Dalirani Dzanja lopulumutsa la Yehova
‘Inu Yehova, . . . mukhale dzanja lathu m’mawa ndi m’mawa, chipulumutso chathunso m’nthaŵi ya mavuto.’—YESAYA 33:2.
1. Kodi Yehova ali ndi dzanja lamphamvu m’lingaliro lotani?
YEHOVA ali ndi dzanja lamphamvu. Indetu, popeza kuti “Mulungu ndiye mzimu,” ilo sidzanja lanyama. (Yohane 4:24) Mu Baibulo, dzanja lophiphiritsira limatanthauza kukhoza kwa kuchita zamphamvu. Motero, Mulungu amapulumutsa anthu ake ndi dzanja lake. Ndithudi, ‘ngati mbusa, Mulungu amadyetsa zoweta zake. Nasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nawatengera pa chifuwa chake.’ (Yesaya 40:11; Salmo 23:1-4) Ha, anthu a Yehova amachimva motani nanga chisungiko m’dzanja lake lachikondi!—Yerekezerani ndi Deuteronomo 3:24.
2. Kodi ndimafunso otani panopa amene tifunikira kuwalingalira?
2 Kodi ndimotani mmene dzanja la Yehova lapulumutsira anthu ake, m’nthaŵi zakale ndi lerolino? Kodi ndichithandizo chotani chimene Mulungu amawapatsa monga mpingo? Ndipo kodi nchifukwa ninji anthu ake angadalire dzanja lake lopulumutsa m’mavuto awo onse?
Dzanja Lopulumutsa la Mulungu Likugwira Ntchito
3. Kodi Malemba amasonyeza kuti ndani anamasula Aisrayeli ku Igupto?
3 Asanamasule Aisrayeli ku ukapolo wa Aigupto zaka 3,500 zapitazo, Mulungu anauza mneneri wake Mose kuti: ‘Nena kwa ana a Israyeli, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aaigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuwombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu.’ (Eksodo 6:6) Malinga ndi mtumwi Paulo, Mulungu anatulutsa Aisrayeli mu Igupto “ndi dzanja lokwezeka.” (Machitidwe 13:17) Ana aamuna a Kora anasonyeza chigonjetso cha Dziko Lolonjezedwa kukhala cha Mulungu, mwakunena kuti: ‘Sanalanda dziko ndi lupanga lawo, ndipo mkono wawo sunawapulumutsa: Koma dzanja lanu lamanja, ndi mkono wanu, ndi kuunika kwa nkhope yanu. Popeza munakondwera nawo.’—Salmo 44:3.
4. Kodi kudalira dzanja lopulumutsa la Yehova kunafupidwa motani m’nthaŵi ya kuukira kwa Asuri?
4 Dzanja la Yehova linathandizanso anthu ake m’masiku a kuukira kwa Asuri. Panthaŵiyo mneneri Yesaya anapemphera kuti: ‘Inu Yehova, mutikomere ife mtima; ife talindira inu; mukhale dzanja lathu m’mawa ndi m’mawa, chipulumutso chathunso m’nthaŵi ya mavuto.’ (Yesaya 33:2) Pemphero limenelo linayankhidwa pamene mngelo wa Mulungu anapha 185,000 mumsasa wa Asuri, kupangitsa Mfumu Sanakeribu kusiya Yerusalemu “ndi nkhope yamanyazi.” (2 Mbiri 32:21; Yesaya 37:33-37) Kudalira dzanja lopulumutsa la Yehova kumafupa nthaŵi zonse.
5. Kodi dzanja lamphamvu la Mulungu linawachitiranji Akristu ozunzidwa kumapeto kwa Nkhondo Yadziko ya I?
5 Dzanja lamphamvu la Mulungu linapulumutsa Akristu odzozedwa ozunzidwa kumapeto kwa Nkhondo Yadziko ya I. Mu 1918 malikulu a Bungwe Lolamulira anaukiridwa mwachiwawa ndi adani awo, ndipo abale odziŵika bwino anaponyedwa m’ndende. Powopa maulamuliro akudziko, odzozedwawo analekeratu ntchito yawo ya kuchitira umboni. Koma iwo anapemphera kuti ayambenso ndikuti ayeretse tchimo lakusagwira ntchito ndi chidetso cha kuchita mantha. Mulungu anayankha mwakuchititsa abale oponyedwa m’ndendewo kumasulidwa, ndipo mwamsanga pambuyo pake milandu yawo inafafanizidwa. Monga chotulukapo cha chowonadi cholongosoledwa pa msonkhano wawo mu 1919 ndi kutsanuliridwa kwa mzimu wa Mulungu wowapatsanso nyonga, odzozedwawo anadzutsidwanso ku utumiki wopanda mantha kwa Yehova m’kukwaniritsidwa komalizira kwa Yoweli 2:28-32.—Chibvumbulutso 11:7-12.
Chithandizo Mumpingo
6. Kodi timadziŵa motani kuti kuli kotheka kupirira mkhalidwe wopereka chiyeso mumpingo?
6 Pamene Mulungu akuchirikiza gulu lake lonse, dzanja lake limalimbikitsanso mmodzi ndi mmodzi wa iwo. Ndithudi, mikhalidwe siyangwiro mumpingo uliwonse chifukwa chakuti anthu onse ali opanda ungwiro. (Aroma 5:12) Chotero atumiki ena a Yehova pa nthaŵi zina angakumane ndi mkhalidwe wopereka chiyeso mumpingo. Mwachitsanzo, ngakhale kuti Gayo anachita ‘chokhulupirika’ mwakulandira mochereza abale ocheza, Diotrefe sanawalandire ndipo anayesa ngakhale kuwachotsa mumpingo aja ochereza. (3 Yohane 5, 9, 10) Komabe, Yehova anamthandiza Gayo ndi ena kupitirizabe kukhala ochereza pochirikiza ntchito yolalikira Ufumu. Kudalira Mulungu mwapemphero kuyenera kutithandiza kupitirizabe kuchita ntchito zokhulupirika pamene tikuyembekeza kuti iye awongolere mkhalidwe umene ungakhale ukuyesa chikhulupiriro chathu.
7. Kodi Akristu okhulupirika anakhala ndi moyo wogwirizana ndi kudzipereka kwawo kwa Mulungu mosasamala kanthu za mikhalidwe yotani yokhala mumpingo wa ku Korinto?
7 Bwanji ngati munayanjana ndi mpingo wa Korinto wa m’zaka za zana loyamba. Panthaŵi ina, mipatuko inawopseza umodzi wake, ndipo kulekerera mikhalidwe yoipa kunadodometsa mzimu wake. (1 Akorinto 1:10, 11; 5:1-5) Okhulupirira anaperekana ku makhoti akudziko, ndipo ena anakangana pa nkhani zosiyanasiyana. (1 Akorinto 6:1-8; 8:1-13) Ndewu, nsanje, mkwiyo, ndi kusamvana kunapangitsa moyo kukhala wovuta. Ena anakaikiradi ulamuliro wa Paulo ndi kunyozera luso lake lakulankhula. (2 Akorinto 10:10) Komabe, okhulupirika oyanjana ndi mpingowo anakhala ndi moyo wogwirizana ndi kudzipereka kwawo kwa Mulungu m’nthaŵi yovuta imeneyo.
8, 9. Kodi tiyenera kuchitanji ngati tiyang’anizana ndi mkhalidwe wotiika pachiyeso mumpingo?
8 Ngati pabuka mkhalidwe wotiika pachiyeso, tifunikira kumamatira kwa anthu a Mulungu. (Yerekezerani ndi Yohane 6:66-69.) Tiyeni tilezerane mtima, tikumazindikira kuti ena zimawatengera nthaŵi yaitali kuposa ena “kuvala umunthu watsopano” ndi kudziveka chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, ndi chipiriro. Popeza kuti atumiki a Mulungu amakhalanso ndi makulidwe osiyana, tonsefe tifunikira kusonyeza chikondi ndi kukhululukirana.—Akolose 3:10-14, NW.
9 Pambuyo pothera zaka zambiri muutumiki wa Yehova, mbale wina anati: “Ngati pali chinthu chofunika koposa kwa ine, ndicho kukhala pafupi ndi gulu lowoneka la Yehova. Zokumana nazo zanga zoyambirira zinandiphunzitsa mmene kuliri kosanunkha kanthu kudalira pa kulingalira kwaumunthu. Pamene maganizo anga anaiwona mfundoyo, ndinatsimikiza mtima kumamatira ku gulu lokhulupirikalo. Kodi ndimwanjira itinso imene munthu angapezere chiyanjo ndi dalitso la Yehova?” Kodi nanunso mumasamalira mwaŵi wanu wa kutumikira Yehova ndi anthu ake achimwemwe? (Salmo 100:2) Ngati nditero, simudzalola chirichonse kukufufunulani ku gulu la Mulungu kapena kuwononga unansi wanu ndi Uyo amene dzanja lake limapulumutsa onse omkonda.
Chithandizo Pamene Tiyesedwa
10. (a) Kodi ndimotani mmene pemphero limathandizira anthu a Mulungu kuyang’anizana ndi chiyeso? (b) Kodi Paulo anapereka chitsimikizo chotani pa 1 Akorinto 10:13?
10 Monga anthu okhulupirika oyanjana ndi gulu la Mulungu, timakhala ndi chithandizo chake m’nthaŵi ya chiyeso. Mwachitsanzo, iye amatithandiza kusunga umphumphu wathu kwa iye pamene tikuyesedwa. Ndithudi, tiyenera kupemphera mogwirizana ndi mawu a Yesu akuti: “Musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo,” Satana Mdyerekezi. (Mateyu 6:9-13) Mwakutero, timapempha Mulungu kusatilola kulephera pamene tiyesedwa kusamvera iye. Iyenso amayankha mapemphero athu kotero kuti nzeru ilake ziyeso. (Yakobo 1:5-8) Ndipo atumiki a Yehova angakhale otsimikiza za chithandizo chake, pakuti Paulo anati: ‘Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.’ (1 Akorinto 10:13) Kodi chiyeso choterocho chimachokera kuti, ndipo ndimotani mmene Mulungu amaikira populumukirapo?
11, 12. Kodi Aisrayeli anagonja ku ziyeso zotani, ndipo kodi zokumana nazo zawo zingatithandize motani?
11 Chiyeso chimachokera ku mikhalidwe imene ingatinyenge kukhala osakhulupirika kwa Mulungu. Paulo anati: ‘Zinthu izi zinachitika, zikhale zotichenjeza ife, kuti tisalakalake zoipa ife, monganso [Aisrayeli] analakalaka. Kapena musakhale opembedza mafano, monga ena a iwo, monga kwalembedwa, Anthu anakhala pansi kudya ndi kumwa, nanyamuka kuseŵera. Kapena tisachite dama monga ena a iwo anachita dama, nagwa tsiku limodzi zikwi makumi aŵiri ndi zitatu. Kapena tisayese [Yehova, NW], monga ena a iwo anayesa, nawonongeka ndi njoka zija. Kapena musadandaula, monga ena a iwo anadandaula, nawonongeka ndi wowonongayo.’—1 Akorinto 10:6-10.
12 Aisrayeli analakalaka zithu zoipa pamene anagonjera ku chiyeso cha kukhala aumbombo m’kusonkhanitsa ndi kudya zinziri zimene Mulungu anapereka mozizwitsa. (Numeri 11:19, 20, 31-35) Poyamba, iwo anakhala olambira mafano pamene kusakhalapo kwa Mose kunapereka chiyeso cha kudziloŵetsa m’kulambira mwana wa ng’ombe. (Eksodo 32:1-6) Zikwizikwi anafa chifukwa chakuti anagonja ku chiyeso nachita dama ndi akazi Achimoabu. (Numeri 25:1-9) Pamene Aisrayeli anagonja ku chiyeso nadandaula ponena za kuwonongedwa kwa Kora, Datani, ndi Abiramu opandukawo, pamodzi ndi anzawo onse, 14,700 anapululuka ndi mliri wotumizidwa ndi Mulungu. (Numeri 16:41-49) Tingapindule ndi zochitika zimenezo ngati tizindikira kuti palibe nchimodzi chomwe cha ziyeso zimenezi chinali chachikulu kwakuti Aisrayeli sakanakhoza kuchilaka. Iwo akanatero ngati akanasonyeza chikhulupiriro, ngati akanayamikira chisamaliro chachikondi cha Mulungu, ndipo ngati akanamvetsetsa kulungama kwa Chilamulo chake. Pamenepo dzanja la Yehova likanawapulumutsa, mongadi momwe lingakhoze kutipulumutsa.
13, 14. Kodi ndimotani mmene Yehova amaikira populumukirapo pamene atumiki ake ayang’anizana ndi chiyeso?
13 Monga Akristu, timayang’anizana ndi ziyeso zofala kwa anthu. Komabe, tikhoza kukhalabe okhulupirika kwa Mulungu mwakupempherera chithandizo chake ndi kuyesayesa kutsutsa chiyeso. Mulungu ali wokhulupirika, ndipo sadzatileka kuti tiyesedwe koposa kumene tingathe kupirira. Ngati tikhala okhulupirika kwa Yehova, sitidzakupeza kukhala kosatheka kuchita chifuniro chake. Iye amaika populumukirapo mwakutilimbitsa kutsutsa chiyeso. Mwachitsanzo, pamene tizunzidwa, tingayesedwe kuti tilolere molakwa kuti tipeŵe kuzunzidwa kapena imfa. Koma ngati tidalira dzanja lamphamvu la Yehova, chiyeso sichimafika pamlingo wakuti iye nkulephera kulimbitsa chikhulupiriro chathu ndi kutipatsa nyonga yokwanira yakuti tisunge umphumphu wathu. Monga momwe mtumwi Paulo ananenera kuti: ‘Ndife osautsika monsemo, koma osapsinjika; osinkhasinkha, koma osakhala kakasi; olondoleka, koma osataika; ogwetsedwa, koma osawonongeka.’—2 Akorinto 4:8, 9.
14 Yehova amachirikizanso anthu ake mwakugwiritsira ntchito mzimu wake monga wokumbutsa ndi mphunzitsi. Umakumbutsa mfundo za m’Malemba ndi kutithandiza kudziŵa mmene tingazigwiritsire ntchito kuti titsutse chiyeso. (Yohane 14:26) Atumiki okhulupirika a Yehova amamvetsetsa nkhani zoloŵetsedwamo m’chiyeso ndipo samanyengedwa kutsatira njira yolakwa. Mulungu waika populumukirapo mwakuwatheketsa kupirira ngakhale kufikira imfa koma osagonja ku chiyeso. (Chibvumbulutso 2:10) Pambali pakuthandiza atumiki ake kupyolera mwa mzimu woyera, Yehova amagwiritsira ntchito angelo ake kuthandiza gulu lake.—Ahebri 1:14.
Chithandizo m’Nkhani Zaumwini
15. Kodi ndichithandizo chaumwini chotani chimene tingapeze mu Nyimbo ya Solomo?
15 Awo amene amayanjana ndi gulu la Yehova amakhala ndi chithandizo chake m’nkhani zawo zaumwini. Mwachitsanzo, ena angakhale akuyesayesa kupeza Mkristu wokwatirana naye. (1 Akorinto 7:39) Ngati munagwiritsidwa mwala, kungakhale kothandiza kulingalira Solomo, mfumu ya Israyeli. Iye analephera kuvomeredwa muukwati ndi namwali Wachisulami chifukwa chakuti namwaliyo anakonda mbusa wodzichepetsa. Cholembedwa cha mfumucho cha nkhani imeneyi chingatchedwe Nyimbo ya Solomo ya Chikondi Chogwiritsidwa Mwala. Tikhoza kugwetsa misozi ngati zoyesayesa zathu za chikondi chofuna winawake zalephera, koma kugwiritsidwa mwala kwa Solomo kunatha, ndipo kwathu nakonso kungatero. Mzimu wa Mulungu ungatithandize kusonyeza kudziletsa ndi mikhalidwe ina yaumulungu. Mawu ake amatithandiza kuvomereza mfundo imene kaŵirikaŵiri imakhala yowawitsa yakuti munthu sangakhale ndi chikondi chofuna munthu aliyense. (Nyimbo ya Solomo 2:7; 3:5) Komabe, Nyimbo ya Solomo imasonyeza kuti kungakhale kotheka kupeza wokhulupirira mnzathu amene amatikonda kwabasi. Chofunika kwambiri, “nyimbo yoposa” imeneyi imakwaniritsidwa m’chikondi cha Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, kwa “mkwatibwi” wake wa otsatira odzozedwa a 144,000.—Nyimbo ya Solomo 1:1; Chibvumbulutso 14:1-4; 21:2, 9; Yohane 10:14.
16. Kodi ‘chisautso m’thupi’ chokhala ndi Akristu okwatirana chingaphatikizepo chiyani?
16 Ngakhale amene anakwatirana ndi wokhulupirira ali ndi ‘chisautso m’thupi.’ (1 Akorinto 7:28) Padzakhala nkhaŵa zoloŵetsamo mwamuna ndi mkazi ndi ana awo. (1 Akorinto 7:32-35) Kudwala kungabweretse mavuto ndi chipsinjo. Chizunzo kapena vuto la zachuma lingakupangitse kukhala kovuta kwa tate Wachikristu kupezera banja lake zofunika za moyo. Makolo ndi ana angalekanitsidwe mwa kuponyedwa m’ndende, ndipo ena angazunzidwe ndipo ngakhale kuphedwa. Koma m’zochitika zonsezi, tikhoza kutsutsa chiyeso chakukana chikhulupiriro ngati tidaliradi dzanja lopulumutsa la Yehova.—Salmo 145:14.
17. Kodi ndivuto la pabanja lotani limene Mulungu anatheketsa Isake ndi Rebeka kulipirira?
17 Tingafunikire kupirira ziyeso zina kwa nthaŵi yaitali. Mwachitsanzo, mwana angasautse makolo ake opembedza mwakukwatira wosakhulupirira. Chimenecho chinachitika m’banja la kholo Isake ndi mkazi wake Rebeka. Esau, mwana wawo wazaka 40 zakubadwa anakwatira akazi aŵiri Ahiti amene “anapweteka mtima wa Isake ndi wa Rebeka.” Kwenikweni, ‘anati Rebeka kwa Isake, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Heti: akatenga Yakobo [mwana wawo wina] mkazi wa ana aakazi a Heti, onga ana aakazi a m’dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?’ (Genesis 26:34, 35; 27:46) Mwachiwonekere, moyo wolungama wa Rebeka unavutika ndi vuto lopitirizabe limeneli. (Yerekezerani ndi 2 Petro 2:7, 8.) Komabe, dzanja la Yehova linachirikiza Isake ndi Rebeka, kuwatheketsa kupirira chiyeso chimenechi pamene ankasunga unansi wolimba ndi Iye.
18. Kodi ndichiyeso chaumwini chotani chimene C. T. Russell anapirira mwa chithandizo cha Mulungu?
18 Zimasautsa pamene chiŵalo cha banja chobatizidwa chibwerera m’mbuyo muutumiki wa Mulungu. (Yerekezerani ndi 2 Timoteo 2:15.) Komabe, ena apirira pamene mnzawo wamuukwati wataika mwauzimu, monga momwe anachitira Charles T. Russell, prezidenti woyamba wa Watch Tower Society. Mkazi wake analeka kugwirizana ndi Sosaite ndi kumsiya mu 1897, pambuyo pa zaka pafupifupi 18 za muukwati. Iye anapempha khoti chilolezo chakulekana ndi mwamuna wake mu 1903, ndipo chinaperekedwa mu 1908. Chisoni cha mwamuna wake chinali chowonekeratu m’kalata imene anamlembera mwamsanga pambuyo pa kulekana kwawo pamene anati: “Ndakupempherera ndi mtima wonse kwa Ambuye. . . . Sindifuna kukuvutitsa mwakukuuza chisoni changa, kapena kuyesa kudzutsa chifundo chako mwakukufotokozera malingaliro anga mwatsatanetsatane, popeza kuti kwa nthaŵi ndi nthaŵi ndimapeza zovala zako ndi zinthu zina zimene zimandikumbutsa bwino lomwe mmene unaliri kale—wodzala ndi chikondi ndi chifundo ndi mzimu wakuthandiza—kusonyeza mzimu wa Kristu. . . . Kalanga ine, talingalira mwapemphero zimene ndifuka kunena. Ndipo khala wotsimikiziridwa kuti chondibaya kumtima kwenikweni, chondivutitsa zedi, sindicho kusukidwa kaamba kokhala ndekha paulendo watsala wa moyo wanga, koma kugwa kwako, wokondedwa wanga, kutaika kwako kosatha, monga momwe ndikuwonera.” Mosasamala kanthu za kupwetekedwa mtima koteroko, Russell anakhalabe ndi chichirikizo cha Mulungu mpaka kumapeto kwa moyo wake wa padziko lapansi. (Salmo 116:12-15) Yehova nthaŵi zonse amachirikiza atumiki ake okhulupirika.
Kutulutsidwa m’Zipsinjo Zonse
19. Kodi tiyenera kukumbukiranji ngati mavuto osautsa aumirira?
19 Anthu a Yehova amamdziŵa kukhala ‘Mulungu wa chipulumutso,’ Uyo amene “tsiku ndi tsiku atisenzera katundu.” (Salmo 68:19, 20) Chotero, monga anthu odzipereka ogwirizana ndi gulu lake la padziko lapansi, tisakhwethemuke konse pamene mavuto osautsa aumirira. Kumbukirani kuti ‘Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso.’ (Salmo 46:1) Chidaliro chathu mwa iye chimafupidwa nthaŵi zonse. ‘Ndinafuna Yehova ndipo anandivomera,’ anatero Davide, ‘nandilanditsa m’mantha anga onse. . . . Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m’masautso ake onse.’—Salmo 34:4-6.
20. Kodi ndifunso lotani limene liyenera kulingaliridwa?
20 Inde, Atate wathu wakumwamba amapulumutsa anthu ake m’masautso onse. Iye amachirikiza gulu lake la padziko lapansi, namapereka chithandizo m’nkhani za mpingo ndi zaumwini. Ndithudi, ‘Yehova sadzasiya anthu ake.’ (Salmo 94:14) Koma tiyeni tsopano tipende njira zina zimene Yehova amathandizira anthu ake mmodzi ndi mmodzi. Kodi ndimotani mmene Atate wathu wakumwamba amachirikizira atumiki ake odwala, opsinjika maganizo, ovutika ndi chisoni chifukwa cha kuferedwa, kapena osautsika mtima chifukwa cha zolakwa zawo? Monga momwe tidzawonera, m’nkhanizi nazonso, tiri ndi chifukwa cha kudalira dzanja lamphamvu la Yehova.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi ndimotani mmene dzanja la Yehova linaperekera chipulumutso m’nthaŵi zakale?
◻ Kodi ndimotani mmene Yehova amathandizira anthu ake mumpingo lerolino?
◻ Kodi ndithandizo lotani limene Mulungu amapereka m’nkhani zaumwini?
◻ Kodi tiyenera kuchitanji ngati mavuto osautsa aumirira?
[Chithunzi pamasamba 8, 9]
Mulungu anatulutsa Aisrayeli mu Igupto “ndi dzanja lokwezeka”