Valani Chifatso!
“Monga osankhidwa a Mulungu, oyera ndi okondedwa, dzivekeni chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa maganizo, chifatso, ndi kuleza mtima.”—AKOLOSE 3:12, NW.
1-3. Pa Akolose 3:12-14, kodi mtumwi Paulo ananenji za chifatso ndi mikhalidwe ina yaumulungu?
YEHOVA amapatsa anthu ake chovala chophiphiritsira chabwino koposa. Kunena zowona, onse amene amakhumba chiyanjo chake ayenera kuvala malaya okhala ndi nkhosi zolimba za kufatsa. Mkhalidwe umenewu uli wotonthoza chifukwa chakuti umachepetsa kupanikizika pamene zinthu zathina. Uwo ulinso woteteza popeza umaletsa mkangano.
2 Mtumwi Paulo anafulumiza Akristu anzake odzozedwa kuti: “Monga osankhidwa a Mulungu, oyera ndi okondedwa, dzivekeni chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa maganizo, chifatso, ndi kuleza mtima.” (Akolose 3:12, NW) Kaimidwe ka liwu la Chigiriki lomasuliridwa “dzivekeni” kamasonyeza ntchito yoyenera kuchitidwa m’lingaliro la kufulumira. Odzozedwa, amene anasankhidwa, oyera, ndi okondedwa ndi Mulungu, sanayenera kuzengereza kudziveka mikhalidwe yotero yonga chifatso.
3 Paulo anawonjezera kuti: “Pitirizanibe kupirirana ndi kukhululukirana mwaufulu ngati aliyense ali ndi chifukwa chodandaulira ndi wina. Monga momwenso Yehova mwaufulu anakukhululukirani teroni inunso. Koma, kuphatikiza pa zinthu zonsezi dzivekeni chikondi, pakuti icho ndicho chomangira changwiro chachigwirizano.” (Akolose 3:13, 14, NW) Chikondi, chifatso, ndi mikhalidwe ina yaumulungu imatheketsa Mboni za Yehova “kukhala pamodzi mu umodzi.”—Salmo 133:1-3, NW.
Abusa Ofatsa Akufunika
4. Kodi Akristu owona amavala chovala chophiphiritsira cholukidwa ndi mikhalidwe yotani?
4 Akristu owona amayesayesa ‘kufetsa ziwalo ziri padziko: dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa ndi chisiriro,’ ndipo amayesayeasa kuvula chovala chirichonse chokhala ndi nsalu yamkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, ndi zonyansa zotuluka mkwamwa. (Akolose 3:5-11) Iwo amavula “umunthu wakale” (m’lingalilo lenileni “munthu wakale”) ndipo amavala “umunthu watsopano” (kapena, “munthu watsopano”) chovala choyenerera. (Aefeso 4:22-24, NW; Kingdom Interlinear) Chovala chawo chatsopano, cholukidwa ndi chifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa maganizo, chifatso ndi kuleza mtima, chimawathandizira kuthetsa mavuto ndi kukhala ndi miyoyo yopembedza.—Mateyu 5:9; 18:33; Luka 6:36; Afilipi 4:2, 3.
5. Kodi nchiyani chimene chiripo ponena za kayendetsedwe ka mpingo Wachikristu chimene chimakupangitsa kukhala kosangalatsa kukhala mbali ya uwo?
5 Amuna olingaliridwa kukhala achipambano m’dziko lino ali kaŵirikaŵiri opanda chifundo, ngakhale ankhanza. (Miyambo 29:22) Ha, nzosiyana motsitsimula chotani nanga mmene ziriri pakati pa anthu a Yehova! Mpingo Wachikristu sumayendetsedwa monga mmene anthu ena amayendetsera bizinesi—mumkhalidwe wachipambano koma waukali umene ungapangitse anthu kukhala opanda chimwemwe. Mmalomwake, kuli kwa chimwemwe kukhala mbali yampingo. Chifukwa chimodzi nchakuti, kufatsa kuli mbali yanzeru yosonyezedwa ndi Akristu onse ndipo makamaka ndi amuna oyeneretsedwa kuphunzitsa okhulupirira anzawo. Inde, chimwemwe chimachokera m’malangizo ndi uphungu zoperekedwa ndi akulu oikidwa amene amaphunzitsa “munzeru yofatsa.”—Yakobo 3:13.
6. Kodi nchifukwa ninji akulu Achikristu ayenera kukhala ofatsa?
6 Mzimu, kapena mkhalidwe waukulu, wa anthu a Mulungu umafuna kuti amuna opatsidwa uyang’aniro mumpingo akhale ofatsa, olingalira, ndi omvetsetsa. (1 Timoteo 3:1-3) Atumiki a Yehova ali ofanana ndi nkhosa zofatsa, osati mbuzi zaliuma, abulu ouma khosi, kapena mimbulu yolusa. (Salmo 32:9; Luka 10:3) Pokhala onga nkhosa, iwo amafunikira kuchitiridwa mofatsa ndi mwachifundo. (Machitidwe 20:28, 29) Inde, Mulungu amayembekezera akulu kukhala ofatsa, okoma mtima, achikondi, ndi oleza mtima kulinga kwa nkhosa zake.—Ezekieli 34:17-24.
7. Kodi ndimotani mmene akulu ayenera kulangizira ena kapena kuthandiza odwala mwauzimu?
7 Monga “kapolo wa Ambuye,” mkulu ayenera “akhale . . . waulele pa onse, wodziŵa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu wawapatsa iwo chitembenuziro, kukazindikira chowonadi.” (2 Timoteo 2: 24, 24) Abusa Achikristu ayenera kusonyeza kulingalira kwachifundo pamene akuyesa kuthandiza odwala mwauzimu, popeza kuti nkhosazo nza Mulungu. Akulu sayenera kuchita nawo monga momwe wolembedwa ntchito akachitira koma afunikira kukhala ofatsa, mofanana ndi Mbusa Wabwino, Yesu Kristu.—Yohane 10:11-13.
8. Kodi nchiyani chinachitika kwa Mose wofatsayo, ndipo chifukwa ninji?
8 Mkulu panthaŵi zina angakupeze kukhala kovuta kusunga mkhalidwe wofatsa. “Mose [anali, NW] wofatsa woposa anthu onse a padziko lapansi.” (Numeri 12:3) Komabe, pamene Aisrayeli anayang’anizana ndi kusoŵa madzi pa Kadesi, anakangana ndi Mose namuimba mlandu wakuwatsogolera kutuluka m’Igupto kupita kuchipululu chouma. Mosasamala kanthu za zonse zimene anapirira mofatsa, iye analankhula mwasontho, mwaukali. Iye ndi Aroni anaimirira pamaso pa anthu nachititsa anthuwo kuyang’ana kwa iwo eni, Mose akumati: “Tamvanitu, opikisana naye inu; kodi tikutulutsireni madzi m’thanthwe umu?” Pamenepo Mose anakantha tanthwe ndi ndodo yake kaŵiri ndipo Mulungu anachititsa “madzi . . . ochuluka” kutuluka kaamba ka anthu ndi zoŵeta zawo. Yehova sanakondwere chifukwa chakuti Mose ndi Aroni sanampatulikitse, chotero Mose sanapatsidwe mwaŵi wakutsogolera Aisrayeli kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.—Numeri 20:1-13; Deuteronomo 32:50-52; Salmo 106:32, 33.
9. Kodi kufatsa kwa mkulu kungayesedwe motani?
9 Kufatsa kwa mkulu Wachikristu kungayesedwenso m’njira zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, Paulo anachenjeza Timoteo kuti pakabuka winawake ‘wotukumuka’ ndi ‘woyalukira pamafunso ndi makani a mawu.’ Paulo anawonjezera kuti: ‘Kumene zichokerako njiru, ndewu, zamwano, mayerekezo oipa; makani opanda pake a anthu oipitsika nzeru ndi ochotseka chowonadi.’ Woyang’anira Timoteo sanayenera kuchita mwaukali koma anayenera ‘kuthaŵa izi,’ ndipo anayenera ‘kutsata chilungamo, chipembedzo, chikhulupiriro, chikondi, chipiriro, chifatso.’—1 Timoteo 6:4, 5, 11.
10. Kodi Tito anayenera kukumbutsa mipingo za chiyani?
10 Ngakhale kuli kwakuti akulu afunikira kukhala ofatsa, iwo ayenera kukhala olimba ponena za chimene chiri cholungama. Tito anali wotero, akumakumbutsa ogwirizana ndi mipingo ku Krete kuti “asachitire mwano munthu aliyense, asakhale a ndewu, akhale aulere, nawonetsere chifatso chonse pa anthu onse.” (Tito 3:1, 2) Akumasonyeza chifukwa chake Akristu ayenera kukhala ofatsa kulinga kwa onse, Tito anasonyeza mmene Yehova wakhalira wokoma mtima ndi wachikondi. Mulungu sanapulumutse okhulupirira chifukwa cha zochita ziri zonse zolungama zimene iwo adachita koma mogwirizana ndi chifundo chake kudzera mwa Yesu Kristu. Kufatsa kwa Yehova ndi kuleza mtima kumatanthauza chipulumutso kwaifenso. Chotero, mofanana ndi Tito, akulu amakono ayenera kukumbutsa mipingo kukhala yogonjera kwa Mulungu, akumatsanzira iye mwakuchitira ena mofatsa.—Tito 3:3-7; 2 Petro 3:9, 15.
Kufatsa Kumatsogolera Phungu Wanzeru
11. Malinga ndi Agalatiya 6:1, 2, kodi uphungu uyenera kuperekedwa motani?
11 Bwanji ngati nkhosa yophiphiritsira yalakwa? Paulo anati: “Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze woteroyo ndi mzimu wachifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso. Nyamuliranani zothodwetsa ndipo kotero mufitse chilamulo cha Kristu.” (Agalatiya 6:1, 2) Uphungu umakhala wogwira mtima koposa ngati uperekedwa mumzimu wa kufatsa. Ngakhale ngati akulu akuyesa kupereka uphungu kwa munthu wokwiya, iwo ayenera kusonyeza kudziletsa, akumazindikira kuti “lilime lofatsa lithyola fupa.” (Miyambo 25:15) Munthu wina amene umunthu wake uli wolimba ngati fupa angafewetsedwe ndi ndemanga yoperekedwa mofatsa, ndipo kulimba kwake kungafewe.
12. Kodi ndimotani mmene mzimu wofatsa umathandizira phungu?
12 Yehova ndi Mlangizi wofatsa, ndipo njira yake yofatsa yophunzitsira iri yogwira mtima mumpingo. Zimenezi ziri choncho makamaka pamene akulu akupeza kukhala koyenera kupereka uphungu kwa awo ofunikira chithandizo chauzimu. Wophunzira Yakobo analemba kuti: “Ndani ali wanzeru, waluso mwa inu? Awonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake munzeru yofatsa.” Chifatso chimachokera mu ulemu ndi chiyamikiro kaamba ka “nzeru yochokera kumwamba,” yogwirizana ndi kuzindikira modekha malire a munthuwe. Mzimu wofatsa ndi wodzichepetsa umatetezera phungu kuti asanene mawu ovulaza ndi olakwa ndipo umapangitsa uphungu wake kulandiridwa mosavuta.—Yakobo 3:13, 17.
13. Kodi “nzeru yofatsa” imayambukira motani mmene uphungu umaperekedwera?
13 “Nzeru yofatsa” imatetezera phungu ku kukhala woumirira mopambanitsa mosalingalira kapena mwaukali. Komabe, nkhaŵa kaamba ka ubwenzi kapena kukhala ndi chivomerezo cha wina siziyenera kusonkhezera mkulu kunena zinthu zolinganizidwa kukondweretsa mmalo mwa kupereka mofatsa uphungu wolondola wozikidwa pa Mawu a Mulungu. (Miyambo 24:24-26; 28:23) Uphungu umene Amnoni analandira kwa msuwani wake unakhutiritsa chikhumbo chake, koma unamtaitsa moyo wake. (2 Samueli 13:1-19, 28, 29) Chotero, akulu amakono, sayenera kululuza malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo kutonthoza chikumbumtima cha munthu wina, popeza kuti kuteroko kukaika pachiswe moyo wake. Mofanana ndi Paulo, akulu sayenera kuleka kuuza ena “uphungu wonse wa Mulungu.” (Machitidwe 20:26, 27; 2 Timoteo 4:1-4) Phungu wachikulire Wachikristu amasonyeza mantha aumulungu ndi kupereka uphungu wolungama ndi kufatsa kwa nzeru.
14. Kodi nchifukwa ninji mkulu ayenera kukhala wosamala kusapanga zosankha zimene ena angadzipangire?
14 Kufatsa kogwirizana ndi nzeru yochokera kumwamba kudzaletsa mkulu kufunsira zopambanitsa. Iye ayeneranso kuzindikira kuti sikwanzeru ndipo nkosayenerera kwa iye kupanga chosankha chimene munthu wina ayenera kudzipangira. Mkulu akakhala ndi thayo kaamba ka zotulukapo ngati iye anapanga zosankha kaamba ka ena, ndipo akagawana liwongo kaamba ka chotulukapo chirichonse choipa. Mkuluyo angasonyeze zimene Baibulo limanena, koma ngati palibe lamulo la Malemba pa nkhaniyo, chosankha cha munthu mwiniyo ndi chikumbumtima ziyenera kutsimikizira zimene iye adzachita kapena kusachita. Monga momwe Paulo ananenera: “Yense adzasenza katundu wake wa iyemwini.” (Agalatiya 6:5; Aroma 14:12) Komabe, wofunsayo angathandizidwe kupanga chosankha choyenera mwakufunsidwa mafunso ndi mkulu amene angathandizire munthuyo kulingalira malemba ogwirizana ndi njira zothekera zimene zingakhale zotseguka kwa iye.
15. Kodi nchiyani chimene chiyenera kuchitidwa ngati mkulu sadziŵa yankho lafunsolo?
15 Ngati mkulu sadziŵa yankho lafunsolo, iye sayenera kuyankha kokha kuti angodzichotsa manyazi. Kufatsa kwa nzeru kukamtetezera ku kungoyerekezera ndipo mwinamwake kupereka yankho lolakwika limene pambuyo pake likachititsa mavuto. Pali “mphindi yakutonthola ndi mphindi yakulankhula.” (Mlaliki 3:7; yerekezerani ndi Miyambo 21:23.) Mkulu ayenera “kulankhula” kokha pamene adziŵa yankho la funsolo kapena wapanga kufufuza kokwanira kupereka yankho loyenera. Kuli kwanzeru kusiya mafunso okaikiritsa osayankhidwa.—Miyambo 12:8; 17:27; 1 Timoteo 1:3-7; 2 Timoteo 2:14.
Phindu la Kuchuluka kwa Aphungu
16, 17. Kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kwa akulu kukambitsirana?
16 Pemphero ndi phunziro zidzathandiza akulu kuyankha mafunso ndi kusamalira nkhani zovuta, koma kuyenera kukumbukiridwa kuti “pochuluka aphungu [zinthu] zikhazikika.” (Miyambo 15:22) Kukambitsirana ndi akulu ena kumachititsa kusonkhanitsidwa pamodzi kopindulitsa kwa nzeru. (Miyambo 13:20) Saali akulu onse omwe ali ndi chidziŵitso chofanana kapena chidziŵitso cha Baibulo. Chifukwa chake, kufatsa kwa nzeru kuyenera kusonkhezera mkulu wachidziŵitso chochepa kukambitsirana ndi akulu okhala ndi chidziŵitso chokulira ndi odziŵa zinthu zochuluka, makamaka pamene nkhani yaikulu ifunikira kusamaliridwa.
17 Pamene akulu asankhidwa kukasamalira nkhani yaikulu, iwo mwachinsinsi angafunefunedi chithandizo. Kuti athandizidwe m’kuweruza Aisrayeli, Mose anasankha “amuna a mtima akuwopa Mulungu, amuna owona, akudana nalo phindu lachinyengo.” Ngakhale kuli kwakuti iwo anali akulu, sanali ndi chidziŵitso ndi kuzoloŵera konga komwe Mose anali nako. Chifukwa chake, “mlandu wakuwalaka amabwera nawo kwa Mose, ndi milandu yaing’ono yonse amaweruza okha.” (Eksodo 18:13-27) Pamenepa, ngati kuli kofunika akulu osamalira mlandu wovuta lerolino moyenerera angafunefune chithandizo kwa oyang’anira ozoloŵera, ngakhale kuli kwakuti amapanga chosankha chomalizira iwo eni.
18. Posamalira nkhani za chiŵeruzo, kodi ndi mbali zofunika ziti zimene zimatsimikiziritsa zosankha zoyenera?
18 Mishnah Yachiyuda imanena kuti m’Israyeli awo opanga makhothi a kumidzi anasiyanasiyana m’chiŵerengero malinga ndi ukulu wa mlanduwo. Pali phindu lenileni m’kuchuluka kwa aphungu, ngakhale kuli kwakuti ziŵerengero zokha sizimatsimikiziritsa chiŵeruzo cholungama, popeza kuti unyinji wa anthu ungalakwe. (Eksodo 23:2) Mbali zazikulu zatsimikiziritsa kuti zosankha zoyenera zidzapangidwa ndi Malemba ndi mzimu wa Mulungu. Nzeru ndi chifatso zidzasonkhezera Akristu kugonjera ku zimenezi.
Kuchitira Umboni Mofatsa
19. Kodi ndimotani mmene kufatsa kumathandizira anthu a Yehova kuchitira umboni kwa ena?
19 Kufatsa kumathandizanso atumiki a Yehova kuchitira umboni kwa anthu a kaimidwe kamaganizo kosiyanasiyana. (1 Akorinto 9:22, 23) Chifukwa chakuti Yesu anaphunzitsa mofatsa, anthu odzichepetsa sanamuwope, monga momwe anachitira ndi atsogoleri achipembedzo. (Mateyu 9:36) Ndithudi, njira zake zofatsa zinakopa “nkhosa” osati “mbuzi” zoipa. (Mateyu 25:31-46; Yohane 3:16-21) Ngakhale kuli kwakuti Yesu anagwiritsira ntchito mawu amphamvu pochita ndi onyenga onga mbuzi, Mboni za Yehova ziyenera kukhala zofatsa pamene zikulengeza mauthenga a chiŵeruzo a Mulungu lerolino chifukwa chakuti ziribe chidziŵitso ndi ulamuliro zofanana ndi zomwe Yesu anali nazo. (Mateyu 23:13-36) Pamene iwo akumva uthenga wa Ufumu ukulalikidwa mofatsa, ‘awo okonzekera bwino lomwe kaamba ka moyo wosatha amakhulupirira,’ monga momwe onga nkhosa amene anamva Yesu anachitira.—Machitidwe 13:48, NW.
20. Kodi wophunzira Baibulo amapindula motani pamene aphunzitsidwa mofatsa?
20 Zotulukapo zabwino zimapezedwa mwa kuchitira umboni ndi kuphunzitsa ena mofatsa ndi mwakuwakopa pa maziko a kulingalira, malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo, ndi chowonadi. “Mumpatulikitse Ambuye Kristu mu mitima yanu,” analemba motero Petro, “okonzeka nthaŵi zonse kuchita chodzikanira pa yense wokufunsani chifukwa cha chiyembekezo chiri mwa inu, komatu ndi chifatso.” (1 Petro 3:15) Wophunzira amene akuphunzitsidwa mwachifatso angaike maganizo pankhiniyo mmalo mwa kupatutsidwa kapena mwinamwake ngakhale kukhumudwitsidwa ndi mkhalidwe waukali ndi wamakani. Mofanana ndi Paulo, aminisitala olangiza mofatsa anganene kuti: “Osapatsa chokhumudwitsa chonse m’chinthu chirichonse kuti utumikiwo usanenezedwe.” (2 Akorinto 6:3) Ngakhale otsutsa nthaŵi zina amalabadira mwachiyanjo kwa awo olangiza mofatsa.
Kufatsa Kumafunidwa kwa Onse
21, 22. Kodi kufatsa kumapindulitsa motani anthu onse a Yehova?
21 Kufatsa kwa Chikristu sikuyenera kuvalidwa kokha kuti tikondweretse anthu kunja kwa gulu la Yehova. Mkhalidwe umenewu ulinso wofunika m’maunansi pakati pa anthu a Mulungu. (Akolose 3:12-14; 1 Petro 4:8) Mipingo imalimbikitsidwa mwauzimu pamene akulu ofatsa ndi atumiki otumikira amagwirira ntchito limodzi mogwirizana. Kusonyeza chifatso ndi mikhalidwe ina yaumulungu kuli kofunika kwa aliyense wa anthu a Yehova chifukwa chakuti pali “lamulo limodzi” kaamba ka onse.—Eksodo 12:49, NW; Levitiko 24:22.
22 Chifatso chimachititsa mtendere ndi chimwemwe cha anthu a Mulungu. Chotero, kuyenera kukhala mbali ya nsalu ya mikhalidwe yopanga chovala chovalidwa ndi Akristu onse panyumba, mumpingo, ndi kwina kulikonse. Inde, atumiki onse a Yehova afunikira kuvala chifatso.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji akulu Achikristu ayenera kukhala ofatsa?
◻ Kodi kufatsa kumatsogolera motani phungu wanzeru?
◻ Kodi phindu la kuchuluka kwa aphungu nlotani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kuchitira umboni mofatsa?
[Chithunzi patsamba 17]
Anthu a Yehova ali onga nkhosa ndipo amafunikira kuchitiridwa mofatsa
[Mawu a Chithunzi]
Garo Nalbandian
[Chithunzi patsamba 19]
Kufatsa kumatheketsa anthu a Yehova kuchitira umboni kwa anthu okhala ndi kaimidwe kamaganizo kosiyanasiyana