Ripoti la Olengeza Ufumu
‘Mbiri Yabwino Kuchokera ku Maiko Akutali’
◻ MU GREENLAND yozizira ofalitsa ena pa ulendo wolalikira anakumana ndi wachichepere wa ku Norway yemwe analandira bukhu la Life—How Did It Get Here? By Evolution or by Creation? Komabe, iye sanasonyeze chikondwerero chokulira. Pa kuchezera kwawo kotsatira ku malo akutali ameneŵa, iye anaŵawuza kuti anali ataŵerenga bukhulo nthaŵi zochulukirapo ndipo anafuna mabukhu owonjezereka. Unyinji wa mabukhu ndi mabroshuwa anasiidwa kwa iye. Iye anaipidwa podziŵa kuti ofalitsawo sakabweranso chaka chinacho komabe anatenga adiresi ya Mbonizo. Mwezi umodzi pambuyo pake, mowadabwitsa, iye anagogoda pa khomo pawo. Iye anasimba kuti anali anagwa m’madzi owundana ndi chipangizo choyendera pamadzi owundana popita ku bwato lake, ndipo kenaka chinamtengera maola asanu ndi limodzi akuyenda kuti afikire Mbonizo. Iye anafuna kupeza mabukhu owonjezereka ndi kukambitsirana chowonadi. Anapezeka pa msonkhano madzulo amenewo napanga makonzedwe akumapezekako kamodzi pa mwezi. Iye anabwera pa kuchezetsa kwa woyang’anira wadera ndipo analimbikitsidwa kwambiri. Iye wachoka ku tchalitchi ndipo tsopano akulalikira mbiri yabwino m’dera lakwawo. Pamene madzi owundana m’nyengo yachisanu amlepheretsa kupita ku misonkhano ndi bwato, iye amapita ndi ndege ya helicopter, yomwe amalipira $150 ulendo umodzi.
Kodi ndi angati a ife amene tiyenera kuyesetsa ife eni ku mlingo umenewu ndi cholinga chofuna kupita patsogolo mu utumiki wathu?
◻ Anthu ambiri akuvomereza ku mbiri yabwino mu Madagascar. Ndi ofalitsa Aufumu 3,200 okha, 16,205 anapezeka pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu. Abalewo akupanga zoyesayesa zamphamvu za kufikira anthu onse pa chisumbucho.
Mwachitsanzo, 17 a ofalitsa 30 a Mpingo wa Isaonjo anasankhapo kuchitira umboni m’gawo limene linali pa mtunda wa makilomita ambirimbiri. Iwo ananyamuka pamudzi theka la ola patapita pakati pausiku. Kwa maola aŵiri iwo anayenda panjira zotsetsereka ndi m’matope. Kenaka analoŵa m’nkhalango yokhuthala pa 2:30 a.m. Popeza kuti mdima unakuta nkhalangoyo, abale ena anagwa m’ming’ankha. Ena anagwera m’zithaphwi za madzi m’matanthwe okumbika. Nkhalangoyo inali ndi misundu, ndipo tizirombo tambiri tinaŵaluma. Ambiri a alongowo anavutika mwanjirayi. Nthaŵi zina matopewo ankafika m’mawondo. Ofalitsa 17 onsewo anavulazidwa mwanjira ina ndi inzake, koma potsirizira pake anatuluka m’nkhalangoyo pa 6:30 a.m.!
Utumiki wakumunda unayamba pa 6:45 a.m. Anthu ambiri analandira ofalitsawo ndi manja aŵiri. Mmodzi amene sanatero poyamba anali mkazi wa mtsogoleri wachipembedzo Chachiprotesitanti. Iye anati: “Ndiri nacho chipembedzo changa; chimenecho nchokwanira kwa ine. Ndidziŵa zonse zimene Baibulo limaphunzitsa.” Mwamsanga pamene wofalitsayo anatulutsa magazine a Nsanja ya Olonda, mkaziyo anaikana iyo mwamwano, akumati: “Ndiri nazo kale zinthu zina zambiri zoŵerenga.” Koma iye anayamba kufunsa mafunso: “Kodi ndinu yani, ndipo muchokera kuti, ndipo ndani amene wakutumani?” Pambuyo poyankha moleza mtima ndi kusimba mwachidule kuyesayesa konse komwe anakupanga kufikira mudzi wake, mkaziyo analandira Nsanja ya Olonda, akumati: “Ndidzaigula. Kodi ndani angadziŵe kuti inu mwatumidwa ndi Mulungu?”
Pa 1:30 p.m., 17 amenewo anachoka m’gawolo namapita kunyumba, akumapanga ulendowo kwa maola ochepera pa anayi chifukwa chakuti anali adakali masana. Iwo anali otopa komabe achisungiko, ndipo nkhope zawo zinaŵala ndi chimwemwe. Iwo anati: “Linali tsiku losaiŵalika kwa ife 17 a mu Mpingo wa Isaonjo.”
Motsimikizirika, mzimu wa Yehova ukufulumiza atumiki ake odzipereka kulalikira mbiri yabwino Yaufumu “kumalekezero a dziko,” ndipo ambiri akuvomereza ku zoyesayesa zabwino za Mbonizo.—Machitidwe 1:8.
[Chithunzi patsamba 31]
Doko la Umanak, Greenland