Zimene Ufumu wa Mulungu Umatanthauza kwa Ambiri
KAŴIRIKAŴIRI Yesu Kristu analankhula za Ufumu wa Mulungu. Ponena za chimenechi, wolemba mbiri H. G. Wells analemba kuti: “Chapadera ndicho chigogomezero chachikulu chimene Yesu anaika pa chiphunzitso cha umene anautcha Ufumu wa Kumwamba, poyerekezera ndi tanthauzo lake lochepa ndi njira yochitira zinthu ndi chiphunzitso cha matchalitchi ambiri Achikristu. Chiphunzitso chimenechi cha Ufumu wa Kumwamba, chomwe chinali chiphunzitso chachikulu cha Yesu, chomwenso chiri ndi mbali yaing’ono m’zikhulupiriro Zachikristu, chiridi chimodzi cha ziphunzitso zosiyana kwambiri zomwe zinadzutsa ndi kusintha malingaliro a anthu.”
Kodi nchifukwa ninji matchalitchi samanena zambiri ponena za Ufumu wa Mulungu? Chifukwa chimodzi chingakhale chakuti sali otsimikizira ponena za Ufumuwo. Kodi pakhala malingaliro otani onena za uwo?
Mmene Ufumuwo Walingaliridwira
Ena agwirizanitsa Ufumu wa Mulungu ndi Tchalitchi cha Katolika. Abishopu atavomereza Wolamulira Constantine kukhala mkulu wawo pa Msonkhano wa ku Nicaea m’chaka cha 325 C.E., tchalitchi chinaloŵa m’ndale, ndipo anthu anauzidwa kuti Ufumuwo unadza kale. Encyclopædia Britannica ikulongosola kuti malinga ndi maphunziro azaumulungu a Augustine (354-430 C.E.), “Ufumu wa Mulungu unayamba kale m’dziko lino pamene tchalitchi chinakhazikitsidwa” ndipo “ukupezeka kale m’madzoma atchalitchi.”
Ena amalingalira Ufumu wa Mulungu kukhala chipambano cha anthu. Bukhu lanazonse limodzimodzilo likunena kuti: “Posakhalitsa Matchalitchi a Chiprotesitanti . . . anakhala ziungwe za matchalitchi a magawo, omwe anayamba kutsendereza chiyembekezo cha nthaŵi yamapeto” ponena za kudza kwa Ufumu wa Mulungu. H. G. Wells analemba kuti: “Anthu anachotsa maziko a miyoyo yawo pa ufumu wa Mulungu ndi ubale wa anthu nawaika pamaboma enieni owoneka olamulira, Falansa ndi Mangalande, Russia Wopatulika, Spanya, Prussia . . . Anali maulamuliro enieni olamulira Yuropu.”
Ndiponso m’nthaŵi zamakono, Ufumuwo walingaliridwa kukhala wakudziko. Encyclopædia Britannica ikulongosola kuti: “Wodziŵika uli mkhalidwe waukulu wakuti munthu iyemwini ayenera kukonzekera chitaganya chamtsogolo changwiro m’njira yomangirira ndi yolinganizika ndikuti ‘kuyembekezera’ ndi ‘kudikirira’ kumaloŵedwa m’malo ndi kuchitapo kanthu kwa anthu.” Ponena za “gulu logwirizanitsa makhalidwe ndi malamulo Achikristu,” bukhu lamaumboni limodzimodzilo likupitiriza kuti: “Gulu limeneli linawona uthenga Wachikristu wa Ufumu wa Mulungu kwakukulukulu monga chisonkhezero chokhazikitsanso mikhalidwe yakudziko yachitaganya m’lingaliro la malamulo a Ufumu wa Mulungu.”
Ayuda ambiri amalingaliranso Ufumuwo kukhala chipambano cha anthu. Mu 1937 msonkhano wa arabi a Chiyuda Chowongoleredwa mu Columbus, Ohio, U.S.A., ananena kuti: “Timailingalira kukhala ntchito yathu yapadera kugwirizana ndi anthu onse m’kukhazikitsa ufumu wa Mulungu, ubale wapadziko lonse, chilungamo, chowonadi ndi mtendere padziko lapansi. Ichi ndicho chonulirapo chathu chaumesiya.”
Lingaliro lina lofala ndilakuti Ufumu wa Mulungu uli mkhalidwe wa mtima wa munthu. Mwachitsanzo, ku United States, Msonkhano wa Southern Baptist unalengeza mu 1925 kuti: “Ufumu wa Mulungu uli kulamulira kwa Mulungu mumtima ndi moyo wa munthu muunansi uliwonse wa anthu, ndi mtundu uliwonse ndi chiungwe cholinganizika cha chitaganya. . . . Ufumu wa Mulungu udzakwanira pamene ganizo lirilonse ndi chifuno cha munthu chidzagonjetsedwa ku kumvera kwa Kristu.”
Pamenepo, kodi tchalitchi ndicho Ufumu wa Mulungu? Kodi Ufumuwo udzabweretsedwa mwanjira yakudziko? Kodi ndiwo mkhalidwe wa mtima? Ndipo kodi Ufumu wa Mulungu ungatanthauzenji kwa inu?