‘Dziyeseni Nokha Ngati Muli m’Chikhulupiriro’
Mfundo Zazikulu Zochokera m’Akorinto Wachiŵiri
MTUMWI Paulo anali wodera nkhaŵa Akristu mu Korinto. Kodi iwo akaulingalira motani uphungu woperekedwa m’kalata yake yoyamba kwa iwo? Iye anali mu Makedoniya pamene Tito anabwera ndi mbiri yabwino yakuti kalata ija inachititsa Akorinto kulapa. Ichi chinapangitsa Paulo kusangalala chotani nanga!—2 Akorinto 7:8-13.
Paulo analembera Akorinto Wachiŵiri m’Makedoniya, mwinamwake kumapeto kwa chaka cha 55 C.E. M’kalata imeneyi, iye anafotokoza masitepe otengedwa kusunga mpingo kukhala woyera, anapanga chikhumbo cha kuthandiza akhulupiriri osowa mu Yudeya, ndi kuchilikiza utumwi wake. Zambiri zimene Paulo ananena zingatithandize ‘kudziyesa tokha ngati tiri m’chikhulupiriro.’ (13:5) Chotero, kodi tingapindulemonji m’kalatayi?
Minisitala wa Mulungu Wachitonthozo
Mtumwiyo anasonyeza kuti pamene Mulungu atitonthoza m’zisautso zathu zonse, tiyenera kutonthozanso ndi kupempherera ena. (1:1–2:11) Chinkana kuti Paulo ndi anzake anali pansi pa chitsenderezo champhamvu, Mulungu anawapulumutsa. Komabe, Akorinto anawathandizira ndi mapemphero, monga mmene ife tiyenera kupempherera ena amene amakupatira chikhulupiriro chowona. Koma bwanji ponena za mwamuna wachisembwere wotchulidwa mu 1 Akorinto mutu 5? Mwachiwonekere anali atachotsedwa koma analapa. Ayenera kukhala anatonthozedwa chotani nanga pamene Akorinto anasonyeza kumkhululukira ndikumbwezera pakati pawo mwachikondi.
Mawu a Paulo angawonjezere chiyamikiro chathu kaamba ka uminisitala Wachikristu, kulimbitsa kaimidwe kathu kaamba ka chikhulupiriro chowona. (2:12–6:10) Eya, aminisitala a chipangano chatsopano ali ndi mwaŵi wa kukhala ‘mumzere wa chipambano’ ndi Mulungu akumatsogolera! Paulo ndi antchito anzake anali ndi chuma cha uminisitala chifukwa cha chifundo chosonyezedwa kwa iwo. Mofanana ndi iwo, odzozedwa amakono ali ndi uminisitala wa kugwirizanitsa. Komabe, Mboni za Yehova zonse zimapangitsa ena kulemerera kupyolera muuminisitala wawo.
Kutsiriza Chiyero ndi Kukhala Owolowa Manja
Paulo akutisonyeza kuti aminisitala Achikristu ayenera kutsiriza chiyero m’kuwopa Yehova. (6:11–7:16) Ngati titi tikhale ochilimika m’chikhulupiriro, tiyenera kupeŵa kumangidwa m’goli ndi osakhulupirira, ndipo tifunikira kuyeretsedwa ku kuipa kwakuthupi ndi kwauzimu. Akorinto anachita ntchito yoyeretsa mwa kuchotsa ochita zoipa achisembwere, ndipo Paulo anasangalala kuti kalata yake yoyamba inawasonkhezera kulapa kaamba ka chipulumutso.
Timaphunziranso kuti aminisitala owopa Mulungu amafupidwa kaamba ka kuwolowa manja kwawo. (8:1–9:15) Ponena za zopereka kaamba ka osoŵa “oyera mtima,” Paulo anatchula chitsanzo chabwino cha Amakedoniya. Iwo anali owolowa manja kuposa pa mphamvu zawo, ndipo anayembekezera kuwona mtundu umenewo wa kuwolowa manja kwa Akorinto. Kupereka kwawo—ndi kwathu—kuyenera kuchokera kumtima, pakuti ‘Mulungu amakonda wopereka mokondwera’ ndipo amalemeretsa anthu ake kaamba ka mtundu uliwonse wa kuwolowa manja.
Paulo—Mtumwi Wachisamaliro
Pamene tikwaniritsa chirichonse muutumiki wa Yehova monga aminisitala, tiyeni tidzitukumulire mwa iye, osati pa ife tokha. (10:1–12:13) Ndiko nkomwe, nkokha mwa zida zauzimu ‘zamphamvu mwa Mulungu’ pamene tingagwetse zolingalira zonyenga. “Atumwi oposatu” odzitukumula pakati pa Akorinto sakalingana konse ndi mbiri ya Paulo ya kupirira monga minisitala wa Kristu. Komabe, kuti asadzikweze mopambanitsa, Mulungu sanamuchotsere “munga m’thupi”—mwinamwake maso osapenya bwino kapena atumwi onyenga aja. Komabe Paulo anadzitamabe m’zifooko zakezo kotero kuti ‘mphamvu ya Kristu’ ingakhale pa iye monga chochinga. Monga munthu amene anachilimika m’chikhulupiriro, iye sadadzitsimikizirepo kukhala wapansi kwa atumwi oposatu amenewo. Akorinto anawona chitsimikiziro cha utumwi chimene Paulo anasonyeza pakati pawo ‘mwa chipiriro, ndi zizindikiro ndi zozizwa ndi ntchito zamphamvu.’
Monga m’minisitala ndipo monga mtumwi, Paulo anali ndi zikondwerero zauzimu za atsatiri anzake pamtima, mongadi mmene nafenso tiyenera kukhalira nazo. (12:14–13:14) Iye ‘akakondwera kwambiri kutumikira kotheratu miyoyo yawo.’ Koma Paulo anawopa kuti pofika m’Korinto, angakapeze ena omwe sanalape ntchito zawo za thupi. Chotero, iye analangiza onse kudzipenyerera okha ngati ali m’chikhulupiriro ndipo anapemphera kuti iwo ‘asachita chinthu cholakwika.’ Pomalizira, iye anawasonkhezera kusangalala, kuwongoleredwa ndi kutonthozedwa, kunena chimodzimodzi, ndi kukhala mumtendere. Ndi uphungu wabwino chotani nanga kwa ife!
Pitirizanibe Kudziyesa!
Chotero kalata yachiŵiri ya Paulo kwa Akristu a m’Korinto ikulingalira njira zosiyanasiyana za kudziyesera ngati tiri m’chikhulupiriro. Mawu ake motsimikizirika ayenera kutifulumiza kutonthoza ena, monga mmene Mulungu amatitonthozera m’zisautso zathu zonse. Zimene mtumwiyo ananena ponena za uminisitala Wachikristu ziyenera kutisonkhezera kuwunyamula mokhulupirika pamene tikutsiriza chiyero m’kuwopa Yehova.
Kugwiritsira ntchito uphungu wa Paulo kungatitheketse bwino kukhala owolowa manja ndi othandiza kwenikweni. Komabe, mawu ake ayenera kutisonkhezera kudzitama mwa Yehova, osati pa ife tokha. Ayenera kuzamitsa kuda kwathu nkhaŵa kwachikondi kaamba ka akhulupiriri anzathu. Ndipo motsimikizirika mfundo izi ndi zina m’Akorinto Wachiŵiri zingatithandize ‘kudziyesa tokha ngati tiri m’chikhulupiriro.’
[Bokosi/Chithunzi patsamba 26]
TIUNIKIRE ULEMERERO WA YEHOVA: Pamene Mose anatsika pa Phiri la Sinai ndi magome Aumboni, nkhope yake inanyezimira chifukwa chakuti Mulungu analankhula naye. (Eksodo 34:29, 30) Paulo anatchula ichi ndikuti: ‘Koma ife tonse ndi nkhope yosaphimbika popenyerera monga mwa kalirole ulemerero wa [Yehova], tisandulika m’chithunzithunzi chomwechi kuchokera kuulemerero, monga ngati kuchokera kwa mzimu wa [Yehova].’ (2 Akorinto 3:7-18) Akalirole akale apamanja anapangidwa ndi zitsulo monga bronze kapena mkuwa ndipo anakometseredwa mwakuya kotero kuti akhale ndi popenyetsa pabwino. Mofanana ndi akalirole, odzozedwa amaunikira ulemerero wa Mulungu umene umawala kwa iwo kuchokera kwa Yesu Kristu, ‘kukumaŵasintha [mopita patsogolo] kukhala chithunzi’ chosonyezedwa ndi ulemerero wa Yehova wounikira Mwanayo. (2 Akorinto 4:6; Aefeso 5:1) Kupyolera mumzimu woyera ndi Malemba, Mulungu amapanga mwa iwo ‘umunthu watsopano,’ chiunikiro cha mikhalidwe yake. (Aefeso 4:24; Akolose 3:10) Kaya chiyembekezo chathu nchakumwamba kapena chapadziko lapansi, tiyeni tisonyeze umunthu umenewo ndi kuwuwona kukhala wamtengo wapatali mwaŵi wa kuwunikira ulemerero wa Mulungu muuminisitala wathu.
[Bokosi/Chithunzi patsamba 27]
“ZIDA ZA CHILUNGAMO”: Njira imodzi imene Paulo ndi oyanjana nawo anzake anadziyamikira okha monga aminisitala a Mulungu inali “kupyolera m’zida za chilungamo kulamanja ndi kulamanzere.” (2 Akorinto 6:3-7, NW) Dzanja lamanja linagwiritsiridwa ntchito kuponyera lupanga, ndipo lamanzere kugwirira chikopa. Ngakhale kuti anaukiridwa kumbali zonse, Paulo ndi antchito anzake anali okonzekeretsedwa kumenya nkhondo yauzimu. Iyi inamenyedwa motsutsana ndi aphunzitsi onyenga ndi “atumwi oposatu” kotero kuti mpingo wa ku Korinto usapatutsidwe pa kudzipereka kwa Kristu. Paulo sanatembenukire ku zida za thupi lochimwa—chinyengo, kunama, kapena machenjera. (2 Akorinto 10:8-10; 11:3, 12-14; 12:11, 16) Mmalo mwake, “zida” zogwiritsiridwa ntchito zinali zachilungamo, kapena zachilunjiko, njira yopititsira patsogolo kulambira kowona motsutsana ndi kuwukira konse. Mboni za Yehova tsopano zimagwiritsira ntchito ‘zida zachilungamo’ zoterozo kaamba ka chifuno chofananacho.