“Madzi a Moyo” Atumphuka ku Cape Verde
“KUKHALAPO ndi kulondola kulambira kwa Mboni za Yehova mu Cape Verde chiyambire chaka cha 1958 kuli chinthu chosangalatsa,” inafotokoza motero nduna yachiweruzo ya Lipabuliki la Cape Verde. Iyo inali kulankhula kwa Mboni ziŵiri zomwe inaziitanira ku ofesi kwake. “Tiri ndi chisoni kuti zinatenga nthaŵi yaitali kuti Mboni za Yehova zizindikiridwe mwalamulo,” anawonjezera motero.
Msonkhano umenewo, womwe unachitidwa pa November 30, 1990, udzakumbukiridwa kwa nthaŵi yaitali ndi Mboni za Yehova mu Cape Verde. Unali chizindikiro cha kuzindikiridwa kwawo mwalamulo monga gulu lachipembedzo lovomerezedwa m’dzikolo. Komabe, kwa Mboni ziŵiri zomwe zinalipozo, chinali chokumana nacho chawo chosangalatsa, popeza kuti munali mu 1958 pamene mmodzi wa iwo—Luis Andrade—anapeza mabuku ena ofotokoza Baibulo ofalitsidwa ndi Watch Tower Society. Pambuyo poŵerenga mabukuwo kuchokera ku chikuto mpaka ku chikuto, anadziŵa kuti wapeza chowonadi. Motenthedwa maganizo, anagaŵana zimene anaphunzira ndi Francisco Tavares, bwenzi lakalekale. Mkati mwa zaka zoŵerengeka zomwe zinatsatirapo, onse aŵiri anapitiriza kumwa madzi a chowonadi mwakuŵerenga magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, olandiridwa pa sabusikripishoni. Zaka khumi pambuyo pake, mu 1968, anabatizidwa paulendo woyamba wa woyang’anira woyendayenda wa ku Cape Verde.
Mbale Andrade ndi Tavares anazindikira thayo lawo lakukhala ndi phande kulengeza chiitano chakuti: ‘Idzani . . . mutenge madzi a moyo kwaulere.’ (Chivumbulutso 22:17) Anali ofunitsitsa kulandira chitokoso cha gawo lawo lomwazikana ndi lovuta. Cape Verde ali ndi zisumbu zazikulu khumi kuphatikizapo zisumbu zina zazing’ono mu Atlantic Ocean, pafupifupi makilomita 560 kumadzulo kwa Dakar, Senegal. Dzinalo Cape Verde, lotanthauza “Chisumbu Chobiriŵira,” poyambirira linasonya kugombe la ku Afirika. Komabe, zisumbu zimenezi siziri konse zobiriŵira, popeza kuti mvula imagwa yochepa, ndipo nzika 350,000 zimapeza movutikira ndalama zokwanira kuchilikiza moyo m’dziko loumali.
M’zaka 30 zapitazo, amishonale ndi apainiya apadera agwira ntchito zolimba monga aminisitala anthaŵi zonse kubweretsa madzi a moyo kwa anthu apachisumbuwo. Kodi zotulukapo za ntchito yoteroyo nzotani? Posachedwapa, woyang’anira woyendayenda wochokera ku Portugal anachezera mipingo mu Cape Verde. Tidzamulola atiuze zimene anapeza.
São Vicente Amva “Chinenero Choyera”
Malo athu oimapo oyambirira mu Cape Verde anali mzinda wa Porto Grande pa chisumbu cha São Vicente. Tikumayenda pagalimoto kuchokera kubwalo landege kumka kutawuniko, tinawona zitunda zamiyala zokutidwa ndi mchenga woulutsidwa ndi mphepo. Chipululu cha ku North Africa chafika kale ku zisumbu za Cape Verde! Kuyambira December mpaka February, mphepo yotentha, youma yotchedwa harmattan—yochokera ku Sahara—imadutsa nyanja ndikukuta zisumbuzo ndi mchenga ndi fumbi. Nthaŵi zina fumbi limakhala lochindikala kwakuti ndege sizingauluke. Zomera zochepa zotsalira zimauma pamene mphepo ya harmattan ifika.
Komabe, m’lingaliro lauzimu, magwero a madzi akupezeka mosavuta. Mboni za Yehova zakhazikitsa mipingo iŵiri mu Porto Grande, ndipo ofalitsa Ufumu 167 ali otanganidwa kupereka madzi opatsa moyo a chowonadi kwa nzika 47,000 za chisumbu cha São Vicente. Kothera kwa mlungu, anthu okwanira 400 amafika kumisonkhano yokambitsirana Baibulo pa Nyumba Yaufumu.
Mkati mwa maulendo a mlungu wathunthuwo, kukonzekera komalizira kwa Msonkhano Wachigawo wa “Chinenero Choyera” wokachitidwira m’holo yamaseŵera yabwino koposa m’mzindamo kunali kuchitidwa. (Zefaniya 3:9, NW) Pamodzi ndi anthu akumaloko, nthumwi zochokera kuchisumbu cha Santo Antão ndi São Nicolau zinachititsa chiŵerengero chapamwamba cha opezekapo 756. Anthu 24 anabatizidwa. Programuyo inaphatikizapo drama ya Baibulo yoseŵeredwa ndi Mbonizo. Munthu wina yemwe anali mtsogoleri wakuyeseza wa kanema anapezekapo pa dramayo ndipo anati: “Tinaphunzira kwa chaka chonse ndipo chikhalirechobe tinali ndi mavuto ambiri. Otengamo mbali m’drama yanu anachita bwino koposa mwakungophunzira kwa miyezi iŵiri yokha.” Pamene msonkhanowo unamalizidwa mwachipambano, inafika nthaŵi yakuti tipite ku mzinda wa Praia, likulu la Lipabuliki la Cape Verde, pachisumbu cha São Tiago.
Anthu Oyeretsedwa
M’zaka zaposachedwa nzika zambiri za zisumbu zina zasamukira ku likulu kukafuna ntchito. Monga chotulukapo, misasa zikwi zambiri yamangidwa kunja kwa mzindawo, kuchepetsa mokulira madzi ndi zimbudzi zopereŵerazo. Pofuna kuwonjezera ndalama zawo, mabanja ambiri amaŵeta mbuzi, nkhumba, ndi nkhuku. Kuli kofala kuwona ziŵetozi zikuyendayenda mwaufulu m’makwalala. Izi zawonjezera kufalikira kwa matenda.
Komabe, mosasamala kanthu za mikhalidwe yovuta yoteroyo, mu Praia tsopano muli mipingo yaikulu iŵiri yokhala ndi chiwonkhetso cha pafupifupi ofalitsa Ufumu okwanira 130. Mboni zachimwemwe zimenezi ‘zapinduladi’ mwakugwiritsira ntchito zimene zinaphunzira m’Baibulo. Pokalimira kukhala anthu oyera ndi opatulika, abale athu ndi ana awo asangalala ndi thanzi labwinopo, ponse paŵiri mwauzimu ndi mwakuthupi. Ngakhale kuti moyo wawo ngovutikira, iwo ali olemera mwauzimu.—Yesaya 48:17; 1 Petro 1:15, 16.
Pamene tinafika, abale anali otanganidwa kukonzekera msonkhano wawo wachigawo. Mboni ndi anthu okondwerera ochokera ku São Tiago limodzi ndi zisumbu za Sal ndi Fogo anafika ku msonkhanoko, ndipo Yehova anawadalitsa ndi chiŵerengero chapamwamba cha opezekapo 472. Aliyense anali wachimwemwe, kuphatikizapo achichepere ambiri okhala ndi nkhope zachimwemwe! Pamene tinakhala pakati pa khamu lomvetsera limenelo, kunali kowonekeratu kuti sitiyenera konse kupeputsa “tsiku la tinthu tating’ono.” (Zekariya 4:10) Zonsezi zachitika chifukwa cha anthu aŵiri omwe anaphunzira chowonadi zoposa zaka 30 zokha zapitazo!
Tisanachoke pachisumbupo, tinapita kukachezera timagulu tiŵiri tating’ono, Vila Assomada ndi Tarrafal, kunja kwa mzindawo. Chisumbucho chinali chazitunda, chosabala, ndi chouma. Koma apa ndi apo, tinawona malo obiriŵira okhala ndi zomera ndi mitengo—minda ya ngole, nthochi, mapapaya, mango, ndi zina zotero. Izi zinatikumbutsa ulosi wa Yesaya wakuti tsiku lina ngakhale zipululu zidzaphuka. (Yesaya 35:1) Mofanana ndi malo a madzi, ngakhale tsopano timagulu tiŵiri tating’ono ta Mbonizo tikupereka chakudya ndi chakumwa chauzimu chochuluka kwa zikwi zokhala kumeneko, m’dziko lopserera mwauzimu, kunena kwake titero.
Changu Chotentha Ngati Moto pa Chisumbu cha Fogo
Chisumbu chotsatira chinali Fogo, kutanthauza “moto.” Chiyambi chake chokhala ndi volokano chimasonyeza tanthauzo la dzinalo. Cano Peak adakali volokano wotukutira. Amatundumuka kuchokera m’nyanja mumpangidwe wozungulira kufika pa nsonga ya mamita 2,800. Chisumbucho chinali chitangolandira mvula yokwanira, yoyamba yochuluka motero m’zaka zambiri. Anthu anali osangalala kwambiri, ndipo anali otanganitsidwa kwambiri ndi mbewu zawo za nyemba ndi chinangwa, chakudya chachikulu cha ku Cape Verde.
Komabe, anthu oyamikirawa sanali otanganidwa kopambanitsa kwakuti nkulephera kumwa madzi a chowonadi ochokera m’Baibulo. Tinakhoza kukumana ndi magulu atatu osiyana, ngakhale kuti kunali kovuta kuwafikira chifukwa chakuti magalimoto anali ochepa ndiponso amkhalidwe woipa. Tinasangalala kwambiri pamene chiwonkhetso cha anthu 162 chinafika pamisonkhano, popeza kuti panali ofalitsa Ufumu 42 okha pachisumbupo. Ichi chinali chisonyezero cha changu cha kagulu kakang’ono ka abale ndi alongo kameneka, amene amathera avareji ya maola 15 mwezi uliwonse kubweretsa madzi ophiphiritsira a chowonadi ndi moyo kwa nzika 32,000 za chisumbu cha Fogo.
Zipatso m’Dziko Lachikatolika
Tinafunikiranso kuchezera abale athu pa zisumbu za Santo Antão ndi São Nicolau. Monga momwe mainawa akusonyezera, Tchalitchi cha Roma Katolika chaika chisonkhezero chake pazisumbuzi kwa zaka mazana ambiri. Ngakhale kuti Chikatolika chidakali chipembedzo chachikulu pa Cape Verde, anthu ambiri owona mtima akutembenukira ku Baibulo kaamba ka madzi ake otsitsimula a chowonadi.
Ofalitsa Ufumu okwanira 49 m’mipingo iŵiri yaing’ono m’mbali zosiyana za Santo Antão amagwira ntchito zolimba kukhutiritsa zosoŵa zauzimu za nzika 44,000. Pamene anthu 512 anafika pa nkhani Yabaibulo yapoyera pa Mpingo wa Porto Novo, kunali kowonekeratu kwa ofalitsa Aufumu 32 kumeneko kuti anthu ambiri onga nkhosa mu Santo Antão ali ndi ludzu la madzi a chowonadi.
Ntchito yolalikira pa chisumbu cha São Nicolau inayamba zaka zingapo zapitazo pamene mlongo yemwe ndimpainiya wa ku Portugal anachititsa phunziro Labaibulo mwakulemberana makalata ndi banja lina pachisumbupo. Ndiyeno, mu 1978, mpainiya wina mu Portugal analingalira zobwerera ku chisumbu chakwawo, São Nicolau, kukagaŵana chowonadi cha Baibulo ndi nzika zake 15,000. Pamene anachititsa msonkhano wa Baibulo woyamba pachisumbupo, wopezekapo anali munthu mmodzi yekha—iyeyo! Koma Yehova Mulungu anayankha mapemphero amphamphu amene anapereka pamsonkhanowo. Mkati mwa kuchezetsa kwathu, ofalitsa 48 m’mipingo itatu anasangalala kuwona kuti chiwonkhetso cha anthu 335 anafika pamisonkhanoyo.
Msonkhano wadera woyamba pachisumbupo unachitidwa mkati mwa kuchezera kwathu, ndipo tinaloledwa kugwiritsira ntchito malo amaseŵera akumaloko kwaulere. Nduna za tawunilo zinapereka zokuzira mawu ndi zoyendera zaulere. Ofalitsa 19 a mpingo wochezetsawo anapereka malo ogona kwa nthumwi 100 ndipo anakonza chakudya cha opezekapo 208. Mosasamala kanthu za zovuta zambiri zimene abale athu amakumana nazo tsiku ndi tsiku, anapereka chopereka ku Thumba la Nyumba Yaufumu la Sosaite.
Khalidwe labwino la Mboni za Yehova nlodziŵika bwino kunoko, ndipo olemba ntchito ambiri amawafuna pamene antchito akufunika. Mwachitsanzo, mwini wa malo amodzi okha ogulitsa petulo pachisumbupo anafunsa Mboni kuti idzimugwirira ntchito, popeza kuti anafuna munthu wowona mtima. Mbaleyo anati anali nayo kale ntchito koma anati akawona ngati angapeze munthu wina. Mwini wakeyo anaumirira nati, “Kokha ngati ali Mboni yobatizidwa!” Miyezi iŵiri pambuyo pake anauza mbale wathuyo kuti: “Mboni za Yehova ndi anthu okha amene ayenera kusamalira ndalama!”
Malo Oimapo Omalizira—Chisumbu cha Sal
Malo athu oimapo omalizira paulendowu anali chisumbu cha Sal. Dzina lake limatanthauza “mchere,” ndipo limasonyeza mosavuta mtundu wa indasitale yaikulu pachisumbuchi. Kunoko mpingo waung’ono uli ndi ofalitsa 22, amene amagwira ntchito zolimba kubweretsa uthenga Waufumu kwa nzika 6,500. Kunali kosangalatsadi kugaŵana mbiri yabwino ndi anthu apachisumbu ameneŵa, popeza kuti tinaitanidwa kuloŵa m’nyumba pafupifupi panyumba iriyonse ndipo tinakhoza kulankhula ndi ziŵalo zingapo za banjalo.
Ulendo wathu unathera pa chisumbu cha Sal. Linali dalitso lotani nanga kugwira ntchito ndi atumiki okhulupirika a Yehova ameneŵa ku Cape Verde! Tsopano pazisumbu zimenezi pali ofalitsa Ufumu 531, ndipo ndithudi chiŵerengero chimenecho chidzawonjezeka pamene anthu 2,567 amene anafika pa Chikumbutso cha imfa ya Kristu mu 1991 apitiriza kulandira chakudya chauzimu. Ngakhale kuti Mboni za Yehova zambiri kunoko nzosauka mwakuthupi, izo nzolemera ndi zodyetsedwa bwino mwauzimu. Ndipo nzoyamikira chotani nanga kuti Yehova akuchititsa madzi a moyo kutumphuka mochuluka pazisumbu zimenezi ku ulemerero ndi chitamando chake!
[Mapu patsamba 24]
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
CAPE VERDE
SANTO ANTÃO
SÃO VICENTE
SÃO NICOLAU
SANTA LUZIA
SAL
BOA VISTA
MAIO
SÃO TIAGO
FOGO
BRAVA
Praia
Atlantic Ocean