonyeza chifundo chakuya pa Nisani 14 ya chaka cha 33 C.E.
17 Ambuye Yesu Kristu sadzalephera kumukumbukira iye nthaŵi ina mkati mwa kulamulira Kwake kwa zaka chikwi. Mosakaikira wochita zoipa womvera chifundo uja, wowukitsidwayo adzasonyeza chiyamikiro chake kaamba ka Mfumu yolamulira, Yesu Kristu, kwa amene iye ali ndi liwongo la chiwukiriro chake, mwa kutsimikizira kukhulupirika kwake kwa Wolamulira wa Chilengedwe Chaponseponse, Yehova Mulungu. Kenaka iye adzaŵerengedwa woyenerera kusangalala ndi kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Paradaiso kwamuyaya limodzi ndi mtundu wonse wa anthu wobwezeretsedwa, womvera.
Moyo m’Munda wa Edene Wobwezeretsedwanso, wa Chiwunda Chonse
18. Kodi ndimotani mmene moyo udzakhalira m’Paradaiso wobwezeretsedwanso?
18 Mu Paradaiso wobwezeretsedwa, aliyense ali bwenzi la aliyense. Zomangira za unansi wa banja la dziko lonse zikumvedwa mwakuya m’moyo wa aliyense. Onse akumvana wina ndi mnzake. Iwo akulankhula chinenero cha dziko chofala. Mwachidziŵikire chiri chinenero choyambirira cha mtundu wa anthu, chimene aliyense pa dziko lapansi analankhula kwa zaka 1,800 za kukhalapo kwa munthu—kuchokera pa kulengedwa kwa Adamu mu 4026 B.C.E. mpaka tsiku la Pelege (2269 mpaka 2030 B.C.E.), chifukwa chakuti “m’masiku ake dziko lapansi [uko ndiko kuti, chiŵerengero cha anthu a dziko lapansi] linagawanikana.” (Genesis 10:25; 11:1) Aliyense akusangalala ndi mwaŵi wa kukhala ndi moyo, ndipo tsiku lirilonse latsopano likulonjeredwa ndi kuyamikira kaamba ka tsiku lowonjezereka la moyo. Kulemala kwakuthupi sikukuwonjezeka pamene nthaŵi ikupita. Mphamvu zakuthupi zikumangirira, ndipo matupi sakutopa.—Yerekezani ndi Yobu 33:25.
19. Kodi nchiyani chomwe chidzawonedwa ponena za awo omwe papitapo anali olemala?
19 Ndipo tawonani! Omwe pa nthaŵi ina anali olemala akuyenda, inde, kudumpha kaamba ka chisangalalo. Mikono ndi miyendo yoduka zabwezeretsedwa mozizwitsa. Omwe kale anali akhungu akuwona, agonthi akumva, osalankhula akulankhula ndi kuyimba kaamba ka chisangalalo chosayerekezeka. (Yerekezani ndi Yesaya 35:5, 6.) Kusawoneka bwino ponena za mkhalidwe wa munthu ndi kapangidwe kukutha. Umuna wa anthu ukulinganizidwa mokongola ndi ukazi wa anthu. (Genesis 2:18) Ungwiro wa anthu ulemekeza Yehova Mulungu, Mlengi wa thupi la munthu lagwiro.
20. Kodi nchiyani chomwe chidzawonedwa ponena za mphamvu zachilengedwe, zopereka zakudya, chilengedwe cha nyama, ndi mmene dziko lapansi lidzagwiritsiridwa ntchito?
20 Dziko lonse lapansi likukhala dontho limodzi la chiwunda chonse lokongola. Palibe mbali iriyonse ya dziko lapansi kumene kuli ripoti lirilonse la chilala kapena la kugwa kwa mvula kodzetsa chiwonongeko kapena kwa mphepo yosakaza, kavuluvulu, namondwe, ndi mkuntho. (Yerekezani ndi Marko 4:37-41.) Mphamvu zonse zachilengedwe zikubweretsedwa ku kulinganizika kwangwiro kaamba ka kupanga dziko lonse malo osangalatsa kukhalamo. Palibe kusoŵeka kwa chakudya paliponse, popeza kuti dziko lapansi likubala zotulutsa zake mokwanira. (Salmo 72:16) Mtendere ndi chisungiko zikupezeka dziko lonse ponse paŵiri kwa munthu ndi nyama, monga momwe Yehova ananenera kuti: “Sizidzaipitsa, sizidzasakaza m’phiri langa lonse loyera.” (Yesaya 11:9; onaninso mavesi 6-8.) Mwanjirayi dziko lapansi lidzapangidwa kukhala malo osangalatsa kukhalamo ndi kupitiriza ndi kulambira ndi utumiki wa Yehova Mulungu, Mlengi ndi Mwini wa dziko lapansi. Ilo pokhala chuma chake mwa kuyenera kwa kulenga, liri loyenerera kugwiritsiridwa ntchito m’njira yomwe imamusangalatsa iye ndi imene imamulemekeza iye.—Yerekezani ndi Yesaya 35:1, 2, 6, 7.
21. Kodi ndimotani mmene mtundu wa anthu wowomboledwa udzawonera chirichonse pa dziko lapansi, ndipo ndi nyimbo yotani yomwe idzamvedwa?
21 Zatsopano motsitsimula—mmenemo ndi mmene chirichonse pa dziko lapansi chiri kaamba ka anthu owomboledwa omwe sanali mkati mwa munda wa Paradaiso wa Edene kumene moyo wa munthu unayambira mu ungwiro wokongola! (Chibvumbulutso 21:5) Ndi nyimbo zosangalatsa chotani nanga, za ziŵiya zoimbira ndi za pakamwa, zomwe kenaka zidzamvedwa—zonsezo zikulemekeza Yehova!—1 Mbiri 23:4, 5; Salmo 150:3-6.
22. Kodi zidzamveka motani kukhala ndi moyo m’dziko latsopano la Paradaiso?
22 Ndi chodabwitsa chotani nanga mmene chidzakhalira kukhala ndi moyo m’dziko lapansi mmene moyo wa munthu ukufalikira mokwanira ndi mmene mbali zonse zatsatanetsatane wa kufa chifukwa cha chimo loyambirira la Adamu zidzakhala zitachotsedwa! (Yerekezani ndi Yohane 10:10.) Inde, lidzakhala dziko lapansi m’limene cholengedwa chaumunthu chirichonse chovomerezedwa chidzawunikira chifanizo ndi kufanana kwa Yehova Mulungu m’chimene mwamuna woyamba Adamu analengedwera! (Genesis 1:26, 27) Dziko lapansi kenaka silidzakhala chonyansa kwa aserafi, akerubi, ndi kwa angelo owala a kumwamba. Pamene iwo atembenuza nkhope zawo zokondeka kulinga ku dziko lapansi, kupenyetsetsa pansi pa ilo lokometsedwa ndi kukongola kwa paradaiso, iwo adzakhala kokha ndi chitamando cha chiyamikiro cha kulongosola kwa Mmodzi amene iwo ali ndi mwaŵi wakuwona nkhope yake mwachindunji—Yehova, Wolamulira wa Chilengedwe Chaponseponse.—Mateyu 18:10.
Mtsogolo Mwachimwemwe, Mosatha
23. Kodi nchiyani chomwe chiri chothekera ponena za Akristu odzozedwa, ndipo ndi chotulukapo chotani ku nzika za Paradaiso wa pa dziko lapansi?
23 Ziri mkati mwa kuthekera ndipo mwachidziŵikire kuti, tsiku lina mtsogolo, maina a Akristu odzozedwa onsewo omwe apanga “kuitanidwa ndi kusankhidwa” kwawo ku Ufumu wa kumwamba kotsimikizirika ndi omwe adalitsidwa ndi chiwukiriro chakumwamba chimenechi adzafalitsidwa mokwanira kaamba ka chidziŵitso cha banja la munthu m’Paradaiso wawo wa pa dziko lapansi. (2 Petro 1:10; Salmo 87:5, 6) Chotero, kusakhalapo kwa ophunzira odzozedwa obadwa ndi mzimu a 144,000 a Yesu Kristu m’Paradaiso wa pa dziko lapansi kudzamvetsetsedwa mokwanira ku chikhutiritso cha aliyense ndi kukondwera kochokera ku mtima pa iwo ndi limodzi nawo.
24. (a) Kodi nchiyani chomwe Yehova adzakhala atakwaniritsa ponena za “chopondapo mapazi” ake? (b) Kodi ndimotani mmmene timadziŵira kuti dziko latsopano silidzatha, ndipo ndi nyimbo yotani ya ulosi yomwe idzakwaniritsidwa?
24 Mwachimwemwe mudzakhala mtsogolo mosatha kaamba ka onse omwe akukhala m’kudzipereka kosasweka kwa Yehova, Wolamulira weniweni wa chilengedwe chaponseponse. Paradaiso wa pa dziko lapansi yodzazidwa mwaubwino idzakhala malo oyenerera, malo odabwitsa, monga “chopondapo mapazi” pa chimene mapazi a Mulungu angapume mophiphiritsira. Inde, ku nthaŵi zosatha Yehova adzakhala atalemekeza ‘malo a mapazi ake,’ ndipo mtundu wonse wa anthu udzakhala wogonjera kwa iye mosagwedezeka! (Mateyu 5:34, 35; Machitidwe 7:49) Dziko latsopano lidzakhala dziko lopanda malekezero chifukwa chakuti “za kuenjezera ulamuliro wake, ndi za mtendere sizidzatha.” (Yesaya 9:7) Kenaka, nyimbo ya ulosi ya angelo a kumwamba pa kubadwa kwa Yesu mu Betelehemu wa Yudeya mu 2 B.C.E. idzakwaniritsidwa: “Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nawo.”—Luka 2:13, 14.
25. (a) Kodi nchiyani chimene awo a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” tsopano akuyamikira? (b) Kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chikhumbo chathu chochokera ku mtima?
25 Awo omwe ali a “khamu lalikulu” la “nkhosa zina” za Mbusa Wabwino amayamikira mawu otenthetsa mtima a lonjezo la Paradaiso wobwezeretsedwanso. Uli mwaŵi wawo kukhala oyanjana ndi gulu la Mulungu tsopano ndi kukhala oloŵetsedwamo mwachangu m’ntchito yonenedweratu ndi Ambuye Yesu Kristu, kulalikira kwa mbiri yabwino ya Ufumu m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni wotsirizira. (Mateyu 24:14; Marko 13:10) Chikhumbo chathu chowona mtima, chochokera ku mtima monga Mboni za Yehova chiri kusungirira umphumphu wathu wosagwedezeka ku nthaŵi zosatha, ku ulemerero wosatha ndi kuyeretsedwa kwa Wolamulira wa Chilengedwe Chaponseponse, Yehova Mulungu, ndi pansi pa kulamulira kwa ufumu wa Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu. “Aleluya!”—Chibvumbulutso 19:1, 3, 4, 6, RSV, New International Version; Miyambo 10:9.
Ndimotani Mmene Mukayankhira?
◻ Kodi ndi lonjezo lotani limene Yehova wapanga ponena za chopondapo mapazi ake chophiphiritsira, dziko lapansi?
◻ Kodi ndani omwe adzathandiza kubwezeretsanso Paradaiso?
◻ Kodi ndi kuchokera pakati pa yani pamene Mfumu, Yesu Kristu, adzaika “akalonga m’dziko lonse lapansi”?
◻ Kodi ndi chokumana nacho chotenthetsa mtima chotani chomwe chingakhale chanu pamene chiwukiriro chichitika?
◻ Kodi ndi mtsogolo motani momwe mukuyembekezera awo okhala ndi kudzipereka kosasweka kwa Yehova?