Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Antchito m’Munda Wampesa
“AMBIRI oyamba,” Yesu wangomaliza kunena kuti, “adzakhala akuthungo, ndi akuthungo adzakhala oyamba.” Tsopano iye akuchitira fanizo ichi mwa kukamba nkhani. “Ufumu wa kumwamba,” iye akuyamba, “ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka m’mamawa kukalembera antchito m’munda wampesa.”
Yesu akupitiriza kuti: “Ndipo pamene [mwini banjayo] adapangana ndi antchito, pa rupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza ku munda wake. Ndipo anatuluka dzuŵa litakwera, nawona ena ataima chabe pabwalo; ndipo kwa iwo anati: Pitani inunso kumunda, ndipo ndidzakupatsani chimene chiri choyenera. Ndipo iwo anapita. Ndiponso anatuluka usana, ndimonso popendeka dzuŵa, nachita chimodzimodzi. Ndipo poyandikira madzulo anatuluka, napeza ena ataima; nanena kwa iwo, Mwaimiranji kuno dzuŵa lonse chabe? Iwo ananena kwa iye, Chifukwa palibe munthu anatilemba. Iye anati kwa iwo, Pitani inunso ku mundawo wampesa.”
Mwini banjayo, kapena mwini wa munda wampesayo, ali Yehova Mulungu, ndipo munda wampesawo uli mtundu wa Israyeli. Antchito m’munda wampesawo ali anthu omwe abweretsedwa mu pangano la Chilamulo; iwo mwachindunji ali Ayuda okhala m’masiku a atumwi. Chiri kokha ndi antchito a tsiku lonse omwe chivomerezo cha malipiro chapangidwa. Malipirowa ali rupiya latheka limodzi tsiku limodzi. Popeza kuti “dzuŵa litakwera” iri nthaŵi ya 9:00 a.m., awo oitanidwa dzuŵa litakwera, usana, popendeka dzuŵa, ndi madzulo akugwira ntchito, aliyense payekha, kokha maora 9, 6, 3, ndi 1.
Antchito a maora 12, kapena tsiku lonse, akuimira atsogoleri Achiyuda omwe akhala otanganitsidwa mopitirizabe mu utumiki wa chipembedzo. Iwo sali ofanana ndi ophunzira a Yesu, omwe, kwa mbali yaikulu ya miyoyo yawo, anakhala olembedwa ntchito m’kusodza kapena ntchito zina zakudziko. Osati kufikira mu chirimwe cha 29 C.E. ndipamene “mwini banja” anatumiza Yesu Kristu kudzasonkhanitsa amenewa kukhala ophunzira ake. Iwo mwakutero anakhala “akuthungo,” kapena antchito a madzulo m’munda wampesa.
Pomalizira, tsiku logwira ntchito lophiphiritsiralo likutha ndi imfa ya Yesu, ndipo nthaŵi ikubwera ya kulipira antchitowa. Lamulo la nthaŵi zonse lolipirira womalizira ndi woyamba likutsatiridwa, monga momwe likulongosoledwera: “Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitawo wake, kaitane antchito nuwapatse iwo kulipira kwawo, uyambe kwa omalizira kufikira kwa woyamba. Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense rupiya latheka limodzi. Ndipo mmene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse rupiya latheka. Koma mmene iwo analandira, anaderera kwa mwini banja, nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing’ono ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapirira kuwawa kwa dzuŵa ndi kutentha kwake. Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa rupiya latheka limodzi? Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. Sikuloleka kodi kwa ine kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena diso lako laipa kodi chifukwa ine ndiri wabwino?” M’kumaliza Yesu anabwereza nsonga yopangidwa poyambirirapo, akumanena kuti: “Omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.”
Kulandiridwa kwa rupiya latheka kunachitika, osati pa imfa ya Yesu, koma pa Pentekoste wa 33 C.E., pamene Kristu, “kapitawo,” anatsanulira mzimu woyera pa ophunzira ake. Ophunzira a Yesu amenewa anali ofanana ndi “omalizira,” kapena antchito otuluka madzulo.
Rupiya lathekalo silinaimire mphatso ya mzimu woyera weniweniwo. Rupiya latheka chinali chinachake cha ophunzirawo kuti achigwiritsire ntchito pano pa dziko lapansi. Chinali chinachake chimene chinatanthauza umoyo wawo, moyo wawo wosatha. Unali mwaŵi wa kukhala Israyeli wauzimu, odzozedwa kulalikira ponena za Ufumu wa Mulungu.
Mwamsanga awo olembedwa ntchito poyamba anawona kuti ophunzira a Yesu analipiridwa, ndipo iwo anawona iwo akugwiritsira ntchito rupiya lawo latheka lophiphiritsira. Koma iwo anafuna zoposa mzimu woyera ndi mwaŵi wake wa Ufumu woyanjana nawo. Kung’ung’udza kwawo ndi zitsutso zinatenga mtundu wa kuzunza ophunzira a Kristu, antchito m’munda wampesa “otuluka madzulo.”
Kodi kukwaniritsidwa kwa m’zana loyamba kumeneku kuli kukwaniritsidwa kokha kwa fanizo la Yesu? Ayi, atsogoleri achipembedzo a Chikristu cha Dziko m’zana la 20 lino, chifukwa cha malo awo ndi mathayo, akhala “oyamba” kulembedwa ntchito m’munda wampesa wophiphiritsira wa Mulungu. Iwo analingalira olalikira odzipereka oyanjana ndi Watch Tower Bible and Tract Society kukhala “omalizira” kukhala ndi thayo lirilonse lotsimikizirika mu utumiki wa Mulungu. Koma, m’chenicheni, ali amenewa amene atsogoleri achipembedzo ananyoza omwe alandira rupiya latheka—ulemu wa kutumikira monga oimira odzozedwa a Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Mateyu 19:30–20:16.
◆ Nchiyani chomwe chikuimiridwa ndi munda wampesa? Ndani omwe akuimiridwa ndi mwini wake wa munda wampesa ndi antchito a maora 12 ndi 1?
◆ Ndi liti pamene tsiku la ntchito lophiphiritsira linatha, ndipo ndi liti pamene malipirowo anaperekedwa?
◆ Nchiyani chomwe chikuimiridwa ndi malipiro a rupiya latheka?