Yendani M’kuwopa kwa Yehova
“Pamene [mpingo] unayenda m’kuwopa kwa Yehova ndi m’chitonthozo cha mzimu woyera unachuluka.”—MACHITIDWE 9:31, “NW.”
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene mpingo Wachikristu unaloŵa m’nyengo ya mtendere? (b) Ngakhale kuti Yehova amalola chizunzo, kodi angachitenso chiyani?
WOPHUNZIRA anayang’anizana ndi chiyeso chachikulu. Kodi iye akasunga umphumphu kwa Mulungu? Inde, akaterodi! Iye anayenda m’kuwopa kwa Mulungu, ndi kunthunthumira kowopa Mpangi wake, ndipo akamwalira monga mboni yokhulupirika ya Yehova.
2 Wosunga umphumphu wowopa Mulungu ameneyo anali Stefano, “munthu wodzala ndi chikhulupiriro ndi [mzimu woyera].” (Machitidwe 6:5) Kuphedwa kwake kunayambitsa mkuntho wa chizunzo, koma pambuyo pake mpingo mu Yudeya monse, Galileya, ndi Samariya inaloŵa m’nyengo ya mtendere ndipo inamangiriridwa mwauzimu. Ndiponso, “pamene unayenda m’kuwopa kwa Yehova ndi m’chitonthozo cha mzimu woyera unachuluka.” (Machitidwe 9:31, NW) Monga Mboni za Yehova lerolino, tingatsimikizire kuti Mulungu adzatidalitsa kaya tikukumana ndi mtendere kapena chizunzo, monga kwasonyezedwera m’Machitidwe mitu 6 mpaka 12. Chotero tiyeni tiyende m’kuwopa kwa Mulungu mwaulemu pamene tikuzunzidwa kapena kugwiritsira ntchito nyengo iriyonse yopanda chizunzo kudzilimbitsa mwauzimu ndi kuchita utumiki wowonjezereka kwa iye.—Deuteronomo 32:11, 12; 33:27.
Wokhulupirika Kufikira Mapeto
3. Kodi ndi vuto lotani limene linalakidwa mu Yerusalemu, ndipo motani?
3 Ngakhale ngati mavuto abuka m’nthaŵi za mtendere, kulinganiza kwabwino kumathandiza kuwathetsa iwo. (6:1-7) Ayuda olankhula Chigiriki mu Yerusalemu anadandaula kuti akazi awo amasiye anali kunyalanyazidwa m’kugaŵira chakudya kwa tsiku ndi tsiku moyanja akhulupiriri Achiyuda olankhula Chihebri. Vutoli linathetsedwa pamene atumwi anaika amuna asanu ndi aŵiri kusamalira “ntchito iyi.” Mmodzi wa iwo adali Stefano.
4. Kodi Stefano anayankha motani zinenezo zonama?
4 Komabe, posakhalitsa Stefano woopa Mulungu anakumana ndi chiyeso. (6:8-15) Panauka amuna ena amene anatsutsana ndi Stefano. Ena anachokera ku ‘Sunagoge wa Anthu Omasulidwa,’ mwinamwake anali Ayuda ogwidwa mu ukapolo ndi Aroma ndipo pambuyo pake anamasulidwa kapena Ayuda otembenuka amene kale adali akapolo. Atalephera kulaka kulankhula kwanzeru ndipo kwauzimu kwa Stefano, adani ake anamutengera ku Bwalo Lalikulu Lamilandu Lachiyuda. Kumeneko mboni zonamazo zinati: ‘Tinamva munthu ameneyu akunena kuti Yesu adzawononga kachisi ndi kusanduliza miyambo imene Mose anatipatsa.’ Chikhalirechobe, ngakhale omutsutsawo anazindikira kuti Stefano sanali wolakwa koma anali ndi nkhope yowala ya mngelo, mthenga wa Mulungu wotsimikizira za chilikizo lake. Anali wosiyana motani nanga ndi nkhope zawo, zokwinyata ndi kuipa chifukwa anadzipereka kugwiritsiridwa ntchito ndi Satana!
5. Kodi ndi mfundo zotani zimene Stefano anapanga pamene ankachitira umboni?
5 Pamene anafunsidwa ndi Mkulu wa Ansembe Kayafa, Stefano anapereka umboni mopanda mantha. (7:1-53) Kubwereramo kwake mu mbiri ya Israyeli kunasonyeza kuti Mulungu analinganiza kuthetsa Chilamulo ndi utumiki wa pakachisi pamene Mesiya akadza. Stefano anadziŵitsa kuti Mose, mpulumutsi amene Myuda aliyense anati anamlemekeza, anakanidwa ndi Aisrayeli, mongadi mmene tsopano iwo sanalandirire Uyo amene akawabweretsera chipulumutso chachikulu. Mwakunena kuti Mulungu sakhala m’nyumba zomangidwa ndi manja, Stefano anasonyeza kuti kachisi ndi dongosolo lake la kulambira zikatha. Koma popeza kuti oweruza ake sanawope Mulungu kapena kufuna kudziŵa chifuniro Chake, Stefano anati: ‘Ouma khosi inu, mukaniza mzimu woyera nthaŵi zonse. Ndiye yani wa aneneri makolo anu sanamzunza? Ndipo anawapha iwo amene anaonetseratu za kudza kwake kwa Wolungamayo; iye amene mwakhala tsopano akumpereka ndi akumupha.’
6. (a) Kodi ndi chokumana nacho cholimbikitsa chikhulupiriro chotani chimene Stefano anali nacho asanaphedwe? (b) Kodi nchifukwa ninji Stefano ananena molondola kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga”?
6 Mawu opanda mantha a Stefano anatsogolera ku kuphedwa kwake. (7:54-60) Oweruzawo anakwiyitsidwa ndi kuvumbula kumeneku kwa liŵongo lawo lakupha Yesu. Koma chikhulupiriro cha Stefano chinalimbikitsidwa motani nanga pamene ‘anayang’ana kumwamba nawona ulemerero wa Mulungu ndi wa Yesu alikuimirira kudzanja Lake lamanja’! Stefano tsopano akayang’anizana ndi adani ake ndi chidaliro chakuti anachita chifuniro cha Mulungu. Ngakhale kuti Mboni za Yehova sizimakhala ndi masomphenya, tingakhale ndi mkhalidwe wabata wofananawo wopatsidwa ndi Mulungu pamene tikuzunzidwa. Pambuyo pomponya Stefano kunja kwa Yerusalemu, adani ake anayamba kumponya miyala, ndipo iye anapempha kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” Chimenechi chinali choyenera chifukwa chakuti Mulungu anampatsa Yesu mphamvu ya kuukitsira ena ku moyo. (Yohane 5:26; 6:40; 11:25, 26) Atagwada pansi, Stefano anafuula nati: “[Yehova, NW], musawaikire iwo chimo ili.” Kenaka anagona tulo taimfa monga wophedwera chikhulupiriro, mongadi mmene atsatiri a Yesu ambiri achitira chiyambire nthaŵiyo, ngakhale m’nthaŵi zamakono.
Chizunzo Chifalitsa Mbiri Yabwino
7. Kodi chinatulukapo nchiyani m’chizunzocho?
7 Kwenikwenidi imfa ya Stefano inatulukapo kufalitsidwa kwa mbiri yabwino. (8:1-4) Chizunzo chinamwaza ophunzira onse kupatulapo atumwi mu Yudeya ndi Samariya yonse. Saulo, amene anavomereza za kuphedwa kwa Stefano, anasakaza mpingo monga chirombo, akumaloŵa nyumba ndi nyumba kukokera atsatiri a Yesu kaamba ka kuikidwa m’ndende. Pamene ophunzira omwazikanawo anapitiriza kulalikira, makonzedwe a Satana oletsa alengezi a Ufumu owopa Mulungu mwa kuwazunza analepheretsedwa. Lerolinonso, kaŵirikaŵiri chizunzo chafalitsanso mbiri yabwino kapena kutcheretsa khutu ku ntchito yolalikira Ufumu.
8. (a) Kodi nchiyani chinachitika monga chotulukapo cha kulalikira kumene kunachitidwa mu Samariya? (b) Kodi Petro anagwiritsira ntchito motani mfungulo yachiŵiri imene Yesu anampatsa?
8 Mlengezi Filipo anapita ku Samariya ‘kukalalikira Kristu.’ (8:5-25) Chikondwerero chachikulu chinadzala mumzindawo pamene mbiri yabwino inalalikidwa, mizimu yoipa inatulutsidwa, ndipo anthu anachiritsidwa. Atumwi mu Yerusalemu anatumiza Petro ndi Yohane ku Samariya, ndipo pamene anapemphera ndi kuika manja awo pa amene anabatizidwa, ophunzira atsopano analandira mzimu woyera. Simoni wobatizidwa chatsopano yemwe kale anali wamatsenga anayesera kugula ulamuliro umenewu, koma Petro anati: ‘Ndalama yako itayike nawe. Pakuti mtima wako suli wolunjika pamaso pa Mulungu.’ Atauzidwa kulapa ndi kupembedzera Yehova kaamba ka chikhululukiro, iye anapempha atumwi kuti ampempherere. Chimenechi chiyenera kusonkhezera owopa Yehova onse lerolino kupempherera thandizo laumulungu m’kuchinjiriza mtima. (Miyambo 4:23) (Pachochitikachi mpamene panachokera liwu lakuti “simony,” “kugula kapena kugulitsa thayo la tchalitchi kapena udindo wa ulaliki.”) Petro ndi Yohane analalikira mbiri yabwino m’midzi yambiri ya Asamariya. Chotero, Petro anagwiritsira ntchito mfungulo yachiŵiri imene Yesu anampatsa kutsegulira khomo la chidziŵitso ndi mwaŵi woloŵa Ufumu wakumwamba.—Mateyu 16:19.
9. Kodi munthu wa ku Aitiopiya amene Filipo anamlalikira anali yani, ndipo kodi nchifukwa ninji mwamunayo anabatizidwa?
9 Pamenepo mngelo wa Mulungu anapatsa Filipo gawo latsopano la ntchito. (8:26-40) Mu gareta pamsewu wopita ku Gaza kuchokera ku Yerusalemu munakwera “mdindo,” nduna yoyang’anira chuma cha mfumu yaikazi Kandake ya ku Aitiopiya. Iye sanali mdindo wakuthupi, woletsedwa mu mpingo Wachiyuda, koma anapita ku Yerusalemu kukapembedza monga wotembenuka wodulidwa. (Deuteronomo 23:1) Filipo anapeza mdindoyo akuŵerenga bukhu la Yesaya. Ataitanidwa kukwera garetayo, Filipo analongosola ulosi wa Yesaya “nalalikira kwa iye Yesu.” (Yesaya 53:7, 8) Posakhalitsa munthu wa ku Aitiopiyayo anadzuma kuti: “Taonapo madzi; chindiletsa ine chiyani ndisabatizidwe?” Palibe chimene chinamuletsa, popeza kuti anadziŵa ponena za Mulungu ndipo tsopano anali ndi chikhulupiriro mwa Kristu. Chotero Filipo anabatiza munthu wa ku Aitiopiyayo, amene pambuyo pake anapita njira yake wokondwera. Kodi pali chirichonse chokuletsani kubatizidwa?
Wozunza Atembenuzidwa
10, 11. Kodi nchiyani chimene chinamchitikira Saulo wa ku Tariso panjira popita ku Damasiko ndiponso mwamsanga pambuyo pake?
10 Panthaŵiyi, Saulo anafuna kupangitsa atsatiri a Yesu kugalukira chikhulupiriro chawo mwa chiwopsyezo cha kuikidwa m’ndende kapena kuphedwa. (9:1-18a) Mkulu wa ansembe (mwachidziŵikire Kayafa) anampatsa makalata opita nawo ku masunagoge mu Damasiko omuloleza kubweretsa ku Yerusalemu amuna ndi akazi otsata “Njirayo” omangidwa, kapena otsatira njira yamoyo yozikidwa pa chitsanzo cha Kristu. Pafupifupi pakati pausana atayandikira ku Damasiko, kuwunika kunathwanima kuchokera kumwamba ndipo liwu linamfunsa kuti: “Saulo, Undilondalonderanji?” Awo amene anali ndi Saulo anamva “mawu” koma sanamvetsetse zimene zinanenedwa. (Yerekezerani ndi Machitidwe 22:6, 9.) Kuvumbulutsidwa kochepa kwa Yesu wolemekezedwa kumeneko kunali kokwanira kuchititsa khungu Saulo. Mulungu anagwiritsira ntchito wophunzira Hananiya kubwezeretsa kuwona kwake.
11 Pambuyo pa ubatizo wake, wozunza wakaleyu anakhala chandamale cha chizunzo. (9:18b-25) Ayuda a ku Damasiko anafuna kumupha Saulo. Komabe, pofika usiku, ophunzirawo anamtsitsira pampata wa linga, mwinamwake mu mtanga waukulu wolukidwa ndi zingwe kapena timitengo tolukidwa. (2 Akorinto 11:32, 33) Mpatawo ungakhale unali zenera la nyumba ya wophunzira yomangidwa pa lingalo. Kuzemba adaniwo ndi kupitirizabe kulalikira sikunali kuwaopa.
12. (a) Kodi nchiyani chimene chinamchitikira Saulo mu Yerusalemu? (b) Kodi mpingo unachita motani?
12 Mu Yerusalemu, Barnaba anathandiza ophunzira kuvomereza Saulo monga wokhulupirira mnzawo. (9:26-31) Kumeneko Saulo mopanda mantha anatsutsana ndi Ayuda olankhula Chigiriki, amenenso anayesera kumupha iye. Atazindikira ichi, abalewo anampereka ku Kaisareya namtumiza ku Tariso, mudzi wakwawo mu Silikiya. Pamenepo mpingo mu Yudeya monse, Galileya, ndi Samariya “unali nawo mtendere, nukhazikika” mwauzimu. Pamene ‘unayenda m’kuwopa kwa Yehova ndi m’chitonthozo cha mzimu woyera, unachuluka.’ Chimenechi nchitsanzo chabwino chotani nanga kwa mipingo yonse lerolino ngati ifuna kulandira dalitso la Yehova!
Akunja Akhala Okhulupirira!
13. Kodi ndi zozizwitsa zotani zimene Mulungu anamtheketsa Petro kuzichita ku Luda ndi Yopa?
13 Petro nayenso anali wotanganidwa. (9:32-43) Ku Luda (tsopano Lod) m’Chigwa cha Sharon, anachiritsa Eneya wamanjenje. Kuchiritsa kumeneku kunapangitsa ambiri kutembenukira kwa Ambuye. Mu Yopa, wophunzira wokondedwa Tabita (Dorika) anadwala namwalira. Pamene Petro anafika, akazi amasiye olirawo anamusonyeza zovala zimene Dorika ankapanga ndi zimene angakhale ankavala. Iye anaukitsa Dorika, ndipo pamene mbiriyo inafalikira, ambiri anakhulupirira. Petro anakhala mu Yopa ndi Simoni wofufuta zikopa, amene nyumba yake inali pafupi ndi nyanja. Ofufuta zikopa anali kuviika zikopa za nyama m’nyanja ndi kuzipaka njereza asanachotse ubweya. Zikopa zimenezi zinasinthidwa kukhala zikopa zouma mwakuzifufuta ndi madzi ochokera ku zomera zina.
14. (a) Kodi Korneliyo adali yani? (b) Kodi nchiyani chimene chinali chowona ponena za mapemphero a Korneliyo?
14 Panthaŵi imeneyo (36 C.E.), chochitika chodziŵika chinachitika kwinakwake. (10:1-8) Mu Kaisareya munali Korneliyo Wakunja wodzipereka, kenturio Wachiroma wolamulira pafupifupi amuna zana limodzi. Iye ankatsogolera “gulu lotchedwa la Italiya,” mwachiwonekere lopangidwa ndi anthu olembedwa ochokera pakati pa nzika Zachiroma ndi anthu omasulidwa a ku Italiya. Ngakhale kuti Korneliyo anawopa Mulungu, iye sanali mtembenuki Wachiyuda. M’masomphenya, mngelo anamuuza kuti mapemphero ake ‘anakwera nakhala chikumbutso pamaso pa Mulungu.’ Ngakhale kuti panthaŵiyo Korneliyo sanali wodzipatulira kwa Yehova, iye analandira yankho ku pemphero lake. Koma monga mmene mngelo analangizira, anaitanitsa Petro.
15. Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Petro anali kupemphera pachindwi cha nyumba ya Simoni?
15 Panthaŵiyo, Petro anaona masomphenya pamene ankapemphera pachindwi pa nyumba ya Simoni. (10:9-23) M’masomphenya, anawona chotengera chonga nsalu chikutsika kuchokera kumwamba chodzaza ndi zamoyo zamiyendo inayi zodetsedwa, zokwawa, ndi mbalame. Atalangizidwa kuti aphe nadye, Petro anati sanadyepo ndi kale lonse zinthu zodetsedwa. “Chimene Mulungu anayeretsa, usachiyesa chinthu wamba,” anauzidwa tero. Masomphenyawo anamuvutitsa Petro, koma anatsatira malangizo a mzimu. Chotero, iye ndi abale Achiyuda asanu ndi mmodzi anatsagana ndi athenga a Korneliyo.—Machitidwe 11:12.
16, 17. (a) Kodi Petro anamuuzanji Korneliyo ndi awo osonkhana panyumba pake? (b) Kodi chinachitika nchiyani pamene Petro ankalankhula?
16 Tsopano Akunja oyamba anali pafupi kumva mbiri yabwino. (10:24-43) Pamene Petro ndi anzake anafika ku Kaisareya, Korneliyo, achibale ake, ndi mabwenzi ake apamtima ankadikirira. Korneliyo anagwa pamapazi a Petro, koma mtumwiyo modzichepetsa anakana kugwadiridwa koteroko. Iye analankhula za mmene Yehova anadzodzera Yesu ndi mzimu woyera ndi kumpatsa mphamvu monga Mesiya ndipo analongosola kuti aliyense wokhulupirira iye amakhululukidwa machimo.
17 Tsopano Yehova anachitapo kanthu. (10:44-48) Petro ali chilankhulire, Mulungu anatsanulira mzimu woyera pa Akunja okhulupirirawo. Panthaŵi yomweyo, anabadwa ndi mzimu wa Mulungu ndipo anauziridwa kulankhula zinenero zachilendo ndi kumulemekeza iye. Chotero, iwo anabatizidwa moyenerera m’dzina la Yesu Kristu. Chotero Petro anagwiritsira ntchito mfungulo yachitatu kutsegulira Akunja owopa Mulungu khomo la chidziŵitso ndi mwaŵi wa kuloŵa mu Ufumu wakumwamba.—Mateyu 16:19.
18. Kodi abale Achiyuda anachita motani pamene Petro analongosola kuti Akunja “anabatizidwa ndi mzimu woyera”?
18 Pambuyo pake, mu Yerusalemu, ochilikiza mdulidwe anatsutsana ndi Petro. (11:1-18) Pamene analongosola mmene Akunja ‘anabatizidwira ndi mzimu woyera,’ abale ake Achiyuda anakhala duu nalemekeza Mulungu, nati: “Potero Mulungu anapatsa kwa amitundunso kutembenukira mtima kumoyo.” Nafenso tiyenera kukhala ovemereza pamene chifuniro chaumulungu chimveketsedwa kwa ife.
Mpingo Wa Akunja Ukhazikitsidwa
19. Kodi ophunzirawo anatchedwa motani Akristu?
19 Tsopano mpingo woyamba wa Akunja unakhazikitsidwa. (11:19-26) Pamene ophunzira anamwazidwa ndi chizunzo chobuka pa Stefano, ena anapita ku Antiokeya, Siriya, wodziŵika ndi kulambira konyansa ndi makhalidwe oipa. Pamene analankhula mbiri yabwino kwa anthu olankhula Chigiriki kumeneko, ‘dzanja la Yehova linali nawo,’ ndipo ambiri anakhala okhulupirira. Kumeneko Barnaba ndi Saulo anaphunzitsa kwa chaka chimodzi, ndipo “[mwachitsogozo chaumulungu, NW] ophunzira anayamba kutchedwa Akristu ku Antiokeya.” Mosakaikira Yehova anatsogoza kuti atchedwe motero, popeza kuti liwu Lachigiriki lakuti khre·ma·tiʹzo limatanthauza “kuitanidwa mwachitsogozo chaumulungu” ndipo nthaŵi zonse limagwiritsidwa ntchito Mwamalemba mogwirizana ndi zimene zachokera kwa Mulungu.
20. Kodi Agabo analosera chiyani, ndipo kodi mpingo wa ku Antiokeya unachita motani?
20 Aneneri owopa Mulungu anabweranso ku Antiokeya kuchokera ku Yerusalemu. (11:27-30) Wina anali Agabo, amene anasonyeza “mwa [mzimu], kuti padzakhala njala yaikulu pa dziko lonse lokhalamo anthu.” Ulosi umenewo unakwaniritsidwa mkati mwa kulamulira kwa wolamulira Wachiroma Klaudiya (41-54 C.E.), ndipo katswiri wa mbiri yakale Josephus akulozera ku “njala yaikulu” imeneyi. (Jewish Antiquities, XX, 51 [ii, 5]; XX, 101 [v, 2]) Pofulumizidwa ndi chikondi, mpingo wa Antiokeya unatumiza zopereka kwa abale osoŵa mu Yudeya.—Yohane 13:35.
Chizunzo Nchosaphula Kanthu
21. Kodi ndi kachitidwe kotani kamene Herode Agripa I anatenga motsutsana ndi Petro, koma ndi chotulukapo chotani?
21 Nyengo ya mtendere inatha pamene Herode Agripa I anayamba kuzunza owopa Yehova mu Yerusalemu. (12:1-11) Herode anapha Yakobo ndi lupanga, mwinamwake kumdula mutu monga mtumwi woyamba kufera chikhulupiriro. Powona kuti chimenechi chinakondweretsa Ayuda, Herode anaika Petro m’ndende. Mwachiwonekere mtumwiyo anamangiriridwa kwa msilikali mmodzi kumbali iriyonse, pamene ena aŵiri ankalonda ndende yake. Herode anakonzekera zomupha iye itapita Paskha ndi masiku a mkate wopanda chotupitsa (Nisani 14-21), koma mapemphero a mpingo m’malo mwake anayankhidwa panthaŵi yake, mongadi mmene athu amayankhidwira kaŵirikaŵiri. Zimenezi zinachitika pamene mngelo wa Mulungu anamasula mozizwitsa mtumwiyo.
22. Kodi chinachitika nchiyani pamene Petro anapita kunyumba kwa Mariya, amake a Marko?
22 Mwamsanga Petro anafika panyumba pa Mariya (amake a Yohane Marko), mwachiwonekere malo okumanira Achikristu. (12:12-19) Mumdima, msungwana wantchito Roda anazindikira liwu la Petro koma anamusiya pakhomo potsekedwa. Poyamba ophunzirawo angakhale anaganiza kuti Mulungu anatumiza mthenga waungelo kuimira Petro nalankhula ndi liwu lake. Komabe, pamene anamuloŵetsa Petro, iye anawauza kuti akawuze Yakobo ndi abale (mwinamwake akulu) za kupulumutsidwa kwake. Pamenepo iye anachoka mobisika osaulula kumene anali kupita kuwopera kuwaika pa vuto kapena iyemwini pofunsidwa. Kufunafuna Petro kwa Herode kunali kosaphula kanthu, ndipo alondawo analangidwa, mwinamwake kuphedwa.
23. Kodi ulamuliro wa Herode Agripa I unatha motani, ndipo kodi tingaphunzirenji m’chimenechi?
23 Mu 44 C.E. ulamuliro wa Herode Agripa I unatha mwadzidzidzi mu Kaisareya pamene anali ndi zaka 54 zakubadwa. (12:20-25) Iye anaipidwa nawo Afonike a ku Turo ndi Sidoni, amene adakopa Blasto mtumiki wake kuti apange bwalo pamene akapempha mtendere. Pa “tsiku lopangira” (paphwandonso lolemekeza Klaudiya Kaisara), Herode anavala zovala zachifumu, nakhala pampando wachifumu, nawafotokozera iwo mawu a pabwalo. Poyankha osonkhanidwawo anafuula nati: “Ndiwo mawu a Mulungu, si a munthu ayi.” Pomwepo, mngelo wa Yehova anamkantha “chifukwa sanampatsa Mulungu ulemerero.” Herode “anadyedwa ndi mphutsi, natsirizika.” Lolani kuti chitsanzo chopereka chenjezochi chitisonkhezere kupitiriza kuyenda m’kuwopa kwa Yehova, kupeŵa kudzikweza ndi kumpatsa ulemerero kaamba ka zimene timachita monga anthu ake.
24. Kodi nkhani yamtsogolo idzasonyezanji ponena za kufutukuka?
24 Mosasamala kanthu za chizunzo chopangidwa ndi Herode, ‘mawu a Yehova anakula, nachulukitsa.’ Kwenikwenidi, monga mmene nkhani yamtsogolo idzasonyezera, ophunzirawo anayenera kuyembekezera kufutukuka kowonjezereka. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti iwo ‘anayenda m’kuwopa kwa Yehova.’
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene Stefano anasonyezera kuti anawopa Yehova, monga mmene atumiki ambiri a Mulungu achitira chiyambire nthaŵiyo?
◻ Kodi imfa ya Stefano inali ndi chiyambukiro chotani pantchito yolalikira Ufumu, ndipo kodi chimenechi chiri ndi kufanana kwamakono?
◻ Kodi ndimotani mmene mzunzi Saulo wa ku Tariso anakhalira wowopa Yehova?
◻ Kodi ndani amene anali okhulupirira Akunja oyamba?
◻ Kodi ndimotani mmene Machitidwe mutu 12 amasonyezera kuti chizunzo sichiletsa owopa Yehova?
[Chithunzi pamasamba 16, 17]
Kuwunika kunathwanima kuchokera kumwamba ndipo liwu linamfunsa kuti: “Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?”