“Kuunika Kunadza ku Dziko Lapansi”
‘Chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika.’—YOHANE 3:19.
1. Kodi nchifukwa ninji aliyense ayenera kukhala wodera nkhaŵa ndi chiweruzo cha Mulungu?
ANTHU ambiri lerolino samadera nkhaŵa kwambiri ndi chiweruzo cha Mulungu. Ena amaganiza mosasamala kuti Mulungu adzawaweruza mwachiyanjo malinga ngati iwo amapita kutchalitchi mokhazikika ndipo sachita zoipa kwa anansi awo. Kwa ambiri, ziphunzitso za Chikristu Chadziko zonena za moto wa helo ndi purigatoriyo zachotseratu lingaliro lonse la chiweruzo chaumulungu. Koma mphwayi yofalikira ndi mabodza a Chikristu Chadziko sizingasinthe chenicheni chakuti pomalizira pake munthu aliyense adzaweruzidwa ndi Mulungu. (Aroma 14:12; 2 Timoteo 4:1; Chibvumbulutso 20:13) Ndipo zambiri zidzadalira pa chiweruzo chimenechi. Awo amene adzaweruzidwa mwachiyanjo adzalandira mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha, pamene awo amene sadzaweruzidwa mwachiyanjo adzalandira malipiro okwanira a tchimo: imfa.—Aroma 6:23.
2. Kodi nchiyani chimene chiri maziko a chiweruzo cha Mulungu?
2 Chotero, Akristu owona amadera nkhaŵa ndi chiweruzo cha Mulungu, ndipo amafunitsitsa kumkondweretsa. Kodi ndimotani mmene angachitire zimenezi? Pa Yohane 3:19, Yesu akupereka mfungulo. Iye akuti: ‘Chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza ku dziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zawo zinali zoipa.’ Inde, chiweruzo cha Mulungu chidzazikidwa pa mfundo yakuti kaya timakonda kuunika m’malo mwa mdima.
“Mulungu Ndiye Kuunika”
3. Kodi mdima nchiyani, ndipo kodi kuunika nchiyani?
3 M’lingaliro lauzimu, mdima umatanthauza umbuli ndi kupanda chiyembekezo kumene kuli m’malo okhala Satana—ngakhale kuti kaŵirikaŵiri Satana amadziyerekezera kukhala “mngelo wa kuunika.” (2 Akorinto 4:4; 11:14; Aefeso 6:12) Kumbali ina, kuunika kumatanthauza kumvetsetsa ndi chiunikiro zomwe zimachokera kwa Yehova Mulungu. Paulo analankhula za kuunika pamene analemba kuti: ‘Pakuti Mulungu amene anati, Kuunika kudzawala kutuluka mumdima, ndiye amene anawala m’mitima yathu kutipatsa chiwalitsiro cha chidziŵitso cha ulemerero wa Mulungu pankhope pa Yesu Kristu.’ (2 Akorinto 4:6) Kuunika kwauzimu kumagwirizanitsidwa mwathithithi ndi Yehova Mulungu kotero kuti mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu ndiye kuunika.”—1 Yohane 1:5; Chibvumbulutso 22:5.
4. (a) Kodi ndimotani mmene Yehova waperekera kuunika? (b) Kodi tingachisonyeze motani chikondi chathu kaamba ka kuunika?
4 Yehova wapereka kuunika kupyolera mwa mawu ake, omwe lerolino amapezeka mosavuta mumpangidwe wolembedwa m’Baibulo Lopatulika. (Salmo 119:105; 2 Petro 1:19) Chifukwa chake, wamasalmo anali kufotokozadi kukonda kwake kuunikako pamene analemba kuti: ‘Ha! Ndikondadi chilamulo chanu; ndilingiriramo ine tsiku lonse. Moyo wanga usamalira mboni zanu; ndipo ndizikonda kwambiri.’ (Salmo 119:97, 167) Kodi mumakonda kuunikako monga momwedi mwachiwonekere anakukondera wamasalmoyo? Kodi mumaŵerenga mokhazikika Mawu a Mulungu, kusinkhasinkha pa iwo, ndikuyesetsa mwamphamvu kugwiritsira ntchito zimene amanena? (Salmo 1:1-3) Ngati nditero, mukufuna kulandira chiweruzo chachiyanjo kwa Yehova.
“Ndiri Kuunika kwa Dziko Lapansi”
5. Kodi kuunika kwaumulungu kumasumika pa yani?
5 Kuunika kopatsa moyo kochokera kwa Yehova kumasumika pa munthuyo Yesu Kristu. M’mawu oyambirira a Uthenga Wabwino wa Yohane, timaŵerenga kuti: “Mwa [Yesu] munali moyo; ndi moyowu unali kuunika kwa anthu. Ndipo kuunikaku kunawala mumdima; ndi mdimawu sunakuzindikira.” (Yohane 1:4, 5) Ndithudi, Yesu ali wogwirizana kwenikweni ndi kuunikaku kotero kuti akutchedwa “kuunika kweni kweni, kumene kuunikira anthu onse.” (Yohane 1:9) Yesu iyemwiniyo anati: “Pakukhala Ine m’dziko lapansi, ndiri kuunika kwa dziko lapansi.”—Yohane 9:5.
6. Kodi nchiyani chimene munthu ayenera kuchita kuti alandire chiweruzo chachiyanjo chotsogolera ku moyo wosatha?
6 Chotero, awo amene amakonda kuunika amakonda Yesu ndipo amamkhulupirira. Nkosatheka kulandira chiweruzo chachiyanjo popanda kusonya kwa Yesu. Inde, kuli kokha mwakuyang’ana kwa iye monga njira yoikidwa ndi Mulungu yachipulumutso pamene tingalandire chiweruzo chachiyanjo. Yesu anati: ‘Iye amene akhulupirira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupirira Mwanayo sadzaona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.’ (Yohane 3:36) Komabe, kodi kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu kumatanthauzanji?
7. Kodi kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu kumatanthauzanso kusonyeza chikhulupiriro mwa yani?
7 Choyamba, Yesu iyemwini anati: ‘Iye wokhulupirira ine, sakhulupirira ine, koma iye wondituma ine. Ndipo wondiona ine aona amene anandituma ine. Ndadza ine kuunika ku dziko lapansi, kuti yense wokhulupirira ine asakhale mumdima.’ (Yohane 12:44-46) Awo amene amakonda Yesu ndikusonyeza chikhulupiriro mwa iye ayeneranso kukhala ndi chikondi chakuya ndi chikhulupiriro mwa Yehova, Mulungu ndi Atate wa Yesu. (Mateyu 22:37; Yohane 20:17) Alionse amene amagwiritsira ntchito dzina la Yesu m’kulambira kwawo koma amalephera kupereka ulemu waukulu kwa Yehova samasonyeza chikondi chenicheni cha kuunikako.—Salmo 22:27; Aroma 14:7, 8; Afilipi 2:10, 11.
‘Mtsogoleri Wamkulu’ wa Mulungu
8. Kodi ndimotani mmene kuunika kwaumulungu kunasumikira pa Yesu ngakhale pamene anali asanabadwe monga munthu?
8 Kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu kumatanthauzanso kuvomereza kotheratu thayo lake m’zifuno za Yehova. Kufunika kwa thayo limeneli kunagogomezeredwa pamene mngelo anati kwa Yohane: ‘Umboni wa Yesu ndiwo mzimu wa chinenero.’ (Chibvumbulutso 19:10; Machitidwe 10:43; 2 Akorinto 1:20) Kuyambira pa ulosi woyamba weniweni m’Edene, maulosi onse ouziridwa ndi Mulungu amakhudza Yesu kotheratu ndi malo ake m’kukwaniritsa zifuno za Mulungu. Mofananamo, Paulo anauza Akristu a ku Galatiya kuti pangano la Chilamulo linali “namkungwi . . . wakutifikitsa kwa Kristu.” (Agalatiya 3:24) Pangano la Chilamulo lakale limenelo linalinganizidwira kukonzekeretsa mtunduwo kaamba ka kudza kwa Yesu monga Mesiya. Choncho ngakhale pamene kubadwa kwake kwaumunthu kusanachitike, kuunika kochokera kwa Yehova kunasumika pa Yesu.
9. Kodi kukonda kuunikako kwaphatikizapo chiyani chiyambire 33 C.E.?
9 Mu 29 C.E., Yesu anadzipereka yekha kaamba ka ubatizo ndipo anadzozedwa ndi mzimu woyera, mwakutero anakhala Mesiya wolonjezedwayo. Mu 33 C.E. iye anafa ali munthu wangwiro, anaukitsidwa, anakwera kumwamba, ndipo kumeneko anapereka mtengo wa moyo wake kaamba ka machimo athu. (Ahebri 9:11-14, 24) Mpambo wa zochitika umenewu unazindikiritsa posinthira m’zochitika za Mulungu ndi anthu. Yesu tsopano anali “Mtsogoleri Wamkulu wa moyo,” ‘Mtsogoleri Wamkulu wa chipulumutso,’ “Mtsogoleri Wamkulu ndi Wokwaniritsa wa chikhulupiriro chathu.” (Machitidwe 3:15, NW; Ahebri 2:10, NW; 12:2, NW; Aroma 3:23, 24) Kuyambira 33 C.E. kumka mtsogolo, okonda kuunika azindikira, ndipo avomereza, kuti popanda Yesu ‘palibe chipulumutso mwa wina yense, pakuti palibe dzina lina pansi pa thambo la kumwamba, lopatsidwa mwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.’—Machitidwe 4:12.
10. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kumvetsera ku mawu a Yesu ndikuwalabadira?
10 Kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu kumatanthauzanso kumvomereza monga ‘Mawu,’ ndi “Phungu Wodabwitsa.” (Yohane 1:1; Yesaya 9:6, NW) Zimene Yesu amanena nthaŵi zonse zimawonetsera chowonadi chaumulungu. (Yohane 8:28; Chibvumbulutso 1:1, 2) Kumvetsera kwa iye ndi nkhani ya moyo ndi imfa. Yesu anauza Ayuda a m’nthaŵi yake kuti: ‘Iye wakumva mawu anga, ndi kukhulupirira iye amene anandituma ine, ali nawo moyo wosatha, ndipo salowa m’kuweruza, koma wachokera ku imfa.’ (Yohane 5:24) M’zaka za zana loyamba la C.E., awo amene anachita mogwirizana ndi mawu a Yesu anawonjoledwa ku mdima wa dziko la Satana ndipo anabwera ku moyo, kunena kwake titero. Iwo analengezedwa olungama m’lingaliro lakukhala olowa nyumba ndi iye mu Ufumu wake wakumwamba. (Aefeso 1:1; 2:1, 4-7) Lerolino, kumvera mawu a Yesu kumatsegulira ambiri njira yakulengezedwa olungama m’lingaliro lakupulumuka Armagedo ndi kukhala ndi moyo waumunthu wangwiro m’dziko latsopano.—Chibvumbulutso 21:1-4; yerekezerani ndi Yakobo 2:21, 25.
“Mutu Pamtu pa Zonse”
11. Kodi ndi ulamuliro wapamwamba wotani umene unaperekedwa kwa Yesu mu 33 C.E.?
11 Pambuyo pa kuuka kwake, Yesu anaululira otsatira ake mbali ina ya kuunika. Iye anati: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa ine kumwamba ndi pa dziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Motero Yesu anakwezedwa kumalo apamwamba m’gulu la chilengedwe chonse la Yehova. Paulo akupereka tsatanetsatane wowonjezereka pamene akunena kuti: ‘[Mulungu] anamuukitsa Kristu kwa akufa, namkhazikitsa pa dzanja lake lamanja m’zakumwamba, pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lirilonse lotchedwa, si m’nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza; ndipo anakonza zonse pansi pa mapazi ake, nampatsa iye akhale mutu pamtu pa zonse, kwa [mpingo, NW] umene uli thupi lake.’ (Aefeso 1:20-23; Afilipi 2:9-11) Chiyambire 33 C.E., kukonda kuunikako kwaphatikizapo kuvomereza malo okwezeka a Yesu ameneŵa.
12. Kodi Akristu odzozedwa anavomereza chiyani mwachimwemwe kuyambira pachiyambi, ndipo kodi ndimotani mmene asonyezera chimenechi mogwira ntchito?
12 Potsirizira pake, anthu onse adzafunikira kuvomereza ulamuliro wa Yesu. (Mateyu 24:30; Chibvumbulutso 1:7) Komabe, mwachimwemwe, okonda kuunikako anakuzindikira kuyambira pachiyambi. Ziŵalo zodzozedwa za mpingo Wachikristu zimamlandira Yesu monga “mutu wa thupi, [mpingowo, NW].” (Akolose 1:18; Aefeso 5:23) Pamene iwo akhala mbali ya thupi limenelo, ‘amalanditsidwa ku ulamuliro wa mdima, nasunthidwira kuloŵa m’ufumu wa Mwana wa chikondi cha Mulungu.’ (Akolose 1:13) Monga chotulukapo, iwo amatsata mofunitsitsa utsogoleri wa Yesu m’mbali iriyonse ya miyoyo yawo, ndipo m’nthaŵi yathu iwo aphunzitsa “nkhosa zina” kuchita zofananazo. (Yohane 10:16) Kuvomereza umutu wa Yesu ndiko chiyeneretso chachikulu cholandirira chiweruzo chachiyanjo.
13. Kodi ndiliti pamene Yesu anayamba kugwiritsira ntchito ulamuliro wa Ufumu, ndipo kodi nchiyani chimene chatsatira pano padziko lapansi?
13 Pamene anakwera kumwamba mu 33 C.E., Yesu sanayambe panthaŵi yomweyo kugwiritsira ntchito ulamuliro wake ku mlingo wotheratu. Ngakhale kuti ndiye Mutu wa mpingo Wachikristu, iye anayembekezera nthaŵi yoyenera yogwiritsira ntchito ulamuliro wotheratu pa anthu onse mwachisawawa. (Salmo 110:1; Machitidwe 2:33-35) Nthaŵi imeneyo inafika mu 1914, pamene Yesu anaikidwa pampando wachifumu monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo “masiku otsiriza” a dzikoli anayamba. (2 Timoteo 3:1) Chiyambire 1919, kusonkhanitsidwa kwa otsalira odzozedwa kwapitiriza kulinga kumapeto ake. Makamaka kuyambira mu 1935, Yesu wakhala akulekanitsa anthu kukhala “nkhosa,” omwe adzalowa “ufumu wokonzedwera [iwo],” ndi “mbuzi,” amene “adzasadzidwa kosatha.”—Mateyu 25:31-34, 41, 46, NW.
14. Kodi ndimotani mmene khamu lalikulu lasonyezera kukonda kuunikako, ndipo kodi nchiyani chidzatulukapo kwa iwo?
14 Mwachimwemwe, nkhosazo zatsimikizira kukhala zambiri m’masiku ano otsiriza. Khamu lalikulu la izo lomafika mamiliyoni lawonekera pankhope ya dziko ‘lochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ Mofanana ndi atsamwali awo, odzozedwa, anthu onga nkhosa ameneŵa amakonda kuunika. Iwo ‘atsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa,’ ndipo akufuula ndi mawu aakulu kuti: ‘Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pa mpando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.’ Chifukwa cha chimenechi, khamu lalikululo monga gulu lidzalandira chiweruzo chachiyanjo. Ziŵalo zake ‘zatuluka m’chisautso chachikulu,’ kupulumuka chiwonongeko cha pa Armagedo cha awo amene amakonda mdima.—Chibvumbulutso 7:9, 10, 14.
“Ana a Kuunika”
15. Kodi ndimotani mmene zochita zathu zimasonyezera kugonjera kwathu kwa Mfumuyo, Yesu Kristu?
15 Komabe, kodi ndimotani mmene okonda kuunikako, kaya odzozedwa kapena nkhosa zina, amagonjerera m’njira yogwira ntchito kwa Yesu monga amene waikidwa ndi Mulungu pampando wachifumu kukhala Mfumu ndi Woweruza? Njira imodzi ndiyo kuyesa kukhala anthu amene Yesu amavomereza. Pamene anali padziko lapansi, Yesu anasonyeza chiyamikiro kaamba ka mikhalidwe yonga ngati kuwona mtima, kudzipereka kwamtima wonse, ndi kutenthedwa maganizo kaamba ka chowonadi, ndipo iye mwiniyo anasonyeza mikhalidwe imeneyi. (Marko 12:28-34, 41-44; Luka 10:17, 21) Ngati tikufuna chiweruzo chachiyanjo, tiyenera kukulitsa mikhalidwe yoteroyo.
16. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kuvula ntchito za mdima?
16 Izi nzowonadi makamaka popeza kuti mdima wa dziko la Satana ukuderaderabe pamene mapeto akuyandikira. (Chibvumbulutso 16:10) Chotero, mawu a mtumwi Paulo kwa Aroma ali oyenerera kwambiri: ‘Usiku wapita, ndi dzuwa layandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ntivale [zida za, NW] kuunika. Tiyendeyende koyenera, monga usana; si m’madyerero ndi kuledzera ayi, si m’chigololo ndi chonyansa ayi; si mu ndewu ndi nkhwidzi ayi.’ (Aroma 13:12, 13) Pamene kuli kwakuti moyo wosatha ndi mphatso yochokera kwa Mulungu, kuwona kwa chikhulupiriro chathu ndi kukonda kwathu kuunikako kumasonyezedwa ndi zochita zathu. (Yakobo 2:26) Chifukwa chake, chiweruzo chimene tidzalandira chidzadalira ku mlingo waukulu pa ukulu umene timachita ntchito zabwino ndikuda ntchito zoipa.
17. Kodi ‘kuvala Ambuye Yesu Kristu’ kumatanthauzanji?
17 Pambuyo popereka uphungu wake pa Aroma 13:12, 13, mtumwi Paulo akumaliza mwakunena kuti: ‘Valani inu Ambuye Yesu Kristu, ndipo musaganizire za thupi kuchita zofuna zake.’ (Aroma 13:14) Kodi ‘kuvala Ambuye Yesu Kristu’ kumatanthauzanji? Kumatanthauza kuti Akristu ayenera kutsatira Yesu mosamalitsa, kudziveka iwo okha, kunena kwake titero, ndi chitsanzo chake ndi mkhalidwe wamaganizo, kuyesayesa kukhala onga Kristu. ‘Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa,’ anatero Petro, ‘pakutinso Kristu anamva zowawa m’malo mwanu, nakusiyirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.’—1 Petro 2:21.
18. Kodi ndikusintha kwakukulu kotani kumene kungafunikire ngati tikufuna kulandira chiweruzo chachiyanjo?
18 Kaŵirikaŵiri ichi chaphatikizapo masinthidwe aakulu m’moyo wa Mkristu. “Pakuti kale munali mdima,” anatero Paulo, ‘koma tsopano muli kuunika mwa Ambuye; yendani monga ana a kuunika, pakuti chipatso cha kuunika tichipeza m’ubwino wonse, ndi chilungamo, ndi chowonadi.’ (Aefeso 5:8, 9) Onse amene amachita ntchito za mdima sali okonda kuunika ndipo sadzalandira chiweruzo chachiyanjo pokhapo ngati apanga masinthidwe.
“Inu Ndinu Kuunika kwa Dziko Lapansi”
19. Kodi ndi m’njira zosiyana zotani zimene Mkristu angawalitsire kuunikako?
19 Pomalizira, kukonda kuunika kumatanthauza kuwalitsa kuunikako kotero kuti ena angakuone ndi kukopedwa nako. “Inu ndinu kuunika kwa dziko lapansi,” anatero Yesu. Ndipo anawonjezera kuti: ‘Muwalitse inu kuunika kwanu pamaso pa anthu, kuti pakuona ntchito zanu zabwino, alemekeze Atate wanu wa kumwamba.’ (Mateyu 5:14, 16) Ntchito zabwino za Mkristu zimaphatikizapo kusonyeza ubwino uliwonse ndi chilungamo ndi chowonadi, popeza kuti mkhalidwe wabwino umenewo umapereka umboni wamphamvu wa chowonadi. (Agalatiya 6:10; 1 Petro 3:1) Izo zimaphatikizapo makamaka kulankhula ndi ena ponena za chowonadi. Lerolino, izi zimatanthauza kukhala ndi phande m’ndawala yadziko lonse yolalikira “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu . . . padziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse.” Zimatanthauza kubwereranso moleza mtima kwa anthu okondwerera, kuphunzira nawo Baibulo, ndikuwathandiza kutulutsa ntchito za kuunika.—Mateyu 24:14, NW; 28:19, 20.
20. (a) Kodi kuunikako kukuwala mokulira chotani lerolino? (b) Kodi ndimadalitso olemera otani amene akusangalalidwa ndi awo amene akuvomereza kuunikako?
20 M’tsiku lathu, chifukwa cha ntchito yolalikira mwachangu ya Akristu okhulupirika, mbiri yabwino ikumvedwa m’maiko oposa 200, ndipo kuunikako kukuwala kuposa ndi kalelonse. Yesu anati: “Ine ndine kuunika kwa dziko lapansi; iye wonditsata Ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala nako kuunika kwa moyo.” (Yohane 8:12) Nkosangalatsa chotani nanga kukhala ndi phande m’kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli! Miyoyo yathu njolemera kwambiri tsopano popeza kuti sitikupupulika mumdima wa dziko la Satana. Ndipo ziyembekezo zathu nzabwino koposadi pamene tikuyang’ana kutsogolo ku chiweruzo chachiyanjo kuchokera kwa Woweruza woikidwa ndi Yehova. (2 Timoteo 4:8) Lingakhale tsoka lotani nanga ngati, titafika ku kuunika, tibwerera mumdima ndikulandira chiweruzo chopanda chiyanjo! M’nkhani yotsatira, tidzakambitsirana mmene tingakhalire olimba m’chikhulupiriro.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi nchiyani chimene chiri maziko a chiweruzo cha Mulungu?
◻ Kodi ndithayo lalikulu lotani limene Yesu ali nalo m’chigwirizano ndi zifuno za Mulungu?
◻ Kodi timasonyeza motani kuti ndife ogonjera kwa Yesu monga amene Yehova wamuika pampando wachifumu kukhala Mfumu?
◻ Kodi tingadzitsimikizire motani kukhala “ana a kuunika”?
◻ Mumdima uno wa dziko, kodi ndimotani mmene kuunikako kukuwalira kuposa ndi kalelonse?
[Chithunzi patsamba 10]
Potsirizira pake, anthu onse adzazindikira ulamuliro wa Yesu
[Chithunzi patsamba 12]
Timasonyeza kuti timakonda kuunikako pamene tikuwalitsa kwa ena