“Onse Okhala Mmanda Achikumbukiro”
KODI mungathe kutsimikizira kuti unyinji wa akufa adzakhalanso ndi moyo? Inde, popeza Yesu anati: “Musazizwe ndi ichi, chifukwa ikudza nthaŵi imene onse ali mmanda achikumbukiro adzamva mawu ake nadzatulukamo.” (Yhane 5:28, 29, NW) Tawonani mawuwo “manda achikumbukiro,” amene amapezeka kokha mu New World Translation. Amatikumbutsa za kufunika kwa chikumbukiro cha Mulungu m’chiukiriro.
Kodi nchifukwa ninji mawu ozoloŵereka akuti, “manda,” sakugwiritsiridwa ntchito? Chifukwa chakuti Yesu sanagwiritsire ntchito zochuluka za liwu Lachigriki lakuti taʹphos, limene limatanthauza “manda” kapena “msitu.” Ndithudi, sionse amene adamwalira anaikidwa m’manda enieni, kapena taʹphoi. Komabe, awo amene Mulungu adzaukitsa m’chiukiriro ali m’chikumbukiro chake. Zimenezi zasonyezedwa ndi kugwiritsira ntchito kwa Yesu mumpangidwe wa zochuluka wa mne·meiʹon, mawu amene ali ogwirizana kwambiri ndi Achigriki amene kwakukulukulu amatanthauza “kukumbukira.” (Mateyu 16:9; Marko 8:18) Greek-English Lexicon yolembedwa ndi H. G. Liddell ndi R. Scott imatembenuza mne·meiʹon kukhala “cholembapo cha chikumbutso, chokumbukirira, mbiri ya munthu kapena chinthu, . . . manda, . . . kŵirikaŵiri, chokumbutsira.”
Motero, New World Translation imasiyanitsa pakati pa mawuwo taʹphos ndi mne·meiʹon. Kulinso kokondweretsa kuwona kuti matembenuzidwe ambiri a Baibulo mofananamo amagwiritsira ntchito mawu osiyana aŵiri pa Mateyu 23:29 pamene mawu aŵiri onsewo Achigriki amapezeka. Revised Standard Version imamasulira mawuwo motere: “Mumamanga manda [mpangidwe wa taʹphos] a aneneri ndi kukometsera zikumbukiro [mpangidwe wa mne·meiʹon] za olungama.”
Mlengi wa munthu samaiwala zitsanzo za moyo wa anthu mamiliyoni zikwi zambiri amene anakhalapo ndi moyo. (Salmo 139:16; 147:4; Mateyu 10:30) M’nthaŵi yake yokwanira, iye adzakumbukira awo okhala “mmanda achikumbukiro” ndikuwabwezeretseranso ku moyo padziko lapansi loyeretsedwa. Tiri olimbikitsidwa ndi otonthozedwa chotani nanga pakudziŵa kuti chikumbukiro changwiro cha Mulungu sichingalephere!—Chivumbulutso 20:11-13.