“Chiyeso cha Kuwona kwa Chikondi Chanu”
KODI mawu ali pamwambawo akukukumbutsani chiyani? Chizunzo ndi zovuta? Kuphedwera chikhulupiriro? Mawu amenewo analembedwa poyambapo ndi mtumwi Paulo m’kalata ya kwa Akristu mu Korinto wakale. Iwo ali a chifuno chokulira kwa anthu a Yehova lerolino chifukwa chakuti ‘kuwona kwa chikondi chawo’ kukuyesedwa mofananamo. Koma motani? Kuti tiyankhe, tiyeni tisanthule kakhazikitsidwe ka mawu a Paulo.
Maziko a Chiyeso
Zaka makumi aŵiri pambuyo pa kupezedwa kwa Chikristu, mpingo wa mu Yerusalemu unali m’kusoŵa kwa ndalama koipitsitsa. Pokhala pamaziko amenewo a chitsutso ndi kunyada Kwachiyuda, Akristu m’zaka zonsezo anali ‘atapirira chitsutso chachikulu cha zowawa,’ ngakhaledi kukumana ndi ‘kulandidwa chuma chawo.’ (Ahebri 10:32-34) Thandizo lochokera kunja linali lofunikadi.
Motsimikizirika, abale awo Akunja angakhale anafulumizidwa kuthandiza ku tsoka lawolo. Ndiiko nkomwe, iwo anali ndi “mangawa” apadera kwa Akristu okhala m’Yerusalemu. Kodi ku Yerusalemu sikumene kunachokera mbiri yabwino kufalikira kupita kwa Akunja? Paulo akupereka lingaliro lakuti: “Ngati Akristu Achiyuda anagawana chuma chawo chauzimu ndi Akunja, Akunja ali ndi thayo lowonekera la kuthandizira ku zosoŵa zawo zakuthupi.”—Aroma 15:27, The New English Bible.
Kulinganiza Zopereka
Paulo anali atalamulidwa ndi bungwe lolamulira “kukumbukira [Akristu] aumphawi.” (Agalatiya 2:10) Chotero iye anatumiza mawu kwa Akristu mu Europe ndi Asia Minor onena za mkhalidwe m’Yerusalemu. Panopa pali malangizo a Paulo: “Koma za chopereka cha kwa oyera mtima, monga ndinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero chitani inunso. Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.”—1 Akorinto 16:1, 2.
Mwa kulinganiza ndalama zawo mwanjirayi, palibe aliyense amene akadzimva kukhala wokakamizidwa kapena kudidikizidwa pamene zopereka zinkatengedwadi. Abale analibe mantha aliwonse kuti ndalama zawo zikadyedwa kapena kuwonongedwa. Kokha ‘amuna ovomerezedwa’ ndi amene akaloledwa kupereka ndalama zoperekedwazo, Paulo akawaperekeza iwo ngati chidawoneka kukhala choyenerera.—1 Akorinto 16:3-5.
Kodi kuvomereza kwa Akorinto kunali kotani? Ngakhale kuti abale mwachiwonekere anachita moyanja chilangizo cha Paulo, zoperekazo sizinatumizidwe nkomwe. (2 Akorinto 8:6, 10, 11) Mwinamwake akulu anakhala otanganitsidwa ndi kuthetsa mikangano mumpingo, chisembwere, ndi mavuto ena amene Paulo anawalembera.
‘Chulukani m’Kupatsa Kwachifundo’
Ngakhale zinali tero, Paulo anawalembera kalata ina akumanena kuti: “Ndipo tikudziŵitsani, abale, chisomo cha Mulungu chopatsika mwa Mipingo ya ku Makedoniya, kuti m’chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chawo, ndi kusauka kwawo kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuwoloŵa mtima kwawo. Pakuti monga mwa mphamvu yawo, ndichitapo umboni, inde koposa mphamvu yawo, anachita eni ake, natiumiriza ndi kutidandaulira za chisomocho, ndi za chiyanjano cha utumiki wa kwa oyera mtima; ndipo, si monga tidayembekeza; koma anayamba kudzipereka okha kwa Ambuye, ndi kwa ife mwa chifuniro cha Mulungu. Kotero kuti tinadandaulira Tito, kuti monga anayamba kale, chomwechonso atsirize kwa inu chisomo ichinso. Koma monga muchulukira m’zonse, m’chikhulupiriro, ndi m’mawu, ndi m’chidziŵitso, ndi m’khama lonse, ndi m’chikondi chanu cha kwa ife, chulukaninso [m’kupatsa uku kwachifundo, NW].”—2 Akorinto 8:1-7.
Chitsanzo cha Amakedoniya odzipereka nsembe chinapatsa Akorinto kulingalirapo. Korinto anali wotchuka chifukwa cha chuma, zosangulutsa, ndi malonda. Ena a abale kumeneko angakhale analiko osauka, komabe, chapamodzi, mosakaikira mpingowo unali bwinopo kuposa Akristu a ku Makedoniya omwe anali ‘osauka kwenikweni.’ Komabe, Amakedoniya anali atapereka “koposa mphamvu yawo.” Iwo sanafunikire kusonkhezeredwanso ndi Paulo kuti apereke. Nkulekeranji, popeza kuti iwo ‘anapempha’ Paulo ‘mochonderera’ kuti agawanemo m’kuperekaku! Ichi chinali chowonekera kuti Akristu a ku Makedoniya mowonadi ‘anadzipereka okha kwa Ambuye [m’kudzipereka kosakakamizidwa] ndi kwa [Paulo ndi mabwenzi ake],’ akumagonjera ku chitsogozo chawo chateokratiki.
Anayesedwa ku Chikondi Chawo ndi Kuwoloŵa Manja
Kodi Akorinto akafulumizidwa mofananamo ‘kuchuluka m’kupatsa kwachifundo’? Pamene anachezera Korinto choyamba, Paulo anakakamizidwa kudzichilikiza iyemwini monga wosoka mahema. (Machitidwe 18:1-3) Iye anapitirizabe ndi kachitidweka ka kudzichilikiza ngakhale pamene mpingo unakula kumeneko, akumakana kugwiritsira ntchito “ulamuliro” wake monga mlengezi wa nthaŵi zonse kulandira chilikizo la ndalama.—1 Akorinto 9:3-12.
Akutero wochitira ndemanga pa Baibulo Thomas Scott kuti: “Mwinamwake, iye anawona zinazake m’kachitidwe ka zinthu ka Akristu a ku Korinto, zimene poyambapo zinampangitsa iye kukana kulandira chilikizo lirilonse kuchokera kwa iwo.” Mwinamwake atayambukiridwa ndi kukondetsa zakuthupi kowazinga, Akorinto olemera ochepera angakhale anali osafunitsitsa kukhala owoloŵa manja. Paulo angakhale anaopanso kuti Akorinto okhoterera ku malonda akakaikira cholinga chake adakalandira chilikizo la ndalama. Pangakhale panalidi awo amene, mofanana ndi ena mu Tesalonika, anali aulesi ndipo anafuna chodzikhululukira cha kukhalirira pa za Akristu anzawo.—2 Atesalonika 3:7-12.
Mulimonse momwe zingakhale zidaliri, Paulo ndi anzake anasankha kudzichilikiza iwo eni, ‘mmalo mwakuti tisaike chokhumudwitsa ku uthenga wabwino wonena za Kristu.’ (1 Akorinto 9:12) Ngakhale ndi tero, m’kupita kwa nthaŵi, Paulo anagwera m’vuto la ndalama, mbiri yake inafikira abale osauka okhala mu Filipi. Paulo anauza Akorinto kuti: “Ndinalanda za mipingo yina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu; ndipo pakukhala nanu, ndi kusoŵa, sindinasaukitsa munthu aliyense; pakuti abale kuchokera ku Makedoniya, [mwachidziŵikire Filipi] anakwaniritsa kusoŵa kwanga; ndipo m’zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.”—2 Akorinto 11:8, 9; yerekezerani ndi Afilipi 4:15, 16.
Zowona, Paulo iyemwini anavomereza kuti ‘sakalandira mphatso’ iriyonse kwa Akorinto. Koma pamene Paulo anayesera kukana kuwoloŵa manja kwa mkazi wa ku Filipi wotchedwa Lidiya, mkaziyo ‘anawaumiriza iwo.’ (Machitidwe 16:15) Kodi Akorinto anasonyeza kudera nkhaŵa kowumirira kofananako kaamba ka ubwino wakuthupi wa Paulo? Nchokaikiritsa. Ngakhale zinali tero, Paulo anazindikira kuti mkhalidwe wokhudza mpingo wa m’Yerusalemu unapereka mwaŵi wa kuyesa kaya Akorinto anali ndi chizoloŵezi cha kusawoloŵa manja kapena ngati iwo anasinthira ku kuwoloŵa manja. Chotero iye anachonderera kuti:
“Sindinena ichi monga kulamulira, koma kuyesa . . . chowonadi cha chikondi chanunso. Pakuti sinditero kuti ena akamasuke, ndi inu musautsidwe [uku ndiko kuti, osati kuti ena akamasuke ndipo inu mukavutike]; koma mwa kulingana kuchuluka kwanu kukwanire kusoŵa kwawo nthaŵi ya makono ano, kutinso kuchuluka kwawo kukwanire kusoŵa kwanu. Kuti pakhale chilingano; monga kwalembedwa, wosonkhetsa chambiri sichinamtsalira; ndi iye wosonkhetsa pang’ono sichinamsowa.”—2 Akorinto 8:8, 13-15.
Mwachiwonekere, Akorinto anapambana chiyeso chawo. Nthaŵi ina pambuyo pake Paulo anasimba kuti: “Pakuti kunakondweretsa a ku Makedoniya ndi Akaya [kumene Korinto anali] kuchereza osauka a kwa oyera mtima a ku Yerusalemu.”—Aroma 15:26.
Kuyang’anizana ndi Chiyesocho Lerolino
Komabe, kodi tikupambana ziyeso za chikondi ndi kuwoloŵa manja zimene zimadzibweretsa zokha lerolino? Tikukhala mu “nthaŵi zovuta kuchita nazo.” (2 Timoteo 3:1-5, NW) Zodidikiza za ndalama zimatsendereza ambiri aife. Ndipo nthaŵi zina “chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo” zimapanga zodidikiza zawo. (1 Yohane 2:16) Ndi chopepuka chotani nanga mmene chiliri kukhala wodzidalira, wosadera nkhaŵa zosoŵa za ena!
Monga gulu, Mboni za Yehova lerolino zakumana ndi ziyeso za chikondi chawo chaubale m’njira yapadera. Mwachitsanzo, pa March 3, 1985, chivomezi chinakantha Santiago, Chile. Mazana angapo a abale anawonongedwera nyumba zawo ndi chuma. Mofulumira, mipingo inalinganiza zoyesayesa zothandiza. “Mkati mwa maola angapo,” akusimba tero abalewo, “ena anayamba kubwera ndi zakudya, zovala, zofunda ndi zinthu zina zofunikira.” Zopereka zinabweranso kuchokera ku dziko lonse. Zochitika zofananazo zachitika nthaŵi zochulukira mkati mwa zaka.
Koma sitifunikira kuyembekezera tsoka kudzatsimikizira chikondi chathu chaubale. Mkristu mnzathu atavutika ndi zodidikiza zandalama, tingakhale ofulumira ku zosoŵa zake, kuchita zoposa kunena kuti, “Mukafunde ndi kukhuta.” (Yakobo 2:15, 16) Ndipo bwanji ponena za omwe ali mu utumiki wa nthaŵi zonse amene “amakhala ndi moyo ndi uthenga wabwino.” Mofanana ndi Paulo, otereŵa samakakamiza kapena kuyembekezera thandizo landalama kwa omwe akuwatumikira. Mosasamala kanthu za izo, ambiri asonkhezeredwa kusonyeza kuwoloŵa manja kwa awo amene amagwira ntchito ‘kufesa zinthu zauzimu’ mmalo mwawo.—1 Akorinto 9:11, 14.
Ndipo kodi bwanji ponena za zosoŵa za gulu la dziko lonse la Mboni za Yehova? 1989 Yearbook of Jehovah’s Witnesses ikusimba kuti “mkati mwa chaka chautumiki cha 1988 Watch Tower Society inawononga $29,834,676.97 m’kusamalira apainiya apadera, amishonale, ndi oyang’anira oyendayenda m’magawo awo autumiki.” Ndalama zambiri zinawonongedwanso m’kusamalira ndi kugula zinthu za nthambi, zipangizo, makina, mapepala—kusatchulapo zowonongedwa zoposapo za kusamalira banja la Beteli la dziko lonse, limene tsopano likufika m’chiwerengero choposa pa 9,000! Kuwonjezerapo, maprojekiti ena ndi kukonzanso 18 pakali pano zidakachitikabe m’nthambi zosiyanasiyana, ndipo 19 pa malikulu athu mu Brooklyn, New York. Kodi mukugaŵanamo m’kupanga zopereka ku ntchito ya dziko lonse imeneyi?
Monga mmene zinaliri m’zaka za zana loyambirira, lerolino onse akugawana m’kusamalira thayo limeneli, kuphatikizapo osauka, amene, ndi zopereka zawo zochepera, atsimikizira kukhala magwero a chilikizo la ndalama la Sosaite. Ena amachipeza kukhala chothandiza kutsatira chitsanzo chokhazikitsidwa pa 1 Akorinto 16:2 ndipo mokhazikika amalinganiza ndalama zawo zaumwini kuperekedwa pa Nyumba Yaufumu ya kumaloko. Ena angasankhenso kupereka ndalama mwachindunji ku Watch Tower Society pa Box 21598, Kitwe, kapena ku imodzi ya maofesi ake anthambi.
Khalani otsimikiziridwa kuti Yehova akuwona awo amene, kupyolera m’kuwoloŵa manja kwawo, amatsimikizira kuwona kwa chikondi chawo. Musadzimane madalitso inu eni! Paulo analonjeza kuti: “Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsa chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m’zinthu zonse, nthaŵi zonse, mukachulukire ku ntchito yonse yabwino.”—2 Akorinto 9:8.
[Bokosi patsamba 26]
MMENE ENA AMAPEREKERA KU NTCHITO YAUFUMU
◻ MPHATSO: Zopereka zaufulu za ndalama zingatumizidwe mwachindunji ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 21598, Kitwe, kapena ku ofesi yanthambi ya Sosaite yakumaloko. Zinthu zonga ngati munda, limodzinso ndi zokometsera kapena zinthu zina zamtengo wapatali, zingaperekedwenso. Kalata yachidule yolongosola kuti zimenezo ziri zopereka zaufulu iyenera kutsagana ndi zopereka zimenezi.
◻ MAKONZEDWE A CHOPEREKA CHOKHALA NDI MALIRE: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuti zisungidwe mwa kuikiziridwa, ndi makonzedwe akuti mwini wake atazifuna, zidzabwezeredwa kwa woperekayo.
◻ INSHUWALANSI: Watch Tower Society ingatchulidwe kukhala yodzapindula ndi makonzedwe a inshuwalansi ya moyo kapena makonzedwe a kuleka ntchito/ndi kulandira penshoni. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe aliwonse oterewo.
◻ KUIKIZIRIDWA: Ndalama zosungidwa ku banki mu yotchedwa savings account zingaikiziridwe ku Sosaite. Ichi chitachitidwa, chonde dziŵitsani Sosaite. Ndalama, mapangano, ndi katundu zingaperekedwenso pansi pa makonzedwe opindulitsa woperekayo mkati mwa moyo wake wonse. Njira imeneyi imathetsa ndalama zowonongedwa ndi kusatsimikizirika kwa lamulo lokhudza chuma chamasiye, pamene chikutsimikiziridwa kuti Sosaite idzalandira katunduyo pa imfa.
◻ MAPANGANO A KUGAŴIRA CHUMA CHAMASIYE: Katundu kapena ndalama zingaikiziridwe ku Watch Tower Society kupyolera mwa pangano la kugaŵa katundu loikidwa mwa lamulo. Kope liyenera kutumizidwa ku Sosaite.
Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka ndi malangizo onena za nkhani zoterezi, lemberani ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 21598, Kitwe, kapena ku ofesi yanthambi ya Sosaite yakumaloko.