Kodi Nkulondoleranji Chilungamo?
M’DZIKO lachiwawa Chigumula chisanadze, mwamuna mmodzi anakhala wosiyana ndi ena. Mwamunayo anali Nowa. Iye ndi banja lake anayenda ndi Mulungu pamene anthu onse anamnyalanyaza Iye. Monga chotulukapo, “Nowa anali munthu wolungama” m’nthaŵi zoipazo, ndipo kwa anthu akudziko osalabadira iye anakhala ‘mlaliki wa chilungamo.’—Genesis 6:9; 2 Petro 2:5.
Panthaŵi ina pafupifupi chaka cha 56 cha Nyengo Yanthu ino, mtumwi Paulo anali m’ndende m’Kaisareya. Pamene anaitanidwa m’ndende yake kukawonekera pamaso pa Bwanamkubwa Felike, Paulo anadyerera mwaŵiwo nalalikira kwa nduna yaikulu ya Roma imeneyi. Kodi ndiiti imene inali mfundo ya mawu ake? ‘Anamfotokozera za chilungamo, ndi chidziletso, ndi chiweruzo chirinkudza.’ (Machitidwe 24:25) Inde, Paulo nayenso anali mlaliki wa chilungamo.
Nkhaŵa imene alambiri a Mulungu okhulupirika aŵiriwa anaisonyeza kaamba ka chilungamo inalidi yoyenerera. Yehova ali “Mulungu wolungama, ndi Mpulumutsi.” (Yesaya 45:21) Chotero, mwambi wouziridwa umatiuza kuti: ‘Njira ya oipa inyansa Yehova; koma akonda wolondola chilungamo.’ (Miyambo 15:9) Atumiki a Mulungu onse ayenera kulondola chilungamo.
Mwachisoni, ambiri lerolino samaulingalira mosamalitsa mkhalidwewu. Iwo amati: ‘Sindimachitira choipa anansi anga, motero ndiri wotsimikiza kuti Mulungu amakondwera nane.’ Kapena angadzitonthoze mwakuti: ‘Pali njira zambiri zosonyezera chilungamo. Zonse zidzakhala bwino malinga ngati ndikhala wowona mtima ndichipembedzo changa.’ Kodi muganiza kuti maganizo a phee oterowo ngolandiridwa ndi Mulungu?
Ena angabutse nkhani yosiyana. Angakhale akudziŵa za ndemanga ya Paulo yakuti: ‘Tsono tayesedwa olungama ndi chikhulupiriro.’ (Aroma 5:1) Polingalira za chimenechi, iwo angadabwe nati: ‘Kodi ndimotani mmene Akristu, oyesedwa kale olungama, angafunikire kupitiriza kulondola chilungamo?’ Kodi mungaliyankhe motani funso loterolo?
Mulungu wa Chilungamo
Mogwirizana ndi dikishonale, chilungamo ndicho kulungama kwa makhalidwe, chilungamo chachiweruzo, kugwirizana ndi lamulo laumulungu kapena lamakhalidwe. Popeza kuti Yehova ali Mulungu wa chilungamo, aliyense wofuna kumkondweretsa ayenera kudera nkhaŵa ponena za mkhalidwe wofunika kwambiri umenewu. “Yehova ndiye wolungama,” anatero wamasalmo. ‘Akonda zolungama: Woongoka mtima adzapenya nkhope yake.’ (Salmo 11:7; Deuteronomo 32:4) Mtumwi Petro anati: ‘Maso a Yehova ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo.’—1 Petro 3:12.
Chotero, sitiyenera kukhala osasamala pamfundoyi, monga momwe Ayuda ambiri analiri. Ambiri a iwo mosakaikira anali anthu odekha amene sanachitire choipa anansi awo. Iwo analinso owona mtima—ngakhale achangu—m’chipembedzo chawo. Koma m’zaka za zana loyamba, ochuluka sanali olungama m’maso mwa Mulungu. Paulo anati: ‘Ndiwachitira iwo umboni kuti ali ndi changu cha kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziŵitso [cholongosoka, NW]. Pakuti pakusadziŵa chilungamo cha Mulungu, ndipo pofuna kukhazikitsa chilungamo cha iwo okha, iwo sanagonja ku chilungamo cha Mulungu.’—Aroma 10:2, 3.
Kodi Ayudawo analakwa poti? Paulo akuti sanalondole chilungamo mogwirizana ndi chidziŵitso cholongosoka. Chitsanzo chawo chopereka chenjezo chimatisonyeza kuti sikokwanira kungokhala ndi umunthu wabwino ndi kupeŵa kuchitira ena choipa. Chimasonyezanso kuti palibe njira zambiri zofikira ku chilungamo. Mwachiwonekere, panali chinthu cholakwika ndinjira yosankhidwa ndi Ayuda ambiri m’tsiku la atumwi. Tingalondole chilungamo mwachipambano kokha ngati timvetsera kwa Mulungu. Bukhu la Miyambo limati: ‘Mwananga, ukalandira mawu anga, ndi kusunga malamulo anga; Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo, zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.’—Miyambo 2:1, 9.
Njira ya Chilungamo
Kuchokera kwa Mose kudzafika kwa Yesu, chilungamo chinagwirizanitsidwa ndi kumvera malamulo a Mulungu monga momwe anasonyezedwera m’Chilamulo cha Mose. Popeza kuti Aisrayeli opanda ungwirowo analephera kusunga malamulowo, iwo anafunikira kupereka nsembe ndi zopereka za uchimo zolangizidwa ndi Chilamulo kotero kuti akhululukidwe liwongo lawo. Mose anauza Aisrayeliwo kuti: ‘Kudzakhala kwa ife chilungamo, ngati tisamalira kuchita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamulira ife.’—Deuteronomo 6:25.
Kwa zaka mazana ambiri palibe munthu amene anatsatira Chilamulocho ndendende. Ngakhale kuli choncho, ambiri anayesayesa mowona mtima kulondola chilungamo mothandizidwa nacho, ndipo Baibulo limatchula ena a ameneŵa kukhala olungama. Mwachitsanzo, makolo a Yohane Mbatizi amafotokozedwa kukhala ‘olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m’malamulo onse ndi zoikika za Yehova osachimwa.’—Luka 1:6.
Komabe, Yesu anatsegula njira yatsopano yolondolera chilungamo. Iye anasunga Chilamulo cha Mose ndendende—munthu yekha yemwe anatha kuchita motero. Yesu anafa pa mtengo wozunzirapo, ndipo Yehova analandira mtengo wa moyo wake wangwiro monga dipo kaamba ka anthu. Kuyambira pamenepo kunka mtsogolo, nsembe za pangano la Chilamulo sizinafunikirenso. Nsembe yangwiro ya Yesu inaphimba machimo a anthu onse a mtima wolungama.—Ahebri 10:4, 12.
Akristu Owona Oyesedwa Olungama
Pamenepa, kuchokera pa imfa ya Yesu, chilungamo chagwirizanitsidwa ndi kusonyeza chikhulupiriro mwa Mwana wolungama ameneyu wa Mulungu. (Yohane 3:16) Pamene kuli kwakuti Ayuda omamatira kumwambo a m’tsiku la Paulo sanapeze chilungamo chifukwa chakuti anakana chidziŵitso cholongosoka chonena za Yesu, timaŵerenga ponena za Akristu okhulupirika kuti: ‘Ayesedwa olungama kwaulere, ndi chisomo chake, mwa chiombolo cha mwa Kristu Yesu.’—Aroma 3:24.
M’mawu apatsogolo ndi pambuyo pa lembali, mawuwa akusonya mwachindunji kwa Akristu odzozedwa amene, chifukwa cha chikhulupiriro chawo m’nsembe ya Yesu, amayesedwa olungama m’lingaliro lakukhala kwawo oloŵa nyumba limodzi ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba. Komabe, lerolino, monga momwe kunawonedweratu ndi mtumwi Yohane, pali khamu lalikulu la Akristu okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi. Awa nawonso amasonyeza chikhulupiriro m’dipo. Iwo ‘amatsuka minjiro yawo ndikuiyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa’ ndipo motero amayesedwa olungama monga mabwenzi a Mulungu ndi lingaliro lakupulumuka kwawo chisautso chachikulu.—Chibvumbulutso 7:9, 14; yerekezerani ndi Yakobo 2:21-26.
Londolanibe Chilungamo
Komabe, onani kuti kulondola kwathu chilungamo sikumagomera pa kukhulupirira Yesu. Timoteo adali Mkristu wodzipereka, wodzozedwa kwa zaka zambiri pamene Paulo anamlembera mawu otsatirawa: ‘Utsate chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso. Limba nayo nkhondo yabwino ya chikhulupiriro.’ (1 Timoteo 6:11, 12; 2 Timoteo 2:22) Kodi nchifukwa ninji Timoteo anafunikira ‘kutsata chilungamo’ ngati Mulungu anali anamyesa kale wolungama?
Chifukwa chakuti liwu lakuti “chilungamo” limagwiritsiridwanso ntchito m’Baibulo m’lingaliro lachisawawa kutanthauza munthu wokhala ndi moyo wamakhalidwe abwino, wowona mtima ndipo amayesayesa monga momwe angathere kumvera malamulo a Mulungu. Ili ndilo lingaliro limene makolo a Yohane Mbatizi analiri olungama. (Luka 1:6) Atate wolera wa Yesu, Yosefe, ndi Yosefe wa ku Arimetiya adalinso olungama mwanjira imeneyi. (Mateyu 1:19; Luka 23:50) Chenicheni chakuti Akristu ayesedwa olungama sichimawachotsera thayo lawo lakulondola chilungamo m’lingaliro limeneli. Ndithudi, Mkristu aliyense amene aleka kukhala ndi moyo wamakhalidwe abwino, wowona mtima kapena kulephera kumvera malamulo a Mulungu adzataya kaimidwe kake kolungama pamaso pa Yehova.
Kulondola Chilungamo—Chitokoso
Kulondola chilungamo ndiko chitokoso. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tonsefe tiri opanda ungwiro ndipo tiri ndi chikhoterero champhamvu kulinga ku chisalungamo. (Genesis 8:21; Aroma 7:21-23) Ndiponso, tikukhala m’dziko limene limalimbikitsa malingaliro ndi machitidwe osalungama ndipo likulamuliridwa ndi Satana Mdyerekezi, “woipayo.” (1 Yohane 5:19; 2 Akorinto 4:4) Nkosadabwitsa kuti polembera Timoteo, Paulo anagwirizanitsa kulondola chilungamo ndi ‘kumenya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro’!—1 Timoteo 6:11, 12.
Kodi tingakhale achipambano mu “nkhondo yabwino” imeneyi? Inde, koma kokha ngati tikulitsa chikondi chochokera mumtima cha miyezo ya Yehova ndi udani wa chimene chiri choipa. Baibulo limati ponena za Yesu: ‘Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa.’ (Ahebri 1:9) Tiyenera kukhala ndi maganizo ofanana awa: chikhumbo champhamvu chakukulitsa kukonda zomkondweretsa Mulungu ndi kuipidwa ndi chirichonse chosamkondweretsa.
Panthaŵi imodzimodzi, tiyenera kukumbukira kuti kulondola chilungamo sindiko mpikisano. Ngati timadzilingalira kukhala abwino kuposa ena, kapena ngati tiri onyada ndi chilungamo chathu, pamenepo tifanana ndi Afarisi Achiyuda. (Mateyu 6:1-4) Anthu amene amalondola chilungamo mwachipambano amadzilingalira modzichepetsa kwenikweni, ‘akumalingalira ena kukhala owaposa.’—Afilipi 2:3.
Paulo anagogomezera kufunika kwa phunziro Labaibulo polondola chilungamo pamene analemba kuti: ‘Lemba lirilonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m’chilungamo.’ (2 Timoteo 3:16) Ngati tiphunzira Baibulo ndi kupezeka pamisonkhano Yachikristu kumene Baibulo limakambitsiridwa, tidzaphunzitsidwa m’chilungamo. Baibulo likhoza kutikonza kotero kuti tivale ‘umunthu watsopano, umene unalengedwa m’chilungamo chenicheni, ndi m’chiyero.’—Aefeso 4:24.
Pamene chilungamo chikhala mbali yaikulu mwa ife, tidzadadi kusayeruzika. Sitidzayesedwa kufunafuna mayanjano oipa adziko lino. (1 Akorinto 15:33) Sitidzasonkhezeredwa kukonda zinthu za dziko lino kapena kugonja ku mapindu a zinthu zakuthupi adziko lino. (Miyambo 16:8; 1 Timoteo 6:9, 10; 1 Yohane 2:15-17) Ndithudi, sitidzakopeka ndi zosangulutsa zoipa ndi zachiwawa zimene zafalikira ponseponse lerolino.—Aefeso 5:3, 4.
Madalitso a Chilungamo
Inde, kulondola chilungamo mwanjira ya Yehova kuli chitokoso, koma nkhondoyo njabwino. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti imatsogolera kukusangalala kwathu ndi unansi waumwini ndi Yehova. Uli mwaŵi wapadera chotani nanga! Baibulo limatiuza kuti: “[Yehova] adalitsa mokhalamo olungama.” “Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.” (Miyambo 3:33; 15:29) Ndiponso, timafika pakumvetsetsa kwenikweni zifuniro za Yehova. ‘Mayendedwe a olungama akunga kuunika kwa mbandakucha, kunkabe kuwala kufikira usana woti mbe.’—Miyambo 4:18.
Baibulo limalonjeza chitetezo kwa ofunafuna chilungamo pamene dongosolo lazinthu losalungama liripoli lifika kumapeto ake. ‘Funani Yehova, ofatsa inu nonse am’dziko, amene munachita chiweruzo chake; funani chilungamo, funani chifatso; kapena mudzabisika tsiku la mkwiyo wa Yehova.’ (Zefaniya 2:3) Kenaka, kwa awo okhala ndi chiyembekezo chapadziko lapansi, Baibulo limapereka lonjezo lozizwitsadi lakuti: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Salmo 37:29.
Ha ndizifukwa zabwino chotani nanga zolondolera chilungamo! Monga momwe Mulungu iyemwini amanenera kuti: ‘Wolondola chilungamo ndi chifundo apeza moyo, ndi chilungamo, ndi ulemu.’—Miyambo 21:21.