Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Kuvumbulidwa ndi Mafanizo a Munda Wampesa
YESU ali ku kachisi. Iye wangogonjetsa kumene atsogoleri achipembedzo amene anafuna kudziŵa kuti anali kuchita zinthu ndi ulamuliro wa yani. Asanachire ku kusokonezeka kwawo, Yesu akufunsa kuti: “Nanga mutani?” Ndipo kenaka mwa kugwiritsira ntchito fanizo akuwasonyeza mtundu wa anthu amene iwo alidi.
“Munthu anali nawo ana aŵiri,” Yesu akusimba tero. “Nadza iye kwa woyamba nati, Mwanawe, kagwire lero ntchito ku munda wampesa. [Poyankha uyu adati, ‘ndidzatero, Mbuyanga,’ koma sanapite, NW]. Ndipo anadza kwa winayo, natero momwemo. Ndipo [poyankha uyu adati, ‘sindidzapita.’ Pambuyo pake analapa napita, NW]. Ndani wa aŵiriwo anachita chifuniro cha atate wake?” Yesu akufunsa tero.
“Wachiŵiriyo,” adani ake akuyankha tero.
Chotero Yesu akulongosola kuti: “Indetu ndinena kwa inu, kuti amisonkho ndi akazi achiŵereŵere amatsogolera inu, kuloŵa Ufumu wa [Mulungu, NW].” Kwenikwenidi, amisonkho ndi akazi achiŵereŵere poyambapo anakana kutumikira Mulungu. Koma kenaka, mofanana ndi mwana wachiŵiriyo, analapa ndipo anamtumikira. Kumbali ina, atsogoleri achipembedzo, mofanana ndi mwana woyamba, anadzinenera kutumikira Mulungu, komabe, monga mmene Yesu akudziŵitsira: “Yohane [Mbatizi] anadza kwa inu m’njira ya chilungamo, ndipo simunamvera iye; koma amisonkho ndi akazi achiŵereŵere anam’mvera iye; ndipo inu, mmene munachiwona, simulapa pambuyo pake, kuti mumvere iye.”
Kenaka Yesu akusonyeza kuti kulephera kwa atsogoleri achipembedzo ameneŵa sikuli kokha m’kunyalanyaza kutumikira Mulungu. Ayi, koma iwo alidi odetsedwa, anthu oipa. “Panali munthu mwini banja,” Yesu akusimba tero, “amene analima munda wampesa, nauzunguniza linga, nakumba umo moponderamo mpesa, namanga nsanja, naukongoletsa kwa olima munda, namuka kwina. Ndipo pamene nyengo ya zipatso inayandikira, anatumiza akapolo ake kwa olima mundawo, kukalandira zipatso zake. Ndipo olimawo anatenga akapolo ake, nampanda mmodzi, wina namupha, wina namponya miyala. Anatumizanso akapolo ena, akuchuluka oposa akuyambawa; ndipo anawachitira iwo momwemo.”
“Akapolo” ali aneneri amene “mwini banja,” Yehova Mulungu, anatumiza kwa “olima” a “munda [wake] wampesa.” Olima ameneŵa ali oimira otsogolera a mtundu wa Israyeli, mtundu umene Baibulo limauzindikiritsa kukhala “munda wampesa” wa Mulungu.
Popeza kuti “olimawo” akuchitira moipa ndi kupha “akapolo,” Yesu akulongosola kuti: “Koma pambuyo pake [mwini wa munda wampesa] anatumiza kwa iwo mwana wake, nati, Adzamchitira mwana wanga ulemu. Koma olimawo mmene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake. Ndipo anamtenga iye, namponya kunja kwa munda, namupha.”
Tsopano, akumalankhula ndi atsogoleri achipembedzowo, Yesu akufunsa kuti: “Tsono atabwera mwini munda, adzachitira olimawo chiyani?”
“Chifukwa chakuti ali oipa,” iwo akuyankha tero, “Iye, adzawononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.”
Chotero atsogoleri achipembedzowo mosafuna akudzibweretsera okha chiweruzo, popeza kuti iwo akuphatikizidwa pakati pa “olima” Achiisrayeli a “munda wampesa” wa Yehova wa mtundu wa Israyeli. Zipatso zimene Yehova akuyembekezera kuchoka kwa olima oterowo ndizo chikhulupiriro mwa Mwana wake, Mesiya weniweni. Chifukwa cha kulephera kwawo kupereka zipatso zoterozo, Yesu akuchenjeza kuti: “Kodi simunaŵerenga konse m’Malembo [pa Salmo 118:22, 23], Mwala umene anaukana omanga nyumba womwewu unakhala mutu wa pangondya: Ichi chinachokera kwa [Yehova, NW], ndipo chiri chozizwitsa m’maso mwathu? Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake. Ndipo iye wakugwa pa mwala uwu adzaphwanyika; koma iye amene udzamgwera, udzampera iye.”
Alembi ndi akulu ansembe azindikira tsopano kuti Yesu akulankhula ponena za iwo, ndipo afuna kumupha, “wolowa” weniweni. Chotero mwaŵi wa kukhala olamulira mu Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa iwo monga mtundu, ndipo mtundu watsopano wa ‘olima munda wampesa’ udzapangidwa, umene udzabala zipatso zoyenera.
Popeza kuti atsogoleri achipembedzo akuwopa anthu, amene amalingalira Yesu kukhala mneneri, iwo sakuyesera kumupha pa chochitika chimenecho. Mateyu 21:28-46; Marko 12:1-12; Luka 20:9-19; Yesaya 5:1-7.
◆ Kodi ana aŵiri a m’fanizo loyamba la Yesu akuimira yani?
◆ Kodi ndani amene akuimiridwa ndi “mwini banja,” “munda wampesa,” “olima,” “akapolo,” ndi “wolowa” m’fanizo lachiŵiri?
◆ Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa ‘olima munda wampesa,’ ndipo kodi ndani amene adzaŵalowa m’malo?