“Chofalitsidwa cha Mboni za Yehova Chofunika Kuŵerengedwa”
Uwu unali mutu wa nkhani yowonekera pa December 23, 1988, mu Creston News Advertiser, ya ku Iowa, U.S.A. “Nthanthi ndi chipembedzo zimandikondweretsa,” akutero wolemba Randy Porter, “koma zofalitsidwazo zirinso ndi nkhani zosiyanasiyana za dziko zokondweretsa. . . .
“Kuwonjezerapo, ena angadabwe kudziŵa kuti magazinewo kaŵirikaŵiri amagwira mawu magwero ena a ukumu, pambali pa Baibulo. . . .
“Mwakutero, chofalitsidwa cha February [8] chimasonyezanso nkhani yaifupi ndi chithunzithunzi cha mtundu cha mwala wa mzinda wa Iowa, geode. Nkhaniyo imanena kuti anthu ali ngati mageode. Ngakhale kuti ali osawoneka bwino kunja, pamene atsegulidwa mageode amavumbula kukongola kwa mkati konyezimira, ndi krustalo. Munthu, nayenso, angakhale wosawoneka bwino kunja, ndi kukhaladi wabata ndi wamanyazi; komabe, pamene munthu apeza nthaŵi ‘kuzoloŵerana naye, iwo amatseguka ndi kukusonyezani kukongola kwa mkati kumene kumanyezimira.’ . . .
“Kope la January [22] (Chingelezi) linali ndi nkhani zina zambiri zomwe mwinamwake sizikanandipitirira! Mwachitsanzo, anthu ambiri amva ponena za njuchi zakupha za mu Afirika, koma nkhani ina inasonyeza mmene akatswiri a tizirombo ‘amaikira kogwirira mawu’ ku njuchizo. Kolinganizidwa ndi ainjiniya a ku Amereka, kachipangizo ka microprocessor kokwana kuikidwa kumbuyo kwa njuchi kamakhozetsa asayansi kulamulira mayendedwe a njuchizo kwa mtunda wa kilomita imodzi kapena aŵiri.”
Galamukani! iri ndi atola nkhani ake m’maiko ambiri kuzungulira dziko motero iyo iri ndi magwero a nkhani omwe ambiri samaŵafikira. Tilingalira kuti mudzapindula ndi kukondwera ndi nkhani zosangalatsa za Galamukani! Iyo iri ndi avereji ya kusindikiza kwa makope 11,250,000 pa magazine amodzi ndipo ikufalitsidwa m’zinenero 53.
Chonde tumizani sabusikripishoni ya chaka chimodzi ya Galamukani! Ndatsekeramo K40 (Zambia) kaamba ka makope 12 a magazine ameneŵa (kope limodzi pa mwezi).