“Mawu a Mulungu Ngamoyo Ndipo Amapereka Mphamvu”
1, 2. (a) Kodi chimachititsa masinthidwe m’miyoyo ya ofikira kukhala Akristu nchiyani? (b) Kodi Baibulo lingasonkhezere munthu mwakuya chotani?
CHAPAKATI pa zaka za zana loyamba C.E, mtumwi Paulo analembera kalata mpingo Wachikristu m’Roma. M’kalatayo iye anagogomezera chofunika chakuti Akristu owona afunikira kupanga masinthidwe. Iye anati: “Musafanizidwe ndi makhalidwe a pansi pano: koma mukhale osandulika, mwa kukonzanso kwa mtima wanu, kuti mukazindikire chimene chiri chifuniro cha Mulungu, chabwino, ndi chokondweretsa, ndi changwiro.” (Aroma 12:2) Kodi nchiyani chimene chimasanduliza otsatira a Yesu, kusintha njira yawo yeniyeni ya maganizo? Kwakukulukulu, ndiyo mphamvu ya Mawu a Mulungu, Baibulo.
2 Paulo anansonyeza mmene Baibulo lingatisonkhezerere kwambiri pamene analemba kuti: “Mawu a Mulungu ngamoyo ndipo amapereka mphamvu ndipo ali akuthwa koposa lupanga lirilonse lakuthwa konsekonse ndipo amapyoza ngakhale ku kugawidwa kwa moyo ndi mzimu, ndi molumikizira ndi mafuta awo a mafupa, ndipo ali okhoza kuzindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.” (Ahebri 4:12, NW) Ndithudi, mphamvu yapadera ya Baibulo kuchititsa masinthidwe otero mwa anthu ndiyo umboni wokopa wakuti sindilo mawu wamba aanthu.
3, 4. Kodi maumunthu a Akristu amasinthidwa kumlingo wotani?
3 Liwu Lachigriki lotembenuzidwa “kusandulizidwa” pa Aroma 12:2 lachokera ku me·ta·mor·phoʹo. Limasonyeza kusintha kotheratu, mofanana ndi mbozi ya nthowa imene imasintha kukhala gulugufe. Imasintha kotheratu kotero kuti Baibulo limalankhula za iyo kukhala kusintha kwaumunthu. M’vesi lina la Baibulo, timaŵerenga kuti: “Mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake, ndipo munavala watsopano, amene ali kukonzeka kwatsopano, kuti akhale nacho chizindikiritso, monga mwa chifaniziro cha iye amene anamulenga iye.”—Akolose 3:9, 10.
4 Polembera mpingo wa ku Korinto, Paulo anasonyeza mlingo wa masinthidwe m’maumunthu umene unachitika m’zaka za zana loyamba. Iye anati: “Adama, kapena opembedza mafano, kapena achigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudzipsa ndi amuna, kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzaloŵa ufumu wa Mulungu. Ndipo ena a inu munali otere; koma munasambitsidwa.” (1 Akorinto 6:9-11) Inde, anthu achisembwere ndi andeu, mbala ndi zidakwa, anasandulizidwa kukhala Akristu abwino.
Masinthidwe Amaumunthu Lerolino
5, 6. Kodi umunthu wa mnyamata wina unasinthidwa kotheratu motani ndi Baibulo?
5 Masinthidwe amaumunthu ofananawo akuwoneka lerolino. Mwachitsanzo, m’nyamata wina wochepa Kumwera kwa Amereka anasiidwa wamasiye pamsinkhu wa zaka zisanu ndi zinayi. Iye anakula popanda chitsogozo cha makolo ndipo anakulitsa mavuto aumunthu adzawoneni. Iye akusimba kuti: “Panthaŵi imene ndinali ndi zaka 18, ndinali womwererekera kotheratu ndi mankhwala ogodomalitsa ndipo ndinali nditaloŵa kale m’ndende kaamba ka kuba kuti ndichilikize chizoloŵezicho.” Komabe, adzakhali ake, anali mmodzi wa Mboni za Yehova, ndipo potsirizira pake anali wokhoza kum’thandiza.
6 M’nyamatayo akulongosola kuti: “Adzakhali anga anayamba kuphunzira nane Babibulo, ndipo pa miyezi isanu ndi iŵiri ndinali wokhoza kuwonjoka m’chizoloŵezi cha mankhwala ogodomalitsa.” Iye anawonjokanso kwa atsamwali ake apapitapo napeza mabwenzi atsopano pakati pa Mboni za Yehova. Iye akupitirizabe kuti: “Mabwenzi atsopano amenewa, limodzi ndi phunziro lokhazikika la Baibulo, zinandikhozetsa kupanga kupita patsogolo ndipo potsirizira pake kupatulira moyo wanga kutumikira Mulungu. Inde, amene kale anali womwerekera ndi mankhwala ogodomalitsa ndi mbala uyu tsopano ali Mkristu wokangalika, ndi waudongo mmoyo wake. Kodi masinthidwe aakulu otere muumunthu anatheka bwanji? Kudzera mwa mphamvu ya Baibulo.
7, 8. Fotokozani mmene chothetsa nzeru chaumunthu chovuta chinathetsedwera mwa chithandizo cha Baibulo.
7 Chitsanzo china chikuchokera kumwera kwa Europe. Konko, m’nyamata wina anakula ali ndi chothetsa nzeru chovuta muumunthu: kukwiya msanga. Anaphatikizidwa m’ndewu mosalekeza. M’kati mwa mkangano wina wa banja, iye anamenya ngakhale atate wake, akuwagwetsera pansi! Komabe, potsirizira pake, iye anaphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova nalabadira lamulo la Mulungu m’bukhu la Aroma lakuti: “Musabwezere munthu aliyense choipa . . . ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pa mkwiyo.”—Aroma 12:17-19.
8 Mawu amenewo anam’thandiza kuzindikira mmene kufoka kwake kunaliri koipa. Chidziŵitso chomakulakula cha Baibulo chinayeretsa chikumbu mtima chake, chimene chinamthandiza kugonjetsa kukwiya kwake msanga. Nthaŵi imodzi, atapanga kupita patsogolo mmaphunziro ake, mlendo wina anamlalatira. Mnyamatayo anamva mkwiyo wozoloŵerekawo ukumakula mkati mwake. Pamenepo anamva kanthu kena: kuchita manyazi; ndipo izi zinamtetezera kukulakidwa ndi mkwiyo wake. Anali atakulitsa kudziletsa, chipatso chofunika cha mzimu. (Agalatiya 5:22, 23) Umunthu wake watsopano unali wosiyana, iyamikiketu mphamvu ya Mawu a Mulungu.
9. Mogwirizana ndi Paulo, kodi umunthu wathu umasinthidwa kupyolera mwa chinthu chiti?
9 Komabe, kodi ndimotani, mmene Baibulo limatulutsira chiyambukiro chotere cha mphamvu? Paulo, pa Akolose 3:10, ananena kuti maumunthu athu amasinthidwa kupyolera mwa chidziŵitso cholongosoka, chidziŵitso chimene chimapezeka m’Baibulo. Koma kodi chidziŵitso chimasintha anthu motani?
Mbali ya Chidziŵitso Cholongosoka
10, 11. (a) Pamene tiŵerenga Baibulo, kodi timaphunziranji ponena za mikhalidwe yofunika ndi yosafunika yaumunthu? (b) Kodi chofunika nchiyani kuwonjezera pa chidziŵitso kuchititsa masinthidwe muumunthu wathu?
10 Choyamba, Baibulo limasonyeza mikhalidwe yaumunthu wosafunika imene ifunikira kuvulidwa. Imeneyi iphatikizapo zinthuzi zonga “maso akunyada, lirime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu mangu mmangu; mboni yonama yonong’ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.” (Miyambo 6:16-19) Chachiŵiri, Baibulo limalongosola mikhalidwe yofunika imene tiyenera kukulitsa, kuphatikizapo “chikondi, chisangalalo, mtendere, kuleza mtima, chifundo, ubwino, chikhulupiriro, chifatso, kudziletsa.”—Agalatiya 5:22, 23.
11 Chidziŵitso cholongosoka choterocho chimathandiza munthu wowona mtima kudzipenda ndikuwona mikhalidwe yaumunthu imene afunikira kukulitsa ndi imene ayenera kugwirira ntchito kuichotsa. (Yakobo 1:25) Komabe, chimenecho ndicho chiyambi chabe. Kuwonjezera pa chidziŵitso, chisonkhezero chiri chofunika, chinthu china chomusonkhezera kotero kuti afune kusintha. Panonso, afunikira chidziŵitso cholongosoka chochokera m’Baibulo.
Kusonkhezeredwa Kukhala Wabwino
12. Kodi ndimotani mmene chidziŵitso cha umunthu wa Mulungu chimatithandizira kusintha?
12 Paulo ananena kuti umunthu watsopano wabwinowu umaumbidwa “mogwirizana ndi chifaniziro cha Iye amene anaulenga.” (Akolose 3:10) Chotero umunthu Wachikristu uyenera kufanana ndi umunthu wa Mulungu. (Aefeso 5:1) Umunthu wa Mulungu wavumbulutsidwa kwa ife, kudzera m’Baibulo. Tikuwona zochita zake ndi anthu ndipo tikuwona mikhalidwe yake yabwino kwambiriyo, monga ngati chikondi chake, kukoma mtima, ubwino, chifundo, ndi chilungamo. Chidziŵitso chotero chimasonkhezera munthu woongoka mtima kukonda Mulungu ndi kufuna kukhala mtundu wa munthu amene Mulungu amayanja. (Mateyu 22:37) Monga ana okondedwa, tifuna kukondweretsa Atate wathu wakumwamba, chotero timayesayesa kutsanzira umunthu wake monga momwe tingathere mumkhalidwe wathu wofoka, ndi wopanda ungwiro.—Aefeso 5:1.
13. Kodi n’chidziŵitso chiti chimene chimatiphunzitsa ‘kukonda chilungamo ndi kuda kusaweruzika’?
13 Chisonkhezero chathu chimalimbikitsidwa ndi chidziŵitso chimene Baibulo limapereka ponena za kumene mikhalidwe yonse iŵiri ya umunthu wabwino ndi ya umunthu woipa imatsogolerako. (Salmo 14:1-5; 15:1-5; 18:20, 24) Timaphunzira kuti Davide anadalitsidwa kaamba ka kudzipereka kwake kwaumulungu ndi chikondi chake cha chilungamo koma kuti iye anavutika pamene anataikiridwa ndi kudziletsa. Timawona zotulukapo zomvetsa chisoni pamene mikhalidwe yabwino kwambiriyo ya Solomo inaipitsidwa muukalamba wake. Madalitso amene anatulukapo pa kuwongoka kwa Yosiya ndi Hezekiya amasiyanitsidwa ndi ziyambukiro zatsoka za kufooka kwa Ahabu ndi mpatuko wa liuma wa Manase. (Agalatiya 6:7) Motero timaphunzira ‘kukonda chilungamo ndi kuda kusayeruzika.’—Ahebri 1:9; Salmo 45:7; 97:10.
14. Kodi nchiyani chimene chiri zifuno za Yehova kaamba ka dziko ndi kaamba ka anthu okhalamo?
14 Chisonkhezero chimenechi chikulimbikitsidwabe mowonjezereka ndi chidziŵitso cholongosoka cha zifuno za Mulungu. Chidziŵitso chotero chimathandiza kusintha ‘mphamvu yosandulizira maganizo athu enieniwo,’ mzimu umene umasonkhezera ndingaliro ndi zochita zathu. (Aefeso 4:23, 24) Pamene tiphunzira Baibulo, timaphunzira kuti Yehova sadzalekerera kuipa kosatha. Mwamsanga, iye adzawononga dziko losalungama lino ndi kubweretsa ‘kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano mmene mukhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:8-10, 13) Kodi ndani amene adzakhala ndi moyo m’dziko latsopano lino? “Owongoka mtima adzakhala mdziko, angwiro nadzatsalamo. Koma oipa adzalikhidwa m’dziko, achiwembu adzadzulidwamo.”—Miyambo 2:21, 22.
15. Ngati tikhulupiriradi zimene Baibulo limanena ponena za zifuno za Yehova, kodi zimenezi zidzatiyambukira bwanji monga anthu?
15 Ngati ife tikhulupiriradi lonjezo limeneli, njira yathu yonse yamaganizo idzayambukiridwa. Mtumwi Petro, atatha kulosera chiwonongeko cha kuipa, akuti: “Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, mmayendedwe opatulika ndi m’chipembedzo, akuyembekezera ndi kufulumira kwa kudza kwake kwa tsiku la Mulungu.” (2 Petro 3:11, 12) Maumunthu athu ayenera kuumbidwa ndi chikhumbo chathu champhamvu cha kukhala pakati pa owongoka mtima amene adzasiidwa pamene oipa awonongedwa.
16. Kodi ndi maumunthu otani amene sadzakhala ndi malo m’dziko latsopano, ndipo kodi chidziŵitso chimenechi chiyenera kutiyambukira motani?
16 Bukhu la Chivumbulutso limalonjeza owongoka mtima kuti, pambuyo pamapeto adziko lino, “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.” Komano ilo limachenjeza kuti “amantha ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse amabodza” adzakanidwa. (Chivumbulutso 21:4, 8) Kuli kwanzeru chotani nanga kupewa mikhalidwe yonyansa imene Mulungu adzakana kuilola m’dziko latsopano!
Chithandizo Chochokera Kunja
17. Kodi nchithandizo chotani chimene Baibulo limatilangiza kufunafuna?
17 Komabe, anthu ngofoka, ndipo kaŵirikaŵiri amafunikira kanthu kena kowonjezera pa chidziŵitso ndi chisonkhezero ngati iwo ati apange masinthidwewo. Iwo afunikira chithandizo chaumwini, ndipo Baibulo limatisonyeza kumene tingapeze chithandizo chimenechi. Mwachitsanzo, ilo limati: “Ukayenda ndi anzeru udzakhala wanzeru: koma mnzawo wa opusa adzapwetekedwa.” (Miyambo 13:20) Mofananamo, ngati tiyanjana ndi awo amene amasonyeza mikhalidwe imene timafuna kuikulitsa, tidzathandizidwa kwambiri kukhala ofanana nawo koposerapo.—Genesis 6:9; Miyambo 2:20; 1 Akorinto 15:33.
18, 19. Kodi tifunikira kuchitanji kuti tipereke maganizo athu ndi mitima ku mzimu woyera?
18 Kuwonjezera apa, Yehova mwiniyo amapereka chithandizo mwampangidwe wa mzimu woyera—mzimu umodzimodziwo umene anagwiritsira ncthito kuchita zozizwitsa m’nthaŵi zamakedzana. Ndithudi, mikhalidwe yofunika koposa ya “chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso” ikutchedwa “zipatso zamzimu.” (Agalatiya 5:22, 23) Kodi timapeza motani chithandizo cha mzimu woyera? Popeza kuti Baibulo linawuziridwa ndi mzimu woyera, pamene tiriŵerenga kapena kulankhula za ilo kwa ena, tikupereka maganizo athu ndi mtima ku mphamvu yosonkhezera ya mzimu umenewo. (2 Timoteo 3:16) Ndithudi, Yesu analonjeza kuti pamene tilankhula kwa ena za chiyemebekezo chathu, tingalandire chichilikizo chachindunji cha mzimu umenewu.—Mateyu 10:18-20.
19 Kuwonjezera apa, Baibulo limalangiza kuti: “Limbikani chilimbikire m’kupemphera.” (Aroma 12:12) Mwapemphero timalankhula ndi Yehova, kutamanda, kumuyamika, ndi kupempha chithandizo chake. Ngati tipempha chithandizo cha kugonjetsa mikhalidwe yaumunthu yosafunikayo, monga ngati kukwiya msanga, liuma, chiwawa, kapena kunyada, mzimu wa Mulungu udzachilikiza zoyesayesa zirizonse zimene tipanga mogwirizana ndi pemphero limenelo.—Yohane 14:13, 14; Yakobo 1:5; 1 Yohane 5:14.
20. Kodi nchifukwa ninji Akristu afunikira kupitirizabe kugwirira ntchito kuvala umunthu watsopano?
20 Pamene Paulo analemba kuti: “Mukhale osandulika, mwakukonzanso kwa mtima wanu,” anali kulembera mpingo wa Akristu obatizidwa, odzozedwa. (Aroma 1:7; 12:2) Ndipo m’Chigriki choyambirira, iye anagwiritsira ntchito mpangidwe wa mneni wotanthauza kachitidwe kopitirizabe. Zimenezi zikupereka lingaliro lakuti kusandulizidwa kochitidwa mwa ife mwa chidziŵitso cholongosoka chochokera m’Baibulo nkopita patsogolo. Ife lerolino—mofanana ndi Akristu mtsiku la Paulo—tazingidwa ndi dziko lodzala ndi zisonkhezero zoipitsa. Ndipo ife—mofanana nawo—tiri opanda ungwiro, okhoterera kukuchita cholakwa. (Genesis 8:21) Chifukwa chake, tifunikira kugwirira ntchito mosalekeza pa kugonjetsa umunthu wakale, wadyera ndi kuvala watsopano, monga momwedi iwo anachitira. Akristu oyambirira anapeza chipambano kumlingo wakuti anali apadera monga osiyana kotheratu ndi dziko lowazinga. Akristu lerolino amachita mofanana.
Anthu “Ophunzitsidwa ndi Yehova”
21. Kodi ndi maulosi ena ati amene akwaniritsidwa pa anthu a Mulungu mmasiku otsiriza ano?
21 Ndithudi, mzimu wa Mulungu lerolino umagwira ntchito osati kokha pa anthu aliwonse paokha koma pa gulu lonse la Akristu, amene chiŵerengero chawo chikufika mamiliyoni angapo. Mawu olosera a Yesaya akwaniritsidwira pa gulu limeneli akutiwo: “Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda mmayendedwe ake.” (Yesaya 2:3) Ulosi wowonjezereka wa Yesaya wakwaniritsidwanso pa iwo: “Ana ako onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova; ndipo mtendere wa ana ako udzakhala waukulu.” (Yesaya 54:13) Kodi amene akusangalala ndi mtendere chifukwa cha kuphunzira ndi Yehova ndani?
22. (a) Kodi ndani lerolino akuphunzitsidwa ndi Yehova? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti akunja amazindikira kuti Mboni za Yehova nzosiyana.
22 Eya, tawonani mawu ogwidwa awa kuchokera m’kalata yolembedwera ku New Haven Register, nyuzipepala ya Kumpoto kwa Amerika: “Kaya mwavutitsidwa maganizo kapena kupsetsedwa mtima [kukwiitsidwa], monga momwe ndachitira ine, mwa ntchito yawo yotembenuza anthu, mufunikira kuchita chidwi ndi kudzipereka kwawo, umphumphu wawo, chitsanzo chawo chapadera cha kudzisungira kwaumunthu ndi kakhalidwe kabwino.” Kodi wolembayo anali kulankhula za yani? Kagulu kamodzimodziko kokambitsiridwa ndi Herald ya ku Buenos Aires, Argentina, pamene inati: “Mboni za Yehova zatsimikizira mkati mwa zaka zonsezi kukhala nzika zokangalika, zolama maganizo, zosawawanya ndi zowopa Mulungu.” Mofananamo, nyuzipepala ya ku Italia ya La Stampa inati: “Iwo samazemba misonkho kapena kufunafuna kupewa malamulo ochititsa kusapeza bwino kaamba ka phindu la iwo eni. Malamulo amakhalidwe abwino achikondi cha pamnansi, kukana ulamuliro, kusachita chiwawa ndi kuwona mtima kwawo . . . zimalowa njira yawo ya moyo ya ‘tsiku ndi tsiku.’”
23. Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova monga gulu ziri zosiyana mwapadera?
23 Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova monga kagulu—mofanana ndi Akristu oyambirira—ziriri zosiyana mwapadera? M’zochitika zambiri, izo nzofanana ndi munthu wina aliyense. Zinabadwa ndi kupanda ungwiro kwaumunthu kofanana, ndipo ziri ndi mavuto a zachuma ofanana ndi zosowa zamaziko. Komabe, monga mpingo wa padziko lonse lapansi, zimalola Mawu a Mulungu kupereka mphamvu m’miyoyo yawo. Chotulukapo chaubale wa m’mitundu yonse wa Akristu owona ndicho umboni wamphamvu wakuti Baibulo liri Mawu ouziridwa a Mulungu.—Salmo 133:1.
Baibulo Nlouziridwa
24. Kodi pemphero lathu nlotani mmalo mwa anthu ena owonjezereka?
24 M’nkhani ziŵiri izi, takambamo maumboni aŵiri okha osonyeza kuti Baibulo ndilo Mawu a Maulungu, osati a munthu. Kaya akulingalira nzeru yosayerekezereka ya Baibulo kapena mphamvu yake ya kusintha anthu—kapena zinthu zina zambiri zimene zimalidziŵikitsa kukhala lapadera—anthu owona mtima sangalephere konse kuzindikira kuti liyenera kukhala lowuziridwa ndi Mulungu. Monga Akristu, tikupemphera kuti ena ambiri adzafikira pakuzindikira chowonadi ichi. Pamenepo iwo adzabwereza mawu achikondwerero a wamasalmo akuti: “Penyani kuti ndikonda malangizo anu; mundipatse moyo, Yehova monga mwa chifundo chanu. Chiwerengero cha mawu anu ndicho chowonadi; ndi maweruzo anu olungama onse akhala kosatha.”—Salmo 119:159, 160.
Kodi mukukumbukira?
◻ Kodi nchiyambukiro chotani chimene Baibulo liri nacho pa Akristu owona?
◻ Kodi chidziŵitso cholongosoka chimathandiza motani kutisanduliza?
◻ Kodi Baibulo limathandiza motani kutisonkhezera kukulitsa mikhalidwe yabwino ndi kugonjetsa yoipa?
◻ Kodi n’chithandizo chotani chopezeka m’kukulitsa mikhalidwe yaumulungu?
◻ Kodi ndi umboni wotani wakuti Baibulo nlouziridwa umene umaonedwa pakati pa anthu a Yehova?
[Chithunzi patsamba 18]
Choturukapo chomvetsa chisoni cha kusakhulupirika kwa Solomo muukalamba wake chiyenera kutisonkhezera kukonda chilungamo ndi kuda kusayeruzika
[Chithunzi patsamba 20]
Ngati tipempha Yehova chithandizo, mzimu wake udzachilikiza zoyesayesa zirizonse zimene tipanga kugonjetsa mikhalidwe yoipa